Kwa Agalatiya
2 Ndiyeno patapita zaka 14, ndinapitanso ku Yerusalemu ndi Baranaba+ ndipo ndinatenganso Tito.+ 2 Ndinapita kumeneko chifukwa ndinauzidwa mʼmasomphenya kuti ndipiteko. Ndipo abale ndinawafotokozera uthenga wabwino umene ndikuulalikira kwa anthu a mitundu ina. Koma ndinachita zimenezi mwachinsinsi kwa abale odalirika okha pofuna kutsimikizira kuti utumiki wanga sukupita pachabe. 3 Ndipo ngakhale kuti Tito,+ amene ndinali naye limodzi anali Mgiriki, sanakakamizidwe kuti adulidwe.+ 4 Koma nkhani imeneyi inayambika chifukwa cha abale achinyengo amene analowa pakati pathu mwakachetechete+ ndiponso mozemba ngati akazitape, nʼcholinga choti asokoneze ufulu+ umene tikusangalala nawo mogwirizana ndi Khristu Yesu, nʼkutisandutsa akapolo.+ 5 Anthu amenewa sitinawagonjere,+ ngakhale kwa kanthawi kochepa,* kuti inuyo mupitirize kukhala ndi choonadi cha uthenga wabwino.
6 Koma kunena za anthu amene ankaoneka ngati apadera aja,+ kaya anali otani, zilibe kanthu kwa ine, chifukwa Mulungu sayangʼana maonekedwe a munthu, amuna odalirika amenewo sanandiphunzitse chilichonse chatsopano. 7 Koma ataona kuti ndapatsidwa ntchito yolalikira uthenga wabwino kwa anthu osadulidwa,+ mofanana ndi Petulo amene anapatsidwa ntchito yoti akalalikire uthenga wabwino kwa anthu odulidwa, 8 pajatu amene anapatsa Petulo mphamvu kuti akhale mtumwi kwa anthu odulidwa ndi amene anandipatsanso ine mphamvu kuti ndikhale mtumwi kwa anthu a mitundu ina.+ 9 Iwo atazindikira kukoma mtima kwakukulu kumene ndinapatsidwa,+ Yakobo,+ Kefa* ndi Yohane, amene anali ngati zipilala, anagwira chanza ineyo ndi Baranaba+ posonyeza kuti agwirizana ndi zoti ife tipite kwa anthu a mitundu ina ndipo iwo apite kwa anthu odulidwa. 10 Iwo anangotipempha kuti tizikumbukira osauka ndipo ndayesetsa moona mtima kuchita zimenezi.+
11 Koma Kefa*+ atabwera ku Antiokeya,+ ndinamudzudzula* pamasomʼpamaso chifukwa zinali zoonekeratu kuti anachita zolakwika. 12 Chifukwa asanafike anthu ena ochokera kwa Yakobo,+ iye ankadya limodzi ndi anthu a mitundu ina.+ Koma anthuwo atafika, iye anasiya kuchita zimenezi ndipo anadzipatula, chifukwa ankaopa anthu odulidwawo.+ 13 Ayuda enawonso anagwirizana naye pochita zachiphamaso* zimenezi. Ngakhale Baranaba nayenso anachita nawo zachiphamasozi.* 14 Koma nditaona kuti sankachita zinthu mogwirizana ndi choonadi cha uthenga wabwino,+ ndinauza Kefa* pamaso pa onse kuti: “Ngati iweyo, ngakhale kuti ndiwe Myuda, ukukhala ngati anthu a mitundu ina, osati ngati Ayuda, nʼchifukwa chiyani ukufuna kuchititsa anthu a mitundu ina kuti azitsatira chikhalidwe cha Ayuda?”+
15 Ifeyo amene ndi a mtundu wa Chiyuda, osati ochimwa ochokera mwa anthu a mitundu ina, 16 tikudziwa kuti munthu amaonedwa kuti ndi wolungama, osati chifukwa chotsatira chilamulo, koma chifukwa chokhulupirira+ Yesu Khristu basi.+ Choncho ifeyo tikukhulupirira Khristu Yesu kuti tionedwe olungama chifukwa chokhulupirira Khristu, osati chifukwa chotsatira chilamulo. Tachita zimenezi chifukwa palibe munthu amene amaonedwa wolungama chifukwa chotsatira chilamulo.+ 17 Ndiye ngati ife tapezekanso kuti ndife ochimwa pamene tikuyesetsa kuti tiyesedwe olungama kudzera mwa Khristu, kodi ndiye kuti Khristu wakhala mtumiki wa uchimo? Ayi ndithu. 18 Ngati ndikumanganso zinthu zimene ndinagwetsa, ndiye kuti ndikusonyeza kuti ndine wophwanya malamulo. 19 Chifukwa choti ndinkatsatira chilamulo, ndinafa ku chilamulo+ kuti ndikhale moyo nʼkumatumikira Mulungu. 20 Ndinakhomereredwa pamtengo limodzi ndi Khristu.+ Si inenso amene ndikukhala ndi moyo,+ koma Khristu ndi amene ali ndi moyo ndipo ndi wogwirizana ndi ine. Zoonadi, moyo umene ndikukhala tsopano, ndikukhala mokhulupirira Mwana wa Mulungu,+ amene anandikonda nʼkudzipereka yekha chifukwa cha ine.+ 21 Sindikukana* kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu,+ chifukwa ngati munthu amakhala wolungama potsatira chilamulo, ndiye kuti Khristu anangofa pachabe.+