MUTU 20
‘Mugawane Dzikoli Kuti Likhale Cholowa Chanu’
MFUNDO YAIKULU: Tanthauzo la kugawana dziko
1, 2. (a) Kodi Ezekieli analandira malangizo otani kuchokera kwa Yehova? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?
EZEKIELI anali atangoona masomphenya amene anamupangitsa kuganizira zam’mbuyo, pafupifupi zaka 900 m’masiku a Mose ndi Yoswa. Pa nthawi imeneyo Yehova anauza Mose malire a Dziko Lolonjezedwa ndipo pambuyo pake anauza Yoswa mmene angagawire dzikolo kwa mafuko onse a Isiraeli. (Num. 34:1-15; Yos. 13:7; 22:4, 9) Koma tsopano m’chaka cha 593 B.C.E., Yehova akupereka malangizo kwa Ezekieli ndi Ayuda anzake amene anali ku ukapolo kuti agawenso Dziko Lolonjezedwa kwa mafuko a Isiraeli.—Ezek. 45:1; 47:14; 48:29.
2 Kodi masomphenyawa anali ndi uthenga wotani kwa Ezekieli ndi Ayuda anzake omwe anali ku ukapolo? N’chifukwa chiyani masomphenyawa ali olimbikitsa kwa anthu a Mulungu masiku ano? Kodi masomphenyawa adzakwaniritsidwa m’njira yaikulu m’tsogolo?
Masomphenyawa Anasonyeza Kuti Padzachitika Zinthu 4
3, 4. (a) Kodi masomphenya omaliza a Ezekieli anapatsa anthu omwe anali ku ukapolo mfundo 4 ziti zolimbikitsa? (b) Kodi m’mutu uno tikambirana mfundo yotsimikizirika iti?
3 Masomphenya omaliza amene Ezekieli anaona akupezeka m’machaputala 9 a buku la Ezekieli. (Ezek. 40:1–48:35) Masomphenyawa anatchula mfundo 4 zolimbikitsa kwa Ayuda omwe anali ku ukapolo, zosonyeza kuti mtundu wa Isiraeli udzabwezeretsedwa. Kodi mfundo zake ndi ziti? Mfundo yoyamba, kulambira koyera kudzabwezeretsedwa m’kachisi wa Mulungu. Mfundo yachiwiri, ansembe komanso abusa olungama adzatsogolera mtundu wobwezeretsedwawo. Mfundo yachitatu, anthu onse amene adzabwerere ku Isiraeli adzapatsidwa malo. Ndipo mfundo ya 4, Yehova adzakhala nawo kapena kuti adzayambiranso kukhala pakati pawo.
4 M’Mutu 13 ndi 14 wa bukuli, tinakambirana mmene mfundo zoyambirira ziwiri zokhudza kubwezeretsa kulambira koyera komanso kutsogoleredwa ndi abusa olungama zidzakwaniritsidwire. M’mutu uno tikambirana mfundo yachitatu yomwe ndi lonjezo lakuti anthu adzalandira dziko kuti likhale cholowa chawo. M’mutu wotsatira tidzakambirana lonjezo lakuti Yehova adzayambiranso kukhala ndi anthu ake.—Ezek. 47:13-21; 48:1-7, 23-29.
“Dziko Limeneli . . . Ndikulipereka kwa Inu Kuti Likhale Cholowa Chanu.”
5, 6. (a) M’masomphenya a Ezekieli, kodi ndi gawo liti limene linkafunika kugawidwa? (Onani chithunzi choyambirira.) (b) Kodi cholinga cha masomphenya ogawa dziko chinali chiyani?
5 Werengani Ezekieli 47:14. M’masomphenyawa Yehova anaonetsa Ezekieli dziko limene posachedwapa lifanane ndi “munda wa Edeni.” (Ezek. 36:35) Kenako Yehova ananena kuti: “Limeneli ndi dera limene mudzagawire mafuko 12 a Isiraeli ngati cholowa chawo.” (Ezek. 47:13) “Dera” limene ankayenera kuwagawiralo linali dziko la Isiraeli lobwezeretsedwa, limene Ayuda amene anali ku ukapolowo ankayenera kubwererako. Kenako malinga ndi Ezekieli 47:15-21, Yehova anapitiriza kufotokoza mwatsatanetsatane malire akunja adziko lonselo.
