Zimene Ufumu wa Mulungu Udzachita
“Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.”—MATEYU 6:10.
1. Kodi kudza kwa Ufumu wa Mulungu kudzatanthauza chiyani?
PAMENE Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azipempherera Ufumu wa Mulungu, iye anadziŵa kuti kudza kwake kudzathetsa ulamuliro wa anthu wosafuna kutsogoleredwa ndi Mulungu womwe wakhalapo kwa zaka zikwizikwi. Panthaŵi yonseyo, chifuniro cha Mulungu sichinali kuchitika mokwanira padziko lapansi. (Salmo 147:19, 20) Koma Ufumu ukadzakhazikitsidwa kumwamba, chifuniro cha Mulungu chidzachitika kulikonse. Nthaŵi ya kusintha kochititsa mantha pochoka mu ulamuliro wa anthu ndi kuyamba ulamuliro wa Ufumu wa kumwamba wa Mulungu ikuyandikira kwambiri.
2. Kodi kusintha kochoka mu ulamuliro wa anthu ndi kuyamba ulamuliro wa Ufumu kudzayambika ndi chiyani?
2 Kusintha kumeneku kudzayambika ndi nthaŵi imene Yesu anaitcha “masauko aakulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.” (Mateyu 24:21) Baibulo silitchula kuti nthaŵi imeneyi idzakhala yaitali chotani, koma masoka amene adzachitika panthaŵi imeneyi adzakhala oopsa kwambiri kuposa masoka ena alionse amene achitikapo padziko lapansi. Chisautso chachikulu chimenechi chikadzangoyamba, padzachitika chinthu china chimene chidzakhala choopsa kwambiri kwa anthu ochuluka padziko lapansi: kuwonongedwa kwa zipembedzo zonse zonyenga. Zimenezi sizidzakhala zodabwitsa kwa Mboni za Yehova, chifukwa chakuti kwa nthaŵi yaitali akhala akudziŵa kuti zidzachitika. (Chivumbulutso 17:1, 15-17; 18:1-24) Chisautso chachikulu chidzatha pa Armagedo pamene Ufumu wa Mulungu udzaphwanya dongosolo lonse la Satana.—Danieli 2:44; Chivumbulutso 16:14, 16.
3. Kodi Yeremiya akuwalongosola motani mapeto a anthu osamvera?
3 Kodi zimenezi zidzatanthauzanji kwa anthu “osam’dziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino” wa Ufumu wake wa kumwamba wolamulidwa ndi Kristu? (2 Atesalonika 1:6-9) Ulosi wa m’Baibulo umatiuza kuti: “Taonani, zoipa zidzatuluka ku mtundu kumka m’mitundu, ndipo namondwe adzauka kuchokera ku malekezero a dziko lapansi. Ndipo akuphedwa a Yehova adzakhala tsiku lomwelo kuchokera ku malekezero ena a dziko lapansi kumka ku malekezero ena a dziko lapansi, sadzaliridwa maliro, sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka.”—Yeremiya 25:32, 33.
Kutha kwa Zoipa
4. N’chifukwa chiyani Yehova ali ndi chifukwa chabwino chothetsera dongosolo loipali?
4 Kwa zaka masauzande ambiri, Yehova Mulungu walolera zoipa kuchitika, nthaŵi yaitali mokwanira mwakuti anthu owongoka mtima atha kuona kuti ulamuliro wa anthu walephereratu. Mwachitsanzo, m’zaka za m’ma 1900 zokha, anthu oposa mamiliyoni 150 anaphedwa m’nkhondo, m’chiwawa chochitika posintha dongosolo la kachitidwe ka zinthu m’mayiko, ndi pazipwirikiti zina ndi zina zochitika m’mayiko, malinga ndi kunena kwa umboni wina. Nkhanza za anthu zinaonekera kwambiri pankhondo yachiŵiri ya padziko lonse pamene anthu ngati mamiliyoni 50 anaphedwa. Ochuluka mwa ameneŵa anafa imfa zomvetsa chisoni zedi m’misasa yachibalo ya Nazi. Monga momwedi Baibulo linaneneratu, ‘anthu oipa ndi onyenga, aipa chiipire’ m’nthaŵi yathu ino. (2 Timoteo 3:1-5, 13) Lerolino, chisembwere, upandu, chiwawa, ziphuphu, ndi kunyansidwa ndi miyezo ya Mulungu zikuchitika paliponse. Chotero, Yehova alidi ndi chifukwa chabwino chothetsera dongosolo loipa lilipoli.
