“Ndakupatsani Inu Chitsanzo”
“Mwayenera kukhala aphunzitsi chifukwa cha nyengoyi.”—AHEBRI 5:12.
1. N’chifukwa chiyani mawu a pa Ahebri 5:12 angachititse Mkristu kudzidera nkhaŵa mwachibadwa?
MUKAMAŴERENGA mawu ouziridwa amene ali mu lemba limene latsogolera nkhani ino, kodi mumadzidera nkhaŵa? Ngati ndi choncho, simuli nokha. Ife monga otsatira a Kristu, tikudziŵa kuti tiyenera kuphunzitsa. (Mateyu 28:19, 20) Tikudziŵa kuti malinga ndi nthaŵi imene tikukhala ino, n’kofunika kuti tiziphunzitsa bwino kwambiri. Ndiponso tikudziŵa kuti kuphunzitsa kwathu kungachititse amene tikuwaphunzitsawo kudzakhala ndi moyo kapena kudzafa! (1 Timoteo 4:16) Mpake kuti mwachibadwa tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndikuphunzitsa monga momwe ndinayenera kuchitira? Kodi ndingatani kuti ndiwongolere?’
2, 3. (a) Kodi mphunzitsi wina anati n’chiyani chimene chimachititsa kaphunzitsidwe kukhala kabwino? (b) Kodi Yesu anatipatsa chitsanzo chotani pankhani ya kuphunzitsa?
2 Nkhaŵa imeneyi siyenera kutifooketsa. Tikamangoganiza kuti kuphunzitsa kumafuna luso linalake lapadera basi, tingaone ngati sitingathe kuwongolera. Komatu, chimene chingachititse kaphunzitsidwe kukhala kabwino si luso lapadera koma chinachake chofunika kwambiri kuposa lusolo. Taonani zimene mphunzitsi wina yemwe anaphunzitsa kwa nthaŵi yaitali analemba pa nkhani imeneyi. Anati: “Kaphunzitsidwe kabwino sikadalira luso lapadera, njira zinazake za kaphunzitsidwe kapena kachitidwe kenakake. . . . Chinthu chachikulu chimene chimafunika pophunzitsa n’chikondi.” Iye anali kunena za kuphunzitsa m’masukulu. Komabe, mfundo yakeyi ingagwire ntchito kwambiri makamaka pa kuphunzitsa kumene ife Akristu timachita. Chifukwa chiyani?
3 Yesu Kristu ndiye Chitsanzo chathu pa nkhani yophunzitsa. Iye anauza otsatira ake kuti: “Ndakupatsani inu chitsanzo.” (Yohane 13:15) Apa anali kunena za chitsanzo chake posonyeza kudzichepetsa. Komabe n’zosachita kufunsa kuti chitsanzo chimene Yesu anatipatsa chikuphatikizapo ntchito yake yofunika kwambiri imene anachita pamene anali munthu padziko lapansi. Imeneyi inali ntchito yophunzitsa anthu uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Luka 4:43) Motero, ngati mutafunika kusankha liwu limodzi kuti mufotokozere utumiki wa Yesu, mosakayika mungasankhe liwu lakuti “chikondi,” sichoncho kodi? (Akolose 1:15; 1 Yohane 4:8) Yesu anali kukonda Atate wake wakumwamba, Yehova, kuposa china chilichonse. (Yohane 14:31) Komabe monga mphunzitsi, iye anasonyeza chikondi m’njira zina ziŵiri. Anakonda choonadi chimene anaphunzitsa ndiponso anakonda anthu amene anali kuwaphunzitsa. Tiyeni tione mbali ziŵiri zimenezi za chitsanzo chimene iye anatipatsa.
