Deuteronomo
24 “Ngati mwamuna wakwatira mkazi koma mkaziyo sakumusangalatsa chifukwa wamupeza ndi vuto linalake, azimulembera kalata yothetsera ukwati+ nʼkumupatsa, ndipo azimuchotsa panyumba pake.+ 2 Akachoka panyumba ya mwamunayo, angathe kupita kukakhala mkazi wa mwamuna wina.+ 3 Ngati mwamuna wachiwiriyo wadana naye* mkaziyo ndipo wamulembera kalata yothetsera ukwati nʼkumupatsa kenako nʼkumuthamangitsa panyumba pake, kapena ngati mwamuna wachiwiriyo, amene anakwatira mkaziyo wamwalira, 4 mwamuna woyamba amene anamuthamangitsa uja sadzaloledwa kumutenganso kuti akhale mkazi wake pambuyo poti waipitsidwa, chifukwa zimenezo ndi zonyansa kwa Yehova. Musamachite machimo amenewa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale cholowa.
5 Mwamuna akakwatira kumene, asamakhale mʼgulu lankhondo, ndiponso asamapatsidwe ntchito iliyonse. Azikhala kunyumba kwa chaka chimodzi osachita zinthu zimenezi kuti asangalatse mkazi wake.+
6 Munthu asamalande mnzake mphero kapena mwala waungʼono woperera ngati chikole cha ngongole,+ chifukwa kutenga zinthu zimenezi kuli ngati kutenga moyo wa munthu ngati chikole.
7 Munthu akapezeka ataba mmodzi mwa abale ake, Aisiraeli, ndipo wamuchitira nkhanza nʼkumugulitsa,+ wakuba munthuyo ayenera kufa.+ Muzichotsa woipayo pakati panu.+
8 Ngati kwabuka matenda a khate,* muzionetsetsa kuti mukuchita zinthu zonse mogwirizana ndi zimene Alevi omwe ndi ansembe akulangizani.+ Muzionetsetsa kuti mukuchita mogwirizana ndi zimene ndinawalamula. 9 Muzikumbukira zimene Yehova Mulungu wanu anachitira Miriamu panjira mutatuluka mʼdziko la Iguputo.+
10 Ngati mwapereka ngongole ya mtundu uliwonse kwa mnzanu,+ musamalowe mʼnyumba yake kukatenga chimene wanena kuti akupatsani kuti chikhale chikole. 11 Muziima panja, ndipo munthu amene munamupatsa ngongoleyo azikubweretserani yekha chikolecho panjapo. 12 Ndipo ngati munthuyo ndi wosauka, musamagone ndi chinthu chake chimene wakupatsani kuti chikhale chikolecho.+ 13 Muzionetsetsa kuti mwamubwezera chikolecho dzuwa likangolowa, kuti azipita kukagona ali ndi chofunda chake.+ Mukatero iye adzakudalitsani, ndipo mudzakhala mutachita chilungamo pamaso pa Yehova Mulungu wanu.
14 Musamabere mwachinyengo waganyu yemwe ndi wovutika ndiponso wosauka, kaya akhale mmodzi wa abale anu kapena mlendo amene akukhala mʼdziko lanu, amene ali mʼmizinda yanu.*+ 15 Muzimupatsa malipiro ake tsiku lomwelo dzuwa lisanalowe,+ chifukwa iye ndi wosauka ndipo akudalira malipiro ake omwewo kuti akhale ndi moyo. Mukapanda kutero adzafuula kwa Yehova chifukwa cha zimene inuyo mwamuchitira ndipo mudzapezeka kuti mwachimwa.+
16 Abambo asamaphedwe chifukwa cha zimene ana awo achita, ndipo ana asamaphedwe chifukwa cha zimene abambo awo achita.+ Munthu aliyense aziphedwa chifukwa cha tchimo lake.+
17 Musamapotoze chiweruzo cha mlandu wa mlendo kapena mlandu wa mwana wamasiye,+ ndipo musamalande chovala cha mkazi wamasiye kuti chikhale chikole.+ 18 Muzikumbukira kuti munali akapolo mʼdziko la Iguputo, ndipo Yehova Mulungu wanu anakuwombolani kumeneko.+ Nʼchifukwa chake ndikukulamulani kuti muzichita zimenezi.
19 Mukaiwala mtolo wa tirigu pokolola mʼmunda mwanu, musamabwerere kukatenga mtolowo. Muzisiyira mlendo wokhala mʼdziko lanu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye.+ Muzichita zimenezi kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa chilichonse chimene mukuchita.+
20 Mukamakwapula mitengo ya maolivi pokolola, musamabwereze kukwapula nthambi zimene mwakwapula kale. Zimene zatsala zizikhala za mlendo wokhala mʼdziko lanu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye.+
21 Mukamakolola mphesa mʼmunda wanu, musamabwerere kukakunkha zotsala. Mphesa zotsalazo zizikhala za mlendo wokhala mʼdziko lanu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye. 22 Muzikumbukira kuti munali akapolo mʼdziko la Iguputo. Nʼchifukwa chake ndikukulamulani kuti muzichita zimenezi.”