Deuteronomo
25 “Amuna akakangana azipita kwa oweruza,+ oweruzawo azigamula mlanduwo. Wolungama azimuweruza kuti alibe mlandu ndipo woipa azimuweruza kuti ali ndi mlandu.+ 2 Ngati woipayo akuyenera kukwapulidwa,+ woweruza azilamula kuti woipayo amugoneke pansi, ndipo azimukwapula pamaso pa woweruzayo. Azimukwapula zikwapu zogwirizana ndi choipa chimene wachita. 3 Akhoza kumukwapula mpaka zikwapu zokwana 40+ koma zisapitirire pamenepo. Ngati atapitiriza kumukwapula zikwapu zina kuwonjezera pamenepa, mʼbale wakoyo angachititsidwe manyazi pamaso pako.
4 Usamange ngʼombe pakamwa pamene ikupuntha mbewu.”+
5 Ngati amuna apachibale akukhala moyandikana, ndiyeno mmodzi nʼkumwalira asanabereke mwana wamwamuna, mkazi wa womwalirayo asakwatiwe ndi mwamuna wochokera mʼbanja lina. Mlamu wake azipita kwa iye nʼkukamutenga kukhala mkazi wake, ndipo azichita ukwati wa pachilamu.+ 6 Mwana woyamba amene mkaziyo angabereke, azitenga dzina la mwamuna womwalira uja,+ kuti dzina la mʼbale wake lisathe mu Isiraeli.+
7 Ndiye ngati mwamunayo sakufuna kukwatira mkazi wamasiye wa mchimwene wakeyo, mkaziyo azipita kwa akulu pageti nʼkuwauza kuti, ‘Mchimwene wa mwamuna wanga wakana kusunga dzina la mchimwene wake mu Isiraeli. Sanavomereze kuchita ukwati wa pachilamu ndi ine.’ 8 Akulu a mzindawo azimuitana nʼkulankhula naye. Iye akapitiriza kukana nʼkunena kuti, ‘Sindikufuna kukwatira mkazi ameneyu,’ 9 mkazi wamasiyeyo aziyandikira mchimwene wa mwamuna wakeyo akuluwo akuona ndipo azimuvula nsapato+ nʼkumulavulira kumaso nʼkunena kuti, ‘Izi nʼzimene ziyenera kuchitikira munthu amene wakana kumanga nyumba ya mchimwene wake.’ 10 Ndiyeno dzina la banja lake* mu Isiraeli lizidziwika kuti, ‘Nyumba ya amene anavulidwa nsapato uja.’
11 Ngati amuna akumenyana ndipo mkazi wa mmodzi mwa amunawo wabwera kudzalanditsa mwamuna wake mʼmanja mwa amene akumumenya, ndipo mkaziyo watambasula dzanja nʼkugwira maliseche a mwamuna winayo, 12 muzidula dzanja la mkaziyo, ndipo musamumvere chisoni.*
13 Mʼthumba lanu musamakhale miyezo iwiri yosiyana yoyezera kulemera kwa chinthu,+ musamakhale ndi muyezo waukulu ndi wina waungʼono. 14 Mʼnyumba mwanu musamakhale zoyezera ziwiri zosiyana,*+ musamakhale ndi muyezo waukulu komanso muyezo waungʼono. 15 Muzikhala ndi muyezo wolondola ndi woyenera woyezera kulemera kwa chinthu komanso muyezo wolondola ndi woyenera woyezera kuchuluka kwa zinthu, kuti masiku anu achuluke mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.+ 16 Chifukwa munthu aliyense wopanda chilungamo amene amachita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova Mulungu wanu.+
17 Muzikumbukira zimene Aamaleki anakuchitirani panjira pamene munkachoka ku Iguputo.+ 18 Iwo anakumana nanu panjira nʼkupha anthu onse amene ankayenda movutika kumbuyo kwanu. Iwo anachita izi pamene munali olefuka ndi otopa ndipo sanaope Mulungu. 19 Ndiye Yehova Mulungu wanu akadzakupumitsani kwa adani anu onse okuzungulirani, mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti mulitenge kukhala cholowa chanu,+ mudzafafanize dzina la Aamaleki pansi pa thambo.+ Musadzaiwale zimenezi.