5, 6. Talongosolani khalidwe loipa lomwe linkachitika m’Kanani wakale.
5 Zinthu panopo zafika pofanana ndi mmene zinalili ku Kanani zaka 3,500 zapitazo. Baibulo limati: “Zilizonse zinyansira Yehova, zimene azida iye, iwoŵa anazichitira milungu yawo; pakuti angakhale ana awo aamuna ndi ana awo aakazi awatentha m’moto, nsembe ya milungu yawo.” (Deuteronomo 12:31) Yehova anauza mtundu wa Israyeli kuti: “Yehova Mulungu wanu awapitikitsa pamaso panu chifukwa cha zoipa za amitundu aŵa.” (Deuteronomo 9:5) Katswiri wa mbiri ya nkhani za m’Baibulo Henry H. Halley anati: “Kulambira Baala, Asitoreti, ndi milungu ina yachikanani kunali kuchitidwa m’mapwando oipitsitsa achisembwere; akachisi awo anali malikulu a khalidwe lonyansa.”
6 Halley anasonyeza kumkitsa kwa kuipa kwawo, popeza kuti m’malo ena mwa malo ambiri otereŵa, akatswiri ofufuza midzi yamakedzana “anapeza mitsuko yambiri momwe munali mafupa a ana amene anaperekedwa nsembe kwa Baala.” Iye anati: “Malo onsewo kwenikweni anali manda a makanda ongobadwa kumene. . . . Akanani ankalambira mwa kuchita chisembwere chosaneneka, monga mwambo wachipembedzo, pamaso pa milungu yawo; kenako, anali kupha ana awo achisamba, monga nsembe ya milungu imeneyi. Zikuoneka kuti dziko la Kanani linali litakhala Sodomu ndi Gomora weniweni wam’kulu. . . . Kodi anthu a khalidwe lonyansa ndi ankhanza ngati amenewo anali ndi ufulu wopitiriza kukhala ndi moyo? . . . Odziŵa za midzi yamakedzana omwe amafukula zotsalira za mizinda yachikanani amadabwa kuti Mulungu sanaiwononge mwamsanga.”
Kulandira Dziko Lapansi
7, 8. Kodi Mulungu adzaliyeretsa motani dziko lapansili?
7 Monga momwe Mulungu anayeretsera dziko la Kanani, iye posachedwapa adzayeretsa dziko lonse lapansi ndi kulipereka kwa anthu ochita chifuniro chake. “Owongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko.” (Miyambo 2:21, 22) Ndiponso wamasalmo anati: “Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti. . . . Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Salmo 37:10, 11) Satana nayenso adzachotsedwapo, kuti “asanyengenso amitundu kufikira kudzatha zaka chikwi.” (Chivumbulutso 20:1-3) Inde, “dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.”—1 Yohane 2:17.
8 Polongosola mwachidule chiyembekezo chachikulucho cha awo amene akufuna kudzakhala padziko lapansi kosatha, Yesu anati: “Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.” (Mateyu 5:5) Zikuoneka kuti anali kunena mawu a pa Salmo 37:29, omwe analosera kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” Yesu anadziŵa kuti chifuniro cha Yehova n’chakuti anthu owongoka mtima adzakhale padziko lapansi kosatha. Yehova amati: “Ine ndinalenga dziko lapansi, anthu ndi nyama zokhala m’dzikomo, ndi mphamvu yanga yaikulu . . . ndipo ndinapereka ilo kwa iye amene ayenera pamaso panga.”—Yeremiya 27:5.
