Udongo wa Makhalidwe Uli Kukongola kwa Uchichepere
“Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; . . . nuyende m’njira za mtima wako, ndi monga maso ako awona; koma dziŵitsa kuti Mulungu adzanena nawe mlandu wa zonsezi.”—MLALIKI 11:9.
1, 2. (a) Kodi nchiyani chimene Yehova amafunira achichepere? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli kopusa kulondola chirichonse chokomera mtima ndi maso anu?
“UCHICHEPERE, kutenthedwa maganizo, ndi kukangalika ziri ngati masiku a nyengo yangululu. M’malo modandaula . . . za kusakhalitsa kwa zimenezi, yeserani kusangalala nazo.” Analemba tero wolemba ndakatulo Wachijeremani wa m’zaka za zana la 19. Mawu amenewo a chilangizo kwa achicheperenu akumveketsanso aja olembedwa zaka zikwi zingapo kalelo m’bukhu la Baibulo la Mlaliki: “Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata [kapena, utsikana] wako, nuyende m’njira za mtima wako, ndi monga maso ako awona.” (Mlaliki 11:9a) Chotero Yehova Mulungu samangokhala ndi kawonedwe koipidwa ndi zomwe zimakomera zikhumbo za achichepere. Iye akufuna kuti musangalale mokwanira ndi mphamvu ndi nyonga ya uchichepere wanu.—Miyambo 20:29.
2 Ngakhale ndi tero, kodi izi zikutanthauza kuti mungalondole chirichonse chokomera mtima ndi maso anu? Kutalitali! (Numeri 15:39; 1 Yohane 2:16) Lembalo likupitirizabe kunena kuti: “Koma dziŵitsa kuti Mulungu adzanena nawe mlandu wa zonsezi [zolondola zimene mumasankha kukhutiritsa zikhumbo zanu].” (Mlaliki 11:9b) Inde, simungapeŵe zotulukapo za machitidwe anu; achichepere, mofanana ndi achikulire, ali oŵerengeredwa ku chiweruzo cha Yehova.—Aroma 14:12.
3, 4. (a) Kodi nkusungiranji muyezo wapamwamba wa udongo wa makhalidwe? (b) Kodi nchididikizo chotani chimene chiri pa inu cha kutayikiridwa kaimidwe kanu kaudongo kwa Mulungu, ndipo kodi ndi mafunso otani amene amadzutsidwa?
3 Kulandira chiweruzo chabwino cha Yehova kumatsogolera osati kokha ku moyo wosatha komanso ku unansi wathithithi ndi Mulungu tsopano. Komabe, muyenera kuchirikiza muyezo wapamwamba wa udongo wa makhalidwe. Salmo 24, mavesi 3 mpaka 5, likuchiika mwanjira iyi: “Adzakwera ndani m’phiri la Yehova? Nadzaima m’malo ake oyera ndani? Woyera m’manja, ndi wowona m’mtima, ndiye; Iye amene sanakweza moyo wake kutsata zachabe, ndipo salumbira monyenga. Iye adzalandira dalitso kwa Yehova, ndi chilungamo kwa Mulungu wa chipulumutso chake.” Inde, ndinu wokongola m’maso mwa Yehova pamene muchirikiza udongo wa makhalidwe.
4 Komabe, pali chididikizo chosalekeza pa inu kuti mutayikiridwe kaimidwe kanu kaudongo pamaso pa Mulungu. Pamene masiku otsiriza ano akuyandikira kumapeto ake, pali mliri wa makhalidwe achisembwere ndi zisonkhezero zopanda udongo. (2 Timoteo 3:1-5) Kulibe ndi kale lonse pamene chitokoso cha kusunga udongo wa makhalidwe chinakhala chokulira motere pa achichepere. Kodi inu mwachipambano mukuchifikira chitokosocho? Kodi mudzapitirizabe kutero?
Chitokoso Chimene Mukuyang’anizana Nacho
5. Kodi ndi ziyambukiro zodetsedwa zotani zimene zikuchipangitsa kukhala chovuta kusungabe kaimidwe koyera pamaso pa Mulungu?
