Deuteronomo
24 “Mwamuna akatenga mkazi kuti akhale mkazi wake, ndiyeno ngati mkaziyo sanamusangalatse chifukwa wam’peza ndi vuto linalake,+ azimulembera kalata yothetsera ukwati+ ndi kum’patsa m’manja mwake, n’kumuchotsa panyumba pake.+ 2 Pamenepo mkaziyo azituluka m’nyumba ya mwamunayo ndi kukakhala mkazi wa mwamuna wina.+ 3 Mwamuna wachiwiriyu akadana nayenso mkaziyo ndipo wamulembera kalata yothetsera ukwati n’kuiika m’manja mwake ndi kum’chotsa panyumba pake, kapena ngati mwamuna wachiwiriyu amene anam’tenga kukhala mkazi wake wamwalira, 4 mwamuna woyamba amene anam’chotsa uja sadzaloledwa kum’tenganso kuti akhale mkazi wake pambuyo poti waipitsidwa.+ Kuchita zimenezo n’konyansa pamaso pa Yehova, chotero usachimwitse dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa monga cholowa.
5 “Mwamuna akatenga mkazi watsopano,+ sayenera kukhala m’gulu lankhondo, ndiponso asakakamizidwe kuchita china chilichonse. Akhale kunyumba osachita zinthu zimenezi kwa chaka chimodzi kuti asangalatse mkazi amene watenga.+
6 “Munthu asalande mnzake mphero kapena mwala woperera monga chikole.+ Kumulanda zimenezi monga chikole ndiko kumulanda moyo.
7 “Munthu akaba+ mmodzi mwa abale ake, ana a Isiraeli, n’kumuchitira nkhanza ndiponso kum’gulitsa,+ wakuba munthuyo afe ndithu. Muzichotsa woipayo pakati panu.+
8 “Samalani ndi mliri wa khate+ ndi kuonetsetsa kuti mukuchita zonse zimene ansembe achilevi adzakulangizani.+ Muzichita mosamala zonse zimene ndawalamula.+ 9 Muzikumbukira zimene Yehova Mulungu wanu anachitira Miriamu panjira mutatuluka m’dziko la Iguputo.+
10 “Ukakongoza mnzako ngongole ya mtundu wina uliwonse,+ usamalowe m’nyumba yake kukatenga chimene walonjeza kukupatsa monga chikole.+ 11 Uziima panja, ndipo munthu amene wam’kongozayo azibweretsa yekha chikolecho kwa iwe, panjapo. 12 Ngati munthuyo ndi wovutika, usagone ndi chinthu chake chimene wakupatsa monga chikolecho.+ 13 Uzionetsetsa kuti wam’bwezera chikolecho dzuwa likangolowa,+ kuti akagone m’chovala chake.+ Pamenepo adzakudalitsa,+ ndipo udzakhala utachita chilungamo pamaso pa Yehova Mulungu wako.+
14 “Usachitire chinyengo waganyu wovutika ndiponso wosauka n’kumubera, kaya akhale mmodzi wa abale ako kapena mmodzi mwa alendo okhala m’dziko lanu, amene ali m’mizinda yanu.+ 15 Uzim’patsa malipiro ake+ tsiku lililonse, ndipo dzuwa lisalowe usanam’patse malipiro ake chifukwa iye ndi wovutika. Iye akuyembekezera malipiro akewo mwachidwi, ndipo angafuule kwa Yehova chifukwa cha zimene iweyo wam’chitira,+ iwe n’kupezeka kuti wachimwa.+
16 “Abambo asaphedwe chifukwa cha machimo a ana, ndipo ana asaphedwe chifukwa cha machimo a abambo.+ Aliyense aziphedwa chifukwa cha tchimo lake.+
17 “Usapotoze chiweruzo cha mlandu wa mlendo+ kapena mlandu wa mwana wamasiye,*+ ndipo usalande mkazi wamasiye chovala chake monga chikole.+ 18 Uzikumbukira kuti unali kapolo m’dziko la Iguputo, ndipo Yehova Mulungu wako anakuwombola kumeneko.+ N’chifukwa chake ndikukulamula kuti uzichita zimenezi.
19 “Ukaiwala mtolo wa tirigu pokolola m’munda wako,+ usabwerere kukatenga mtolowo. Uzisiyira mlendo wokhala m’dziko lanu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye.+ Uzichita zimenezi kuti Yehova Mulungu wako akudalitse pa chilichonse chimene dzanja lako likuchita.+
20 “Pokolola maolivi mwa kukwapula mitengo yake, usabwerere m’mbuyo kukaona ngati m’nthambi zake muli zipatso zotsala. Zimenezo zikhale za mlendo wokhala m’dziko lanu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye.+
21 “Pokolola mphesa m’munda wako, usabwerere kukakunkha zotsala. Mphesa zotsalazo zikhale za mlendo wokhala m’dziko lanu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye. 22 Uzikumbukira kuti unali kapolo m’dziko la Iguputo.+ N’chifukwa chake ndikukulamula kuti uzichita zimenezi.+