Kalata Yopita kwa Aheberi
9 Pangano loyamba lija linali ndi malamulo ake a utumiki wopatulika ndiponso malo ake oyera+ apadziko lapansi. 2 Chifukwa panamangidwa chipinda choyamba cha chihema ndipo mʼchipindamo munali choikapo nyale,+ tebulo ndi mikate yoonetsa kwa Mulungu,*+ ndipo chinkatchedwa “Malo Oyera.”+ 3 Koma kuseri kwa nsalu yotchinga yachiwiri+ kunali chipinda chinanso chotchedwa “Malo Oyera Koposa.”+ 4 Mmenemu munali chiwaya chagolide chofukizira nsembe+ ndi likasa la pangano+ lokutidwa ndi golide.+ Mulikasamo munali mtsuko wagolide wokhala ndi mana,+ ndodo ya Aroni imene inaphuka ija+ komanso miyala yosema+ ya pangano. 5 Pamwamba pa likasalo panali akerubi aulemerero amene zithunzithunzi zawo zinkafika pachivundikiro.*+ Koma ino si nthawi yofotokoza zinthu zimenezi mwatsatanetsatane.
6 Zinthu zimenezi zitakonzedwa chonchi, nthawi ndi nthawi ansembe ankalowa mʼchipinda choyamba kukachita mautumiki opatulika.+ 7 Koma mʼchipinda chachiwiricho, mkulu wa ansembe yekha ndi amene ankalowamo kamodzi pa chaka,+ ndipo sankalowa popanda kutenga magazi.+ Magaziwo ankawapereka chifukwa cha iyeyo,+ komanso chifukwa cha machimo a anthu+ amene anawachita mosadziwa. 8 Choncho mzimu woyera umatithandiza kumvetsa bwino kuti njira yolowera kumalo oyera inali isanaonekere pamene chihema choyambacho chinalipo.+ 9 Chihema chimenecho chinali chifaniziro cha nthawi inoyo+ ndipo mogwirizana ndi chifanizirocho, mphatso ndiponso nsembe zimaperekedwa.+ Komabe, zimenezi sizipangitsa munthu amene akuchita utumiki wopatulikayo kukhala ndi chikumbumtima choyera.+ 10 Mʼmalomwake, zimangokhudza zakudya, zakumwa ndi miyambo yosiyanasiyana yoyeretsa zinthu ndi madzi.*+ Zimenezo zinali zofunika mogwirizana ndi malamulo okhudza thupi+ ndipo anazikhazikitsa mpaka nthawi yokonzanso zinthu.
11 Komabe, pamene Khristu anabwera monga mkulu wa ansembe wa zinthu zabwino zimene zakwaniritsidwa, anadzera mʼchihema chachikulu ndi changwiro kwambiri chimene sichinapangidwe ndi manja a anthu, kutanthauza kuti sichipezeka padzikoli. 12 Iye analowa mʼmalo oyera ndi magazi ake,+ osati ndi magazi a mbuzi kapena a ngʼombe zazingʼono zamphongo. Analowa kamodzi kokha mʼmalo oyerawo ndipo anatipulumutsa kwamuyaya.+ 13 Chifukwa ngati magazi a mbuzi ndi a ngʼombe zamphongo+ komanso phulusa la ngʼombe yaikazi,* zimene amawaza nazo anthu odetsedwa, zimawayeretsa mpaka kukhaladi oyera pamaso pa Mulungu,+ 14 kuli bwanji magazi a Khristu,+ amene anadzipereka wopanda chilema kwa Mulungu kudzera mwa mzimu woyera?* Kodi magazi amenewo sadzayeretsa zikumbumtima zathu ku ntchito zakufa,+ kuti tichite utumiki wopatulika kwa Mulungu wamoyo?+
15 Ndiye chifukwa chake iye ndi mkhalapakati wa pangano latsopano+ kuti anthu amene aitanidwa alandire lonjezo la moyo wosatha.+ Izi zatheka chifukwa cha imfa yake, imene inali ngati dipo lowamasula+ ku machimo amene iwo anali nawo mʼpangano lakale lija. 16 Pamene pali pangano, pamafunikanso kuti munthu wochita naye panganoyo afe. 17 Chifukwa pangano limagwira ntchito ngati wina wafapo, popeza siligwira ntchito ngati munthu wochita naye panganoyo ali ndi moyo. 18 Ndiye chifukwa chake ngakhale pangano loyamba lija silinakhazikitsidwe popanda magazi. 19 Mose akauza anthu onsewo lamulo lililonse la mʼChilamulo, ankatenga magazi a ngʼombe zazingʼono zamphongo, magazi a mbuzi ndiponso madzi nʼkuwaza bukulo* ndi anthu onse pogwiritsa ntchito ubweya wa nkhosa wofiira kwambiri ndi timitengo ta hisope. 20 Iye ankawauza kuti: “Awa ndi magazi a pangano limene Mulungu wakulamulani kuti mulisunge.”+ 21 Ndipo anawazanso magazi aja pachihema ndi ziwiya zonse zogwiritsa ntchito pa utumiki wopatulika.+ 22 Mogwirizana ndi Chilamulo, pafupifupi zinthu zonse zimayeretsedwa ndi magazi+ ndipo popanda kukhetsa magazi anthu sangakhululukidwe machimo awo.+
23 Choncho zinali zofunika kuti zifaniziro+ za zinthu zakumwamba ziyeretsedwe mʼnjira imeneyi.+ Koma zinthu zakumwamba zenizenizo zimafunika kuyeretsedwa ndi nsembe zabwino kuposa zimenezi. 24 Khristu sanalowe mʼmalo oyera opangidwa ndi manja a anthu,+ amene ndi chithunzi cha malo enieniwo,+ koma analowa kumwamba kwenikweniko.+ Panopa iye ali kumwamba kuti azionekera pamaso pa Mulungu mʼmalo mwa ifeyo.+ 25 Iye sanapite kumwambako kuti azikadzipereka nsembe mobwerezabwereza, ngati mmene mkulu wa ansembe amachitira. Paja mkulu wa ansembe amalowa mʼmalo oyera chaka ndi chaka+ atatenga magazi a nyama, osati ake. 26 Zikanatero, akanavutika mobwerezabwereza kuyambira pamene dziko linakhazikitsidwa. Koma tsopano iye waonekera kamodzi kokha pamapeto a nthawi* ino kuti achotse uchimo kudzera mu nsembe yake.+ 27 Mofanana ndi zimene zimachitikira anthu kuti amayembekezera kufa kamodzi kokha, kenako nʼkudzalandira chiweruzo, 28 nayenso Khristu anaperekedwa nsembe kamodzi kokha kuti anyamule machimo a anthu ambiri.+ Nthawi yachiwiri imene adzaonekere sadzaonekera nʼcholinga chochotsa uchimo. Ndipo amene adzamuone ndi anthu amene akumuyembekezera ndi mtima wonse kuti awapulumutse.+