Numeri
15 Yehova analankhulanso ndi Mose kuti: 2 “Lankhula ndi Aisiraeli ndipo uwauze kuti, ‘Mukakafika mʼdziko limene ndikukupatsani kuti muzikakhalamo,+ 3 ndipo mukamakapereka kwa Yehova nsembe yowotcha pamoto, kaya ndi ya ngʼombe kapena ya nkhosa, kuti ikhale nsembe yopsereza,+ kapena nsembe imene mukuipereka chifukwa cha lonjezo lapadera,+ kapena nsembe yaufulu, kapenanso nsembe imene mukupereka pa nthawi ya zikondwerero zanu,+ kuti ikhale kafungo kosangalatsa* kwa Yehova,+ 4 munthu amene akupereka nsembeyo, azikaperekanso kwa Yehova nsembe yambewu ya ufa wosalala+ wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.* Ufawo uzikakhala wothira mafuta okwana gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini.* 5 Muzikaperekanso vinyo kuti akhale nsembe yachakumwa. Azikakhala wokwana gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini. Vinyoyo muzikamupereka limodzi ndi nsembe yopsereza,+ kapena ndi nsembe ya mwana wa nkhosa wamphongo. 6 Komanso popereka nsembe ya nkhosa yamphongo, muzikaipereka limodzi ndi nsembe yambewu yokwana magawo awiri a magawo 10 a ufa wosalala a muyezo wa efa. Ufawo uzikakhala wothira mafuta okwana gawo limodzi mwa magawo atatu a muyezo wa hini. 7 Ndiponso muzikapereka vinyo kuti akhale nsembe yachakumwa. Azikakhala wokwana gawo limodzi mwa magawo atatu a muyezo wa hini, kuti akhale nsembe yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova.
8 Koma ngati mukupereka ngʼombe yamphongo kuti ikhale nsembe yopsereza,+ kapena nsembe imene mukuipereka chifukwa cha lonjezo lapadera,+ kapenanso kuti ikhale nsembe yamgwirizano kwa Yehova,+ 9 munthu amene akuperekayo azikapereka ngʼombe yamphongoyo limodzi ndi nsembe yambewu.+ Nsembe yambewuyo izikakhala yokwana magawo atatu a magawo 10 a ufa wosalala a muyezo wa efa. Ufawo azikauthira mafuta okwana hafu ya muyezo wa hini. 10 Ndiponso muzikapereka vinyo kuti akhale nsembe yachakumwa.+ Vinyoyo azikakhala wokwana hafu ya muyezo wa hini. Akakhale nsembe yowotcha pamoto, yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova. 11 Izi nʼzimene mukuyenera kumakachita popereka ngʼombe yamphongo iliyonse, nkhosa yamphongo iliyonse, mwana wa nkhosa wamphongo aliyense kapena mbuzi iliyonse. 12 Muzikachita zimenezi ndi nyama iliyonse imene mukuipereka nsembe, ngakhale zitachuluka bwanji. 13 Munthu aliyense amene ndi nzika mu Isiraeli azikachita zimenezi popereka nsembe yowotcha pamoto, yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova.
14 Ngati mlendo amene akukhala nanu kapena amene wakhala nanu kwa mibadwomibadwo, akufuna kupereka nsembe yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova, azikachita ngati mmene inu mukuchitira.+ 15 Inu amene ndinu mpingo wa Isiraeli komanso mlendo amene akukhala pakati panu, mukhale ndi malamulo ofanana. Muzitsatira malamulo amenewa mʼmibadwo yanu yonse mpaka kalekale, mlendo komanso inuyo nʼchimodzimodzi pamaso pa Yehova.+ 16 Pakhale malamulo ndi zigamulo zofanana kwa inu ndi kwa alendo amene akukhala nanu.’”
17 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 18 “Lankhula ndi Aisiraeli ndipo uwauze kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukupititsani, 19 muzikapereka chopereka kwa Yehova pa chakudya chilichonse chamʼdzikolo,+ chimene muzikadya. 20 Muzikapereka mikate yozungulira yoboola pakati ya ufa wamisere kuti ikhale chopereka cha zipatso zoyambirira kucha.+ Muzikaipereka ngati mmene mumaperekera chopereka chochokera popunthira mbewu. 21 Muzikapereka kwa Yehova ufa wamisere wa zina mwa zipatso zanu zoyambirira ku mibadwo yanu yonse.
