2 Samueli
5 Patapita nthawi, mafuko onse a Isiraeli anapita kwa Davide ku Heburoni+ nʼkumuuza kuti: “Ife ndi inu ndife magazi amodzi.*+ 2 Kale, pamene Sauli anali mfumu yathu, inuyo ndi amene munkatsogolera Aisiraeli kunkhondo.*+ Ndipo Yehova anakuuzani kuti, ‘Udzaweta anthu anga Aisiraeli ndipo udzakhala mtsogoleri wa Aisiraeli.’”+ 3 Choncho akulu onse a Isiraeli anabwera kwa mfumu ku Heburoni ndipo Mfumu Davide inachita nawo pangano+ ku Heburoniko pamaso pa Yehova. Kenako iwo anadzoza Davide kuti akhale mfumu ya Isiraeli.+
4 Davide anakhala mfumu ali ndi zaka 30 ndipo analamulira kwa zaka 40.+ 5 Ku Heburoni anakhala mfumu ya Yuda kwa zaka 7 ndi miyezi 6. Ku Yerusalemu+ analamulira Isiraeli yense ndi Yuda kwa zaka 33. 6 Ndiyeno mfumu ndi anthu ake anapita ku Yerusalemu kukamenyana ndi Ayebusi+ amene ankakhala kumeneko. Ayebusi anayamba kunyoza Davide kuti: “Sudzalowa mumzinda uno, chifukwa ngakhale anthu osaona ndi olumala adzakuthamangitsa.” Iwo ankaganiza kuti: ‘Davide sadzalowa mumzinda muno.’+ 7 Koma Davide analanda malo amene anali mumpanda wolimba kwambiri mu Ziyoni, umene panopa ndi Mzinda wa Davide.+ 8 Tsiku limenelo, Davide ananena kuti: “Aliyense wokaukira Ayebusi adutse mʼngalande zamadzi nʼkukapha ‘anthu olumala ndi osaona,’ anthu amene ine Davide ndimadana nawo!” Nʼchifukwa chake pali mawu akuti: “Wosaona ndi wolumala sadzalowa mʼnyumba.” 9 Kenako Davide anayamba kukhala mʼmalo omwe anali mumpanda wolimba kwambiri, ndipo ankadziwika kuti* Mzinda wa Davide. Iye anayamba kumanga malo onsewo kuyambira ku Chimulu cha Dothi*+ mpaka mkati.+ 10 Choncho Davide anapitiriza kukhala wamphamvu+ ndipo Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba anali naye.+
11 Ndiyeno Hiramu+ mfumu ya Turo anatumiza anthu kwa Davide. Anatumizanso matabwa a mkungudza,+ akalipentala komanso anthu oswa miyala yomangira makoma ndipo anayamba kumanga nyumba* ya Davide.+ 12 Davide anadziwa kuti Yehova wachititsa kuti ufumu wake ukhazikike mu Isiraeli,+ komanso kuti ukhale wamphamvu+ chifukwa cha anthu a Mulungu, Aisiraeli.+
13 Davide atachoka ku Heburoni nʼkupita ku Yerusalemu anakwatiranso akazi ena komanso anali ndi akazi apambali+ ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.+ 14 Ana amene Davide anabereka ku Yerusalemu ndi awa: Samuwa, Sobabu, Natani,+ Solomo,+ 15 Ibara, Elisua, Nefegi, Yafiya, 16 Elisama, Eliyada ndi Elifeleti.
17 Afilisiti atamva kuti Davide amudzoza kukhala mfumu ya Isiraeli,+ onse anabwera kudzamufunafuna.+ Davide atamva zimenezi, anapita kumalo ovuta kufikako.+ 18 Kenako Afilisitiwo anafika ndipo anamwazikana mʼchigwa cha Arefai.+ 19 Ndiyeno Davide anafunsira kwa Yehova+ kuti: “Kodi ndipite kukamenyana ndi Afilisitiwa? Kodi muwapereka mʼmanja mwanga?” Yehova anauza Davide kuti: “Pita, Afilisitiwa ndiwapereka ndithu mʼmanja mwako.”+ 20 Choncho Davide anapita ku Baala-perazimu ndipo anapha Afilisiti kumeneko. Atatero anati: “Yehova wayenda patsogolo panga ngati madzi a chigumula nʼkuwononga adani anga.”+ Nʼchifukwa chake malowo anawapatsa dzina lakuti Baala-perazimu.*+ 21 Afilisiti anasiya mafano awo kumeneko ndipo Davide ndi anthu ake anawatenga nʼkuwawononga.
22 Patapita nthawi, Afilisiti aja anabweranso nʼkumwazikana mʼchigwa cha Arefai.+ 23 Davide anafunsira kwa Yehova koma anamuyankha kuti: “Usapite kukakumana nawo. Uwazembere kumbuyo nʼkuwaukira kutsogolo kwa zitsamba za baka.* 24 Ukakamva phokoso la kuguba pamwamba pa zitsamba za baka, ukanyamuke mwamsanga, chifukwa Yehova adzakhala atatsogola kukapha asilikali a Afilisiti.” 25 Davide anachitadi zimene Yehova anamulamula, moti anapha Afilisiti+ kuchokera ku Geba+ mpaka kukafika ku Gezeri.+