Baibulo
Tanthauzo: Mawu olembedwa a Yehova Mulungu kwa anthu. Anagwiritsira ntchito alembi aumunthu okwanira 40 mkati mwa nyengo ya zaka mazana 16 kulilemba, koma Mulungu mwiniyo anatsogoza kwenikweni kulembedwako mwa mzimu wake. Chotero liri louziridwa ndi Mulungu. Mbali yaikulu ya cholembedwacho njopangidwa ndi mawu enieni onenedwa ndi Yehova ndi malongosoledwe onena za ziphunzitso ndi ntchito za Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu. Mmenemu timapezamo mawu onena za malamulo a Mulungu kaamba ka atumiki ake ndi zimene adzachita kukwaniritsa chifuno chake chachikulu kaamba ka dziko lapansi. Kuti azamitse chiyamikiro chathu kaamba ka zinthu zimenezi, Yehova anasunganso m’Baibulo cholembedwa chosonyeza zimene zimachitika pamene anthu ndi mitundu amvetsera Mulungu ndi kugwira ntchito mogwirizana ndi chifuno chake, kudzanso chotulukapo pamene ayenda m’njira ya iwo eni. Kupyolera mwa cholembedwa cha m’mbiri chodalirika chimenechi Yehova amatidziŵitsa ntchito zake ndi anthu ndipo motero ndi umunthu wake wodabwitsa.
Zifukwa zophunzirira Baibulo
Baibulo lenilenilo limati nlochokera kwa Mulungu, Mlengi wa anthu
2 Tim. 3:16, 17: “Lemba lirilonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iriyonse yabwino.”
Chiv. 1:1: “Chivumbulutso cha Yesu Kristu, chimene Mulungu anamvumbulutsira achiwonetsere akapolo ake, ndicho cha izi ziyenera kuchitika posachedwa.”
2 Sam. 23:1, 2: “Atero Davide mwana wa Jese . . . mzimu wa Yehova unalankhula mwa ine, ndi mawu ake anali pa lilime langa.”
Yes. 22:15: “Atero Ambuye Yehova wamakamu.”
Tikayembekezera uthenga wa Mulungu kwa anthu onse kukhala wopezeka kuzungulira dziko lapansi. Baibulo, lathunthu kapena mbali yake, latembenuzidwira m’zinenero zokwanira 1 800. Kufalitsidwa kwake, kukufikira mabiliyoni ambiri. The World Book Encyclopedia imati: “Baibulo ndiro bukhu loŵerengedwa mofala koposa mabukhu onse m’mbiri. Mwinamwake lirinso lachisonkhezero kuposa onse. Makope ochulukirapo a Baibulo agaŵiridwa kuposa a bukhu lina lirilonse. Latembenuziridwanso m’zinenero zochulukirapo kuposa bukhu lina lirilonse.”—(1984), Vol. 2, p. 219.
Ulosi wa Baibulo umalongosola tanthauzo la mikhalidwe ya dziko
Atsogoleri adziko ambiri amavomereza kuti mtundu wa anthu uli pa mphembenu pa tsoka. Baibulo lidaneneratu mikhalidwe imeneyi kalekale; limalongosola tanthauzo lake ndi chimene chidzakhala chotulukapo chake. (2 Tim. 3:1-5; Luka 21:25-31) Limasimba zimene tiyenera kuchita kuti tipulumuke chiwonongeko choyandikiracho chadziko, kuti tikhale ndi mwaŵi wa kupeza moyo wamuyaya m’mikhalidwe yolungama pano padziko lapansi.—Zef. 2:3; Yoh. 17:3; Sal. 37:10, 11, 29.
Baibulo limatikhozetsa kuzindikira chifuno cha moyo
Limayankha mafunso onga akuti: Kodi moyo unachokera kuti? (Mac. 17:24-26) Kodi nchifukwa ninji tiri pano? Kodi ndiko kokha kuti tikhale ndi moyo zaka zoŵerengeka, kupeza zimene tingathe m’moyo, ndiyeno nkufa?—Gen. 1:27, 28; Aroma 5:12; Yoh. 17:3; Sal. 37:11; Sal. 40:8.
