2 Mafumu
23 Choncho mfumuyo inatumiza uthenga ndipo anasonkhanitsa akulu onse a ku Yuda ndi ku Yerusalemu.+ 2 Ndiyeno mfumuyo inapita kunyumba ya Yehova pamodzi ndi amuna onse a ku Yuda, anthu onse okhala ku Yerusalemu, ansembe, aneneri ndi anthu onse kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu. Mfumuyo inayamba kuwawerengera mawu onse amʼbuku+ la pangano+ limene linapezeka mʼnyumba ya Yehova.+ 3 Mfumuyo inaima pafupi ndi chipilala ndipo inachita* pangano pamaso pa Yehova,+ kuti idzatsatira Yehova ndiponso kusunga malamulo ake ndi zikumbutso zake. Idzachita zimenezi ndi mtima wonse ndi moyo wonse potsatira mawu a pangano olembedwa mʼbukulo. Ndipo anthu onsewo anavomereza panganolo.+
4 Kenako mfumuyo inalamula Hilikiya+ mkulu wa ansembe, ansembe ena ndiponso alonda apakhomo kuti atulutse mʼkachisi wa Yehova ziwiya zonse zimene anapangira Baala, mzati wopatulika*+ ndi gulu lonse la zinthu zakuthambo. Itatero, inakazitentha kunja kwa Yerusalemu pamalo otsetsereka a ku Kidironi ndipo phulusa lake inapita nalo ku Beteli.+ 5 Mfumuyo inachotsa ntchito ansembe a milungu yachilendo amene mafumu a Yuda anawaika kuti azipereka nsembe zautsi pamalo okwezeka mʼmizinda ya Yuda ndi malo ozungulira Yerusalemu. Inachotsanso ntchito ansembe opereka nsembe zautsi kwa Baala, kwa dzuwa, kwa mwezi, kwa magulu a nyenyezi ndiponso kwa gulu lonse la zinthu zakuthambo.+ 6 Mfumuyo inatulutsa mzati* wopatulika+ umene unali mʼnyumba ya Yehova ndipo inapita nawo kuchigwa cha Kidironi kunja kwa mzinda wa Yerusalemu nʼkukautentha.+ Itatero, inauperapera nʼkuwaza fumbi lake pamanda a anthu wamba.+ 7 Inagwetsanso nyumba za mahule aamuna apakachisi+ zimene zinali mʼnyumba ya Yehova mmene akazi ankalukiramo matenti a akachisi a mzati wopatulika.*
8 Kenako inaitanitsa ansembe onse kuchokera mʼmizinda ya Yuda. Ndipo malo okwezeka amene ansembewo ankaperekako nsembe yautsi, kuyambira ku Geba+ mpaka ku Beere-seba,+ inawachititsa kuti akhale osayenera kulambirako. Inagwetsanso malo okwezeka a pageti amene anali pakhomo lapageti la Yoswa mkulu wa mzindawo. Getilo linali mbali ya kumanzere munthu akamalowa pageti la mzindawo. 9 Ansembe a malo okwezekawo sankatumikira kuguwa lansembe la Yehova ku Yerusalemu.+ Koma ankadya mikate yopanda zofufumitsa limodzi ndi abale awo. 10 Mfumuyo inachititsanso kuti ku Tofeti,+ mʼChigwa cha Ana a Hinomu,*+ kukhale kosayenera kulambirako. Inachita zimenezi kuti munthu aliyense asamawotcheko* mwana wake wamwamuna kapena wamkazi pomupereka kwa Moleki.+ 11 Komanso inaletsa mahatchi amene mafumu a Yuda anawapereka kwa dzuwa kuti asamalowenso mʼnyumba ya Yehova kudzera mʼchipinda chodyera cha Natani-meleki, nduna yapanyumba ya mfumu, chimene chinali pakhonde. Inatenthanso pamoto magaleta a dzuwa.+ 12 Mfumuyo inagumulanso maguwa ansembe amene mafumu a Yuda anamanga padenga+ la chipinda chapamwamba cha Ahazi. Inagumulanso maguwa ansembe amene Manase anamanga pamabwalo awiri a nyumba ya Yehova.+ Kenako inawaperapera ndipo fumbi lake inakaliwaza kuchigwa cha Kidironi. 13 Komanso inachititsa kuti malo okwezeka akutsogolo kwa Yerusalemu omwe anali kumʼmwera* kwa Phiri Lachiwonongeko,* amene Solomo mfumu ya Isiraeli inamangira Asitoreti mulungu wamkazi wonyansa wa Asidoni, Kemosi mulungu wonyansa wa Amowabu ndi Milikomu+ mulungu wonyansa wa Aamoni,+ akhale osayenera kulambirako. 14 Inaphwanyaphwanya zipilala zopatulika ndipo inagwetsanso mizati* yopatulika.+ Pamalo pamene panali zimenezi inadzazapo mafupa a anthu. 15 Komanso mfumuyo inagumula guwa lansembe limene linali ku Beteli ndi malo okwezeka amene Yerobowamu mwana wa Nebati anamanga omwe anachititsa kuti Aisiraeli achimwe.+ Itagwetsa guwa lansembelo komanso malo okwezeka, inatentha malo okwezekawo nʼkuwaperapera mpaka kusanduka fumbi kenako inatenthanso mzati* wopatulika.+
16 Yosiya atatembenuka nʼkuona manda amene anali paphiri, anauza anthu kuti akatenge mafupa mʼmandawo ndipo anawatentha paguwa lansembelo. Anachititsa guwalo kukhala losayenera kulambirapo, mogwirizana ndi mawu a Yehova amene munthu wa Mulungu woona uja ananena, yemwe analosera kuti zimenezi zidzachitika.+ 17 Kenako iye anati: “Kodi chipilala chimene ndikuchiona apocho nʼcha chiyani?” Amuna amumzindawo anamuyankha kuti: “Ndi manda a munthu wa Mulungu woona amene anachokera ku Yuda,+ yemwe analosera zinthu zotsutsa guwa lansembe la ku Beteli, zimene mwachitazi.” 18 Iye anati: “Musakhudze mafupa ake. Asiyeni choncho.” Ndipo iwo sanakhudzedi mafupa akewo komanso mafupa a mneneri amene anachokera ku Samariya.+
19 Yosiya anachotsanso akachisi onse a mʼmalo okwezeka amene anali mʼmizinda ya ku Samariya,+ omwe mafumu a Isiraeli anamanga kuti akwiyitse Mulungu. Zimene anachita ndi akachisiwa zinali zofanana ndi zimene anachita ku Beteli.+ 20 Iye anapha ansembe onse a mʼmalo okwezeka nʼkuwapereka nsembe pamaguwa ansembe kumeneko. Kenako anawotcha mafupa a anthu pamaguwa ansembewo.+ Atatero anabwerera ku Yerusalemu.
