Yoswa
10 Adoni-zedeki mfumu ya Yerusalemu anamva zoti Yoswa walanda mzinda wa Ai nʼkuuwononga. Anamva kuti wawononga mzindawo ndi kupha mfumu yake+ ngati mmene anachitira ndi mzinda wa Yeriko ndi mfumu yake.+ Anamvanso kuti anthu a ku Gibiyoni agwirizana za mtendere ndi Aisiraeli+ ndipo akukhala pakati pawo. Atangomva zimenezi, 2 anachita mantha kwambiri+ chifukwa Gibiyoni unali mzinda waukulu ngati mzinda wolamulidwa ndi mfumu. Komanso mzindawo unali waukulu kuposa mzinda wa Ai,+ ndipo amuna onse akumeneko anali asilikali. 3 Choncho Adoni-zedeki mfumu ya ku Yerusalemu anatumiza uthenga kwa Hohamu mfumu ya ku Heburoni,+ Piramu mfumu ya ku Yarimuti, Yafiya mfumu ya ku Lakisi ndi Debiri mfumu ya ku Egiloni.+ Uthengawo unali wakuti: 4 “Bwerani mudzandithandize. Tiyeni tikamenyane ndi Agibiyoni, chifukwa agwirizana ndi Yoswa ndi Aisiraeli.”+ 5 Choncho mafumu 5 a Aamoriwo,+ limodzi ndi magulu awo ankhondo, anasonkhana pamodzi ndipo anakamanga msasa pafupi ndi anthu a ku Gibiyoni nʼcholinga choti amenyane nawo. Mafumuwo anali mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Heburoni, mfumu ya ku Yarimuti, mfumu ya ku Lakisi ndi mfumu ya ku Egiloni.
6 Zitatero, amuna a ku Gibiyoni anatumiza uthenga kwa Yoswa kumsasa ku Giligala,+ kuti: “Bwerani msanga mudzatithandize ndi kutipulumutsa. Mafumu onse a Aamori okhala kudera lamapiri asonkhana kuti amenyane nafe. Musatisiye tokha ife akapolo anu.”+ 7 Choncho Yoswa ananyamuka ku Giligala limodzi ndi amuna onse ankhondo ndiponso asilikali amphamvu.+
8 Ndiyeno Yehova anauza Yoswa kuti: “Usawaope,+ chifukwa ndawapereka mʼmanja mwako.+ Ndipo palibe aliyense amene adzatha kulimbana nawe.”+ 9 Yoswa anayenda usiku wonse kuchokera ku Giligala, ndipo anafika kwa adaniwo modzidzimutsa. 10 Yehova anasokoneza adaniwo pamaso pa Aisiraeli.+ Ndipo Aisiraeli anapha adani ambirimbiri ku Gibiyoni. Anawathamangitsa kulowera kuchitunda cha Beti-horoni ndipo anapitiriza kuwapha mpaka kukafika ku Azeka ndi ku Makeda. 11 Atafika pamalo otsetsereka otchedwa Beti-horoni pothawa Aisiraeli, Yehova anayamba kuwagwetsera matalala akuluakulu mpaka kukafika ku Azeka ndipo adaniwo ankafa. Amene anaphedwa ndi matalalawo anali ambiri kuposa amene Aisiraeli anawapha ndi lupanga.
12 Pa tsiku limene Yehova anapereka Aamori kwa Aisiraeli, mʼpamene Yoswa analankhula ndi Yehova pamaso pa Aisiraeli kuti:
13 Choncho dzuwa linaimadi, ndiponso mwezi sunayende mpaka mtunduwo utalanga adani ake. Kodi sizinalembedwe mʼbuku la Yasari?+ Dzuwa linaima kumwamba pakatikati, ndipo linaimabe choncho pafupifupi maola 24.* 14 Palibe tsiku ngati limeneli, kaya pambuyo pake kapena patsogolo pake, limene Yehova anamvera mawu a munthu mʼnjira imeneyi,+ popeza Yehova anamenyera nkhondo Isiraeli.+
15 Zitatero, Yoswa ndi Aisiraeli onse anabwerera kumsasa ku Giligala.+
16 Koma mafumu 5 aja anathawa nʼkukabisala kuphanga la ku Makeda.+ 17 Ndiyeno Yoswa analandira uthenga wakuti: “Mafumu 5 aja apezeka atabisala kuphanga la ku Makeda.”+ 18 Choncho Yoswa anati: “Gubuduzirani miyala ikuluikulu pakhomo pa phangalo ndipo musankhe amuna oti azilonderapo. 19 Koma enanu musangoima. Thamangitsani adani anu ndipo mukapeza aliyense muzimupha.+ Musawalole kuti akalowe mʼmizinda yawo, chifukwa Yehova Mulungu wanu wawapereka mʼmanja mwanu.”
