Musamangidwe M’goli ndi Osakhulupirira
“Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira osiyana; pakuti . . . okhulupirira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi osakhulupirira?”—2 AKORINTO 6:14, 15.
1. Kodi ndimotani mmene mlongo wina anakwatiwira ndi wosakhulupirira?
MMODZI wa Mboni za Yehova wa pakati pa dera lakumadzulo kwa United States anaferedwa mwamuna wake m’ngozi ya galimoto zaka zingapo kumbuyoko. “Ndinakhwethemulidwa poyambapo,” iye akukumbukira tero, “koma ndinali wogamulapo kusalola chimenechi kudodometsa utumiki wanga kwa Yehova. Ngakhale ndi tero, pambuyo pa zaka zingapo, ndinayamba kudzimva ngati chiyenda yekha pakati pa okwatirana mu mpingo. Mwana wanga wamkazi ndi ine sitinkaitanidwa kaŵirikaŵiri ku mapwando a banja. Pamene ndinkawona okwatirana Achikristu akusonyezana chikondi, ndinadzimvadi wonyalanyazidwa. Palibe aliyense yemwe anawoneka kukhala akuwona kuti ndinkafookerafookera mwauzimu. Chotero pamene mwamuna wakudziko yemwe ndinadziŵa pa ntchito anandipempha kupita naye ku chakudya chamasana, ndinapita. Ndisanachizindikire icho, ndinamkonda iye. Pomalizira pake, ndinafooka koposa ndipo ndinalakidwa ndi kusungulumwa kotero kuti ndinavomera kukwatiwa naye.”
2. Kodi nchifukwa ninji chilakolako cha kukwatira chiri chachibadwa, ndipo kodi nchiyani chimene ukwati unalinganizidwira kupanga?
2 Inde, chilakolako cha kugawana moyo ndi mnzanu wa mu ukwati chingakhale champhamvu koposa, ndiponso nchachibadwa. Monga momwe Yehova iyemwini anachiikira kuti: “Si kwabwino kuti munthu akhale yekha; ndidzampangira, womthangatira [“mnzake,” chinachake choyenerera kwa iye] iye.” (Genesis 2:18, New World Translation Reference Bible, mawu am’munsi) Ukwati unalinganizidwa kupanga chomangira cha umodzi wathithithi, wa nthaŵi yonse pakati pa mwamuna ndi mkazi. Sanali Adamu koma Yehova yemwe adaati: “Mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi.” (Genesis 2:22-24; yerekezani ndi Mateyu 19:4-6.) Mwinamwake mtima wanu umalakalaka mnzanu woteroyo.
3, 4. (a) Kodi ndimotani mmene Baibulo limachenjezera motsutsana ndi kugwirizana mwathithithi ndi osakhulupirira? (b) Kodi ndi m’njira yotani mmene uphungu wa Paulo wonena za kudzimanga m’goli ndi wosiyana ungagwirire ntchito ku ukwati? (c) Kodi ndimotani mmene Akristu a ku Korinto anamvetsetsera liwu lakuti “osakhulupirira”? (Onani mawu am’munsi.)
3 Ngakhale ndi tero, Baibulo limachenjeza za kusagwirizana mwathithithi ndi osakhulupirira. Monga momwe mtumwi Paulo adachiikira icho kuti: “Musakhale omangidwa m’goli [“Musadziphatike inu eni m’gulu losiyana,” The Jerusalem Bible] ndi osakhulupirira osiyana.a Pakuti . . . okhulupirira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi osakhulupirira?”b (2 Akorinto 6:14, 15) Paulo angakhale ankaganiza za Chilamulo cha Mose choletsa kumanga pamodzi m’goli ng’ombe yamphongo ndi bulu kuti zilime. (Deuteronomo 22:10) Bulu ngwamng’ono msinkhu ndipo ngwopanda mphamvu zambiri ndipo angavutike monga chotulukapo cha kumangidwa m’goli kosiyana koteroko. Popeza kuti ukwati uli ngati goli lomwe limamanga pamodzi mwamuna ndi mkazi, kuti Mkritsu akwatire wosakhulupirira kukatulukapo kumangidwa m’goli kosiyana. (Mateyu 19:6) Goli loterolo kaŵirikaŵiri limabweretsa chididikizo chowonjezereka ndi chipsyinjo ku ukwati.—Yerekezani ndi 1 Akorinto 7:28.