5 Kuwulutsa kwa zosangulutsa kukukantha achichepere ndi zinthu zomwe zimakankhira pambali zinthu zaulemu ndi kulemekezeratu zachisembwere. Mwachitsanzo, pamene mpambo umodzi wa mafilimu a chiŵaŵa chowopsya unatulutsidwa, wosuliza akanema wina analemba kuti: “Kusinthasintha kwa m’zakugonana, kudabwitsa m’kuphana, ndi kudabwitsa m’chinenero choipa kuli kokulira m’kuonetsedwa kwa chithunzichi. Ngati chimasunga zolembera za opezekapo, icho chidzasonyezanso kutsika kwina kokulira m’kunyonyotsoka kwa . . . ubwino wa akanema.” Kuwonjezera ku akanema oterowo pali nyimbo zokhala ndi mawu otchula zakugonana ndi maprogramu a pa wailesi ya kanema omwe amalemekeza kugonana kopanda lamulo. Kodi mungadzivumbule inu eni ku zisonyezero zoterozo za “kusefukira komwe kwa chitayiko” ndi kuchirikizabe kaimidwe kanu kaudongo pamaso pa Mulungu? (1 Petro 4:4) Monga momwe mwambi ukunenera kuti: “Kodi mwamuna angatenge moto pa chifuwa chake, osatentha zovala zake?”—Miyambo 6:27.
6. Kodi ndi chididikizo chotani chimene achichepere akuyang’anizana nacho kuchokera kwa mabwenzi awo?
6 Chididikizo chomwe chiri pa inu kuti mutayikiridwe kaimidwe kanu kaudongo ndi Mulungu chimachokeranso ku magwero ena—mabwenzi anu. Msungwana wa kudziko wa zaka 17 zakubadwa anachitira chisoni kuti: “Ndinakhala ndi kugonana kwa nthaŵi yoyamba pa zifukwa zolakwika zokhazokha: chifukwa chakuti bwenzi langa lalimuna linakuumirira ndipo chifukwa chakuti ndinaganiza kuti aliyense ankachichita.” Palibe aliyense amafuna kusekedwa. Nchachibadwa kufuna kukondedwa ndi ena. Koma pamene mutenga kaimidwe ka makhalidwe a Baibulo, achichepere ena angakusekeni. Chifuno cha kufanana nawo, kukhala wolandirika kwa mabwenzi anu, chingakuikeni pansi pa chididikizo cha kuchita chinachake chimene mukudziŵa kuti ncholakwa.—Miyambo 13:20.
7. Kodi nchifukwa ninji kulimbana ndi zisonkhezero zodetsedwa kulidi kovuta kwa achichepere, koma kodi nchiyani chimene zikwi za achichepere m’gulu la Yehova adzisonyeza kukhala?
7 Kulimbana ndi zisonkhezero zimenezi kulidi kovuta mkati mwa “unamwali,” pamene zikhumbo za kugonana ziri zamphamvu. (1 Akorinto 7:36) Nchosadabwitsa kuti gulu limodzi lofufuza linamaliza kuti: “Ali wachichepere wapadera kwenikweni yemwe sanakhalepo ndi kugonana ukwati usanakhale pofika msinkhu wa zaka 19.” Komabe, zikwi za achichepere inu m’gulu la Yehova mwadzisonyeza kukhala apadera. Mukuyang’anizana ndi chitokoso mokwanira ndi kuchirikiza udongo wa makhalidwe.
8. Kodi nchifukwa ninji achichepere ena Achikristu alola makhalidwe achisembwere a kudziko kuwayambukira, ndipo ndi chotulukapo chotani?
8 Ngakhale ndi tero, nchachisoni kuti unyinji wa achichepere Achikristu alola mikhalidwe yachisembwere ya dziko kuwayambukira. Pamene kuli kwakuti angadzinenere kukonda chomwe chiri chabwino, iwo sadana nacho choipa; samachida mokwanira. (Salmo 97:10) M’nkhani zina, iwo amawonekeradi kuchikonda icho. Monga momwe Salmo 52:3 likuchiikira icho kuti: “Ukonda choipa koposa chokoma; ndi bodza koposa kunena chilungamo.” Ena amafikadi pa kukaniratu chitsogozo cha gulu la Yehova pa zinthu zonga ngati kupita kocheza, zosangulutsa, ndi makhalidwe abwino. Monga chotulukapo, iwo kaŵirikaŵiri amadzetsa manyazi ponse paŵiri kwa iwo eni ndi kwa makolo awo. Iwo amatayikiridwanso kukongola kwawo m’maso mwa Mulungu.—2 Petro 2:21, 22.