6 Kodi cholinga cha masomphenya amenewa okhudza kugawa dziko chinali chiyani? Kufotokoza malire oyezedwa bwino adzikolo kunatsimikizira Ezekieli komanso Ayuda omwe anali nawo ku ukapolo kuti dziko lawo lokondedwa lidzabwezeretsedwadi. Zimene Yehova anafotokozazi ziyenera kuti zinalimbikitsa kwambiri Ayuda amene anali ku ukapolo. Kodi anthu a Mulungu akale analandiradi dziko limene anapatsidwa ngati cholowa chawo? Inde analandiradi.
7. (a) Kodi n’chiyani chimene chinayamba kuchitika mu 537 B.C.E., ndipo zimatikumbutsa chiyani? (b) Kodi choyamba tikambirana funso liti?
7 Mu 537 B.C.E., patadutsa zaka 56 kuchokera pamene Ezekieli anaona masomphenyawa, anthu ambirimbiri amene anali ku ukapolo anayamba kubwerera ku Isiraeli kuti akatenge dzikolo kukhala lawo. Zinthu zochititsa chidwi zimene zinachitika kalelo zikutikumbutsa zinthu zofanana ndi zimenezi, zomwe zachitika pakati pa anthu Mulungu masiku ano. Tinganene kuti nawonso analandira dziko ngati cholowa chawo. Kodi zimenezi zinatheka bwanji? Yehova analola atumiki ake kulowa m’dziko lauzimu n’kulitenga kuti likhale lawo. Pa chifukwa chimenechi, kubwezeretsedwa kwakale kwa Dziko Lolonjezedwa kungatiphunzitse zambiri zokhudza kubwezeretsedwa kwauzimu kwa anthu a Mulungu masiku ano. Koma tisanakambirane mfundo zimenezi, choyamba tiyeni tikambirane funso lakuti, “N’chifukwa chiyani tinganene kuti paradaiso wauzimu alipodi masiku ano?”
8. (a) Kodi Yehova anachititsa kuti mtundu wa Isiraeli weniweni ulowedwe m’malo ndi ndani? (b) Kodi paradaiso wauzimu ndi chiyani? (c) Kodi paradaiso ameneyu anakhalapo liti ndipo ndi ndani amene akukhala mmenemo?
8 Masomphenya amene Yehova anaonetsa Ezekieli m’mbuyomu, anasonyeza kuti ulosi wokhudza kubwezeretsedwa kwa Aisiraeli udzakwaniritsidwa m’njira yaikulu pambuyo poti ‘mtumiki wake Davide,’ yemwe ndi Yesu Khristu, wayamba kulamulira monga Mfumu. (Ezek. 37:24) Zimenezi zinachitika mu 1914 C.E. Pofika nthawi imeneyi, Aisiraeli omwe anali anthu a Mulungu anali atalowedwa m’malo ndi Isiraeli wauzimu amene ndi Akhristu odzozedwa. (Werengani Mateyu 21:43; 1 Petulo 2:9.) Sikuti Yehova anangochititsa kuti mtundu weniweni wa Aisiraeli ulowedwe m’malo ndi Isiraeli wauzimu koma anachititsanso kuti dziko lenileni la Isiraeli lilowedwe m’malo ndi paradaiso wauzimu. (Yes. 66:8) Monga mmene tinaonera m’Mutu 17 wa bukuli, paradaiso wauzimu ndi malo otetezeka auzimu ndipo m’malo amenewa mumachitika zinthu zambiri. Akhristu odzozedwa amene adakali padziko lapansi akhala akulambira Yehova m’malo amenewa kuyambira mu 1919. (Onani bokosi 9B lakuti, “N’chifukwa Chiyani Tikuti Chinali Chaka cha 1919?”) Pamene nthawi imapita, anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi kapena kuti a “nkhosa zina” nawonso anayamba kukhala m’paradaiso wauzimuyu. (Yoh. 10:16) Ngakhale kuti paradaiso wauzimuyu akupitiriza kukula masiku ano, madalitso ake tidzasangalala nawo mokwanira pambuyo pa Aramagedo.