21 Mfumuyo inalamula anthu onse kuti: “Chitirani Pasika+ Yehova Mulungu wanu, mogwirizana ndi zimene zalembedwa mʼbuku la panganoli.”+ 22 Pasika ngati ameneyu anali asanachitikepo kuyambira mʼmasiku amene oweruza ankaweruza Isiraeli komanso mʼmasiku onse a mafumu a Isiraeli ndi mafumu a Yuda.+ 23 Koma mʼchaka cha 18 cha Mfumu Yosiya, iwo anachitira Yehova Pasika ameneyu ku Yerusalemu.
24 Yosiya anachotsanso anthu olankhula ndi mizimu, olosera zamʼtsogolo,+ zifaniziro za aterafi,*+ mafano onyansa* ndi zonyansa zonse zimene zinali ku Yuda ndi ku Yerusalemu, kuti atsatire mawu a Chilamulo+ amene analembedwa mʼbuku lomwe wansembe Hilikiya analipeza mʼnyumba ya Yehova.+ 25 Iye asanakhale mfumu, panalibe mfumu ina imene inabwerera kwa Yehova ndi mtima wake wonse ndi moyo wake wonse+ ndi mphamvu zake zonse, mogwirizana ndi Chilamulo chonse cha Mose. Ndipo pambuyo pake sipanakhalenso mfumu ina ngati iyeyo.
26 Komabe Yehova sanabweze mkwiyo wake waukulu umene anakwiyira Yuda, chifukwa cha zinthu zonse zonyansa zimene Manase anachita nʼkumukwiyitsa.+ 27 Yehova anati: “Yuda nayenso ndidzamʼchotsa pamaso panga+ ngati mmene ndinachotsera Isiraeli+ ndipo ndidzakana mzinda wa Yerusalemu umene ndinausankha, ndi nyumba imene ndinanena kuti, ‘Dzina langa lizikhala kumeneko.’”+
28 Nkhani zina zokhudza Yosiya ndiponso zonse zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda. 29 Mʼmasiku ake, Farao Neko mfumu ya Iguputo anapita kukakumana ndi mfumu ya Asuri pamtsinje wa Firate ndipo Mfumu Yosiya, anapita kukamenyana ndi Neko. Koma mfumu ya Iguputoyo itaona Yosiya inamupha ku Megido.+ 30 Choncho atumiki ake ananyamula mtembo wake pagaleta kuchokera ku Megido nʼkupita nawo ku Yerusalemu ndipo anakamuika mʼmanda ake. Kenako anthu amʼdzikolo anatenga Yehoahazi mwana wa Yosiya nʼkumudzoza ndiponso kumuveka ufumu mʼmalo mwa bambo ake.+
31 Yehoahazi+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 23 ndipo analamulira miyezi itatu ku Yerusalemu. Mayi ake anali a ku Libina ndipo dzina lawo linali Hamutali+ mwana wa Yeremiya. 32 Iye anayamba kuchita zoipa pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zonse zimene makolo ake akale anachita.+ 33 Farao Neko+ anamanga Yehoahazi ku Ribila+ mʼdziko la Hamati, kuti asalamulirenso ku Yerusalemu. Kenako Farao Neko analamula kuti dzikolo lipereke matalente* 100 a siliva ndi talente imodzi ya golide.+ 34 Komanso Farao Neko anaika Eliyakimu mwana wa Yosiya kukhala mfumu mʼmalo mwa Yosiya bambo ake, nʼkumusintha dzina kuti akhale Yehoyakimu. Atatero anatenga Yehoahazi nʼkupita naye ku Iguputo+ ndipo patapita nthawi anamwalira komweko.+ 35 Yehoyakimu anapereka siliva ndi golide kwa Farao. Koma ankatolera msonkho kwa anthu a mʼdzikolo kuti apereke siliva amene Farao anamulamula. Iye anauza munthu aliyense kuchuluka kwa golide ndi siliva woti azipereka, kuti amupatse Farao Neko.
36 Yehoyakimu+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 25 ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu.+ Mayi ake anali a ku Ruma ndipo dzina lawo linali Zebida mwana wa Pedaya. 37 Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova,+ mogwirizana ndi zonse zimene makolo ake akale anachita.+