Kukonda Choonadi cha Mulungu Kuyambira Kale
4. Kodi Yesu anayamba bwanji kukonda zimene Yehova anaphunzitsa?
4 Mmene mphunzitsi amaonera phunziro lake zingachititse kaphunzitsidwe kake kukhala kabwino kapena ayi. Ngati salikonda phunziro lakelo zingaonekere mosavuta ndipo zingachititsenso ophunzirawo kusalikonda phunzirolo. Yesu anali kukonda choonadi cha mtengo wapatali chimene anali kuphunzitsa chonena za Yehova ndi Ufumu Wake. Iye anali kukonda kwambiri choonadi chimenechi. Anayamba kukonda choonadi chimenechi ali wophunzira. Kwa zaka zonse zimene analiko asanakhale munthu, Mwana wobadwa yekha ameneyu anali wophunzira wachidwi. Pa Yesaya 50:4, 5 pali mawu omuyenera akuti: “Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira, kuti ndidziŵe kunena mawu akuchirikiza iye amene ali wolema. Iye andigalamutsa m’mawa ndi m’mawa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira. Ambuye Yehova watsegula khutu langa, ndipo sindinakhala wopanduka ngakhale kubwerera m’mbuyo.”
5, 6. (a) Kodi Yesu ayenera kuti anakumbukira chiyani pa ubatizo wake, ndipo zimenezi zinam’khudza bwanji? (b) Kodi pali kusiyana kotani pakati pa Yesu ndi Satana pa nkhani ya kagwiritsidwe ntchito ka Mawu a Mulungu?
5 Pamene anali kukula monga munthu padziko lapansi, Yesu anapitiriza kukonda nzeru za Mulungu. (Luka 2:52) Ndiyeno, pa nthaŵi ya ubatizo wake anaona chinthu chapadera. Luka 3:21 amati: “Panatseguka pathambo.” Mwachionekere, Yesu anakumbukira nthaŵi imene analiko asanakhale munthu. Zitatero iye anasala kudya kwa masiku 40 kuchipululu. Ayenera kuti anakondwera kwambiri kusinkhasinkha za nthaŵi zambiri zimene Yehova anali kum’phunzitsa ali kumwamba. Komabe posakhalitsa, kukonda kwake choonadi cha Mulungu kunayesedwa.
6 Yesu atatopa ndiponso atamva njala, Satana anamuyesa. Palitu kusiyana kwambiri pakati pa ana a Mulungu aŵiri ameneŵa. Onse anagwira mawu Malemba Achihebri, koma ali ndi maganizo osiyana kotheratu. Satana anapotoza Mawu a Mulungu, kuwagwiritsa ntchito mopanda ulemu pofuna kukwaniritsa zolinga zake zadyera. Kunena zoona, wopanduka ameneyu sanali kulemekeza choonadi cha Mulungu. Mosiyana ndi iyeyo, Yesu anagwira mawu Malemba akuwakonda, kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu mosamala pa mayankho ake onse. Yesu anakhalako nthaŵi yaitali mawu ouziridwawo asanayambe kulembedwa, komabe anali kuwalemekeza. Mawuwo anali mfundo za choonadi cha mtengo wapatali zochokera kwa atate wake wakumwamba. Iye anauza Satana kuti mawu a Yehova amenewo anali ofunika kwambiri kuposa chakudya. (Mateyu 4:1-11) Kunena zoona, Yesu anali kukonda mfundo zonse za choonadi zimene Yehova anam’phunzitsa. Komabe, kodi anasonyeza bwanji chikondi chimenecho monga mphunzitsi?
Kukonda Choonadi Chimene Anaphunzitsa
7. N’chifukwa chiyani Yesu anapeŵa kuphunzitsa maganizo akeake?
7 Nthaŵi zonse Yesu ankaoneka kuti anali kukonda choonadi chimene anaphunzitsa. Komatu, kunali kosavuta kuti akhale ndi maganizo akeake. Iye anali kudziŵa zambiri ndipo anali ndi nzeru zapamwamba. (Akolose 2:3) Komabe, iye anali kukumbutsa omvera ake mobwerezabwereza kuti zimene anali kuphunzitsa zinachokera kwa Atate wake wakumwamba osati za m’mutu mwake. (Yohane 7:16; 8:28; 12:49; 14:10) Ankakonda kwambiri choonadi cha Mulungu moti anapeŵa kuphunzitsa maganizo akeake m’malo mwa choonadi chimenechi.
