Miyambo
19 Ndi bwino kukhala wosauka nʼkumachita zinthu mokhulupirika+
Kusiyana nʼkukhala munthu wopusa nʼkumalankhula mabodza.+
3 Kupusa kwa munthu nʼkumene kumapotoza njira yake,
Ndipo mtima wake umakwiyira Yehova.
4 Chuma chimachititsa kuti munthu akhale ndi anzake ambiri,
Koma munthu wosauka amasiyidwa ngakhale ndi mnzake weniweni.+
5 Mboni yonama sidzalephera kulangidwa,+
Ndipo amene amalankhula zabodza zokhazokha sadzathawa chilango.+
6 Anthu ambiri amafuna kukondedwa ndi munthu wolemekezeka,*
Ndipo aliyense ndi bwenzi la munthu wopereka mphatso.
Iye amawachonderera kuti amuthandize, koma palibe amene amamuyankha.
8 Munthu amene wapeza nzeru amakonda moyo wake.+
Amene amaona kuti kukhala wozindikira nʼkofunika kwambiri zinthu zidzamuyendera bwino.+
10 Nʼzosayenera kuti munthu wopusa azikhala moyo wawofuwofu.
Chimodzimodzinso kuti munthu wantchito alamulire anthu audindo!+
11 Kuzindikira kumachititsa kuti munthu abweze mkwiyo wake,+
Ndipo kunyalanyaza cholakwa kumamʼchititsa kukhala wokongola.+
12 Mkwiyo wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango wamphamvu,+
Koma kukoma mtima kwake kuli ngati mame pazomera.
13 Mwana wopusa amabweretsa mavuto kwa bambo ake,+
Ndipo mkazi wolongolola* ali ngati denga limene silisiya kudontha.+
14 Nyumba komanso chuma ndi cholowa chochokera kwa makolo,
Koma mkazi wanzeru amachokera kwa Yehova.+
19 Munthu wosachedwa kupsa mtima ayenera kulipira,
Chifukwa ukayesa kumʼpulumutsa, uzichita zimenezi kawirikawiri.+
21 Munthu amakhala ndi mapulani ambiri mumtima mwake,
Koma zolinga za Yehova nʼzimene zidzakwaniritsidwe.+
22 Chinthu chosiririka mwa munthu ndi chikondi chake chokhulupirika,+
Ndipo ndi bwino kukhala wosauka kusiyana nʼkukhala munthu wonama.
23 Kuopa Yehova kumathandiza munthu kuti apeze moyo.+
Munthu amene amachita zimenezi amagona tulo tokoma ndipo zoipa sizimugwera.+
25 Menya munthu wonyoza+ kuti wosadziwa zinthu achenjere,+
Ndipo dzudzula munthu womvetsa zinthu kuti awonjezere zimene akudziwa.+
26 Munthu amene amazunza bambo ake ndiponso kuthamangitsa mayi ake,
Ndi mwana wochititsa manyazi ndi wonyozetsa.+
27 Mwana wanga ukasiya kumvera malangizo,
Udzasochera nʼkusiya kutsatira mawu anzeru.