Baibulo limasonyeza mmene tingakhalire ndi zinthu zenizenizo zimene okonda chilungamo amakhumba koposa
Limatiuza kumene tingapeze atsamwali abwino amene amakondanadi wina ndi mnzake (Yoh. 13:35), chimene chingatipatse chitsimikiziro chakuti tidzakhala ndi chakudya chokwanira kaamba ka ife eni ndi mabanja athu (Mat. 6:31-33; Miy. 19:15; Aef. 4:28), mmene tingakhalire achimwemwe mosasamala kanthu za mikhalidwe yovuta yotizinga.—Sal. 1:1, 2; 34:8; Luka 11:28; Mac. 20:35.
Limalongosola kuti Ufumu wa Mulungu, boma lake, udzachotsa dongosolo loipa liripoli (Dan. 2:44), ndipo mu ulamuliro wake anthu adzakhoza kukhala ndi thanzi langwiro ndi moyo wamuyaya.—Chiv. 21:3, 4; yerekezerani ndi Yesaya 33:24.
Ndithudi bukhu limene limanena kuti nlochokera kwa Mulungu, limene limalongosola ponse paŵiri tanthauzo la mikhalidwe yadziko ndi chifuno cha moyo, ndi limene limasonyeza mmene mavuto athu adzathetsedwera nloyenera kulingaliridwa.
Maumboni a kuuziridwa
Nlodzala ndi maulosi osonyeza chidziŵitso chokwanira chamtsogolo—chinthu chosatheka kwa anthu
2 Pet. 1:20, 21: “Palibe chinenero cha lembo chitanthauzidwa pachokha, pakuti kale lonse chinenero sichinadza ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu ogwidwa ndi mzimu woyera analankhula.”
◼ Ulosi: Yes. 44:24, 27, 28; 45:1-4: “Yehova . . . amene nditi kwa nyanja yakuya, Iphwa, ndipo ndidzaumitsa nyanja zako; ndi kunena za Koresi, Iye ndiye mbusa wanga, ndipo adzachita zofuna zanga zonse; ndi kunena za Yerusalemu, Adzamangidwa; ndi kwa Kachisi, Maziko ake adzaikidwa. Atero Yehova kwa wodzozedwa wake kwa Koresi, amene dzanja lake lamanja ndaligwiritsa, kuti agonjetse mitundu ya anthu pamaso pake, ndipo ndidzamasula m’chuuno mwa mafumu; atsegule zitseko pamaso pake ndi zipata sizidzatsekedwa: ndidzakutsogolera ndi kusalaza pokakala; ndidzathyolathyola zitseko zamkuwa, ndi kudula pakati akapichi achitsulo . . . chifukwa cha Yakobo mtumiki wanga ndi Israyeli wosankhidwa wanga; ndakuwonjezera dzina.” (Kulemba kwa Yesaya komalizidwa pafupifupi 732 B.C.E.)
◻ Kukwaniritsidwa: Koresi anali asanabadwe pamene ulosiwu unalembedwa. Ayuda anali asanatengeredwe kuundende ku Babulo kufikira 617-607 B.C.E., ndipo Yerusalemu ndi kachisi wake zinali zisanawonongedwe kufikira 607 B.C.E. Ulosiwo unakwaniritsidwa mokwanira kuyambira mu 539 B.C.E. Koresi anapatutsa madzi a Mtsinje wa Firate kukhala nyanja yokumba, zipata za kumtsinje wa Babulo zinasiyidwa zotseguka mosasamala mkati mwa nthaŵi yamadyerero mumzindawo, motero Babulo anagwa kwa Amedi ndi Aperisi pansi pa Koresi. Pambuyo pa nthaŵiyo, Koresi anamasula andende Achiyuda nawabwezera ku Yerusalemu limodzi ndi malangizo a kumanganso kachisi wa Yehova kumeneko.—The Encyclopedia Americana (1956), Vol. III p. 9; Light From the Ancient Past (Princeton, 1959), Jack Finegan, pp. 227-229; “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial” (New York, 1983), pp. 282, 284, 295.
◼ Ulosi: Yer. 49:17, 18: “Edomu adzakhala chizizwitso; ndipo yense wakupitapo, adzazizwa, ndipo adzatsonyera zovuta zake zonse. Monga m’kupasuka kwa Sodomu ndi Gomora ndi midzi inzake, ati Yehova, munthu aliyense sadzakhala m’menemo, mwana wa munthu aliyense sadzagona m’menemo.” (Kulemba kwa Yeremiya maulosiwo kunamalizidwa pokwanira 580 B.C.E.)