4 Komabe, monga momwe chitsanzo choyambacho chikusonyezera, Akristu ena asankha kukwatira osakhulupirira. Kodi nchifukwa ninji ena amachipeza kukhala chovuta kukwatira “kokha mwa Ambuye”?—1 Akorinto 7:39.
Chifukwa Chimene Ena Amayang’anira Kwina
5. Chitirani chitsanzo chifukwa chimene ena amakhalira odziloŵetsa m’chikondi ndi wosakhulupirira.
5 Sikuti amangofuna kunyalanyaza uphungu wa Mulungu ayi. Lingalirani mkhalidwe wa mlongo Wachikristu yemwe angafune kukwatiwa. Iye angalakalake mwamuna Wachikristu, koma sipakuwoneka kukhala abale ambiri oyenerera m’gulu la mabwenzi ake okhulupirira. Iye ali wozindikira za msinkhu wake. Angalakalake kukhala ndi banja. Nkhaŵa ya kukalamba ali yekha ndi chifuno cha kukhala wokondedwa zingampangitse kukhala m’nkhole. Pamenepo, ngati mwamuna wakudziko asonyeza chikondwerero mwa iye, chingakhale chovuta kukana. Mwamunayo angawoneke kukhala wachifundo ndi wodekha. Iye angakhale wosasuta kapena wosagwiritsira ntchito chilankhulo choipa. Ndiyeno pamadza zodzikhululukira: ‘Nkulekeranji, iye ali wabwino kuposa abale ochulukira omwe ndimadziŵa!’ ‘Iye ali wokondwerera m’kuphunzira.’ ‘Ndimadziŵa zochitika zina m’zimene mlongo anakwatiwa ndi wosakhulupirira ndipo pambuyo pake mwamunayo anakhala wokhulupirira mnzake.’ ‘Pali maukwati ena Achikristu amene amalephera!’—Onani Yeremiya 17:9.
6, 7. (a) Kodi ndimotani mmene mlongo wina wosakwatiwa analongosolera kukhumudwitsidwa kwake? (b) Kodi ndi funso lotani limene tiyenera kulilingalira?
6 Inde, kungakhale kokhumudwitsa kwa mbeta Yachikristu yofuna kukwatira. Ena amafikira pa kudzimva othedwa nzeru. “Chiŵerengero cha abale oyenerera nchaching’ono kwambiri,” anatero mlongo wosakwatiwa wina polongosola mkhalidwewo m’dera lakwawo. “Koma chiŵerengero cha alongo osakwatiwa nchachikulu kwambiri. Pamene mlongo akuwona utsikana wake ukutha, amangotsala ndi chosankha cha kusakwatiwa konse kapena kukwatiwa pa mwaŵi uliwonse womwe angapeze.”
7 Mosasamala kanthu za izo, uphungu wa Baibulo ngwachimvekere: ‘Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira.’ (2 Akorinto 6:14) Kodi chenjezo laumulungu limeneli liri lankhanza kapena losalingalira?
Chisonyezero cha Chisamaliro Chachikondi cha Mulungu
8. Kodi Yehova wasonyeza motani kuti amatifunira zikondwerero zabwino koposa?
8 Yehova ngwodera nkhaŵa mozama ponena za ubwino wathu wokhalitsa. Kodi sanalole kutayikiridwa mokulira, mwa kupereka Mwana wake monga “dipo la anthu ambiri”? (Mateyu 20:28) Kodi iye sindiye ‘Amene akutiphunzitsa kupindula’? (Yesaya 48:17) Kodi iye sakutilonjeza kuti ‘sadzatilola kuyesedwa koposa kumene tikhoza’? (1 Akorinto 10:13) Chotero, nchanzeru kuti, pamene akutiwuza kusadzimanga m’goli ndi osakhulupirira, iye ayenera kukhaladi ndi zikondwerero zathu zabwino koposa! Lingalirani mmene chenjezo limeneli liriri chisonyezero cha chisamaliro chake chachikondi kwa ife.
9. (a) Kodi ndi chenjezo lotani limene Paulo akupereka motsutsana ndi Mkristu kupanga chomangira chathithithi ndi wosakhulupirira? (b) Kodi liwu Lachigriki lolembedwa kuti “mogwirizana” limatanthauzanji, ndipo kodi ndimotani mmene limasonyezera vuto lomwe limakhalapo pamene Mkritsu adziika m’goli ndi wosakhulupirira?
