Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Yesu Atumiza Kunja 70 Ena Kukalalikira
IRI ngululu ya 32 C.E., zaka zitatu zathunthu kuyambira pa ubatizo wa Yesu. Iye ndi ophunzira ake apezekapo posachedwapa pa Phwando la Misasa m’Yerusalemu, ndipo mwachiwonekere iwo adakali pafupi. M’chenicheni, Yesu akuthera yambiri ya miyezi isanu ndi umodzi yomalizira ya utumiki wake kaya m’Yudeya kapena kokha kutsidya lina la Mtsinje wa Yordano mu boma la Pereya. Gawo limeneli likufunikira kukwaniritsidwanso.
Zowona, pambuyo pa Paskha wa 30 C.E., Yesu anathera chifupifupi miyezi isanu ndi itatu akulalikira m’Yudeya. Koma pambuyo pa kuyesera kwa Ayuda kumupha iye kumeneko pa Paskha wa 31 C.E., iye anathera chaka chotsatiracho ndi theka kuphunzitsa chifupifupi kotheratu m’Galileya. Mkati mwa nthaŵi imeneyo, iye wakulitsa gulu lalikulu, lophunzitsidwa la alaliki, chinachake chimene iye anali asanachichitepo poyambirirapo. Chotero iye tsopano akuyambitsa ndawala yamphamvu yomalizira yochitira umboni m’Yudeya.
Yesu ayambitsa ndawala imeneyi mwakusankha ophunzira 70 ndi kuwatumiza iwo kunja aŵiri aŵiri. Chotero, pali onse pamodzi magulu 35 a alaliki a Ufumu kukagwira ntchito m’gawolo. Awa apita patsogolo mu mzinda uliwonse ndi m’malo alionse kumene Yesu, mwachiwonekere wotsagana ndi atumwi ake, akukonzekera kubwera.
M’malo mwa kulangiza 70’wo kupita ku masunagoge, Yesu akuwauza iwo kulowa m’nyumba zapadera, akumalongosola: “Ndipo nyumba yonse mukalowamo muthange mwanena, ‘Mtendere ukhale panyumba iyi.’ Ndipo mukakhala mwana wa mtendere m’menemo, mtendere wanu udzapumula pa iye.” Nchiyani chimene chiyenera kukhala uthenga wawo? “Nimunene nawo,” Yesu akutero, “ufumu wa Mulungu wayandikira kwa inu.” Ponena za ntchito ya 70’wo, Matthew Henry’s Commentary ikusimba kuti: “Mofanana ndi Mbuye wawo, kulikonse kumene anachezera, iwo analalikira kunyumba ndi nyumba.”
Malangizo a Yesu kwa 70’wo anali ofanana ndi awo operekedwa kwa 12 pamene anatumiza awa pa ndawala yolalikira m’Galileya chifupifupi chaka chimodzi kumayambiriro. Iye sanachenjeze kokha 70’wo za chitsutso chimene iwo adzakumana nacho, kuwakonzekeretsa iwo kupereka uthenga wawo kwa eninyumba, koma iye akuwapatsa mphamvu ya kuchiritsa odwala. Chotero, pamene Yesu afika mwamsanga pambuyo pake, ambiri akakhala ofunitsitsa kukumana ndi Mbuye wa ophunzira amene ali okhoza kuchita zinthu zodabwitsa zoterozo.
Kulalikira kwa 70’wo ndi ntchito ya Yesu yotsatira inatha kwa nthaŵi yochepa. Mwamsanga magulu 35 a olalikira a Ufumuwo ayamba kubwerera kwa Yesu. “Ambuye,” iwo akunena mwachimwemwe, “ngakhale ziwanda zinatigonjera ife m’dzina lanu.” Ripoti la utumiki labwino loterolo ndithudi likumkondweretsa Yesu, popeza iye akuvomereza kuti: “Ndinawona Satana alinkugwa ngati mphezi kuchokera kumwamba. Tawonani! ndakupatsani ulamuliro wakuponda pa njoka ndi zinkhanira.”
Yesu akudziŵa kuti pambuyo pa kubadwa kwa Ufumu wa Mulungu panthaŵi ya mapeto, Satana ndi ziwanda zake akachotsedwa kumwamba. Koma tsopano kuchotsedwa uku kwa ziwanda zosawoneka ndi anthu wamba kukutumikira monga chitsimikiziro chowonjezereka cha kudza kwa chochitika chimenecho. Chotero, Yesu akulankhula za kugwa kwa mtsogolo kwa Satana kuchokera kumwamba monga ngati chinthu chotsimikizirika. Chotero, muli m’lingaliro lophiphiritsira kuti 70’wo anapatsidwa ulamuliro wa kupondereza njoka ndi zinkhanira. Komabe, Yesu akunena kuti: “Koma musakondwera nako kuti mizimu idakugonjerani, koma kondwerani kuti maina anu alembedwa m’mwamba.”
Yesu wakondweretsedwa kwambiri ndipo mwapoyera akutamanda Atate wake kaamba ka kugwiritsira ntchito atumiki ake odzichepetsa amenewa m’njira yamphamvu yoteroyo. Akutembenukira kwa ophunzira ake, iye akunena kuti: “Odala masowo akuwona zimene muwona. Pakuti ndinena ndi inu kuti aneneri ndi mafumu ambiri anafuna kuwona zimene inu muziwona, koma sanaziwona; ndi kumva zimene mukumva, koma sanazimva.” Luka 10:1-24; Mateyu 10:1-42; Chivumbulutso 12:7-12.
◆ Ndi kuti kumene Yesu analalikira mkati mwa zaka zitatu zoyambirira za utumiki wake, ndipo ndi gawo liti limene iye anakwaniritsa m’miyezi yake yomalizira isanu ndi umodzi?
◆ Ndi kuti kumene Yesu akutsogoza 70 kukapeza anthu?
◆ Nchifukwa ninji Yesu ananena kuti anawona kale Satana akugwa kuchokera kumwamba?
◆ Ndi m’lingaliro lotani mmene 70’wo anaponderezera njoka ndi zinkhanira?