Mika
3 Ine ndinati: “Tamverani inu atsogoleri a mbadwa za Yakobo
Ndiponso inu olamulira a nyumba ya Isiraeli.+
Kodi simukuyenera kudziwa chilungamo?
2 Koma mumadana ndi zinthu zabwino+ ndipo mumakonda zinthu zoipa.+
Mumasenda khungu la anthu anga nʼkuchotsa mnofu pamafupa awo.+
3 Mumadyanso mnofu wa anthu anga,+
Ndipo mumasenda khungu lawo.
Mumaswa mafupa awo nʼkuwaphwanyaphwanya.+
Ngati zinthu zimene zaphikidwa mumphika* komanso ngati nyama imene ili mumphika.
4 Pa nthawiyo adzafuulira Yehova kuti awathandize,
Koma sadzawayankha.
5 Izi nʼzimene Yehova wanena zomwe zidzachitikire aneneri amene akusocheretsa anthu a mtundu wanga.+
Amene amalengeza kuti ‘Mtendere!’+ kwinaku akuluma ndi mano awo.*+
Koma munthu akapanda kuika chakudya mʼkamwa mwawo, amakonzekera zokamenyana naye:
6 ‘Usiku udzakufikirani,+ koma simudzaona masomphenya.+
Kuzidzakhala mdima, koma inu simudzaloseranso.
Aneneri amenewa dzuwa lidzawalowera.
Ndipo mdima udzawagwera masanasana.+
Onsewa adzaphimba ndevu zawo zapamulomo,*
Chifukwa Mulungu sadzawayankha.’”
8 Koma ine ndapatsidwa mphamvu ndi mzimu wa Yehova.
Ndipo ndine wokonzeka kuchita chilungamo ndiponso kusonyeza mphamvu,
Kuti ndiuze mbadwa za Yakobo za kugalukira kwawo, komanso Isiraeli za tchimo lake.
9 Tamverani izi inu atsogoleri a nyumba ya Yakobo
Komanso inu olamulira a nyumba ya Isiraeli,+
Amene mumadana ndi chilungamo ndiponso mumapotoza zinthu zonse zowongoka,+
10 Inu amene mumapha anthu kuti mumange Ziyoni ndiponso mumachita zinthu zopanda chilungamo kuti mumange Yerusalemu.+
11 Atsogoleri amumzindawo saweruza asanalandire ziphuphu,+
Ansembe ake amaphunzitsa kuti apeze malipiro,+
Ndipo aneneri ake amalosera kuti apeze ndalama.+
Komatu iwo amanena kuti amadalira Yehova ndipo amati:
“Yehovatu ali nafe,+
Ndipo tsoka silidzatigwera.”+