22 Koma mukalakwitsa zinthu nʼkulephera kusunga malamulo onsewa amene Yehova walankhula kudzera mwa Mose, 23 zonse zimene Yehova wakulamulani kudzera mwa Mose, kuchokera pa tsiku limene Yehova analamula mpaka mʼtsogolo mʼmibadwo yanu yonse, 24 ngati mwalakwitsa mosazindikira, ndipo gulu lonselo silinadziwe, gulu lonselo lizikapereka ngʼombe yaingʼono yamphongo kuti ikhale nsembe yopsereza yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova. Muzikapereka nsembeyo limodzi ndi nsembe yake yambewu ndiponso nsembe yake yachakumwa potsatira dongosolo la nthawi zonse.+ Muzikaperekanso mbuzi yaingʼono imodzi kuti ikhale nsembe yamachimo.+ 25 Wansembe azikapereka nsembe yophimba machimo a gulu lonse la Aisiraeli. Akatero, anthuwo adzakhululukidwa+ chifukwa analakwitsa mosazindikira, komanso chifukwa apereka nsembe yopsereza kwa Yehova ndiponso apereka nsembe yamachimo kwa Yehova chifukwa cha zimene analakwitsazo. 26 Gulu lonse la Aisiraeli lidzakhululukidwa limodzi ndi mlendo amene akukhala nawo, chifukwa anthu onsewo analakwitsa zinthu mosazindikira.
27 Munthu aliyense akachimwa mosazindikira, azidzapereka mbuzi yaikazi yosapitirira chaka chimodzi kuti ikhale nsembe yamachimo.+ 28 Wansembe azidzapereka nsembe yophimba tchimo la munthu amene walakwa pochimwira Yehova mosazindikira, ndipo adzakhululukidwa.+ 29 Munthu akachita tchimo mosazindikira,+ padzakhale lamulo lofanana kwa munthu amene ndi nzika mu Isiraeli ndi kwa mlendo wokhala pakati pawo.
30 Koma munthu amene wachita tchimo mwadala,+ kaya akhale nzika kapena mlendo, ndiye kuti wanyoza Yehova ndipo ayenera kuphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu ake. 31 Chifukwa chakuti wanyoza mawu a Yehova komanso waphwanya lamulo lake, munthuyo aziphedwa ndithu.+ Aziyankha mlandu wa tchimo lakelo.’”+
32 Aisiraeli ali mʼchipululumo, tsiku lina anapeza munthu wina akutola nkhuni pa tsiku la Sabata.+ 33 Amene anamupeza akutola nkhuniwo anapita naye kwa Mose ndi Aroni ndiponso kumene kunali gulu lonselo. 34 Iwo anamutsekera+ chifukwa panalibe lamulo lachindunji la zimene ayenera kuchita ndi munthuyo.
35 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Munthuyo aphedwe basi.+ Gulu lonse likamuponye miyala kunja kwa msasa.”+ 36 Choncho gulu lonselo linapita naye kunja kwa msasa kumene linakamuponya miyala mpaka kufa, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
37 Yehova anauzanso Mose kuti: 38 “Lankhula ndi Aisiraeli ndipo uwauze kuti azisokerera ulusi mʼmphepete mwa zovala zawo, ku mibadwo yawo yonse. Azisokereranso chingwe cha buluu pamwamba pa ulusi wa mphepete mwa zovalazo.+ 39 ‘Zovala zanu zizikhala ndi ulusi kuti mukaziona muzikumbukira malamulo onse a Yehova ndi kuwasunga.+ Musamatsatire zilakolako za mitima yanu ndi maso anu, chifukwa nʼzimene zikukupangitsani kuti musakhale okhulupirika kwa ine.*+ 40 Lamulo limeneli likuthandizani kuti muzikumbukira komanso kusunga malamulo anga onse ndiponso kukhala oyera kwa Mulungu wanu.+ 41 Ine ndine Yehova Mulungu wanu,+ amene ndinakutulutsani mʼdziko la Iguputo, kuti ndisonyeze kuti ndine Mulungu wanu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”+