◻ Kukwaniritsidwa: “Iwo [Aedomu] anathamangitsidwa m’Palestina m’zaka za zana la 2 B.C. ndi Judas Maccabæus, ndipo mu 109 B.C. John Hyrcanus, mtsogoleri wa Amaccabæ, anawonjezera ufumu wa Yuda kuphatikizapo mbali yakumadzulo ya maiko a Aedomu. M’zaka za zana la 1 B.C. kuwonjezereka kwa Roma kunaphatikizapo chigawo chotsirizira cha ulamuliro wodzigangira wa Aedomu . . . Pambuyo pa chiwonongeko cha Yerusalemu chochitidwa ndi Aroma mu 70 A.D. . . . dzina lakuti Idumæa [Edomu] linazimiririka m’mbiri.” (The New Funk & Wagnalls Encyclopedia, 1952, Vol. 11, p. 4114) Tawonani kuti kukwaniritsidwa kukukokera kufikira kutsiku lathu. Sikunganenedwe mwanjira iriyonse kuti ulosi umenewu unalembedwa pambuyo pa kuchitika kwa zinthuzo.
◼ Ulosi: Luka 19:41-44; 21:20, 21: “Mmene [Yesu Kristu] anayandikira, anawona mudziwo [Yerusalemu] naulirira, nanena, . . . Masiku adzakudzera, ndipo adani ako adzakuzingira linga, nadzakuzungulira iwe kwete, nadzakutsekereza ponsepo; ndipo adzakupasula iwe, ndi ana ako mwa iwe; ndipo sadzasiya mwa iwe mwala wina pamwala unzake; popeza sunazindikira nyengo ya mayang’aniridwe ako.” Masiku aŵiri pambuyo pake, analangiza ophunzira ake kuti: “Pamene pali ponse mudzawona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipululutso chake chayandikira, pamenepo iwo ali m’Yudeya athaŵire kumapiri, ndi iwo ali mkati mwa uwo atuluke.” (Ulosi wonenedwa ndi Yesu Kristu mu 33 C.E.)
◻ Kukwaniritsidwa: Yerusalemu anapandukira Roma, ndipo mu 66 C.E. magulu ankhondo a Roma otsogozedwa ndi Cestius Gallus anaukira mzindawo. Koma, monga momwe wolemba mbiri Wachiyuda Josephus, akusimbira kazembe Wachiromayo “mwadzidzidzi analamula ankhondo akewo kubwerera, nataya chikhulupiriro ngakhale kuli kwakuti sanagonjetsedwe, mosayembekezereka anachoka mu Mzindawo.” (Josephus, the Jewish War, Penguin Classics, 1969, p. 167) Zimenezi zinapereka mwaŵi kwa Akristu wa kuthaŵa mu mzindawo, zimene iwo anachita, akumasamukira ku Pela, kutsidya kwa Yordano, mogwirizana ndi kunena kwa Eusebius Pamphilus mu Ecclesiastical History yake. (Yotembenuzidwa ndi C. F. Crusé, London, 1894, p. 75) Ndiyeno pafupi ndi panthaŵi ya Paskha m’chaka cha 70 C.E. Kazembe Wankhondo Tito anazinga mzindawo, mpanda wozungulira mtunda wokwanira mamailo 4.5 (7.2 km) unaimikidwa m’masiku atatu okha, ndipo pambuyo pa miyezi isanu Yerusalemu anagwa. “Yerusalemuyo anawonongedwa mwadongosolo kotheratu ndipo Kachisi anapululutsidwa. Mabukhu a okumba mabwinja amatisonyeza lerolino mmene kwenikweni chiwonongeko cha nyumba Zachiyuda chinaliri chowonekera bwino lomwe m’dziko lonselo.”—The Bible and Archaeology (Grand Rapids, Mich.; 1962), J. A. Thompson, p. 299.
