Numeri
20 Mʼmwezi woyamba, gulu lonse la Aisiraeli linafika mʼchipululu cha Zini, ndipo anthuwo anakhala ku Kadesi.+ Kumeneko nʼkumene Miriamu+ anafera nʼkuikidwa mʼmanda.
2 Koma anthuwo anasowa madzi pamalopo,+ ndipo anasonkhana nʼkuukira Mose ndi Aroni. 3 Anthuwo anayamba kukangana ndi Mose+ kuti: “Zikanakhala bwino tikanangofera limodzi ndi abale athu aja amene anafa pamaso pa Yehova. 4 Nʼchifukwa chiyani mwabweretsa mpingo wa Yehova kuchipululu kuno kuti ife limodzi ndi ziweto zathu tifere kuno?+ 5 Nʼchifukwa chiyani munatitulutsa mʼdziko la Iguputo nʼkutibweretsa kumalo oipa ano?+ Kuno sikungamere mbewu iliyonse ndipo kulibe mitengo ya nkuyu, mitengo ya mpesa kapena mitengo ya makangaza. Ndi madzi akumwa omwe kulibe.”+ 6 Zitatero Mose ndi Aroni anachoka pamaso pa mpingowo nʼkupita kukhomo la chihema chokumanako. Kumeneko, anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi, ndipo ulemerero wa Yehova unayamba kuonekera kwa iwo.+
7 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 8 “Tenga ndodo ndipo iweyo ndi mʼbale wako Aroni, musonkhanitse gulu lonse la anthuwo. Muuze thanthwe pamaso pawo kuti litulutse madzi. Utulutse madzi mʼthanthweli kuti upatse gululo, kuti limwe limodzi ndi ziweto zawo.”+
9 Choncho Mose anatenga ndodo ija pamaso pa Yehova+ mogwirizana ndi zimene anamulamula. 10 Kenako Mose ndi Aroni anasonkhanitsa mpingo wonse pamodzi patsogolo pa thanthwelo, ndipo Mose anawauza kuti: “Tsopano tamverani anthu opanduka inu! Kodi tikutulutsireni madzi mʼthanthweli?”+ 11 Mose atatero, anakweza dzanja lake nʼkumenya thanthwelo kawiri ndi ndodo yake. Ndiyeno madzi ambiri anayamba kutuluka ndipo gulu lonselo linayamba kumwa madziwo limodzi ndi ziweto zawo.+
12 Pambuyo pake Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: “Chifukwa simunasonyeze chikhulupiriro mwa ine ndipo simunandilemekeze pamaso pa Aisiraeli, simudzalowetsa mpingowu mʼdziko limene ndidzawapatse.”+ 13 Madzi amenewo anatchedwa madzi a ku Meriba,*+ kumene Aisiraeli anakangana ndi Yehova ndipo anawasonyeza kuti iye ndi woyera.
14 Kenako Mose anatumiza anthu kuchokera ku Kadesi kupita kwa mfumu ya Edomu+ kukanena kuti: “Abale anu Aisiraeli+ akuti, ‘Inu mukudziwa bwino za mavuto onse amene takumana nawo. 15 Paja makolo athu anapita ku Iguputo+ ndipo tinakhala kumeneko zaka zambiri.*+ Aiguputowo ankatizunza ifeyo limodzi ndi makolo athu.+ 16 Potsirizira pake, tinalirira Yehova+ ndipo iye anamva kulira kwathu. Iye anatitumizira mngelo+ nʼkutitulutsa mʼdziko la Iguputo. Tsopano tili kuno ku Kadesi, mzinda umene uli mʼmalire a dziko lanu. 17 Chonde mutilole tidutse mʼdziko lanu. Sitidutsa mʼmunda wanu uliwonse, kapena mʼmunda wa mpesa uliwonse. Sitimwa madzi apachitsime chanu chilichonse. Tizingoyenda mu Msewu wa Mfumu, osakhotera kudzanja lamanja kapena lamanzere, mpaka titadutsa mʼdziko lanu.’”+
18 Koma mfumu ya Edomu inawayankha kuti: “Musadzere mʼdziko lathu. Mukadzera, ndibwera ndi lupanga kudzamenyana nanu.” 19 Aisiraeliwo anayankha kuti: “Ife tidzangodutsa mumsewu waukulu, ndipo ngati ifeyo kapena ziweto zathu tingamwe madzi anu, tidzakulipirani.+ Sitikufuna chilichonse ayi, koma kungodutsa mʼdziko lanu basi.”+ 20 Koma iye anakanabe kuti: “Ayi, musadzere mʼdziko lathu.”+ Mfumu ya Edomu itanena zimenezi, inatuluka ndi chigulu cha anthu komanso asilikali amphamvu.* 21 Choncho mfumu ya Edomu inakana kulola Aisiraeli kudzera mʼdziko lake. Zitatero, Aisiraeli analambalala dziko la Edomu.+
22 Gulu lonse la Aisiraeli linanyamuka ku Kadesi kuja nʼkukafika kuphiri la Hora.+ 23 Kenako Yehova anauza Mose ndi Aroni mʼphiri la Hora, mʼmalire a dziko la Edomu kuti: 24 “Aroni aikidwa mʼmanda ngati mmene zinakhalira ndi makolo ake.*+ Iye sadzalowa mʼdziko limene ndidzapatse Aisiraeli chifukwa awirinu munapandukira malangizo anga okhudza madzi a ku Meriba.+ 25 Utenge Aroni ndi mwana wake Eleazara nʼkukwera nawo phiri la Hora. 26 Mʼphirimo, ukamuvule Aroni zovala zake zaunsembe,+ nʼkuveka mwana wake Eleazara+ ndipo Aroni akamwalira kumeneko.”
27 Choncho Mose anachitadi zimene Yehova anamulamula. Iwo anakwera mʼphiri la Hora anthu onsewo akuona. 28 Kumeneko, Mose anavula Aroni zovala zake zaunsembe nʼkuveka mwana wake Eleazara. Pambuyo pake, Aroni anamwalira pamwamba pa phiripo.+ Potsirizira pake, Mose ndi Eleazara anatsika mʼphirimo. 29 Gulu lonse la anthuwo litaona kuti Aroni wamwalira, nyumba yonse ya Isiraeli inalira maliro a Aroni kwa masiku 30.+