Thandizo m’Kufikira Chitokosocho
9. Kodi chofunikira nchiyani kufikira chitokoso cha kukhalabe waudongo mwamakhalidwe?
9 Kodi mungachifikire motani chitokoso cha kukhalabe waudongo mwa makhalidwe? Wamasalmo adafunsa funso limodzimodzilo kuti: “Mnyamata adzayeretsa mayendedwe ake bwanji?” Kenaka iye anapereka yankho kuti: “Akawasamalira monga mwa mawu anu.” (Salmo 119:9) Inde, mumafunikira chitsogozo kuchokera ku Mawu a Mulungu. Ndipo Atate wathu wakumwamba wachikondi wakhozetsa kuti gulu lake lipereke chitsogozo choterocho kukuthandizani kutsutsa zididikizo zodetsedwa za dzikoli.
10, 11. (a) Kodi ndi mabukhu otani amene akonzekeredwa kuthandiza achichepere kukhalabe oyera mwamakhalidwe? (b) Kodi ndimotani mmene achichepere ena athandizidwira ndi mpambo wa “Achichepere Akufunsa Kuti . . . ”? (c) Kodi inu mwaumwini mwapindula motani ndi mpambo wa “Achichepere Akufunsa Kuti . . . ”?
10 M’zaka zapita unyinji wa mabukhu akonzedwa mwapadera pokhala ndi achichepere m’maganizo, monga bukhu la Your Youth—Getting the Best out of It. Chiyambire 1982, mpambo wa “Achichepere Akufunsa Kuti . . . ” m’magazine a Galamukani! wapereka uphungu wothandiza kwambiri pa nkhani zonga ngati zithunzi zosonyeza umaliseche, mabukhu onena za chikondi, ndi mkhalidwe wabwino mkati mwa kupalana ubwenzi. Kodi chidziŵitso choterocho chathandizadi achichepere? Lingalirani chitsanzo. Nkhani zochulukira za mpambowo zinalongosola kuchita mphyotomphyoto, kusonyeza kuti chizoloŵezicho chimadzutsa “chilakolako cha kugonana” ndipo chingapangitse wina kugwera m’chisembwere cha kugonana mosavuta.a (Akolose 3:5) Malingaliro ogwira ntchito anaperekedwa osonyeza mmene tingalimbanire ndi chizoloŵezicho ndi mmene tingachitire titagweramo. Pokambapo ku nkhanizo, achichepere ena adalemba kuti: “Ndakhala ndi vuto la kuchita mphyotomphyoto chiyambire pamene ndinali ndi zaka 12 zakubadwa. Tsopano ndiri ndi zaka 18, ndipo ndikuchira pang’onopang’ono, ndiyamikira nkhani zanu.” “Tsopano popeza ndagwiritsira ntchito uphungu woperekedwa m’nkhanizo, ndiri mu mkhalidwe wabwino koposa wa maganizo. Ndikudzimva woyererako kuposa ndi kale lonse.”
11 Chimatenga nthaŵi kuŵerenga ndi kuphunzira chidziŵitso choterocho, koma kutero kungakuthandizeni kukhala waudongo mwa makhalidwe. Kodi mukugwiritsira ntchito mokwanira nkhani zofalitsidwa zoterozo? Pokambapo ku nkhani ya mu “Achichepere Akufunsa Kuti . . . ” ya “Kugonana Ukwati Usadakhale—Kulekeranji?”b msungwana wina wachichepere, yemwe pa nthaŵiyo anali wophunzira wa Baibulo, analemba kuti: “Ndidziŵa malingaliro a kuipidwa, liŵongo, ndi kusadzidalira omwe amadza pambuyo pa kugonana ukwati usadakhale, ndipo ndimachita nazodi chisoni. Tsiku lirilonse ndimayamikira Yehova chifukwa cha kundilandira ndi kukhululukira kwake. Ndiganiza kuti nkhani yanu idzathandiza enanso asanachite monga momwe ndinachitira. Zimapwetekadi. Tsopano ndikumvetsetsa chifukwa chimene Yehova Mulungu amafunira kuti ‘tipeŵe dama.’”—1 Atesalonika 4:3.