Kugawa Dziko Mwachilungamo
9. Kodi Yehova anapereka malangizo atsatanetsatane otani okhudza kugawa dziko?
9 Werengani Ezekieli 48:1, 28. Atamaliza kufotokoza malire akunja a dzikolo, Yehova anafotokoza mwatsatanetsatane mmene akuyenera kuligawira. Iye analamula kuti dzikolo aligawe mofanana pakati pa mafuko 12 aja, kuyambira kumpoto kukafika kum’mwera. Analamula kuti ayambe ndi fuko la Dani kumpoto kwenikweni kwa dzikolo, n’kumaliza ndi fuko la Gadi kum’mwera kwenikweni kwa dzikolo. Malo aliwonse amene fuko lililonse linalandira pa mafuko 12 amenewo, anayambira kumalire akum’mawa adzikolo kukafika ku Nyanja Yaikulu kapena kuti nyanja ya Mediterranean komwe ndi kumadzulo.—Ezek. 47:20.
10. Kodi mbali imeneyi ya masomphenya iyenera kuti inawatsimikizira chiyani Ayuda omwe anali ku ukapolo?
10 Kodi mbali imeneyi ya masomphenya iyenera kuti inalimbikitsa bwanji Ayuda amene anali ku ukapolo? Mmene Ezekieli anafotokozera mwatsatanetsatane mmene dzikolo lidzagawidwire, zinathandiza Ayuda omwe anali ku ukapolo kudziwa kuti dzikolo lidzagawidwa mwadongosolo. Kuwonjezera pamenepo, kugawa dzikolo mofanana kwa mafuko onse 12, kunasonyeza kuti aliyense amene adzabwerere kwawo adzalandira cholowa m’dziko limene lidzabwezeretsedwe. Palibe amene adzabwerere kwawo n’kupezeka kuti alibe malo okhala.
11. Kodi tingaphunzire chiyani pa masomphenya a ulosi okhudza kugawa dziko? (Onani bokosi lakuti “Kugawa Dziko.”)
11 Kodi tikuphunzira chiyani m’masomphenyawa zomwe zikutilimbikitsa masiku ano? Dziko Lolonjezedwa lobwezeretsedwa linali ndi malo kumene kunkakhala ansembe, alevi komanso atsogoleri. Koma panalinso malo ena kumene kunkakhala anthu ena onse ochokera m’mafuko 12 aja. (Ezek. 45:4, 5, 7, 8) Mofanana ndi zimenezi, sikuti m’paradaiso wauzimu muli malo a odzozedwa okha amene adakali padziko lapansi komanso a “khamu lalikulu” okha amene akutsogolera, koma mulinso malo a anthu ena onse amene ali m’gulu la khamu lalikulu.a (Chiv. 7:9) Ngakhale zitakhala kuti sitichita zambiri m’gulu la Yehova, tili ndi malo komanso ntchito yofunika kwambiri m’paradaiso wauzimu. Zimenezitu n’zolimbikitsa kwambiri.
Kodi Kusiyana kwa Malangizo Awiriwa Kukutanthauza Chiyani Masiku ano?
12, 13. Kodi Yehova anapereka malangizo osapita m’mbali otani, okhudza kugawira malo mafuko?
12 Malangizo ena amene Yehova anapereka kwa Ezekieli okhudza kugawa dzikolo ayenera kuti anamudabwitsa chifukwa chakuti ankasiyana ndi malangizo amene Mulungu anapereka kwa Mose. Tiyeni tione njira ziwiri zimene malangizowa ankasiyanirana. Kusiyana koyamba kunkakhudza dzikolo ndipo kusiyana kwachiwiri kunkakhudza anthu amene ankakhala m’dzikolo.
13 Kusiyana koyamba kokhudza dzikolo. Mose anauzidwa kuti mafuko omwe anali akuluakulu awapatse malo aakulu kusiyana ndi mafuko ang’onoang’ono. (Num. 26:52-54) Koma m’masomphenya a Ezekieli, Yehova anapereka malangizo osapita m’mbali akuti fuko lililonse lilandire gawo “lofanana ndi la mnzake.” (Ezek. 47:14) Choncho mtunda wochokera kumalire akumpoto a cholowa cha fuko lililonse, kukafika kumalire akumwera, unkayenera kukhala wofanana pa mafuko onse 12 aja. Aisiraeli onse, mosatengera fuko lawo, ankayenera kukhala ndi mwayi wofanana wopeza zinthu zabwino za m’Dziko Lolonjezedwalo.