Dziko Latsopano Losangalatsa
9. Kodi Ufumu wa Mulungu udzayambitsa dziko lotani?
9 Armagedo itadutsa, Ufumu wa Mulungu udzayambitsa “dziko latsopano” losangalatsa mmene “mukhalitsa chilungamo.” (2 Petro 3:13) Udzakhalatu mpumulo waukulu zedi kwa opulumuka Armagedo poona dongosolo la zinthu loipali ndi lopondereza litachotsedwapo! Iwo adzakondwera kwambiri kuloŵa m’dziko latsopano lolungama lolamulidwa ndi boma la Ufumu wa kumwamba, momwe adzaona madalitso osangalatsa zedi ndi kukhala ndi moyo wosatha!—Chivumbulutso 7:9-17.
10. Ndi zinthu zoipa ziti zomwe sizidzakhalaponso mu ulamuliro wa Ufumu?
10 Anthu sadzaopanso nkhondo, upandu, njala, kapena ngakhale nyama zolusa. “Ndidzapangana [ndi anthu anga] pangano la mtendere, ndi kuleketsa zilombo zoipa m’dzikomo . . . Ndi mitengo ya kuthengo idzapereka zobala zawo, ndi nthaka idzapereka zipatso zake, ndipo adzakhazikika m’dziko mwawo.” “Iwo adzasula malupanga awo akhale makasu, ndi mikondo yawo ikhale mazenga, mtundu wa anthu sudzasamulira mtundu unzake lupanga, kapena kuphunziranso nkhondo. Koma adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa.”—Ezekieli 34:25-28; Mika 4:3, 4.
11. N’chifukwa chiyani tingakhale ndi chidaliro chakuti matenda adzatha?
11 Matenda, zochitika zomvetsa chisoni, ngakhalenso imfa zidzachotsedwapo. “Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala; anthu okhala mmenemo, adzakhululukidwa mphulupulu zawo.” (Yesaya 33:24) “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita. . . . Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano.” (Chivumbulutso 21:4, 5) Pamene anali padziko lapansi, Yesu anasonyeza kuti amatha kuchita zinthu zimenezo mwa mphamvu yopatsidwa ndi Mulungu. Mochirikizidwa ndi mzimu woyera, Yesu anayendayenda m’dziko lonselo kuchiritsa olumala ndi odwala.—Mateyu 15:30, 31.
12. Kodi tili ndi chiyembekezo chotani ponena za akufa?
12 Yesu anachitanso zina. Anaukitsa akufa. Kodi anthu odzichepetsa anamva bwanji? Ataukitsa mtsikana wa zaka 12 zakubadwa, makolo ake “anadabwa pomwepo ndi kudabwa kwakukulu.” (Marko 5:42) Chimenechi n’chitsanzo china cha zimene Yesu adzachita padziko lonse lapansi pamene Ufumu udzakhala ukulamulira, popeza kuti panthaŵiyo “kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15) Tangolingalirani kudabwa kwakukulu ndi chisangalalo chimene chidzakhalako pamene magulumagulu a akufa adzakhalanso ndi moyo ndi kugwirizananso ndi okondedwa awo! N’zosakayikitsa kuti padzakhala ntchito yaikulu yophunzitsa motsogozedwa ndi Ufumu kotero kuti “dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”—Yesaya 11:9.
