Gwirani Ntchito Zolimba Kaamba ka Chipulumutso cha Banja Lanu
“Muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.”—AEFESO 6:4.
1, 2. Kodi ndi zovuta zotani zimene zikuyang’anizana ndi makolo lerolino?
MAGAZINI otchukawo anakutcha kuti kusintha. Imeneyi inali nkhani imene inalongosola za masinthidwe ododometsa amene achitika m’banja m’zaka zaposachedwapa. Ameneŵa ananenedwa kukhala “chotulukapo cha mliri wa chisudzulo, kukwatiranso, kusudzulanso, ana apathengo, ndi mavuto atsopano m’mabanja olimba.” Zipsinjo zotero ndi mavuto si zodabwitsa, pakuti Baibulo linaneneratu kuti anthu akayang’anizana ndi “nthaŵi zoŵaŵitsa” mkati mwa “masiku otsiriza” ano.—2 Timoteo 3:1-5.
2 Chifukwa chake makolo lerolino amayang’anizana ndi zovuta zosadziŵidwa ndi mibadwo yapita. Ngakhale kuti makolo ena pakati pathu alera ana awo m’njira zaumulungu “kuyambira ukhanda,” mabanja ambiri angoyamba posachedwapa “kuyenda m’choonadi.” (2 Timoteo 3:15; 3 Yohane 4) Ana awo angakhale anali osinkhukirapo pamene makolowo anayamba kuwaphunzitsa njira za Mulungu. Ndiponso, chiŵerengero chomawonjezereka cha mabanja a kholo limodzi ndi mabanja olera chikupezeka pakati pathu. Mulimonse mmene mikhalidwe yanu ilili, chilangizo cha mtumwi Paulo chimagwira ntchito: “Muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.”—Aefeso 6:4.
Makolo Achikristu ndi Mbali Zawo
3, 4. (a) Kodi ndi zinthu zotani zimene zachititsa mbali ya atate kuzimiririka? (b) Kodi nchifukwa ninji atate Achikristu ayenera kukhala oposa opezera mabanja zofunika?
3 Onani kuti Paulo ananena mawu ake a pa Aefeso 6:4 kwakukulukulu kwa “atate.” Wolemba wina akufotokoza kuti m’mibadwo yapitayo “atate anali ndi thayo la maleredwe a khalidwe ndi auzimu a ana awo; atate anali ndi thayo la maphunziro a ana awo. . . . Koma Kusintha kwa Maindasitale kunachotseratu kuyandikana kumeneku; atate anasiya minda yawo ndi masitolo, anasiya nyumba zawo kuti akagwire ntchito m’mafakitale ndipo pambuyo pake m’maofesi. Anakubala anatenga ntchito zambiri zimene poyamba zinali thayo la atate. Mowonjezereka, utate unangokhala dzina lokha.”
4 Amuna Achikristu: Musakhutiritsidwe ndi kungokhala opezera mabanja zofunika, mukumasiyira kuphunzitsidwa ndi kusamaliridwa konse kwa ana anu kwa akazi anu. Miyambo 24:27 inafulumiza atate a nthaŵi zakale kuti: “Longosola ntchito yako panjapo, nuikonzeretu kumunda; pambuyo pake ndi kumanga nyumba yako.” Mofananamo lerolino, monga mwamuna wogwira ntchito, mungafune kugwira ntchito kwa nthaŵi yaitali ndiponso zolimba kuti mupeze ndalama. (1 Timoteo 5:8) Komabe, pambuyo pake, chonde patulani nthaŵi ya ‘kumanga nyumba yanu’—mwamalingaliro ndi mwauzimu.