9 Ukwati unalinganizidwa ndi Mlengi kupanga chomangira chathithithi pakati pa anthu, chotenga mwamuna ndi mkazi kukhala “thupi limodzi.” (Genesis 2:24) Kodi nkwanzeru kuti Mkristu apange chomangira chathithithi choterocho ndi wosakhulupirira? Paulo akuyankha mwa kubutsa mpambo wa mafunso opyoza, lirilonse la iwo likuwoneka kukhala ndi yankho lokana: “Pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuwunika kuyanjana bwanji ndi mdima? Ndipo Kristu [agwirizana, NW] [m’Chigriki, sym·phoʹne·sis] bwanji ndi Beliyali [Satana]? Kapena wokhulupirira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupirira?” (2 Akorinto 6:14, 15) Liwu Lachigriki lakuti sym·phoʹne·sis m’lingaliro lenileni limatanthauza “kumvekera pamodzi” (kuchokera ku syn, “ndi,” ndi pho·neʹ, “kumveka”). Limalozera ku chigwirizano chotulutsidwa ndi ziŵiya zoimbira. Ndithudi, palibe chigwirizano pakati pa Kristu ndi Satana. Mofananamo, m’goli lomangidwa ndi wosiyana, nkovutadi kwa mwamuna ndi mkazi ‘kuyimba ndi liwu lofanana.’ Iwo ali ngati ziŵiya zoimbira ziŵiri zomwe sizikugwirizana, zikumatulutsa mawu aphokoso m’malo mwa nyimbo.
10. Kodi ndi ziti zomwe ziri mbali zofunika mu ukwati wachimwemwe, ndipo kodi ndi mapindu otani omwe amakhalapo ngati pali kumangidwa m’goli kolingana?
10 Pamenepa, kodi munthu wauzimu angasangalale motani ndi chigwirizano chotheratu ndi wachibadwidwe? (1 Akorinto 2:14) Zikhulupiriro zofala, malamulo a makhalidwe abwino, ndi zonulirapo ziri mbali zofunika mu ukwati wachimwemwe. Palibe china chirichonse chimene chimalimbitsa ukwati mokulira kuposa kudzipereka mogwirizana kwa Mlengi. Ngati pali kumangidwa m’goli kogwirizana, mwamuna ndi mkazi angalimbikitsane m’kulambira. Aŵiriwo angayang’ane Malemba kuthetsa mikangano yawo. Pamenepa, kodi sikuli kowonekeratu kuti Yehova akutiuza kusadzimanga m’goli ndi osakhulupirira chifukwa chakuti amafuna kuti tisangalale ndi chomangira chathithithi chothekera ndi mnzathu wa mu ukwati?
11. Kodi nchifukwa ninji kuloŵa mu ukwati ndi wosalambira kunaletsedwa mu Israyeli, ndipo kodi ndi funso lodzutsa maganizo lotani lomwe likudzutsidwa?
11 Kulabadira chenjezo la Baibulo kumatipulumutsanso ku zotulukapo zowaŵitsa zimene kaŵirikaŵiri zimatulukapo pamene Mkristu adzimanga m’goli ndi wosakhulupirira. Mwachitsanzo, pali kuthekera kwakuti wosakhulupirira adzapatutsa mnzake Wachikristu kuleka kutumikira Yehova. Lingalirani chenjezo la Yehova kwa Israyeli wakale. Kuloŵa m’ukwati ndi wosalambira kunaletsedwa. Chifukwa ninji? “Popeza adzapatutsa mwana wanu aleke kunditsata ine,” Yehova anachenjeza tero, “kuti atumikire milungu ina.” (Deuteronomo 7:3, 4) Poyang’anizana ndi chitsutso kuchokera kwa mnzanu wosakhulupirira, pangakhale chikhoterero cha kupatukira m’njira ya kukhala wosatsutsa kwenikweni. Nkosavuta kuganiza kuti, ‘Sichidzachitika kwa ine!’ Koma chinachitika kwa mwamuna wanzeru Solomo. Kodi chofananacho sichingachitike kwa inu?—1 Mafumu 11:1-6; yerekezani ndi 1 Mafumu 4:29, 30.
12. Kodi ndimotani mmene lamulo la Mulungu loletsa kukwatira alendo linatumikira monga chitetezo kwa Aisrayeli? Chitirani fanizo.