Zamkatimo ziri zogwirizana ndi sayansi pankhani zimene ofufuza aumunthu anatulukira kokha m’zaka zapambuyo pake
Magwero a chilengedwe: Gen. 1:1: “Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.” Mu 1978, katswiri wa za kuthambo Robert Jastrow analemba kuti: “Tsopano tikuwona mmene umboni wa zakuthambo umagwirizanira ndi lingaliro la Baibulo lonena za chiyambi cha dziko. Kufotokoza kumasiyana, koma mfundo zofunika m’cholembedwa cha chilengedwe cha zakuthambo ndi cholembedwa cha Baibulo cha Genesis nzofanana: mtandadza wa zochitika zimene zikutifikitsa kwa munthu unayamba mwadzidzidzi ndi mofulumira panyengo ya nthaŵi yotsimikizirika, m’kuthwanima kwa kuunika ndi nyonga.”—God and the Astronomers (New York, 1978), p. 14.
Mpangidwe wa Planeti Dziko Lapansi: Yes. 40:22, NW: “Kuli Uyo amene amakhala pamwamba pa mbulunga ya dziko lapansi.” M’nthaŵi zamakedzana lingaliro lofala linali lakuti dziko lapansi linali lathyathyathya. Sikunali kotero kufikira zaka 200 pambuyo pooti lemba Labaibulo limeneli lalembedwa kuti sukulu ya anthanthi Achigiriki inalingalira kuti mwinamwake dziko lapansi linali lobulungika, ndipo pafupifupi m’zaka zina 300 wopenda makamu azakumwamba Wachigiriki anaŵerengera mbwambi mwa dziko lapansi. Koma lingaliro la kubulungika kwa dziko lapansi silinali lingaliro lofala ngakhale panthaŵiyo. Kokha m’zaka za zana la 20 kuti kwakhala kotheka kwa anthu kuyenda maulendo apandege ndipo pambuyo pake kupita kutali mumlengalenga ndipo ngakhale kumwezi, chotero kukumawapangitsa kuwona bwino lomwe mawonekedwe a “mbulunga” ya dziko lapansi ali kutali.
Zinyama: Lev. 11:6: “Kalulu . . . abzikula.” Ngakhale kuli kwakuti zimenezi zinatsutsidwa ndi osuliza ena, kubzikula kwa kalulu potsirizira pake kunawonedwa ndi mwamuna wina Wachingelezi William Cowper m’zaka za zana la 18. Njira yachilendo imene zimenezi zimachitidwiramo inalongosoledwa mu 1940 mu Proceedings of the Zoological Society of London, Vol. 110, Series A, pp. 159-163.
Kugwirizana kwake kwa mkati kuli kwapadera
Makamaka zimenezi ziri choncho chifukwa cha chenicheni chakuti mabukhu a Baibulo analembedwa ndi anthu okwanira 40 kuphatikizapo mfumu, mneneri, mbusa, wokhometsa msonkho, ndi sing’anga. Analemba kwanyengo ya zaka 1 610 zapitazo; chotero panalibe mpata wa kuipitsidwa. Komabe zolembedwa zawo nzogwirizana, ngakhale pamalongosoledwe ochepetsetsa. Kuti muzindikire mlingo umene mbali zosiyanasiyana za Baibulo ziriri zogwirizana ina ndi inzake, muyenera kuliŵerenga ndi kuliphunzira nokha.
Kodi tingatsimikizire motani kuti Baibulo silinasinthidwe
“M’chiŵerengero cha ma MSS. [malemba apamanja] akale otsimikizira malembo, ndi chiŵerengero cha zaka zimene zidapita pakati pa ma MSS. oyambirira ndi otsimikizirira, Baibulo liri loposa kwambiri zolembedwa zakale [za Homer, Plato, ndi ena]. . . . Onse pamodzi ma MSS. akale ali ochepa kwambiri poyerekezera ndi a Baibulo. Palibe bukhu lakale limene liri lotsimikiziridwa bwino lomwe kwambiri mofanana ndi Baibulo.”—The Bible From the Beginning (New York, 1929), P. Marion Simms, pp. 74, 76.
Lipoti lofalitsidwa mu 1971 likusonyeza kuti pali mwina makope olembedwa pamanja 6 000 okhala ndi Malemba Achihebri onse kapena mbali zake; akale koposa akumafikira ku zaka za zana lachitatu B.C.E. Ponena za Malemba Achikristu Achigiriki, pali 5 000 m’Chigiriki, akale koposa akumakhala ndi deti la kuchiyambiyambi kwa zaka za zana lachiŵiri C.E. Palinso makope ochuluka a matembenuzidwe oyambirira a zinenero zina.