5. Kodi ndimotani mmene akazi Achikristu angagwirire ntchito kaamba ka chipulumutso cha mabanja awo?
5 Akazi Achikristu: Nanunso muyenera kugwira ntchito zolimba kaamba ka chipulumutso cha mabanja anu. Miyambo 14:1 imati: “Mkazi yense wanzeru amanga banja lake.” Monga mabwenzi a muukwati, inuyo ndi amuna anu muli ndi thayo la kuphunzitsa ana anu. (Miyambo 22:6; Malaki 2:14) Zimenezi zingaloŵetsemo kulanga ana anu, kuwakonzekeretsa kaamba ka misonkhano Yachikristu ndi utumiki wakumunda, kapena ngakhale kuchititsa phunziro la banja pamene mwamuna wanu ali wosakhoza kutero. Mungachitenso zochuluka mwa kuphunzitsa ana anu ntchito zapanyumba, makhalidwe abwino, ukhondo wakuthupi, ndi zinthu zina zambiri zothandiza. (Tito 2:5) Pamene amuna ndi akazi agwirira ntchito pamodzi mwanjira imeneyi, akhoza kukwaniritsa bwino kwambiri zosoŵa za ana awo. Kodi zina za zosoŵa zimenezo nziti?
Kusamalira Zosoŵa Zawo Zamalingaliro
6. Kodi ndi mbali zotani zimene anakubala ndi atate amachita m’kakulidwe ka malingaliro a ana awo?
6 Pamene “mlezi afukata ana ake a iye yekha,” iwo amaona kukhala otetezereka, osungika, okondedwa. (1 Atesalonika 2:7; Salmo 22:9) Anakubala oŵerengeka angakanize chisonkhezero cha kupereka chisamaliro chochulukitsitsa kwa makanda awo. Mneneri Yesaya anafunsa kuti: “Kodi mkazi angaiŵale mwana wake wa pabere, kuti iye sangachitire chifundo mwana wombala iye?” (Yesaya 49:15) Motero anakubala amachita mbali yofunika m’kakulidwe ka malingaliro ka ana. Chikhalirechobe, atate nawonso amachita mbali yofunika pa nkhani imeneyi. Wolangiza banja Paul Lewis akuti: “Sindinakhalepo ndi aliyense wa ogwira ntchito zothandiza mabanja amene anali ndi mwana [wopulupudza] amene ananena kuti anali ndi unansi wabwino ndi bambo wake. Osati ngakhale mmodzi mwa mazana ambiri.”
7, 8. (a) Kodi ndi umboni wotani umene ulipo wa chomangira champhamvu pakati pa Yehova Mulungu ndi Mwana wake? (b) Kodi ndimotani mmene atate angakulitsire chomangira chachikondi ndi ana awo?
7 Chifukwa chake nkofunika kuti atate Achikristu akulitse mosamalitsa chomangira chachikondi ndi ana awo. Mwachitsanzo, talingalirani za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu. Paubatizo wa Yesu, Yehova analengeza kuti: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, mwa Iwe ndikondwera.” (Luka 3:22) Muli zambiri m’mawu ochepa amenewo! Yehova (1) anavomereza Mwana wake, (2) anasonyeza poyera chikondi chake pa Yesu, ndipo (3) anadziŵikitsa chiyanjo chake pa Yesu. Komabe, imeneyi sinali nthaŵi yokha imene Yehova anasonyeza chikondi chake pa Mwana wake. Pambuyo pake Yesu anati kwa Atate wake: “Munandikonda Ine lisanakhazikike dziko lapansi.” (Yohane 17:24) Kodi ndithudi ana onse aamuna ndi aakazi omvera samafuna chivomerezo, chikondi, ndi chiyanjo kuchokera kwa atate awo?
8 Ngati ndinu atate, mwachionekere mungachite zambiri kukulitsa chomangira chachikondi ndi ana anu mwa kupanga zisonyezero zoyenera za kuthupi ndi za mawu za chikondi nthaŵi zonse. Zoona, nkovuta kwa amuna ena kusonyeza chikondi chawo, makamaka ngati iwo sanasonyezedwe chikondi poyera ndi atate a iwo eni. Komabe ngakhale kuyesayesa kovuta kumeneku kwa kusonyeza chikondi kwa ana anu kungathe kukhala ndi chiyambukiro champhamvu. Ndi iko komwe, “chikondi chimangirira.” (1 Akorinto 8:1) Ngati ana anu aona kukhala osungika chifukwa cha chikondi chanu chautate, adzakhala okhoterera kwambiri pa kukhala ‘ana aamuna ndi ana aakazi enieni’ ndi kukhala omasuka kukusimbirani za kukhosi.—Miyambo 4:3.