12 Ngakhale ngati wokhulupirirayo sanapatutsidwe pa kulambira kowona, padakali mavuto ndi zididikizo zopezeka kaŵirikaŵiri m’nyumba yogawanika mwachipembedzo. Lingaliraninso, lamulo la Mulungu kwa Israyeli. Tangolingalirani kuti msungwana Wachiisrayeli anavomera kukwatiwa ndi mwamuna Wachikanani. Polingalira machitidwe a kugonana omwe anali ofala m’dziko la Kanani, kodi ndi ulemu wotani womwe mwamunayo akakhala nawo ku lamulo la Mulungu wa mkaziyo? Mwachitsanzo, kodi mwamunayo, mwaufulu akaleka kugonana ndi mkazi wake mkati mwa nyengo ya kusamba, monga momwe zinafunikira ndi Chilamulo cha Mose?c (Levitiko 18:19; 20:18; yerekezani ndi Levitiko 18:27.) Ponena za mwamuna Wachiisrayeli yemwe akakwatira mkazi Wachikanani, kodi mkaziyo akakhala wachichirikizo motani pamene mwamuna akapita ku Yerusalemu katatu chaka chirichonse kukapezeka ku mapwando a nyengo zoikika? (Deuteronomo 16:16) Motsimikizirika, kuletsa kwa lamulo la Mulungu maukwati oterowo kunatumikira monga chitetezo kwa Aisrayeli.
13. (a) Kodi nchifukwa ninji munthu wakudziko sakhala ndi chikumbumtima Chachikristu, chophunzitsidwa ndi Baibulo? (b) Kodi ndi zididikizo zotani ndi mavuto omwe amayang’anizana ndi ena m’nyumba zogawikana mwachipembedzo?
13 Bwanji ponena za lerolino? Miyezo ya makhalidwe ya anthu akudziko njosiyana kutalitali ndi ija ya Baibulo. Mosasamala kanthu za mmene anthu akudziko angaonekere abwino, iwo alibe chikumbumtima Chachikristu, chophunzitsidwa ndi Baibulo. Iwo sanathe zaka akuphunzira Mawu a Mulungu, ‘kusintha maganizo awo’ ndi ‘kuvula umunthu wakale.’ (Aroma 12:2; Akolose 3:9) Chifukwa chake, Mkristu yemwe amadzimanga m’goli ndi wosakhulupirira kaŵirikaŵiri amadzivumbula iyemwini ku kulaswa mtima kochuluka ndi chisoni. Ena amayang’anizana ndi zididikizo zobwerezabwereza za kukhala ndi phande m’machitachita akugonana koipa kapena kukondwerera matchuthi akudziko. Ndipo ena amadandaula za kusungulumwa. Monga mmene mlongo wina analembera kuti: “Kusungulumwa komwe umakhala nako pamene wakwatiwa ndi winawake wosakonda Yehova kuli kusungulumwa koipa kotheratu. Talingalirani, mulibe aliyense wogawana naye chowonadi, chomwe chiri chinthu chofunika koposa m’moyo wanu.”
14. (a) M’nyumba zogawikana, kodi nchifukwa ninji kuli kovuta kulera ana “m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova]”? (b) Kodi nchiyani chimene chingakhale chiyambukiro pa ana m’nyumba zogawikana?
14 M’nyumba yogawanika, kungakhale kovuta kulera ana “m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova].” (Aefeso 6:4) Mwachitsanzo, kodi wosakhulupirirayo, mofunitsitsa adzalola ana kupezeka ku misonkhanao kapena kukhala ndi phande mu utumiki wakumunda? Kaŵirikaŵiri ana amakhala ogawanikana m’zokonda zawo—iwo amakondabe makolo onse aŵiri, koma kholo limodzi lokha ndilo limakonda Yehova. Anatero mlongo wina yemwe anakwatiwa ndi wosakhulupirira kuti: “Ndinapyola m’zowawitsa zambiri mkati mwa ukwati wanga wa zaka 20. Ana anga aamuna anakula ndi masoka ambirimbiri ndi kupsyinjika maganizo ndipo tsopano ali mbali ya dziko. Mwana wanga wamkazi kaŵirikaŵiri amaipidwa posakhala ndi ine mokwanira chifukwa cha kuyenera kwa kuchezera kwa atate wake. Mavuto onseŵa alipo chifukwa chakuti pamene ndinali wa zaka 18, ndinasankha kunyalanyaza limodzi la malamulo a makhalidwe abwino a Yehova.” Lamulo la makhalidwe abwino lotani? Musadzimange m’goli ndi osakhulupirira!
