Oweruza
4 Ehudi atamwalira, Aisiraeli anayambiranso kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+ 2 Choncho Yehova anawapereka* kwa Yabini mfumu ya ku Kanani,+ amene ankalamulira ku Hazori. Mkulu wa gulu lake lankhondo anali Sisera, ndipo ankakhala ku Haroseti-ha-goimu.+ 3 Aisiraeli anayamba kulirira Yehova+ chifukwa Yabini anawapondereza kwambiri+ kwa zaka 20, ndipo iye anali ndi magaleta ankhondo 900 okhala ndi zitsulo zazitali komanso zakuthwa.+
4 Pa nthawi imeneyo mneneri Debora,+ yemwe anali mkazi wa Lapidoti, anali woweruza wa Isiraeli. 5 Iye ankakhala pansi pa mtengo wake,* wa kanjedza pakati pa mzinda wa Rama+ ndi wa Beteli,+ mʼdera lamapiri la Efuraimu ndipo Aisiraeli ankapita kwa iye kuti akawaweruze. 6 Debora anatumiza uthenga kwa Baraki+ mwana wa Abinowamu, yemwe anali ku Kedesi-nafitali,+ womuuza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli walamula kuti, ‘Tenga amuna 10,000 a fuko la Nafitali ndi la Zebuloni ndipo mukasonkhane paphiri la Tabori. 7 Ine ndidzabweretsa kwa iwe kumtsinje* wa Kisoni,+ Sisera mkulu wa gulu lankhondo la Yabini, pamodzi ndi magaleta ake ankhondo ndi asilikali ake ndipo ndidzamʼpereka mʼmanja mwako.’”+
8 Ndiyeno Baraki anauza Debora kuti: “Ngati ungapite nane, ndipita, koma ngati supita nane, sindipita.” 9 Debora anayankha kuti: “Tipitiradi limodzi. Koma ulemerero sukhala wako pa nkhondo imeneyi, chifukwa Yehova adzapereka Sisera mʼmanja mwa munthu wamkazi.”+ Atatero, Debora ananyamuka nʼkupita ndi Baraki ku Kedesi.+ 10 Baraki anasonkhanitsa amuna 10,000 a fuko la Zebuloni ndi la Nafitali+ ku Kedesi ndipo amunawo anayamba kumutsatira. Debora nayenso anapita nawo.
11 Zinangochitika kuti Hiberi Mkeni+ anasiyana ndi Akeni, ana a Hobabu mpongozi wa Mose+ ndipo anamanga tenti yake pafupi ndi mtengo waukulu ku Zaananimu, ku Kedesi.
12 Ndiyeno kunafika uthenga kwa Sisera wakuti Baraki, mwana wa Abinowamu, wapita kuphiri la Tabori.+ 13 Nthawi yomweyo, Sisera anasonkhanitsa magaleta ake onse ankhondo, magaleta 900 okhala ndi zitsulo zazitali komanso zakuthwa. Anasonkhanitsanso asilikali ake onse kuchokera ku Haroseti-ha-goimu ndipo anapita kumtsinje* wa Kisoni.+ 14 Kenako Debora anauza Baraki kuti: “Nyamuka, chifukwa lero ndi limene Yehova apereke Sisera mʼmanja mwako. Yehova akuyendatu patsogolo pako.” Baraki anatsikadi mʼphiri la Tabori, amuna 10,000 akumʼtsatira. 15 Zitatero Yehova anasokoneza Sisera,+ magaleta ake onse ankhondo komanso asilikali ake onse pamaso pa Baraki. Kenako Sisera anatsika mʼgaleta lake nʼkuyamba kuthawa wapansi. 16 Baraki anathamangitsa magaleta ankhondowo ndi asilikali onsewo mpaka ku Haroseti-ha-goimu. Asilikali onse a Sisera anaphedwa ndi lupanga moti sipanatsale ngakhale mmodzi.+
17 Koma Sisera anathawa wapansi kupita kutenti ya Yaeli,+ mkazi wa Hiberi+ Mkeni, chifukwa panali mtendere pakati pa Yabini+ mfumu ya Hazori ndi banja la Hiberi Mkeni. 18 Ndiyeno Yaeli anatuluka kukachingamira Sisera nʼkumuuza kuti: “Fikani mbuyanga, lowani. Musaope.” Choncho anapita nʼkukalowa mutenti ya Yaeli ndipo anamʼfunditsa bulangete. 19 Kenako Sisera anamuuza kuti: “Ndipatse madzi akumwa, chifukwa ndili ndi ludzu.” Choncho anatsegula thumba lachikopa la mkaka ndi kumʼpatsa kuti amwe.+ Atatero, anamʼfunditsanso. 20 Sisera anauza Yaeli kuti: “Uime pakhomo la tenti, ndipo pakabwera munthu nʼkukufunsa kuti, ‘Kodi pali mwamuna aliyense pano?’ umuuze kuti, ‘Palibe.’”
21 Ndiyeno Yaeli mkazi wa Hiberi anatenga chikhomo cha tenti ndi hamala. Kenako analowa mutentimo, akuyenda monyangʼama.* Apa nʼkuti Sisera ali mʼtulo tofa nato chifukwa anali atatopa kwambiri. Yaeli anakhoma chikhomocho mʼmutu mwa Sisera pafupi ndi khutu. Chikhomocho chinalowa mpaka kufika pansi ndipo anafera pompo.+
22 Zitatero Baraki anatulukira akusakasaka Sisera. Kenako Yaeli anapita kukamuchingamira, ndipo anamuuza kuti: “Bwerani ndikuonetseni munthu amene mukumʼfunafunayo.” Iye anamʼtsatira ndipo anangoona Sisera ali kwala atafa, mʼmutu mwake muli chikhomo pafupi ndi khutu.
23 Choncho pa tsikuli Mulungu anagonjetsa Yabini mfumu ya Kanani, pamaso pa Aisiraeli.+ 24 Ndipo dzanja la Aisiraeli linapitiriza kukula mphamvu pomenyana ndi Yabini mfumu ya Kanani,+ mpaka anapha Yabini mfumu ya Kanani.+