Genesis
15 Zimenezi zitachitika, Yehova analankhula ndi Abulamu mʼmasomphenya kuti: “Usaope+ Abulamu. Ine ndine chishango chako.+ Mphoto yako idzakhala yaikulu kwambiri.”+ 2 Abulamu anayankha kuti: “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, mudzandipatsa chiyani ine? Taonani ndilibe mwana ndipo Eliezere wa ku Damasiko ndi amene adzatenge katundu wanga yense monga cholowa chake.”+ 3 Abulamu ananenanso kuti: “Simunandipatse mwana*+ ndipo mtumiki wanga ndi amene adzatenge katundu wanga yense monga cholowa chake.” 4 Koma Yehova anamuyankha kuti: “Munthu ameneyu sadzatenga katundu wako monga cholowa chake, koma mwana wako ndi amene adzatenge kuti chikhale cholowa chake.”+
5 Kenako Mulungu anauza Abulamu kuti atuluke panja nʼkumuuza kuti: “Kweza maso ako kumwamba, uwerenge nyenyezizo ngati ungathe kuziwerenga.” Anamuuzanso kuti: “Umu ndi mmene mbadwa* zako zidzakhalire.”+ 6 Abulamu anakhulupirira zimene Yehova anamuuza,+ ndipo Mulunguyo anamuona kuti ndi wolungama.+ 7 Anamuuzanso kuti: “Ine ndine Yehova, amene ndinakuchotsa ku Uri, mzinda wa Akasidi, kuti ndidzakupatse dzikoli likhale lako.”+ 8 Ndipo iye anayankha kuti: “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, nditsimikiza bwanji kuti dzikoli ndidzalitengadi nʼkukhala langa?” 9 Iye anauza Abulamu kuti: “Utenge ngʼombe yazaka zitatu yomwe sinaberekepo, mbuzi yaikazi yazaka zitatu, nkhosa yamphongo yazaka zitatu, ndiponso njiwa yaingʼono ndi mwana wa nkhunda.” 10 Choncho iye anatenga zonsezi nʼkuzidula pakati ndipo anaika mbali iliyonse moyangʼanizana ndi inzake, koma mbalamezo sanazidule. 11 Kenako mbalame zodya nyama zinayamba kutera pa nyama zophedwazo. Koma Abulamu ankazithamangitsa.
12 Dzuwa litatsala pangʼono kulowa, Abulamu anagona tulo tofa nato. Kenako mdima wandiweyani komanso woopsa unafika pa iye. 13 Ndiyeno Mulungu anauza Abulamu kuti: “Udziwe ndithu kuti mbadwa* zako zidzakhala alendo mʼdziko la eni ndipo anthu adzazisandutsa akapolo ndi kuzizunza kwa zaka 400.+ 14 Koma mtundu umene adzautumikirewo ndidzauweruza.+ Pambuyo pake, iwo adzachokako ndi katundu wambiri.+ 15 Pamene iweyo, udzamwalira mwamtendere* utakhala ndi moyo wabwino komanso wautali+ ndipo udzaikidwa mʼmanda. 16 Koma mʼbadwo wa 4 wa mbadwa zako ndi umene udzabwerere kuno,+ chifukwa nthawi yoti Aamori alangidwe sinakwane.”*+
17 Dzuwa litalowa komanso mdima utayamba, ngʼanjo yofuka utsi inaonekera ndipo muuni wamoto unadutsa pakati pa nyama zodulidwazo. 18 Pa tsiku limeneli Yehova anachita pangano ndi Abulamu+ kuti: “Dziko ili ndidzalipereka kwa mbadwa* zako,+ kuyambira kumtsinje wa ku Iguputo mpaka kumtsinje waukulu, mtsinje wa Firate.+ 19 Ndidzapereka kwa mbadwa zako dziko la Akeni,+ Akenizi, Akadimoni, 20 Ahiti,+ Aperezi,+ Arefai,+ 21 Aamori, Akanani, Agirigasi ndiponso la Ayebusi.”+