15. Kodi nchifukwa ninji Yehova amatilangiza kusadzimanga m’goli ndi osakhulupirira?
15 Momvekera, Yehova amafuna kuti tipeze zabwino koposa m’moyo wathu. Zomwe akufuna kuti ife tichite, kuphatikizapo uphungu wake wa kusadzimanga m’goli ndi osakhulupirira, ziri ku ubwino wathu. (Deuteronomo 10:12, 13) Kukwatira wosakhulupirira kuli kunyalanyaza uphungu Wamalemba, nzeru yogwira ntchito, ndi zomwe kaŵirikaŵiri zakhala zokumana nazo zowawitsa kwa ena.
Mafunso Omwe Amafunsidwa Mofala
16, 17. (a) Ngati sindife osamala, kodi ndimotani mmene malingaliro angasokonezere zoganiza zabwino? (b) Kodi uphungu wa Mulungu uyenera kunyalanyazidwa chifukwa cha mikhalidwe yapadera mu imene Mkristu anakwatira wosakhulupirira ndipo tsopano onse aŵiriwo akutumikira Yehova? Fotokozani.
16 Komabe, ngati sindife osamala, malingaliro angasokoneze zoganiza zabwino. Tingayambe kulingalira kuti chathu chingakhale chochitika chosiyanako. Lingalirani ena a mafunso ofunsidwa mofala.
17 Bwanji ponena za zochitika zimene mbale kapena mlongo anakwatira wosakhulupirira, ndipo tsopano onse aŵiriwo akutumikira Yehova? Chikhalirechobe, malamulo a makhalidwe abwino a Yehova anaswedwa. Kodi chotulukapo chingalungamitse chiyambi? Chochitika cha Ayuda obwerera kuchoka mu ukapolo ku Babulo chimasonyeza kawonedwe ka Mulungu ka awo onyalanyaza uphungu wake. Pamene ena anadzitengera akazi akunja, alembi a Baibulo, Ezara ndi Nehemiya sanazengereze kutsutsa machitidwe awo. Ayuda amenewo “anachita mosakhulupirika,” anachita “cholakwa chachikulu,” ndipo anakhala a “liŵongo.” (Ezara 10:10-14; Nehemiya 13:27, NW) Nachi chinachake chofunikira kulingalira: Pamene tinyalanyaza uphungu wa Mulungu, tingadzivulaze ife eni mwauzimu, tikumapsyereza chikumbumtima chathu. Mlongo wina amene mwamuna wake wosakhulupirira pambuyo pake anakhala wokhulupirira anati: ‘Ndikuvutikabe ndi zipsyera za malingaliro. Sindingathe kukuuzani mmene ndimaipidwira pamene ena amanena za ife kuti, “Koma zinagwira ntchito kwa iwo.”’
18. Kodi ndi iti yomwe iri njira yanzeru ngati mwakonda wina wake yemwe sanabatizidwebe, ndipo mwakutero kodi nchiyani chimene mudzasonyeza?
18 Bwanji ngati mwakonda winawake yemwe akuphunzira Baibulo ndi kupezeka pa misonkhano, ngakhale kuti mwamunayo kapena mkaziyo sanabatizidwebe? Timasangalala pamene aliyense asonyeza chikondwerero m’chowonadi cha Baibulo. Ngakhale ndi tero, funso nlakuti: Kodi muyenera kulondola chofuna chanucho? Mosapita mbali, njira yanzeru ndiyo kuyembekezera kufikira nthaŵi ina pambuyo pakuti bwenzi lanulo labatizidwa ndipo likupanga kupita patsogolo m’kusonyeza zipatso za mzimu wa Mulungu musanayambe kupita kocheza. (Agalatiya 5:22, 23) Kungakhale kovuta kugwiritsira ntchito uphunguwu, koma mwakutero mudzasonyeza chikhulupiriro ku malamulo a makhalidwe abwino Abaibulo; kuteroko kudzayala maziko abwino a chimwemwe chenicheni mu ukwati. Ngati bwenzi lanulo mowonadi limakusamalani ndipo likumkondadi Yehova, mosakaikira mwamunayo (kapena mkaziyo) adzakhala wofunitsitsa kuyembekezera kufikira nonsenu muli “mwa Ambuye”—odzipereka ndi obatizidwa—musanapalane ubwenzi. Kumbukiraninso kuti chikondi chenicheni sichimavulazidwa ndi kupita kwa nthaŵi.—1 Akorinto 7:39; Genesis 29:20.
19. Kodi nchiyani chimene muyenera kusunga m’maganizo ngati muli ndi vuto la kupeza mnzanu wa mu ukwati pakati pa akhulupiriri anzanu?
