Yoswa
12 Awa ndi mafumu amene Aisiraeli anagonjetsa nʼkulanda madera awo kumʼmawa kwa mtsinje wa Yorodano, kuchokera kuchigwa cha Arinoni+ kukafika kuphiri la Herimoni+ ndi ku Araba konse, chakumʼmawa:+ 2 Sihoni+ mfumu ya Aamori, yemwe ankakhala ku Hesiboni ndipo ankalamulira kuyambira kumzinda wa Aroweli,+ womwe unali mʼmbali mwa chigwa cha Arinoni+ komanso kuyambira pakatikati pa chigwachi, ndi hafu ya Giliyadi mpaka kukafika kuchigwa cha Yaboki, kumalire ndi Aamoni. 3 Ankalamuliranso ku Araba mpaka kunyanja ya Kinereti*+ chakumʼmawa kwa nyanjayi, mpaka kukafika kunyanja ya Araba, yomwe ndi Nyanja Yamchere.* Komanso ankalamulira kumʼmawa, cha ku Beti-yesimoti ndiponso chakumʼmwera, kumunsi kwa Pisiga.+
4 Mfumu ina ndi Ogi+ wa ku Basana yemwe anali mmodzi wa Arefai+ otsala, ndipo ankakhala ku Asitaroti ndi ku Edirei. 5 Ankalamulira kuphiri la Herimoni, ku Saleka ndi ku Basana+ konse, mpaka kukafika kumalire a Agesuri ndi Amaakati.+ Ankalamuliranso hafu ya Giliyadi mpaka kumalire ndi dera limene Sihoni, mfumu ya Hesiboni, ankalamulira.+
6 Mose mtumiki wa Yehova ndi Aisiraeli anagonjetsa mafumuwa.+ Kenako Mose mtumiki wa Yehova anapereka maderawa kwa fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase kuti akhale awo.+
7 Yoswa ndi Aisiraeli anagonjetsa mafumu akudera lakumadzulo kwa mtsinje wa Yorodano, kuchokera ku Baala-gadi+ kuchigwa cha Lebanoni+ mpaka kuphiri la Halaki,+ limene lili moyangʼanizana ndi Seiri.+ Atawagonjetsa, Yoswa anapereka dzikolo kwa mafuko a Isiraeli poligawa mʼmagawomagawo.+ 8 Dzikoli linkaphatikizapo dera lamapiri, dera la Sefela, chigwa cha Araba, malo otsetsereka, chipululu ndi Negebu.+ Limeneli linali dziko la Ahiti, Aamori,+ Akanani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi.+ Mafumu awo anali awa:
9 Mfumu ya Yeriko,+ imodzi. Mfumu ya Ai+ pafupi ndi Beteli, imodzi.
10 Mfumu ya Yerusalemu, imodzi. Mfumu ya Heburoni,+ imodzi.
11 Mfumu ya Yarimuti, imodzi. Mfumu ya Lakisi, imodzi.
12 Mfumu ya Egiloni, imodzi. Mfumu ya Gezeri,+ imodzi.
13 Mfumu ya Debiri,+ imodzi. Mfumu ya Gederi, imodzi.
14 Mfumu ya Horima, imodzi. Mfumu ya Aradi, imodzi.
15 Mfumu ya Libina,+ imodzi. Mfumu ya Adulamu, imodzi.
16 Mfumu ya Makeda,+ imodzi. Mfumu ya Beteli,+ imodzi.
17 Mfumu ya Tapuwa, imodzi. Mfumu ya Heferi, imodzi.
18 Mfumu ya Afeki, imodzi. Mfumu ya Lasaroni, imodzi.
19 Mfumu ya Madoni, imodzi. Mfumu ya Hazori,+ imodzi.
20 Mfumu ya Simironi-meroni, imodzi. Mfumu ya Akasafu, imodzi.
21 Mfumu ya Taanaki, imodzi. Mfumu ya Megido, imodzi.
22 Mfumu ya Kadesi, imodzi. Mfumu ya Yokineamu+ ku Karimeli, imodzi.
23 Mfumu ya Dori kumapiri a Dori,+ imodzi. Mfumu ya Goimu ku Giligala, imodzi.
24 Mfumu ya Tiriza, imodzi. Mafumu onse analipo 31.