Nehemiya
10 Amene anatsimikizira panganoli ndi chidindo chawo+ anali awa:
Nehemiya amene anali bwanamkubwa,* mwana wa Hakaliya,
Zedekiya, 2 Seraya, Azariya, Yeremiya, 3 Pasuri, Amariya, Malikiya, 4 Hatusi, Sebaniya, Maluki, 5 Harimu,+ Meremoti, Obadiya, 6 Danieli,+ Ginetoni, Baruki, 7 Mesulamu, Abiya, Miyamini, 8 Maaziya, Biligai ndi Semaya. Amenewa anali ansembe.
9 Panalinso Alevi awa: Yesuwa, mwana wamwamuna wa Azaniya, Binui wochokera kwa ana a Henadadi, Kadimiyeli+ 10 ndi abale awo awa, Sebaniya, Hodiya, Kelita, Pelaya, Hanani, 11 Mika, Rehobu, Hasabiya, 12 Zakuri, Serebiya,+ Sebaniya, 13 Hodiya, Bani ndiponso Beninu.
14 Panalinso atsogoleri awa: Parosi, Pahati-mowabu,+ Elamu, Zatu, Bani, 15 Buni, Azigadi, Bebai, 16 Adoniya, Bigivai, Adini, 17 Ateri, Hezekiya, Azuri, 18 Hodiya, Hasumu, Bezai, 19 Harifi, Anatoti, Nebai, 20 Magipiasi, Mesulamu, Heziri, 21 Mesezabele, Zadoki, Yaduwa, 22 Pelatiya, Hanani, Anaya, 23 Hoshiya, Hananiya, Hasubu, 24 Halohesi, Pila, Sobeki, 25 Rehumu, Hasabina, Maaseya, 26 Ahiya, Hanani, Anane, 27 Maluki, Harimu ndiponso Bana.
28 Anthu ena onse, ansembe, Alevi, alonda apageti, oimba, atumiki apakachisi* ndiponso aliyense amene anadzipatula kwa anthu amʼmayikowo kuti asunge Chilamulo cha Mulungu woona,+ akazi awo, ana awo aamuna ndi aakazi ndiponso aliyense wodziwa zinthu komanso woti akhoza kumvetsa zimene zikunenedwa, 29 anagwirizana ndi abale awo, anthu otchuka. Iwo analumbira* kuti azitsatira Chilamulo cha Mulungu woona chimene chinaperekedwa kudzera mwa Mose mtumiki wa Mulungu woona komanso kuti azitsatira mosamala malamulo onse, ziweruzo ndi mfundo za Yehova Ambuye wathu. 30 Komanso kuti sitidzapereka ana athu aakazi kwa anthu amʼdzikoli ndiponso sitidzatenga ana awo aakazi nʼkuwapereka kwa ana athu aamuna.+
31 Tinalumbira kuti anthu amʼdzikolo akabwera kudzagulitsa katundu ndi mbewu zamtundu uliwonse* pa tsiku la Sabata,+ sitidzawagula chilichonse pa Sabata kapena pa tsiku lililonse lopatulika.+ Tinalumbiranso kuti sitizilima minda yathu mʼchaka cha 7+ ndipo tizikhululuka ngongole zonse.+
32 Kuwonjezera pamenepo, tinalonjeza kuti chaka chilichonse aliyense azipereka ndalama zasiliva zolemera magalamu 4* kuti akazigwiritse ntchito pa utumiki wapanyumba* ya Mulungu wathu.+ 33 Akazigwiritsenso ntchito pokonza mkate wosanjikiza,*+ nsembe yambewu+ yoperekedwa nthawi zonse, nsembe yopsereza yoperekedwa nthawi zonse pa Masabata+ ndi pa masiku amene mwezi watsopano waoneka,+ madyerero a pa nthawi yoikidwiratu,+ zinthu zopatulika, nsembe yamachimo+ yophimba machimo a Isiraeli komanso pa ntchito zonse zapanyumba ya Mulungu wathu.
34 Komanso tinachita maere okhudza nkhuni zimene ansembe, Alevi ndi anthu ankayenera kubweretsa kunyumba ya Mulungu wathu, mogwirizana ndi nyumba za makolo athu. Ankayenera kuzibweretsa pa nthawi zoikidwiratu, chaka chilichonse kuti aziziyatsa paguwa lansembe la Yehova Mulungu wathu, mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼChilamulo.+ 35 Tinalonjezanso kuti chaka chilichonse tizibweretsa kunyumba ya Yehova zipatso zoyambirira kupsa zamʼdziko lathu komanso za mtengo uliwonse.+ 36 Tizibweretsanso ana athu aamuna oyamba kubadwa ndiponso a ziweto zathu+ mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼChilamulo. Tizibweretsa ana oyamba kubadwa a ngʼombe ndi nkhosa zathu. Tizibweretsa zimenezi kunyumba ya Mulungu wathu, kwa ansembe amene amatumikira mʼnyumba ya Mulungu wathu.+ 37 Komanso tizibweretsa ufa woyambirira wamisere,+ zopereka zathu, zipatso za mtengo uliwonse,+ vinyo watsopano ndi mafuta+ kwa ansembe mʼzipinda zosungira katundu* mʼnyumba ya Mulungu wathu.+ Tifunikanso kubweretsa chakhumi kwa Alevi pa zinthu zochokera mʼdziko lathu+ chifukwa Aleviwo ndi amene amatolera chakhumi kuchokera mʼmizinda yathu yonse ya zaulimi.
38 Wansembe, mwana wamwamuna wa Aroni, azikhala ndi Alevi pamene iwo akutolera chakhumi. Aleviwo azipereka gawo limodzi pa magawo 10 a chakhumicho kunyumba ya Mulungu wathu+ kuzipinda* za nyumba yosungira katundu. 39 Chifukwa Aisiraeli ndi Alevi ayenera kubweretsa zopereka+ zambewu, vinyo watsopano ndi mafuta+ kuzipinda zosungira katundu.* Kumeneku nʼkumene kuli ziwiya zakumalo opatulika, ansembe amene amatumikira, alonda apageti ndiponso oimba. Sitidzanyalanyaza nyumba ya Mulungu wathu.+