Hoseya
Ndipo mvetserani inu a mʼnyumba ya Isiraeli.
Inunso a mʼnyumba ya mfumu mvetserani,
Popeza chiweruzochi chikukhudza inuyo,
Chifukwa mwakhala msampha ku Mizipa
Ndiponso ngati ukonde paphiri la Tabori.+
2 Anthu amene andipandukira apha anthu ambiri,
Ndipo ine ndikuwachenjeza onsewo.
3 Inetu ndimamudziwa bwino Efuraimu,
Ndipo Isiraeli si wobisika kwa ine.
Iwe Efuraimu wachita zachiwerewere,
Ndipo Isiraeli wadziipitsa.+
4 Zochita zawo zikuwalepheretsa kubwerera kwa Mulungu wawo,
Chifukwa iwo ali ndi mtima wachiwerewere+
Ndipo akana kuzindikira kuti ine Yehova ndine Mulungu wawo.
5 Kunyada kwa Isiraeli kwakhala umboni womutsutsa,+
Ndipo Isiraeli ndi Efuraimu apunthwa ndi zolakwa zawo.
Nayenso Yuda wapunthwa nawo limodzi.+
6 Iwo anapita kukafunafuna Yehova ali ndi nkhosa ndiponso ngʼombe zawo,
Koma sanamupeze.
Chifukwa anali atawachokera.+
Tsopano mwezi udzawadya* limodzi ndi zinthu zawo.*
8 Lizani lipenga la nyanga ya nkhosa+ ku Gibeya ndi lipenga ku Rama!+
Fuulani mfuu ya nkhondo ku Beti-aveni:+ Tsogola iwe Benjamini!
9 Iwe Efuraimu, udzakhala chinthu choopsa pa tsiku limene udzalangidwe.+
Inetu ndauza mafuko a Isiraeli zinthu zimene zidzawachitikiredi.
10 Akalonga a Yuda ali ngati anthu osuntha malire.+
Ndidzawakhuthulira mkwiyo wanga ngati madzi.
13 Efuraimu ataona matenda ake ndiponso Yuda ataona chilonda chake,
Efuraimu anapita ku Asuri+ komanso anatumiza anthu kwa mfumu yaikulu.
Koma mfumuyo sinathe kukuchiritsani.
Ndipo sinathe kupoletsa chilonda chanu.
14 Ine ndidzakhala ngati mkango wamphamvu kwa Efuraimu,
Ndiponso ngati mkango wamphamvu kwa anthu a mʼnyumba ya Yuda.
15 Kenako ndidzabwerera kumalo anga mpaka iwo atakumana ndi zotsatira za zolakwa zawo,
Ndipo adzayamba kundifunafuna kuti ndiwakomere mtima.+
Akadzakumana ndi mavuto, adzandifuna.”+