14. Kodi malangizo a Yehova okhudza alendo anaposa bwanji malangizo amene anapereka m’Chilamulo cha Mose?
14 Kusiyana kwachiwiri kokhudza anthu amene ankakhala m’dzikolo. Chilamulo cha Mose chinkateteza anthu ochokera m’mayiko ena ndipo chinkawalola kuti nawonso azilambira Yehova, koma sankalandira cholowa m’dzikolo. (Lev. 19:33, 34) Koma zimene Yehova akuuza Ezekieli tsopano, zikuposa zimene ananena m’Chilamulo. Yehova akumupatsa malangizo akuti: “Mlendo aliyense muzimupatsa cholowa mʼdera la fuko limene akukhala.” Popereka lamulo limeneli, Yehova anachotsa kusiyana kwakukulu kumene kunalipo pakati pa “nzika za Isiraeli,” ndi alendo amene ankakhala m’dzikolo. (Ezek. 47:22, 23) M’masomphenya a dziko lobwezeretsedwa limene Ezekieli anaona, anthu amene ankakhala m’dzikomo ankachita zinthu zofanana komanso ankalambira limodzi mogwirizana.—Lev. 25:23.
15. Kodi malangizo amene Yehova anapereka okhudza dziko komanso anthu okhala m’dzikomo anatsindika mfundo yotani yokhudza Yehova?
15 Malangizo awiri ochititsa chidwi amene Ezekieli analandira okhudza dziko komanso anthu, ayenera kuti analimbikitsa Ayuda omwe anali ku ukapolo. Iwo ankadziwa kuti Yehova adzawapatsa malo ofanana ndi a anthu ena onse kaya ndi nzika za Isiraeli kapena alendo amene ankalambira Yehova. (Ezara 8:20; Neh. 3:26; 7:6, 25; Yes. 56:3, 8) Malangizo amenewa anatsimikizira mfundo yolimbikitsa komanso yosasintha yakuti, kwa Yehova atumiki ake onse ndi ofanana ndiponso ndi a mtengo wapatali. (Werengani Hagai 2:7.) Masiku ano, kaya tikuyembekezera kudzapita kumwamba kapena kudzakhala padziko lapansi, timakhulupirira mfundo zofanana za choonadi.
16, 17. (a) Kodi tikupindula bwanji pophunzira mfundo zokhudza dziko komanso anthu okhala m’dzikomo? (b) Kodi tidzaphunzira chiyani m’mutu wotsatira?
16 Kodi kukambirana mfundo zimenezi zokhudza dziko komanso anthu okhala m’dzikomo n’kothandiza bwanji? Zikutikumbutsa kuti mgwirizano komanso kuchita zinthu mosakondera zikuyenera kumaonekera mosavuta pakati pa atumiki a Yehova padziko lonse lapansi. Yehova alibe tsankho. Ndiye tizidzifunsa kuti: ‘Kodi ndimasonyeza kuti ndilibe tsankho mofanana ndi Yehova? Kodi munthu aliyense amene ndikulambira naye Mulungu, ndimamulemekeza kuchokera pansi pamtima, mosaganizira mtundu wake kapena mmene zinthu zilili pa moyo wake?’ (Aroma 12:10) Tikusangalala kuti Yehova watilola tonsefe kuti tikhale m’paradaiso wauzimu, mmene timatumikira Atate wathu wakumwamba ndi mtima wonse ndipo timasangalala ndi madalitso ake.—Agal. 3:26-29; Chiv. 7:9.
17 Tsopano tiyeni tikambirane mfundo ya 4 yolimbikitsa imene ikupezeka m’mbali yomalizira ya masomphenya a Ezekieli. Mfundo yake ndi yakuti, Yehova adzakhala ndi anthu amene anatengedwa kupita ku ukapolo. Kodi tikuphunzira chiyani kuchokera pa lonjezo limeneli? Tipeza yankho la funso limeneli m’mutu wotsatira.