8. Poyamba utumiki wake, kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani pa kudalira Mawu a Mulungu?
8 Yesu atayamba utumiki wake kwa anthu onse, iye nthaŵi yomweyo anapereka chitsanzo. Taganizani mmene anauzira anthu a Mulungu koyamba kuti iye anali Mesiya wolonjezedwa. Kodi anangopita pa gulu la anthu n’kulengeza kuti iye anali Kristu, ndiyeno n’kuchita zozizwitsa kuti atsimikizire mawu akewo? Ayi. Anapita ku sunagoge, kumene anthu a Mulungu mwachizoloŵezi ankaŵerenga Malemba. Ndiyeno anaŵerenga mofuula ulosi wa Yesaya 61:1, 2 ndi kufotokoza kuti mfundo za choonadi za ulosi zimenezi zikunena za iye. (Luka 4:16-22) Zozizwitsa zambiri zimene anachita zinathandiza kutsimikizira kuti Yehova anali kum’thandiza. Ngakhale zinali choncho, iye anali kudalira Mawu a Mulungu pophunzitsa.
9. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kukonda kwake Mawu a Mulungu mokhulupirika polimbana ndi Afarisi?
9 Pamene anthu achipembedzo otsutsa anakayikira Yesu, iye sanagwiritse ntchito nzeru zake kuti awagonjetse, ngakhale kuti pankhani ngati imeneyi iye akanatha kuwagonjetsa mosavuta. M’malo mwake, iye analola kuti Mawu a Mulungu awatsutse. Mwachitsanzo, taganizani za nkhani ina pamene Afarisi anaimba mlandu Yesu kuti ophunzira ake anaswa lamulo la Sabata pobudula ngala zingapo za tirigu m’munda n’kumadya pamene anali kudutsa. Yesu anayankha kuti: “Kodi simunaŵerenga chimene anachichita Davide, pamene anali ndi njala, ndi iwo amene anali naye?” (Mateyu 12:1-5) Inde, anthu odziona ngati olungama amenewo ayenera kuti anaŵerengapo nkhani youziridwa imeneyi imene ili pa 1 Samueli 21:1-6. Ngati anatero, iwo analephera kuzindikira phunziro lofunika m’nkhani imeneyi. Koma Yesu sanangoŵerenga chabe nkhaniyi. Anasinkhasinkha tanthauzo lake ndipo anatengapo mfundo imene nkhaniyi ikuphunzitsa. Anakonda mfundo zimene Yehova anaphunzitsa kudzera m’ndime imeneyo. Motero, iye anagwiritsa ntchito nkhaniyi pamodzi ndi chitsanzo cha m’Chilamulo cha Mose posonyeza kuti Chilamulo sichinali chokhwimitsa zinthu. Mofananamo, chikondi chokhulupirika cha Yesu chinam’chititsa kukhalira kumbuyo Mawu a Mulungu polimbana ndi zolinga za atsogoleri achipembedzo zopotoza mawuŵa kuti akwaniritse zofuna zawo kapena pofuna kuwasokoneza ndi miyambo ya anthu.
10. Kodi Yesu anakwaniritsa bwanji maulosi onena za kaphunzitsidwe kake?
10 Kukonda choonadi chimene anali kuphunzitsa kunachititsa Yesu kupeŵa kuphunzitsa mooneka ngati anangoloŵeza, motopetsa, kapena mosaganizira amene anali kuwaphunzitsawo. Maulosi ouziridwa ananena kuti Mesiya adzalankhula ndi ‘chisomo pa milomo yake,’ kugwiritsa ntchito “mawu abwino.” (Salmo 45:2; Genesis 49:21) Yesu anakwaniritsa maulosi amenewo mwa kuchititsa uthenga wake kukhala wosangalatsa ndiponso wokhudza mtima. Anagwiritsa ntchito “mawu a chisomo” pamene anali kuphunzitsa choonadi chimene anali kuchikonda. (Luka 4:22) Mosakayika, changu chake chinali kuonekera pa nkhope yake, ndipo maso ake anali kuwala posonyeza kukonda kwake choonadi chimenechi. Ziyenera kuti zinali zosangalatsa kumumvetsera akulankhula, ndipo ndi chitsanzo chabwinotu kwambiri choti titsatire pouza ena zimene taphunzira.