12. Kodi nchiyani chimene chidzatisonkhezera kufuna kukondweretsa Yehova?
12 Izizo zikutifikitsa ku chinachake chimene chidzakuthandizani kufikira chitokosocho mwachipambano: Muyenera kuzindikira kuti Yehova ndiye Wolamulira Wachilengedwe Chaponseponse ndipo ayenera kulabadiridwa. (Chibvumbulutso 4:11) Ngakhale ndi tero, iye alinso Atate wakumwamba wachikondi, ndipo amafunadi kutikondweretsa. (Miyambo 2:20-22; Yesaya 48:17) Malamulo ake alinganizidwira kutichinjiriza, osati kukhala oletsa mosafunikira. Chotero kuwalabadira iwo ndiko njira yanzeru. (Deuteronomo 4:5, 6) Kumvetsetsa bwino chifukwa chimene Yehova amawumirira pa udongo wa makhalidwe kudzakuthandizani kuwona kukongola kwenikweni kumene kulimo ndipo kudzakufulumizani kufuna kumkondweretsa.—Salmo 112:1.
13. Kodi mungalongosole motani kuti lamulo la Yehova loletsa dama liri kaamba ka ubwino wathu?
13 Lingalirani nsonga yakuti Mulungu amalola kugonana mu ukwati mokha ndi kuletseratu dama. (Ahebri 13:4) Kodi kumvera lamulo limeneli kumakumanani chabwino chirichonse? Kodi Atate wakumwamba wachikondi angapange lamulo lokulandani chisangalalo m’moyo? Ndithudi ayi! Yang’anani pa zimene zikuchitika m’miyoyo ya mabwenzi anu omwe amanyalanyaza malamulo a makhalidwe abwino a Mulungu. Mimba zosafunidwa kaŵirikaŵiri zimaŵatsogolera ku kuzichotsa izo kapena, mwinamwake, ku maukwati a paubwana. M’zochitika zambiri chimatanthauza kulera mwana popanda mwamuna. Kuwonjezerapo, achichepere omwe amachita dama ‘akuchimwira matupi a iwo eni’ namadzipereka iwo eni ku matenda opatsirana mwakugonana. (1 Akorinto 6:18) Ndipo pamene wachichepere wodzipereka kwa Yehova achita dama, ziyambukiro zoipa za maganizo zingakhale zosakaza. Kuyesera kupondereza chipsyinjo cha chikumbumtima chaliŵongo kungapangitse kuthodwa maganizo ndi kusoŵa tulo. (Salmo 32:3, 4; 51:3) Pamenepa, kodi sikuli kowonekeratu kuti lamulo la Yehova loletsa dama lalinganizidwa kukutetezerani? Muli phindu lenileni m’kuchirikiza udongo wa makhalidwe!
14. Ponena za kanenedwe kakuti ukwati waubwana uli chitetezero, longosolani mmene tiyenera kuwonera mawu a Paulo pa 1 Akorinto 7:9 ndi 7:36.
14 Mosabisa, sikuli kopepuka kumamatira ku malamulo osamalitsa a Mulungu pa makhalidwe abwino. Chifukwa cha zimenezi, achichepere ena amaliza kuti chinjirizo labwino koposa ndilo kukwatira pamene adakali m’zaka zawo zauchichepere. ‘Ndiiko komwe,’ iwo amatero, ‘kodi 1 Akorinto 7:9 samanena kuti: “Ngati sadziŵa kudziletsa, akwatitsidwe; pakuti nkwabwino kukwatira koposa kutentha mtima”?’ Ngakhale ndi tero, lingaliro loterolo liri losapenya patali. Mawu a Paulo sakulunjikitsidwa kwa achichepere koma kwa awo ‘opitirira unamwali wawo.’ (1 Akorinto 7:36) Kaŵirikaŵiri aja omwe adakali mu unamwali wawo sadafikepo mokwanira mwamaganizo ndi uzimu kuchita ndi zididikizo ndi mathayo omwe amadza ndi ukwati. Journal of Marriage and the Family ikusimba kuti: “Anthu amene amakwatira mofulumira amakhala ndi chikhutiro chochepera chaukwati chifukwa chakuti samakonzekera kachitidwe ka thayo laukwati. Kusamalira thayo kosafikapo kumachepetsa chikhutiritso, komwe pambuyo pake kumatsogolera ku kusakhazikika kwaukwati.” Chotero yankho sindilo kukwatira pamene muli wachichepere, koma kusunga umbeta woyera kufikira mutakulitsa mikhalidwe yonse yofunikira kupanga ukwati wachipambano.