Kusamalira Zosoŵa Zawo Zauzimu
9. (a) Kodi ndimotani mmene makolo Achiisrayeli owopa Mulungu anasamalilira zosoŵa zauzimu za mabanja awo? (b) Kodi ndi mipata yotani imene Akristu ali nayo yophunzitsira ana awo mwamwaŵi?
9 Ana alinso ndi zosoŵa zauzimu. (Mateyu 5:3) Mose analangiza makolo Achiisrayeli kuti: “Mawu awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.” (Deuteronomo 6:6, 7) Ngati ndinu kholo Lachikristu, mungachite kuphunzitsa kwanu kochuluka mwamwaŵi, monga ngati “poyenda inu panjira.” Nthaŵi yotheredwa mukuyenda pa galimoto la banja, kukagula zinthu, kapena kuyendera pamodzi ndi ana anu kukhomo ndi khomo mu utumiki Wachikristu imapereka mipata yabwino ya kupereka malangizo mumkhalidwe womasuka. Nthaŵi yachakudya ili makamaka nthaŵi yabwino kuti mabanja adzikambitsirana. “Timagwiritsira ntchito nthaŵi yachakudya kukambitsirana zinthu zimene zachitika tsikulo,” kholo lina likufotokoza motero.
10. Kodi nchifukwa ninji phunziro la banja nthaŵi zina limakhala lovuta, ndipo kodi ndi kutsimikiza mtima kotani kumene makolo ayenera kukhala nako?
10 Komabe, malangizo olinganizidwa mwanjira ya phunziro lokhazikika la Baibulo ndi ana anu alinso ofunika. Zoonadi, “utsiru umangidwa mumtima” mwa ana. (Miyambo 22:15) Makolo ena amanena kuti ana awo angathe kusokoneza mosavuta phunziro la banja. Motani? Mwakuchita mosakhazikika ndi kunyong’onyeka, mwa kuyambitsa zododometsa zokwiyitsa (monga ngati kumenyana ndi abale awo), kapena mwa kunyengezera kusadziŵa choonadi cha Baibulo cha maziko. Ngati zimenezi zifika pamfundo ya kukhala nkhondo ya chifuniro, chifuniro cha kholo chiyenera kukhala champhamvu koposa. Makolo Achikristu sayenera kugonja ndi kulola ana kulamulira banja.—Yerekezerani ndi Agalatiya 6:9.
11. Kodi ndimotani mmene phunziro la banja lingakhalire losangalatsa?
11 Ngati ana anu samasangalala ndi phunziro la banja, mwinamwake masinthidwe ena angapangidwe. Mwachitsanzo, kodi phunzirolo likugwiritsiridwa ntchito monga chodzikhululukira chopendera zophophonya za ana anu zaposachedwapa? Mwinamwake kukakhala bwino koposa kukambitsirana mavuto otero mwamtseri. Kodi phunziro lanu limachitidwa nthaŵi zonse? Ngati muliimitsa chifukwa cha seŵero lokondedwa la pawailesi yakanema kapena chochitika cha maseŵero, mwachionekere ana anu sadzaona phunzirolo mwamphamvu. Kodi ndinu akhama ndi otenthedwa maganizo m’chizolowezi chanu cha kuchititsa phunziro? (Aroma 12:8) Inde, phunziro liyenera kukhala losangalatsa. Yesani kuloŵetsamo ana onse. Khalani wotsimikiza ndi womangirira, mukumayamikira ana anu mwachikondi chifukwa cha kutenga mbali kwawo. Ndithudi, musangofola chabe nkhaniyo, koma yesani kufika mitima.—Miyambo 23:15.
