Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira
17 Mmodzi wa angelo 7 amene anali ndi mbale 7 aja,+ anabwera nʼkundiuza kuti: “Bwera, ndikuonetse chiweruzo cha hule lalikulu limene lakhala pamadzi ambiri,+ 2 limene mafumu a dziko lapansi anachita nalo chiwerewere,*+ ndipo linaledzeretsa anthu amene akukhala padziko lapansi ndi vinyo wa chiwerewere* chake.”+
3 Mu mphamvu ya mzimu, mngeloyo ananditengera kuchipululu. Ndipo ndinaona mkazi atakhala pachilombo chofiira kwambiri, chimene chinali ndi mayina onyoza Mulungu paliponse komanso chinali ndi mitu 7 ndi nyanga 10. 4 Mkaziyo anavala zovala zapepo+ ndi zofiira kwambiri ndipo anadzikongoletsa ndi golide, miyala yamtengo wapatali ndiponso ngale.+ Mʼdzanja lake, anali ndi kapu yagolide yodzaza ndi zonyansa ndi zinthu zodetsedwa zokhudzana ndi chiwerewere* chake. 5 Pachipumi pake panalembedwa dzina lachinsinsi lakuti: “Babulo Wamkulu, mayi wa mahule+ ndiponso mayi wa zonyansa zapadziko lapansi.”+ 6 Ndinaona kuti mkaziyo anali ataledzera ndi magazi a oyera ndiponso magazi a mboni za Yesu.+
Nditamuona, ndinadabwa kwambiri. 7 Ndiye mngelo uja anandifunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani ukudabwa? Ndikuuza chinsinsi cha mkazi+ ameneyu komanso cha chilombo chimene wakwerapo, chimene chili ndi mitu 7 ndi nyanga 10:+ 8 Chilombo chimene waona, chinalipo, koma panopa kulibe, komabe chatsala pangʼono kutuluka kuphompho,+ ndipo chipita kuchiwonongeko. Anthu amene akukhala padziko lapansi, amene mayina awo sanalembedwe mumpukutu wa moyo+ kuyambira pamene dziko linakhazikitsidwa, adzadabwa kwambiri akadzaona kuti chilombocho chinalipo, panopa kulibe, koma chidzakhalaponso.
9 Apa mʼpamene pakufunika kuchenjera ndiponso kukhala ndi nzeru: Mitu 7+ ikuimira mapiri 7, amene mkazi uja wakhala pamwamba pake. 10 Palinso mafumu 7. Mafumu 5 agwa, imodzi ilipo, inayo sinafikebe. Koma ikafika, ikuyenera kudzakhala kanthawi kochepa. 11 Ndipo chilombo chimene chinalipo, koma panopa kulibe,+ ndi chimenenso chili mfumu ya 8, koma yatuluka mwa mafumu 7 aja ndipo ikupita kuchiwonongeko.
12 Nyanga 10 zimene unaona zija, zikuimira mafumu 10 amene sanalandirebe ufumu wawo. Koma adzalandira ulamuliro monga mafumu ndipo adzalamulira limodzi ndi chilombo kwa ola limodzi. 13 Mafumuwa ali ndi maganizo ofanana, choncho adzapereka mphamvu zawo ndi ulamuliro wawo kwa chilombocho. 14 Iwo adzamenyana ndi Mwanawankhosa,+ koma chifukwa chakuti iye ndi Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu,+ Mwanawankhosayo adzawagonjetsa.+ Komanso oitanidwa aja, omwe ndi osankhidwa mwapadera ndiponso okhulupirika, nawonso adzagonjetsa naye limodzi.”+
15 Mngelo uja anandiuza kuti: “Madzi amene wawaona aja, pamene hule lija lakhala, akuimira mitundu ya anthu, magulu a anthu, mayiko komanso zilankhulo.+ 16 Nyanga 10+ zimene waziona zija komanso chilombo,+ zidzadana ndi hulelo.+ Zidzatenga zinthu zake zonse nʼkulisiya lamaliseche ndipo zidzadya minofu yake nʼkulipsereza ndi moto.+ 17 Chifukwa Mulungu anaika pulani mʼmitima yawo kuti zichite mogwirizana ndi maganizo ake+ komanso kuti zikwaniritse maganizo awo ofanana aja, popereka ufumu wawo kwa chilombo+ mpaka mawu a Mulungu atakwaniritsidwa. 18 Ndipo mkazi+ amene unamuonayo akuimira mzinda waukulu umene ukulamulira mafumu a dziko lapansi.”