Dzisungeni Waudongo!
15. Kodi ndi njira zamphamvu zotani zimene zimafunikira ngati muti mukhalebe waudongo mwamakhalidwe?
15 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chifukwa chake fetsani ziŵalozo ziri padziko; dama, chidetso, chifunitso cha manyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chiri kupembedza mafano.” (Akolose 3:5) Inde, njira zolimba zifunikira; muyenera kufunitsitsadi kukhalabe waudongo m’makhalidwe. Kuchitira ndemanga pa mneni wolembedwa kuti “fetsani,” The Expositor’s Bible Commentary imati: “Mneniyu amasonyeza kuti sitimangofunikira kupondereza kapena kuletsa machitidwe ndi maganizo oipa. Tiyenera kuzichotsa, kuthetseratu njira yakale ya moyo. ‘Kupha kotheratu’ kungalongosole mphamvu yake. . . . Ponse paŵiri tanthauzo la mneniyo ndi mphamvu ya mawuwo zimasonyeza kachitidwe kamphamvu, kowawitsa ka chigamulo chaumwini.”—Yerekezani ndi Mateyu 5:27-30.
16. Kuti mukhalebe waudongo mwamakhalidwe, kodi nchifukwa ninji muyenera kuchita mwamphamvu kudzisunga waudongo mwamaganizo, ndipo kodi mungapambane motani pochita chimenecho?
16 Ngakhale ndi tero, kodi ndimotani mmene ‘mungaphere kotheratu’ kapena ‘kuchotseratu’ machitidwe ndi maganizo oipa? Yesu anafika pa nsonga ya vutolo pamene ananena kuti: “Pakuti mkati mwake mwa mitima ya anthu, [mutuluka malingaliro oipa: za dama, NW] . . . zachigololo, masiriro.” (Marko 7:21, 22) Mtima wophiphiritsira umaphatikizapo mphamvu za kuganiza, chomwe chiri chifukwa chake ukugwirizanitsidwa ndi “malingaliro.” Pamenepa, kuti mukhale waudongo m’makhalidwe, muyenera kukalamira kudzisunga waudongo m’maganizo. Motani? Popeza kuti maganizo amadyetsedwa mwa kuwona ndi kumva, mufunikira kuchenjera ndi zomwe mukupenya ndi maso anu, kupeŵa mabukhu, maprogramu a pa TV, kapena akanema omwe amasonyeza kapena kulola chisembwere cha kugonana. Ndiponso, mufunikira kukhala osamala ponena za zimene mumamvetsera ndi makutu anu, kupeŵa nyimbo zokhala ndi mawu olongosola kugonana. Kutenga kaimidwe koteroko kumafunikiradi kulimba mtima, makamaka pamaso pa mabwenzi anu, koma kuteroko kudzakuthandizani kukhalabe waudongo mwa makhalidwe ndi kusungabe ulemu wanu.