M’mawu oyamba a mavoliyamu ake asanu ndi aŵiri The Chester Beatty Biblical Papyri, Bwana Frederic Kenyon analemba kuti: “Chosankha choyamba ndi chofunika koposa chopezedwa m’kupendedwa kwake [gumbwa] chiri chokhutiritsa kotero kuti kumatsimikizira kusalakwa kwamalemba amene alipo. Palibe kusiyana kwakukulu kapena kodetsa nkhaŵa kumene kumasonyezedwa kaya m’Chipangano Chakale kapena Chatsopano. Mulibe mawu osiyidwa kapena owonjezeredwa odetsa nkhaŵa kwambiri, ndipo mulibe kusiyana kumene kumayambukira maumboni ofunika kapena ziphunzitso. Kusiyana kwa lemba kumayambukira nkhani zazing’ono monga ngati za mawu kapena mawu enieni ogwiritsiridwa ntchito . . . Koma chofunika chawo chachikulu ndicho kutsimikiza kwake, mwaumboni wakale koposa wopezeka panthaŵiyo, kukhulupirika kwa malembo athu amene alipo.”—(London, 1933), p. 15.
Nzowona kuti matembenuzidwe ena a Baibulo amamamatira kwambiri ku zimene ziri m’zinenero zoyambirira koposa ena. Ochitira ndemanga amakono a Baibulo achita mopambanitsa kotero kuti nthaŵi zina amasintha tanthauzo la poyamba. Otembenuza ena alola zikhulupiriro zawo kuipitsa matembenuzidwe awo. Koma zofooka zimenezi zingathe kudziŵika mwa kuyerekezeredwa kwa matembenuzidwe osiyanasiyana.
Ngati Wina Anena Kuti—
‘Sindimakhulupirira Baibulo’
Mungayankhe Kuti: ‘Koma mumakhulupirira kuti Mulungu aliko, kodi sichoncho? . . . Kodi ndingafunse kuti nchiyani m’Baibulo chimene mumachiwona kukhala chovuta kuchivomereza?’
Kapena munganene kuti: ‘Ndingafunse kuti, Kodi inu nthaŵi zonse mwalingalira motero? . . . Ndamva ena akunena zimenezo, ngakhale kuli kwakuti sanaphunzire Baibulo mosamalitsa. Koma popeza kuti Baibulo momvekera bwino limanena kuti liri uthenga wochokera kwa Mulungu mwiniyo ndi kuti akutilonjeza moyo wamuyaya ngati tikhulupirira ndi kukhala ndi moyo mogwirizana ndi zimene limanena, kodi simukuvomereza kuti kukakhala koyenerera kwambiri kulipenda kuti tidziŵe kuti kaya zimene limanena nzowona kapena ayi? (Gwiritsirani ntchito mawu a patsamba 54-57.)’
‘Baibulo limadzitsutsa’
Mungayakhe kuti: ‘Pali anthu ena amene anandiuza zimenezo, koma palibe ndi mmodzi yemwe amene anayamba wandisonyeza chimene chiri kudzitsutsa kumeneko. Ndipo m’kuŵerenga Baibulo kwa ine mwini sindinapeze nkumodzi komwe. Kodi mungandipatse chitsanzo?’ Ndiyeno mwinamwake mungawonjezere kuti: ‘Zimene ndapeza nzakuti anthu ambiri sanapeze chabe mayankho a mafunso amene Baibulo linawachititsa kuwasinkhasinkha. Mwachitsanzo, kodi Kaini anapeza kuti mkazi wake? (Gwiritsirani ntchito mawu a patsamba 235.)’
