1 Mbiri
10 Afilisiti anayamba kumenyana ndi Aisiraeli ndipo asilikali a Isiraeli ankathawa moti ambiri anaphedwa mʼphiri la Giliboa.+ 2 Afilisiti anayandikira kwambiri Sauli ndi ana ake ndipo anapha Yonatani, Abinadabu ndi Malikisuwa,+ ana a Sauli. 3 Nkhondo inamukulira kwambiri Sauli, moti kenako oponya mivi ndi uta anamupeza nʼkumuvulaza.+ 4 Kenako Sauli anauza womunyamulira zida kuti: “Solola lupanga lako undibaye kuti anthu osadulidwawa asandipeze nʼkundipha mwankhanza.”+ Koma womunyamulira zidayo sankafuna chifukwa ankachita mantha kwambiri. Choncho Sauli anatenga lupanga lake nʼkuligwera.+ 5 Womunyamulira zidayo ataona kuti Sauli wafa, nayenso anagwera lupanga lake nʼkufa. 6 Choncho Sauli ndi ana ake atatu anafa ndipo anthu onse amʼnyumba yake anafera limodzi.+ 7 Aisiraeli onse amene anali mʼchigwa ataona kuti aliyense wathawa komanso Sauli ndi ana ake afa, anayamba kuthawa mʼmizinda yawo. Kenako Afilisiti anabwera nʼkuyamba kukhala mʼmizindayo.
8 Tsiku lotsatira, Afilisiti atabwera kudzatenga zinthu za anthu amene anaphedwa, anapeza Sauli ndi ana ake atafa paphiri la Giliboa.+ 9 Iwo anamuvula Sauli zida zake nʼkumudula mutu. Kenako anauza anthu mʼdziko lonse la Afilisiti kuti afalitse uthengawu kwa mafano awo+ ndiponso kwa anthu onse. 10 Kenako anakaika zida zakezo mʼnyumba* ya mulungu wawo ndipo mutu wake anaumangirira kunyumba ya Dagoni.+
11 Anthu onse a ku Yabesi+ ku Giliyadi anamva zonse zimene Afilisiti anamuchita Sauli.+ 12 Ndiyeno asilikali onse anapita kukanyamula mtembo wa Sauli ndi mitembo ya ana ake nʼkupita nayo ku Yabesi. Atatero anakwirira mafupa a anthuwo pansi pa mtengo waukulu ku Yabesiko.+ Kenako anasala kudya masiku 7.
13 Choncho Sauli anafa chifukwa chakuti anasonyeza kuti ndi wosakhulupirika pamaso pa Yehova. Iye sanamvere mawu a Yehova+ komanso anapita kukafunsa kwa wolankhula ndi mizimu+ 14 mʼmalo mofunsa kwa Yehova. Choncho iye anamupha nʼkupereka ufumuwo kwa Davide mwana wa Jese.+