19 Bwanji ngati muli ndi vuto la kupeza mnzanu wa mu ukwati woyenerera pakati pa akhulupiriri anzanu? “Ndine mbeta ya zaka 26 zakubadwa, ndipo wosungulumwadi,” anatero mlongo wina. Nzowona, kukhala mbeta kungakhale kovuta kwa inu, koma mavuto omwe amatuluka m’kukhala womangidwa m’goli losiyana mu ukwati angakhale ovutitsitsa! Kulabadira uphungu wa Mulungu kungafunike chikhulupiriro, kudziletsa, ndi kuleza mtima, koma khalani ndi chitsimikizo chakuti Yehova amadziŵa ndipo amakufunirani zabwino koposa. (1 Petro 5:6, 7) Ipangeni iyo kukhala nkhani ya pemphero, kenaka yembekezerani pa Yehova. (Salmo 55:22) M’dongosolo iri la zinthu, palibe aliyense yemwe ali ndi moyo wokhutiritsa mwangwiro. Mtima wanu ungalakalake mnzanu wa mu ukwati. Ngakhale ndi tero, ena ali ndi mbali yawo ya mavuto, omwe ena ngwosachiritsika m’dongosolo lino. Kokha m’dziko latsopano likudzalo ndi mmene ‘chokhumba cha zamoyo’ chidzakwaniritsidwa kotheratu.—Salmo 145:16.
20. Kodi ndimotani mmene mlongo wina wosakwatiwa anasonyezera chosankha chake, ndipo mwakukhala wogamulapo mofananamo, kodi ndi chikhutiritso chotani chimene mungakhale nacho?
20 Pakalipano, khalani wogamulapo kusadzimanga m’goli ndi osakhulupirira. Mlongo wosakwatiwa wa zaka 36 zakubadwa analongosola chosankhapo chake motere: “Ndimapemphera kwa Yehova tsiku lirilonse kufuna mnzanga wa mu ukwati. Ndiribe chikhumbo cha kuyang’ana kunja kwa gulu la Yehova, koma ziyeso ziripobe. Pakalipano, ndikupanga makonzedwe a kugwirira ntchito pa mikhalidwe yomwe idzandiwongolera monga munthu kotero kuti ndikakhale mtundu wa mkazi wauzimu amene mwamuna wauzimu akufunafuna.” Kodi ndinu wogamulapo mofananamo? Ngati ndi tero, mungakhale ndi chikhutiritso chomwe chimadza mwa kukhalabe wokhulupirika kwa Mulungu wa chilungamo chaumulungu.—Salmo 37:27, 28.
[Mawu a M’munsi]
a Pa 1 Akorinto 14:22, Paulo anagwiritsira ntchito liwu lakuti “osakhulupirira” mosiyana ndi “okhulupirira,” kapena anthu obatizidwa. Pamenepa, Akorinto akamvetsetsa liwu lakuti “osakhulupirira” kulozera kwa anthu osabatizidwa.—Onani Machitidwe 8:13; 16:31-34; 18:8.
b “Mu mkhalidwe wofutukulidwa lamulo lake lingalongosoledwe kukhala: ‘Musapange unansi uliwonse, kaya wakanthaŵi kapena wokhalitsa, ndi osakhulupirira womwe ungatsogolere ku kulolera molakwa miyezo Yachikristu kapena kufooketsa kukhazikika kwa mboni Yachikristu. Ndipo nchifukwa ninji kulekana koteroko? Chifukwa chakuti wosakhulupirira alibe phande m’miyezo, zisoni, kapena zonulirapo za Mkristuyo.’”—The Expositor’s Bible Commentary, Volyumu 10, tsamba 359.
c Onani The Watchtower ya September 15, 1972, masamba 575-6.
Kodi Mungalongosole?
◻ Kodi Baibulo limachenjeza motani kutsutsa kugwirizana mwathithithi ndi osakhulupirira?
◻ Kodi nchifukwa ninji Akristu ena odzipereka amayang’ana kunja kwa mpingo kufuna mnzawo wa mu ukwati?
◻ Kodi ndimotani mmene chenjezo la Yehova lonena za kudzimanga m’goli ndi wosiyana liridi chisonyezero cha chikondi chake chotisamalira?
◻ Kodi ndi mafunso otani onena za kupeza mnzanu wa mu ukwati amene amafunsidwa mofala, ndipo kodi mukawayankha motani?