Kuyenera kwa Yehova Kokhala Wolamulira Kutsimikiziridwa
13. Kodi zidzaonekera motani kuti Mulungu ndiye woyeneradi kulamulira?
13 Podzafika kumapeto kwa zaka 1,000 za ulamuliro wa Ufumu, banja la anthu lidzakhala litakhalanso ndi maganizo angwiro ndi matupi angwiro. Dziko lonse lapansi lidzakhala munda wa Edene, paradaiso. Padzakhala mtendere, chimwemwe, chisungiko, ndi anthu achikondi. Zimenezi sizinachitikepo m’mbiri yonse ya anthu ulamuliro wa Ufumu usanakhalepo. Ha! Padzakhalatu kusiyana kwakukulu poyerekeza zaka masauzande ambiri za ulamuliro wa anthu woyambitsa mavuto ndi ulamuliro wosangalatsa zedi wa Ufumu wa kumwamba wa Mulungu wa zaka 1,000! Ulamuliro wa Mulungu kudzera mu Ufumu wake udzaonekeratu kuti ndi wapamwamba kwambiri m’njira iliyonse. Padzakhala chitsimikizo chonse chokwanira chakuti Mulungu ndiye ayenera kulamulira.
14. Kodi n’chiyani chidzachitikira opanduka pamapeto a zaka 1,000?
14 Pamapeto a zaka 1,000 zimenezo, Yehova adzalola anthu angwirowo kudzisankhira okha kuti adzatumikira ndani. Baibulo limanena kuti “adzamasulidwa Satana m’ndende yake.” Adzayesanso kusokeretsa anthu, ndipo ena adzasankhadi kusalamulidwa ndi Mulungu. Kuti ‘nsautso isaukenso kachiŵiri,’ Yehova adzawononga Satana, ziwanda zake, ndi onse amene adzapandukira ufumu wa Yehova. Palibe amene angadzanene kuti anthu amene adzawonongedwa kosatha panthaŵiyo sanapatsidwe mpata wabwino kapena kuti njira yawo yoipayo n’chotsatira cha kupanda ungwiro. Iyayi, iwo adzakhala angwiro monga momwe analili Adamu ndi Hava, amene anachita kusankha kupandukira ulamuliro wolungama wa Yehova.—Chivumbulutso 20:7-10; Nahumu 1:9.
15. Kodi anthu okhulupirika adzakhala paunansi wotani ndi Yehova?
15 Komabe, zikuoneka kuti anthu ochuluka zedi adzasankha kuchirikiza ufumu wa Yehova. Mpandu wina aliyense atawonongedwa, olungama adzaimirira pamaso pa Yehova, atakhoza mayeso omalizira a kukhulupirika. Kenako anthu okhulupirika ameneŵa adzalandiridwa ndi Yehova monga ana ake aamuna ndi aakazi. Chotero adzakhalanso muunansi ngati womwe Adamu ndi Hava anali nawo pamaso pa Mulungu asanapanduke. Chotero Aroma 8:21 adzakwaniritsidwa: “Cholengedwa chomwe [mtundu wa anthu] chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.” Mneneri Yesaya analosera kuti: “[Mulungu] wameza imfa ku nthaŵi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse.”—Yesaya 25:8.
Chiyembekezo cha Moyo Wosatha
16. N’chifukwa chiyani kuyembekeza mphoto ya moyo wosatha sikulakwa?
16 Anthu okhulupirika ali ndi tsogolo losangalatsatu kwambiri, kudziŵa kuti Mulungu adzawatsanulira madalitso akuthupi ndi auzimu kunthaŵi zosatha! Wamasalmo ananenetsa kuti: “Muwoloŵetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo [chabwino].” (Salmo 145:16) Yehova akulimbikitsa anthu omwe adzakhale padziko lapansi kukhala ndi chiyembekezo chimenechi cha moyo wa m’Paradaiso posonyeza chikhulupiriro mwa iye. Ngakhale kuti nkhani ya ufumu wa Yehova ndi yofunika kwambiri, iye sauza anthu kum’tumikira popanda chiyembekezo cha mphoto iliyonse. M’Baibulo lonse, kukhala wokhulupirika kwa Mulungu ndi chiyembekezo cha moyo wosatha zimayendera limodzi nthaŵi zonse monga mbali zofunika za chikhulupiriro cha Mkristu mwa Mulungu. “Iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye.”—Ahebri 11:6.