Kulanga m’Chilungamo
12. Kodi nchifukwa ninji chilango nthaŵi zonse sichimaphatikizapo kulanga kwakuthupi?
12 Ana alinso ndi kufunikira kwamphamvu kwa chilango. Monga kholo, muyenera kuwaikira malire. Miyambo 13:24 imati: “Wolekerera mwanake osammenya amuda; koma womkonda amyambize kumlanga.” Komabe, Baibulo silimatanthauza kuti nthaŵi zonse chilango chiyenera kuperekedwa ndi mkwapulo. Miyambo 8:33 imati: “Imvani mwambo,” ndipo tikuuzidwa kuti “chidzudzulo chiloŵa mkati mwa wozindikira, kopambana ndi kukwapula wopusa kwambiri.”—Miyambo 17:10.
13. Kodi chilango cha mwana chiyenera kuperekedwa motani?
13 Nthaŵi zina, chilango china chakuthupi chingakhale choyenera. Komabe, ngati chiperekedwa mokwiya, nkwachidziŵikire kuti chikakhala chopambanitsa ndi chosagwira ntchito. Baibulo limachenjeza kuti: “Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima.” (Akolose 3:21) Ndithudi, “nsautso iyalutsa wanzeru.” (Mlaliki 7:7) Wachichepere wopwetekedwa mtima angapandukiredi miyezo yolungama. Motero makolo ayenera kugwiritsira ntchito Malemba kulangira ana awo m’chilungamo m’njira yamphamvu komabe yachikatikati. (2 Timoteo 3:16) Chilango chaumulungu chimaperekedwa mwachikondi ndi mwa chifatso.—Yerekezerani ndi 2 Timoteo 2:24, 25.a
14. Kodi nchiyani chimene makolo ayenera kuchita ngati adziona kukhala ogonjera ku mkwiyo?
14 Zoonadi, “timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri.” (Yakobo 3:2) Ngakhale kholo lachikondi mwachibadwa lingathe kugonjera ku chitsenderezo cha kanthaŵi ndi kunena kanthu kena ka nkhanza kapena lingasonyeze mkwiyo. (Akolose 3:8) Ngati zimenezo zingachitike, musalole dzuŵa kuloŵa mwana wanu ali wovutika maganizo kwambiri kapena inuyo muli mumkhalidwe wokwiya. (Aefeso 4:26, 27) Thetsani nkhaniyo ndi mwana wanu, mukumapepesa ngati zimenezo zionekera kukhala zoyenera. (Yerekezerani ndi Mateyu 5:23, 24.) Kusonyeza kudzichepetsa kotero kungakokere inu ndi mwana wanu pamodzi. Ngati mulingalira kuti simungathe kulamulira mtima wanu ndipo mudzagonjera ku mkwiyo, funafunani chithandizo kwa akulu oikidwa a mumpingo.
Mabanja a Kholo Limodzi ndi Mabanja Olera
15. Kodi ndimotani mmene ana okhala m’banja la kholo limodzi angathandizidwire?
15 Komabe, si ana onse amene ali ndi chichirikizo cha makolo aŵiri. Mu United States, mwana 1 mwa 4 akuleredwa ndi kholo limodzi. ‘Ana amasiye’ anali ambiri m’nthaŵi za Baibulo, ndipo nkhaŵa kaamba ka iwo yatchulidwa mobwerezabwereza m’Malemba. (Eksodo 22:22) Mofananamo lerolino, mabanja Achikristu a kholo limodzi amayang’anizana ndi zitsenderezo ndi zovuta, koma amatonthozedwa podziŵa kuti Yehova ndiye “atate wa ana amasiye, ndi woweruza wa akazi amasiye.” (Salmo 68:5) Akristu akufulumizidwa “[kuyang’anira, NW] ana amasiye ndi akazi amasiye m’chisautso chawo.” (Yakobo 1:27) Okhulupirira anzawo angachite zambiri kuthandiza mabanja a kholo limodzi.b
16. (a) Kodi nchiyani chimene makolo okhala okha ayenera kuchitira mabanja awo? (b) Kodi nchifukwa ninji chilango chingakhale chovuta, koma kodi nchifukwa ninji chiyenera kuperekedwa?