‘Anthu analemba Baibulo’
Mungayankhe kuti: ‘Nzowona. Pafupifupi 40 a iwo anakuchita. Koma linauziridwa ndi Mulungu.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Kodi zimenezo zitanthauzanji? Kuti Mulungu anatsogoza kulembedwako, mofanana ndi mmene mwini bizinesi amagwiritsirira ntchito mlembi kumlembera makalata.’ (2) ‘Lingaliro la kulandira mauthenga ochokera kwa munthu wa kutali m’mlengalenga siliyenera kutidabwitsa. Ngakhale anthu atumiza mauthenga ndi zithunzi kuchokera pamwezi. Kodi anakuchita motani? Mogwiritsira ntchito malamulo amene anayambitsidwa kalekale ndi Mulungu mwiniyo.’ (3) ‘Koma kodi ndimotani mmene tingakhalire otsimikizira kuti zimene ziri m’Baibulo nzochokeradi kwa Mulungu? Liri ndi chidziŵitso chimene sichikanachokera kumagwero aumunthu. Cha mtundu wanji? Malongosoledwe amtsogolo; ndipo amenewa nthaŵi zonse atsimikizira kukhala olondola kotheratu. (Mwachitsanzo, wonani tsamba 54-56, ndiponso tsamba 261-266, pamutu wakuti “Masiku Otsiriza.”)’
‘Aliyense ali ndi matanthauziridwe ake ake a Baibulo’
Mungayankhe kuti: ‘Ndipo mwachiwonekere sionse amene ali olondola.’ Pamenepo mwinamwake mungawonjezere kuti: (1) ‘Kupotoza Malemba kuti ayenerane ndi maganizo athu kungachititse chivulazo chosatha. (2 Pet. 3:15, 16)’ (2) ‘Zinthu ziŵiri zingathe kutithandiza kumvetsetsa Baibulo molondola. Choyamba, pendani mawu apatsogolo ndi apambuyo (mavesi ozungulira) a mawu alionse. Kenako, yerekezerani malembawo ndi mawu ena m’Baibulo amene amanena za nkhani imodzimodziyo. Mwanjira imeneyo timalola Mawu a Mulungu mwiniyo kutsogoza kuganiza kwathu, ndipo kutanthauzira sikwathu koma kwake. Ndimo mmene mabukhu a Watch Tower amachitira.’ (Wonani tsamba 276, pamutu wakuti “Mboni za Yehova.”)
‘Siliri lopindulitsa m’tsiku lathu’
Mungayankhe kuti: ‘Timakondwera ndi zinthu zopindulitsa kaamba ka tsiku lathu, kodi sichoncho?’ Ndiye mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Kodi mungavomereze kuti kuthetsa nkhondo kukakhala kopindulitsa? . . . Kodi simukuvomereza kuti ngati anthu ataphunzira kukhalira pamodzi mu mtendere ndi a mitundu ina, kumeneku kukakhala chiyambi chabwino? . . . Baibulo linaneneratu zimenezo kumene. (Yes. 2:2, 3) Monga chotulukapo cha kuphunzira Baibulo, zimenezi zikuchitika lerolino pakati pa Mboni za Yehova.’ (2) ‘Kanthu kenanso kakufunika—kuchotsedwa kwa anthu onse ndi mitundu imene imachititsa nkhondo. Kodi chinthu choterocho chidzachitikadi? Inde, Baibulo limalongosola mmene zidzachitikira. (Dan. 2:44; Sal. 37:10, 11)’
Kapena munganene kuti: ‘Ndikuyamikira nkhaŵa yanu. Ngati bukhu lamalangizo linali losapindulitsa, tikakhala opusa kuligwiritsira ntchito, kodi sichoncho?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: ‘Kodi mungavomereze kuti bukhu lopereka uphungu wabwino umene ungatikhozetse kukhala ndi moyo wabanja wachimwemwe nlopindulitsa? . . . Nthanthi ndi zizoloŵezi zonena za moyo wabanja zasintha nthaŵi zambiri, ndipo zotulukapo zimene timawona lerolino siziri zabwino. Koma awo amene amadziŵa ndi kugwiritsira ntchito zimene Baibulo limanena ali ndi mabanja okhazikika, achimwemwe. (Akol. 3:12-14, 18-21)’
‘Baibulo ndibukhu labwino, koma kulibe chinthu chonga chakuti chowonadi chenicheni’
Mungayankhe kuti: ‘Nzowona kuti munthu aliyense akuwonekera kukhala ndi lingaliro losiyana. Ndipo ngakhale ngati munthu aganiza kuti walinganiza chinthu chake, kaŵirikaŵiri amapeza kuti pali chinthu chimodzi chimene sanalingalire. Koma pali munthu wina amene alibe kupereŵera kotero. Kodi ameneyo angakhale yani? . . . Inde, Mlengi wachilengedwe chonse.’ Pamenepo mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Ndicho chifukwa chake Yesu Kristu anati kwa iye: “Mawu anu ndichowonadi.” (Yoh. 17:17) Chowonadi chimenecho chiri m’Baibulo. (2 Tim. 3:16, 17)’ (2) ‘Mulungu samafuna kuti tipwayirepwayire mosadziŵa; iye wanena kuti chifuniro chake kwa ife nchakuti tifike pa chidziŵitso cholongosoka cha chowonadi. (1 Tim. 2:3, 4) Mwanjira yokhutiritsa kwambiri Baibulo limayankha funso longa lakuti . . . ’ (Kuthandiza anthu ena, inu choyamba mungafunikire kukambitsirana umboni wa kukhulupirira kukhalapo kwa Mulungu. Wonani tsamba 306-313, pamutu wakuti “Mulungu.”)