20 Yoswa ndi Aisiraeli atamaliza kupha adani awo onse, kupatulapo amene anathawa nʼkukalowa mʼmizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri, 21 Aisiraeli onse anabwerera bwinobwino kwa Yoswa kumsasa, ku Makeda. Ndipo palibe munthu amene ananena zamtopola kwa Aisiraeliwo. 22 Ndiyeno Yoswa anati: “Tsegulani phangali munditulutsire mafumu 5 amene ali mmenemowo.” 23 Iwo anatseguladi phangalo nʼkutulutsa mafumu 5 aja: Mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Heburoni, mfumu ya ku Yarimuti, mfumu ya ku Lakisi ndi mfumu ya ku Egiloni.+ 24 Atapita nawo kwa Yoswa, iye anaitana amuna onse a Isiraeli amene anapita naye kunkhondoko nʼkuuza atsogoleri awo kuti: “Bwerani apa muponde kumbuyo kwa makosi a mafumuwa.” Iwo anapita nʼkupondadi kumbuyo kwa makosi a mafumuwo.+ 25 Ndiyeno Yoswa anawauza kuti: “Musaope kapena kuchita mantha.+ Khalani olimba mtima ndipo muchite zinthu mwamphamvu, chifukwa zimenezi ndi zimene Yehova azichitira adani anu onse amene muzimenyana nawo.”+
26 Kenako Yoswa anawapha nʼkuwapachika pamitengo 5, ndipo anakhala pamenepo mpaka madzulo. 27 Dzuwa likulowa, Yoswa analamula kuti awatsitse pamitengoyo+ nʼkuwaponyera mʼphanga limene anabisalamo lija. Kenako anaika miyala ikuluikulu pakhomo la phangalo, ndipo ilipobe mpaka lero.
28 Tsiku limenelo, Yoswa analanda mzinda wa Makeda+ ndipo anapha anthu amumzindawo ndi lupanga. Anapha mfumu ya mzindawo ndi anthu ake onse, ndipo anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka.+ Mfumu ya ku Makeda+ anaichita zofanana ndi zomwe anaichita mfumu ya ku Yeriko.
29 Zitatero, Yoswa ndi Aisiraeli onse amene anali naye anachoka ku Makeda nʼkupita kukamenyana ndi anthu a ku Libina.+ 30 Yehova anaperekanso mzindawo ndi mfumu yake mʼmanja mwa Isiraeli.+ Choncho Aisiraeli anapha anthu onse amumzindawo ndi lupanga, ndipo anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka. Mfumu ya ku Libina anaichita zofanana ndi zomwe anaichita mfumu ya ku Yeriko.+
31 Kenako Yoswa ndi Aisiraeli onse anachoka ku Libina nʼkupita ku Lakisi.+ Atafika anamanga msasa nʼkuyamba kumenyana ndi anthu akumeneko. 32 Yehova anapereka Lakisi mʼmanja mwa Isiraeli, moti analanda mzindawo pa tsiku lachiwiri. Anapha ndi lupanga anthu onse amumzindawo,+ ngati mmene anachitira ku Libina.
33 Zitatero Horamu mfumu ya ku Gezeri+ anapita kukathandiza anthu a ku Lakisi. Koma Yoswa anapha Horamu ndi anthu ake onse, moti sipanatsale wopulumuka.
34 Kenako Yoswa ndi Aisiraeli onse anachoka ku Lakisi nʼkupita ku Egiloni.+ Kumeneko anamanga msasa nʼkuyamba kumenyana ndi anthu amumzindawo. 35 Analanda mzindawo tsiku lomwelo nʼkupha ndi lupanga anthu onse mumzindawo ngati mmene anachitira ku Lakisi.+
36 Kenako Yoswa ndi Aisiraeli onse anachoka ku Egiloni nʼkupita kukamenyana ndi anthu amumzinda wa Heburoni.+ 37 Analanda mzindawo ndipo anapha ndi lupanga mfumu yake, anthu ake onse komanso anthu amʼmidzi yake yonse. Anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka. Choncho anawononga mzindawo ndi aliyense amene anali mmenemo ngati mmene anachitira ku Egiloni.
38 Pomaliza, Yoswa ndi Aisiraeli onse anapita kukamenyana ndi anthu amumzinda wa Debiri.+ 39 Analanda mzindawo ndi midzi yake yonse nʼkugwiranso mfumu yake. Ndiyeno anapha ndi lupanga munthu aliyense amene anali mmenemo+ ndipo anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka.+ Anachitira mzinda wa Debiri ndi mfumu yake zimene anachitira mzinda wa Heburoni komanso mzinda wa Libina ndi mfumu yake.
40 Choncho Yoswa anagonjetsa anthu amʼdera lonse lamapiri, anthu a ku Negebu, a ku Sefela,+ ndi amʼmadera otsetsereka pamodzi ndi mafumu awo onse. Anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka ndipo anapha chamoyo chilichonse*+ mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wa Isiraeli analamula.+ 41 Yoswa anagonjetsa anthuwa kuchokera ku Kadesi-barinea+ mpaka ku Gaza+ ndi dera lonse la Goseni+ mpaka ku Gibiyoni.+ 42 Yoswa anagonjetsa mafumu onsewa nʼkulanda malo awo pa nthawi imodzi, chifukwa Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi amene ankawamenyera nkhondo.+ 43 Kenako Yoswa ndi Aisiraeli onse anabwerera kumsasa ku Giligala.+