16 Ngati ndinu kholo limodzi, kodi mungachitenji inu mwininu kuti mupindulitse banja lanu? Mufunikira kukhala wakhama ponena za phunziro la Baibulo la banja, kufika pamisonkhano, ndi utumiki wakumunda. Komabe, chilango chingakhale thayo lovuta kwambiri. Mwinamwake mudakali wachisonibe chifukwa cha kutayikiridwa ndi mnzanu wa muukwati mu imfa. Kapena mungakhale mukulimbana ndi malingaliro a liwongo kapena amkwiyo pakusweka kwa ukwati. Ngati pali mwana wofunikira kugaŵana chisamaliro chake, mungawoperedi kuti mwana wanuyo angakonde kukhala ndi mnzanu wa muukwati wolekana naye kapena wosudzulana nayeyo. Mikhalidwe yotero ingakupangitse kukhala kovuta mwamalingaliro kupereka chilango chachikatikati. Komabe, Baibulo limatiuza kuti “mwana womlekerera achititsa amake manyazi.” (Miyambo 29:15) Chotero musagonjere pa liwongo, chisoni, kapena pa kupsinjidwa maganizo kochititsidwa ndi amene kale anali mnzanu wa muukwati. Ikani miyezo yabwino ndi yosasintha. Musalolere molakwa pa malamulo amkhalidwe a Baibulo.—Miyambo 13:24.
17. Kodi ndimotani mmene mbali za ziŵalo za banja zingasokonezekere m’banja la kholo limodzi, ndipo kodi nchiyani chimene chingachitidwe kuletsa zimenezi?
17 Komabe, zovuta zingabuke, ngati nakubala amene ali kholo lokha achitira mwana wake wamwamuna monga woloŵa mmalo wa mnzake wamuukwati—mwamuna wa panyumbapo—kapena mwana wake wamkazi monga womuululira zakukhosi, kumlemetsa ndi mavuto achinsinsi. Kuchita motero nkosayenera ndipo kumasokoneza mwana. Pamene mbali za kholo ndi za mwana zikhala zosokonezeka, chilango chingalephereke. Kudziŵiketu kuti inu ndinu kholo. Ngati ndinu nakubala amene akufuna uphungu wozikidwa m’Baibulo, ufunefuneni kwa akulu kapena mwinamwake kwa alongo achikulire achidziŵitso.—Yerekezerani ndi Tito 2:3-5.
18, 19. (a) Kodi ndi zitokoso zina ziti zimene zikuyang’anizana ndi mabanja olera? (b) Kodi ndimotani mmene makolo ndi ana a m’banja lolera angasonyezere nzeru ndi luntha?
18 Mofananamo mabanja olera akuyang’anizana ndi zitokoso. Kaŵirikaŵiri, makolo olera amaona kuti “chikondi cha panthaŵi yomweyo” sichimachitika kaŵirikaŵiri. Mwachitsanzo, ana owapeza angakhale onyumwira kwambiri pa kuonekera ngati kukondera kulikonse kochitidwira ana enieni a khololo. (Yerekezerani ndi Genesis 37:3, 4.) Kunena zoona, ana owapeza angakhale akulimbana ndi chisoni chifukwa cha kholo lomwalira ndi kuwopera kuti kukonda kholo loŵapeza mwinamwake kukakhala kusakhulupirika kwa atate kapena amayi awo enieni. Zoyesayesa za kupereka chilango chofunika zingakumane ndi chikumbutso chowopsa chakuti, ‘Simuli kholo langa lenileni!’
19 Miyambo 24:3 imati: “Nzeru imangitsa nyumba; luntha liikhazikitsa.” Inde, kumafunikira nzeru ndi luntha kumbali za onse kuti banja lolera lipambane. M’kupita kwa nthaŵi, ana ayenera kuvomereza choonadi chovuta chakuti zinthu zasintha. Makolo olera mofananamo afunikira kuphunzira kukhala oleza mtima ndi achifundo, osafulumira kukhumudwa pamene ayang’anizana ndi kukanidwa koonekera. (Miyambo 19:11; Mlaliki 7:9) Musanayambe kupitiriza mbali ya wolanga, yesayesani kukhazikitsa ubwenzi ndi mwana wopezedwayo. Ena angakulingalire kukhala kwabwino kwambiri kulola kholo lenileni kupereka chilango, kufikira ubwenzi umenewo utakhazikitsidwa. Pamene mavuto abuka, zoyesayesa za kulankhulana ziyenera kupangidwa. “Omwe [amakambitsirana, NW] ali ndi nzeru,” pakutero pa Miyambo 13:10.c
Pitirizanibe Kugwira Ntchito Kaamba ka Chipulumutso cha Banja Lanu!