11. N’chifukwa chiyani luso la kaphunzitsidwe la Yesu silinam’chititse kudzitukumula?
11 Kodi kudziŵa kwambiri choonadi kwa Yesu ndi kalankhulidwe kake kogwira mtima kanam’chititsa kuyamba kudzitukumula? Izi n’zimene aphunzitsi aumunthu amachita nthaŵi zambiri. Komabe, kumbukirani kuti Yesu anali ndi nzeru zosonyeza kuti anali kuopa Mulungu. Nzeru zimenezi sizimafuna kuti munthu adzitukumule, chifukwa “nzeru ili ndi odzichepetsa.” (Miyambo 11:2) Koma palinso chinthu china chimene chinachititsa Yesu kusanyada kapena kusadzitukumula.
Yesu Anakonda Anthu Amene Anawaphunzitsa
12. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti sanafune kuti ophunzira ake azimuopa kwambiri?
12 Yesu nthaŵi zonse pamene anali kuphunzitsa anasonyeza kukonda kwambiri anthu. Kaphunzitsidwe kake sikanachitse anthu kudziona ngati opanda pake, mosiyana ndi kaphunzitsidwe ka anthu onyada. (Mlaliki 8:9) Petro ataona chozizwitsa china cha Yesu anadabwa kwambiri ndipo anagwa pa maondo Ake. Koma Yesu sanafune kuti om’tsatira azimuopa mopambanitsa. Ananena mokoma mtima kuti, “Usaope,” ndiyeno anauza Petro za ntchito yochititsa chidwi yopanga ophunzira imene Petroyo adzagwira nawo. (Luka 5:8-10) Yesu anafuna kuti ophunzira akewo azilimbikitsidwa ndi kukonda kwawo choonadi chamtengo wapatali chonena za Mulungu, osati kuopa mphunzitsi wawoyo.
13, 14. Kodi Yesu anamvera chisoni bwanji anthu?
13 Chikondi cha Yesu kwa anthu amene anali kuwaphunzitsa chinaonekeranso pa mmene anali kuwamvera chisoni. “Koma iye, poona makamuwo, anagwidwa m’mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” (Mateyu 9:36) Anawachitira chifundo chifukwa cha mmene anthuwo anali kumvetsera chisoni ndipo zimenezi zinam’chititsa kuwathandiza.
14 Taonaninso mmene Yesu anamvera chisoni nthaŵi ina. Pamene mkazi wina wodwala nthenda ya kukha mwazi anapita kwa iye kudutsa m’chikhamu cha anthu ndi kukhudza chovala chake, anachira mozizwitsa. Yesu anazindikira kuti mphamvu inatuluka m’thupi lake, koma sanaone amene anachiritsidwa. Iye anaunguzaunguza kuti am’peze mkaziyo. Chifukwa chiyani? Anatero osati n’cholinga choti am’dzudzule chifukwa chophwanya Chilamulo kapena malamulo a alembi ndi Afarisi, zimene mkaziyo ayenera kuti ankaopa. M’malo mwake anamuuza kuti: “Mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakupulumutsa; muka mumtendere, nukhale wochira chivutiko chako.” (Marko 5:25-34) Onani mmene mawuwo akusonyezera chisoni. Sanangonena kuti, “Chira.” M’malo mwake, anati: ‘Khala wochira chivutiko chako.’ Marko pano anagwiritsa ntchito liwu limene kwenikweni lingatanthauze “kukwapula,” kumene nthaŵi zambiri kunkachitika pozunza munthu. Motero, Yesu anadziŵa kuti mkaziyo anavutika kwambiri ndi matenda akewo, mwina kuvutika kwadzaoneni m’thupi ndi m’maganizo. Anamumvera chisoni kwambiri.
15, 16. Kodi ndi zochitika ziti za muutumiki wa Yesu zimene zikusonyeza kuti anayang’ana mbali zabwino za anthu?