17. Kodi nchifukwa ninji chidetso chamakhalidwe sichifunikira ngakhale kutchulidwa pakati panu?
17 Mtumwi Paulo anaperekanso uphungu wakuti: “Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima.” (Aefeso 5:3; onaninso vesi 12.) Chotero chidetso cha makhalidwe sichiyenera ngakhale kutchulidwa, ndiko kuti, kukambitsirana kapena kuchipanga kukhala mutu wankhani yanjerengo. Nkulekeranji? Monga momwe katswiri wa Baibulo William Barclay akuchiikira icho kuti: “Kulankhula ponena za chinthu, kuchitira chinthu njerengo, kuchipanga kukhala mutu wankhani wa kukambitsirana wakaŵirikaŵiri kuli kuchizamitsa m’maganizo, ndi kubweretsa pafupi kachitidwe kenikeni ka icho.” (Yakobo 1:14, 15) Chimafunikiradi kugamulapo kwenikweni ‘kusunga pakamwa panu ndi cha mkamwa,’ makamaka pamene achichepere ena akusimba njerengo zoipa kapena kugwiritsira ntchito chilankhulo chopeka kulongosola machitidwe a kugonana. (Salmo 39:1) Koma mwakukhala wowongoka ndi waudongo, mudzakondweretsa mtima wa Yehova.—Salmo 11:7; Miyambo 27:11.
18. (a) Kuti mupambane nkhondo yolimbana ndi chidetso chamakhalidwe, nchifukwa ninji sikokwanira kukana maganizo ndi kalankhulidwe kodetsedwa? (b) Kodi mungapindule motani ndi uphungu wa Paulo kwa Afilipi?
18 Kuti mupambane nkhondo yolimbana ndi chidetso chamakhalidwe, sikuli kokwanira kukana malingaliro ndi kalankhulidwe koipa. Mwambi wa ku China umanena kuti: “Maganizo opanda kanthu ali otseguka ku malingaliro onse.” (Yerekezani ndi Mateyu 12:43-45.) Paulo anazindikira kufunika kwa kudzaza maganizo ndi malingaliro abwino, oyera. Nchifukwa chake, iye anasonkhezera Afilipi kuti: “Zinthu zirizonse zowona, zirizonse zolemekezeka, zirizonse zolungama, zirizonse zoyera, zirizonse zokongola, zirizonse zomveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi [‘zipangeni kukhala nkhani ya chiwunikiro chosamalitsa’c].”—Afilipi 4:8.
19. Kodi nchifukwa ninji muyenera kupanga phunziro lakhama la Mawu a Mulungu, ndipo kodi ndi m’njira yotani kuteroko kudzakuthandizirani kukhalabe waudongo mwamakhalidwe?
19 Izi zimatanthauza kupanga phunziro lakhama la Mawu a Mulungu. (Yoswa 1:8; Salmo 1:2) Iko kudzalimbitsa maganizo ndi mtima wanu ndipo kudzakuthandizani kukulitsa unansi waumwini wathithithi ndi Yehova. Chotero mudzakhala m’malo abwinopo kwambiri kutsutsa ziyeso za kudziloŵetsa m’machitidwe opanda udongo. Mwakutero simudzadzetsa ngozi ya kunyozetsa dzina la Yehova ndi chitonzo ku banja lanu ndi mpingo. M’malomwake, mudzagwiritsira ntchito mphamvu ndi nyonga ya uchichepere wanu m’njira imene pambuyo pake simudzachitira chisoni. Inde, mudzatsatira njira ya udongo wa makhalidwe, kukongoladi kwa achichepere opezedwa akutumikira Yehova!—Miyambo 3:1-4.
[Mawu a M’munsi]
a Onani makope a Galamukani! a March 8, 1988, masamba 12-14; November 8, 1987, masamba 18-20 (Chingelezi); ndi March 8, 1988, masamba 20-3 (Chingelezi).
b Galamukani! September 8, 1986, masamba 10-12.
c The Expositor’s Greek Testament.
Achichepere—Kodi Mukayankha Motani?
◻ Kodi nchifukwa ninji muyenera kusunga muyezo wapamwamba wa udongo wa makhalidwe?
◻ Kodi ndi zididikizo zotani zimene zimapangitsa kusungabe kaimidwe kaudongo kwa Mulungu kukhala chitokoso?
◻ Kodi nchiyani chimene chingakuthandizeni kufikira chitokoso cha kukhalabe waudongo mwamakhalidwe?
◻ Kodi ndi njira zamphamvu zotani zimene zimafunikira ngati muti mudzisunge waudongo?
[Chithunzi patsamba 13]
Ambiri a awo omwe adakali mu kukula kwa uchichepere adakali aang’ono kuti asamalire mathayo aukholo