Mika
4 Mʼmasiku otsiriza,
Phiri la nyumba ya Yehova+
Lidzakhazikika pamwamba penipeni pa mapiri akuluakulu,
Ndipo lidzakwezedwa kupitirira mapiri angʼonoangʼono.
Anthu a mitundu yosiyanasiyana adzapita kumeneko.+
2 Anthu ochokera mʼmitundu yosiyanasiyana adzabwera nʼkunena kuti:
“Bwerani, tiyeni tipite kuphiri la Yehova,
Tipite kunyumba ya Mulungu wa Yakobo.+
Iye akatiphunzitsa njira zake,
Ndipo ife tidzayenda mʼnjira zakezo.”
Chifukwa chilamulo,* chidzaphunzitsidwa mu Ziyoni
Ndipo mawu a Yehova adzaphunzitsidwa mu Yerusalemu.
3 Mulungu adzaweruza mitundu yambiri ya anthu,+
Ndipo adzakonza zinthu zolakwika zokhudza anthu ochokera mʼmitundu yamphamvu yakutali.
Iwo adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo,
Ndiponso mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzira mitengo.+
Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake,
Ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.+
4 Aliyense adzakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu,+
Ndipo sipadzakhala wowaopseza,+
Chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena zimenezi.
5 Anthu a mtundu uliwonse adzayenda mʼdzina la mulungu wawo.
Koma ife tidzayenda mʼdzina la Yehova Mulungu+ wathu mpaka kalekale.
6 Yehova wanena kuti, “Pa tsiku limenelo,
Ndidzasonkhanitsa anthu amene ankayenda motsimphina.
Ndidzasonkhanitsanso anthu amene anamwazikana,+
Komanso anthu amene ndinawalanga.
7 Anthu amene ankayenda motsimphina, ndidzawasonkhanitsanso ngati anthu otsala.+
Anthu amene anachotsedwa mʼdziko lawo nʼkupita kutali, ndidzawasandutsa mtundu wamphamvu.+
Ndipo Yehova adzakhala mfumu yawo mʼphiri la Ziyoni,
Kuyambira panopa mpaka kalekale.
8 Koma iwe nsanja ya gulu la nkhosa,
Malo okwera a mwana wamkazi wa Ziyoni,*+
Ulamuliro udzabwerera. Ulamuliro woyamba udzabwerera kwa iwe,+
9 Ndiye nʼchifukwa chiyani ukufuula kwambiri?
10 Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni udzamva ululu woopsa,
Ngati mkazi amene akubereka.
Chifukwa tsopano uchoka mʼtauni nʼkupita kukakhala kumudzi.
Ukafika mpaka ku Babulo,+
Ndipo kumeneko udzapulumutsidwa.+
Kumeneko Yehova adzakuwombola mʼmanja mwa adani ako.+
11 Anthu amitundu yosiyanasiyana adzasonkhana kuti akuukire.
Anthuwo adzanena kuti, ‘Tiyeni timuwononge,
Ndipo maso athu aone zimenezi zikuchitikira Ziyoni.’
12 Koma iwo sakudziwa maganizo a Yehova.
Iwo sakumvetsa cholinga chake.
Chifukwa adzawasonkhanitsa pamalo opunthira mbewu ngati mmene amasonkhanitsira tirigu amene angomumweta kumene.
13 Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, nyamuka upunthe tirigu.+
Chifukwa nyanga zako ndidzazisandutsa chitsulo.
Ziboda zako ndidzazisandutsa kopa.*
Ndipo udzanyenyanyenya mitundu yambiri ya anthu.+
Phindu limene iwo apeza mwachinyengo, udzalipereka kwa Yehova.
Ndipo zinthu zawo udzazipereka kwa Ambuye woona wa dziko lonse lapansi.”+