15 Yesu anasonyezanso kukonda anthu mwa kuyang’ana makhalidwe bwino a anthuwo. Taonani zimene zinachitika atakomana ndi Natanayeli, amene kenako anakhala mtumwi. “Yesu anaona Natanayeli alinkudza kwa Iye, nanena za iye, Onani, Mwisrayeli ndithu, mwa iye mulibe chinyengo!” Yesu anaona mozizwitsa mumtima mwa Natanayeli, n’kudziŵa zambiri za iye. Komatu, Natanayeli sanali wangwiro. Anali ndi zofooka monga mmene tilili ena tonsefe. Ndipotu, atamva za Yesu, iye ananyoza kuti: “Ku Nazarete n’kutha kuchokera kanthu kabwino kodi?” (Yohane 1:45-51) Komabe, pa makhalidwe onse a Natanayeli, Yesu anasankha kuikira mtima pa khalidwe lake labwino, kupanda chinyengo kwake.
16 N’chimodzimodzinso ndi mkulu wa asilikali yemwe ayenera kuti anali Wachikunja, wachiroma, amene anapita kwa Yesu ndi kum’pempha kuti akachiritse kapolo wake amene anali kudwala. Yesu anadziŵa kuti msilikaliyo anali ndi zolakwa zambiri. Mkulu wa asilikali wa nthaŵi imeneyo anali woti mosakayika m’mbuyomo anachita chiwawa chosaneneka, kukhetsa mwazi kwadzaoneni, ndiponso kulambira mafano. Komabe, Yesu anayang’ana mbali yabwino ya munthuyo—chikhulupiriro chake cholimba. (Mateyu 8:5-13) Patapita nthaŵi, Yesu polankhula kwa wochita zoipa amene anapachikidwa pa mtengo wozunzirapo pafupi naye, sanamudzudzule chifukwa cha umbanda umene anachita kale, mmalo mwake anamulimbikitsa ndi chiyembekezo cha zinthu zabwino m’tsogolo. (Luka 23:43) Yesu anadziŵa kuti kumangodzudzula ena mosayenera kuzingowakhumudwitsa. Mosakayika, kuyesetsa kwake kupeza zabwino mwa anthu ena kunalimbikitsa ambiri kuwongolera.
Kufuna ndi Mtima Wonse Kutumikira Anthu
17, 18. Povomera kubwera padziko lapansi, kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anafuna ndi mtima wonse kutumikira ena?
17 Umboni wina waukulu wosonyeza kuti Yesu anali kukonda anthu amene anali kuwaphunzitsa ndiwo kufuna kwake ndi mtima wonse kuwatumikira. Nthaŵi imene analiko asanakhale munthu, Mwana wa Mulungu ameneyu nthaŵi zonse anali kukonda anthu. (Miyambo 8:30, 31) Iye monga “Mawu” kapena wolankhulira Yehova, ayenera kuti anachita zinthu zosiyanasiyana ndi anthu. (Yohane 1:1) Komabe mwa zina, iye “anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe a kapolo,” kusiya malo ake aulemerero kumwamba kuti aphunzitse anthu mwachindunji. (Afilipi 2:7; 2 Akorinto 8:9) Yesu ali padziko lapansi, sanayembekezere kuti anthu azimutumikira. M’malo mwake anati: “Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.” (Mateyu 20:28) Yesu anakwaniritsadi mawu amenewo.
18 Yesu anatumikira modzichepetsa zofuna za anthu amene anali kuwaphunzitsa, kudzipereka ndi mtima wonse m’malo mwawo. Anayendayenda m’Dziko Lolonjezedwa maulendo apansi, kuyenda makilomita ambirimbiri uku akulalikira n’cholinga choti alalikire anthu ambiri. Mosiyana ndi Afarisi ndi alembi onyada, iye anali wodzichepetsa ndiponso wosavuta kulankhula naye. Anthu onse, kaya a maudindo aakulu, asilikali, maloya, akazi, ana, osauka, odwala, ngakhalenso anthu amene anzawo ankawaona ngati osafunika, analankhula naye momasuka ndiponso mopanda mantha. Ngakhale kuti anali wangwiro, Yesu anali munthu ndipo ankatopa ndi kumva njala. Komabe, ngakhale pamene anali atatopa kapena kufuna kupuma kapenanso kukhala poduka mphepo kuti apemphere, iye anaika zofuna za anthu ena patsogolo pa zofuna zake.—Marko 1:35-39.