‘Baibulo ndibukhu la azungu’
Mungayankhe kuti: ‘Nzowonadi kuti iwo asindikiza makope ambiri a Baibulo. Koma Baibulo silimanena kuti fuko lina ndilabwino kwambiri koposa lina.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Baibulo nlochokera kwa Mlengi wathu, ndipo iye ngwopanda tsankho. (Mac. 10:34, 35)’ (2) ‘Mawu a Mulungu amalonjeza mwaŵi wa kukhala ndi moyo kosatha pansi pano pansi pa Ufumu wake kwa anthu amitundu yonse ndi mafuko. (Chiv. 7:9, 10, 17)’
Kapena munganene kuti: ‘Kutalitali! Mlengi wa anthu ndiye amene anasankha amuna amene akawauzira kulemba mabukhu 66 a Baibulo. Ndipo ngati anasankha kugwiritsira ntchito anthu akhungu loyera, limenelo linali thayo lake. Koma uthenga wa Baibulo sunali wa anthu oyera okha.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Wonani chimene Yesu ananena . . . (Yoh. 3:16) “Yense” amaphatikizapo anthu a khungu lamawonekedwe ali onse. Ndiponso, asanakwere kumwamba, Yesu ananena mawu otsazikira awa kwa ophunzira ake . . . (Mat. 28:19)’ (2) ‘Mokondweretsa, Machitidwe 13:1 amanena za munthu wina wotchedwa Nigeri, dzina limene limatanthauza kuti “wakuda.” Iye anali mmodzi wa aneneri ndi aphunzitsi ampingo wa Antiokeya, Siriya.’
‘Ndimakhulupirira kokha King James Version’
Mungayankhe kuti: ‘Ngati lanu liri pafupi, ndingakonde kugaŵana nanu kanthu kena kamene ndakawona kukhala kolimbikitsa kwambiri.’
Kapena munganene kuti: ‘Anthu ambiri amagwiritsira ntchito matembenuzidwe amenewo a Baibulo, ndipo ine mwinine ndiri nalo m’laibulale langa.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Kodi munadziŵa kuti pachiyambiyambi Baibulo linalembedwa m’chinenero Chachihebri, Chachiaramu, ndi Chigiriki? . . . Kodi inu mumaŵerenga zinenero zimenezo? . . . Chotero tiri okondwera kuti Baibulo latembenuzidwira m’Chicheŵa.’ (2) ‘Tchati ichi (“Mpambo wa Mabukhu a Baibulo,” mu NW) chimasonyeza kuti Genesis, bukhu loyamba la Baibulo, linamalizidwa mu 1513 B.C.E. Kodi munadziŵa, kuti pambuyo pa kulembedwa kwa Genesis, panapita zaka 2 900 Baibulo lonse lathunthu lisanatembenuziridwe m’Chingelezi? Ndipo zoposa zaka 200 zinapita matembenuzidwe a King James Version asanamalizidwe (1611 C.E.).’ (3) ‘Kuyambira zaka za zana la 17, Chingelezi chakhala ndi masinthidwe ambiri. Tawona zimenezo m’nthaŵi ya moyo wathu, kodi sichoncho? . . . Chotero tikuyamikira matembenuzidwe amakono amene amasonyeza mosamalitsa chowonadi choyambirira chimodzimodzicho m’chinenero chimene timalankhula makono.’
‘Muli ndi Baibulo lanu’
Wonani mutu waukulu wakuti “New World Translation.”