20. Kodi nchiyani chimene mitu ya mabanja Achikristu iyenera kupitirizabe kuchita?
20 Mabanja olimba Achikristu samangochitika mwangozi. Mitu ya mabanjanu pitirizanibe kugwira ntchito zolimba kaamba ka chipulumutso cha mabanja anu. Khalani maso, mukumapenyetsetsa mikhalidwe yoipa kapena zikhoterero zadziko. Ikani chitsanzo chabwino m’kulankhula, khalidwe, chikondi, chikhulupiriro, ndi chiyero. (1 Timoteo 4:12) Sonyezani chipatso cha mzimu wa Mulungu. (Agalatiya 5:22, 23) Kuleza mtima, kulingalira, kukhululukira, ndi kukoma mtima kudzalimbitsa zoyesayesa zanu za kuphunzitsa ana anu njira za Mulungu.—Akolose 3:12-14.
21. Kodi ndimotani mmene mkhalidwe wachikondi ndi wachimwemwe ungasungidwire m’banja la munthu?
21 Ndi chithandizo cha Mulungu, yesani kusunga mzimu wachimwemwe, wachikondi m’banja mwanu. Therani nthaŵi muli pamodzi monga banja, mukumayesayesa kudyera pamodzi chakudya mwinamwake kamodzi kokha tsiku lililonse. Misonkhano Yachikristu, utumiki wakumunda, ndi phunziro la banja nzofunika. Komabe, palinso “mphindi yakuseka; . . . ndi mphindi yakuvina.” (Mlaliki 3:1, 4) Inde, linganizani nyengo za kusanguluka kolimbikitsa. Maulendo a ku myuziyamu, ku malo osungira nyama zakuthengo, ndi malo ofanana nawo amakhala osangalatsa banja lonse. Kapena mungazime TV ndi kuthera nthaŵi pa kuimba, kumvetsera nyimbo, kuseŵera maseŵero, ndi kucheza. Zimenezi zingathandize banja kuyandikirana pamodzi.
22. Kodi muyenera kugwiriranji ntchito zolimba kaamba ka chipulumutso cha banja lanu?
22 Makolo Achikristu nonsenu pitirizanitu kugwira ntchito kukondweretsa Yehova mokwanira ‘pamene mukupitirizabe kubala zipatso mu ntchito iliyonse yabwino ndi kuwonjezereka m’chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu.’ (Akolose 1:10, NW) Mangani banja lanu pamaziko olimba a kumvera Mawu a Mulungu. (Mateyu 7:24-27) Ndipo khalani otsimikizira kuti zoyesayesa zanu za kulera ana anu “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye” zidzavomerezedwa ndi iye.—Aefeso 6:4.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Lingaliro la Baibulo: ‘Nthyole ya Chilango’—Kodi Njachikale?” mu Galamukani! wa September 8, 1992.
b Onani Nsanja ya Olonda ya March 15, 1981, masamba 12-26.
c Onani Nsanja ya Olonda ya April 15, 1985, masamba 21-5.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ndimotani mmene mwamuna ndi mkazi angagwirizanire m’kumanga banja lawo?
◻ Kodi nziti zimene zili zina za zosoŵa za malingaliro za ana, ndipo kodi zimenezi zingakwaniritsidwe motani?
◻ Kodi ndimotani mmene mitu ya mabanja ingaphunzitsire ana awo ponse paŵiri molinganizidwa ndi mwamwaŵi?
◻ Kodi ndimotani mmene makolo angalangire m’chilungamo?
◻ Kodi nchiyani chimene chingachitidwe kaamba ka phindu la mabanja a kholo limodzi ndi mabanja olera?
[Chithunzi patsamba 16]
Chikondi cha atate ndi chivomerezo nzofunika pamakulidwe a malingaliro a mwana