19. Kodi Yesu anapereka bwanji chitsanzo pochita zinthu ndi ophunzira ake modzichepetsa, moleza mtima, ndiponso mwachifundo?
19 Yesu anafunanso ndi mtima wonse kutumikira ophunzira ake. Anachita zimenezo mwa kuwaphunzitsa mwachifundo ndiponso moleza mtima. Ophunzirawo akamachedwa kumvetsa phunziro lina lofunika, iye sanali kugwa ulesi, kupsa mtima, kapena kuwakalipira. Anali kupezabe njira zatsopano zowathandiza kuti amvetse. Mwachitsanzo, tangoganizani za nthaŵi zambiri zimene ophunzirawo anali kukangana kuti wamkulu ndani pakati pawo. Yesu mobwerezabwereza, mpaka pa usiku woti aphedwa mawa, anali kupeza njira zatsopano zowaphunzitsira kuti azitumikirana modzichepetsa wina ndi mnzake. Pankhani imeneyi ya kudzichepetsa, monganso mmene zilili pankhani zina zonse, mpake kuti Yesu anati: “Ndakupatsani inu chitsanzo.”—Yohane 13:5-15; Mateyu 20:25; Marko 9:34-37.
20. Kodi ndi njira ya kaphunzitsidwe yotani imene inachititsa Yesu kukhala wosiyana ndi Afarisi, ndipo n’chifukwa chiyani njira imeneyi inali yogwira mtima?
20 Onani kuti Yesu sanangowauza ophunzirawo kuti chitsanzocho chinali chakutichakuti; iye ‘anapereka chitsanzocho.’ Anawaphunzitsa mwa kuchita zimene anali kuwaphunzitsazo. Sanawauze mowanyoza mosonyeza kuti iye anali wapamwamba, ngati kuti anadziona kukhala wofunika kwambiri moti sakanachita zimene anali kuwauza ophunzirawo kuti achite. Zimenezo n’zimene Afarisi ankachita. Yesu ananena za iwo kuti: “Iwo amalankhula, koma samachita.” (Mateyu 23:3) Yesu modzichepetsa anasonyeza ophunzira ake tanthauzo lenileni la zimene anali kuphunzitsa mwa kuchita zomwezo iyeyo. N’chifukwa chake, pamene analimbikitsa ophunzira ake kuti azikhala moyo wosalira zambiri, osakonda chuma, iwo sanavutike kuganiza kuti akutanthauzanji. Anali kuona zimene iye anali kunenazo zikuchitika. Anati: “Ankhandwe ali nazo nkhwimba zawo, ndi mbalame za m’mlengalenga zisa zawo, koma Mwana wa munthu alibe potsamira mutu wake.” (Mateyu 8:20) Yesu anatumikira ophunzira ake mwa kuwapatsa chitsanzo modzichepetsa.
21. Kodi tikambirana chiyani m’nkhani yotsatirayi?
21 N’zosachita kufunsa kuti Yesu anali Mphunzitsi wamkulu woposa wina aliyense amene anakhalako. Anthu oona mtima onse amene anamuona ndi kumumva akulankhula, anazindikira kukonda kwake zimene anali kuphunzitsa ndiponso kukonda anthu amene anali kuwaphunzitsa. Ndi mmenenso lerolino tikuonera ife amene tikuphunzira chitsanzo chimene anapereka. Koma kodi tingatani kuti titsanzire chitsanzo chake changwiro? Nkhani yotsatirayi iyankha funso limeneli.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi n’chiyani chingachititse kaphunzitsidwe kukhala kabwino, ndipo ndani anapereka chitsanzo pa nkhani imeneyi?
• Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anakonda choonadi chimene anali kuphunzitsa?
• Kodi Yesu anasonyeza bwanji kukonda anthu amene anali kuwaphunzitsa?
• Kodi ndi zitsanzo ziti zimene zikusonyeza kuti Yesu modzichepetsa anafuna ndi mtima wonse kutumikira amene anali kuwaphunzitsa?
[Chithunzi patsamba 12]
Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankakonda mfundo za m’Mawu a Mulungu?