17. Kodi Yesu anasonyeza motani kuti ndi bwino kumaganizira za chiyembekezo chathu popirira mavuto?
17 Yesu anati: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.” (Yohane 17:3) Pamenepa, kudziŵa Mulungu ndi zifuno zake anakuphatikiza ndi mphoto yochita zimenezi. Mwachitsanzo, wolakwa wina atapempha Yesu kuti akam’kumbukire mu Ufumu wake, Yesu anati: “Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” (Luka 23:43) Sanauze mwamunayo kuti angosonyeza chikhulupiriro ngakhale kuti sadzalandira mphoto. Anadziŵa kuti Yehova amafuna kuti atumiki ake akhale ndi chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso kuti chiziwathandiza kupirirabe pamene akumana ndi mayesero osiyanasiyana m’dzikoli. Chotero, kukhala ndi chiyembekezo cha mphotoyo n’kothandiza kwambiri popirira monga Mkristu.
Tsogolo la Ufumuwo
18, 19. N’chiyani chidzachitikira Mfumu ndi Ufumu pamapeto a Ulamuliro wa Zaka 1,000?
18 Popeza kuti Ufumuwo udzakhala boma logwirizira lomwe Yehova adzagwiritsa ntchito posintha dziko lapansi ndi anthu okhalamo kuti akhale angwiro ndi kuyanjananso naye, kodi Mfumu Yesu Kristu ndi mafumu ndi ansembe 144,000 adzakhala ndi ntchito yotani zaka 1,000 zitatha? “Pomwepo pali chimaliziro, pamene adzapereka ufumu kwa Mulungu, ndiye Atate, atatha kuthera chiweruzo chonse, ndi ulamuliro wonse, ndi mphamvu yomwe. Pakuti ayenera kuchita ufumu kufikira ataika adani onse pansi pa mapazi ake.”—1 Akorinto 15:24, 25.
19 Kristu akadzapereka Ufumuwo kwa Mulungu, kodi tinganene kuti malemba onena za Ufumuwo kuti udzakhalako kosatha adzatanthauzanji? Tanthauzo lake lidzakhala lakuti zomwe udzakwaniritsa zidzakhalapo kosatha. Kristu adzalandira ulemu kosatha chifukwa cha ntchito imene anachita posonyeza umboni wakuti Mulungu ndiye woyenera kulamulira. Koma popeza kuti uchimo ndi imfa zidzakhala zitachotsedwapo kotheratu, ndipo anthu adzakhala atawomboledwa, Yesuyo sadzafunikiranso kukhala Muwomboli. Ulamuliro wa zaka 1,000 wa Ufumuwo udzakhala utakwaniritsidwa wonse; chotero sipadzafunikiranso boma logwirizira lokhala pakati pa Yehova ndi anthu omvera. Chotero, “Mulungu akhale zonse mu zonse.”—1 Akorinto 15:28.
20. Kodi tingadziŵe bwanji tsogolo la Kristu ndi a 144,000?
20 Kodi Kristu ndi anzake olamulira nawo adzakhala ndi ntchito yotani Ulamuliro wa Zaka 1,000 ukadzatha? Baibulo silinenapo kalikonse. Koma tingakhale otsimikizira kuti Yehova adzawapatsa ntchito zinanso zochuluka zoti achite m’chilengedwe chake chonse pom’tumikira. Tonsefe lerolino tiyeni tichirikize ufumu wa Yehova kuti tilandire moyo wosatha, kuti m’tsogolomo, tidzakhalepo ndi kuona zimene Yehova wasungira Mfumu ndi mafumu ndi ansembe anzake, komanso chilengedwe chake chonse chodabwitsachi!