Pangani Chiphunzitso Cholamitsa Kukhala Njira Yanu ya Moyo
“Chipembedzo chipindula zonse.”—1 TIMOTEO 4:8.
1, 2. Kodi anthu amafika pati posonyeza nkhaŵa kaamba ka thanzi lawo, ndi zotulukapo zotani?
ANTHU ochuluka amavomereza msanga kuti thanzi labwino lili limodzi la chuma chamtengo wapatali koposa m’moyo. Amawonongera nthaŵi yaikulu kwambiri ndi ndalama zochuluka pa kusungitsa thanzi lawo lakuthupi ndi kutsimikizira kuti akulandira chisamaliro choyenera cha mankhwala pamene chifunikira. Mwachitsanzo, ku United States, mtengo wapachaka wosamalira thanzi m’chaka chaposachedwapa unali woposa $900,000,000,000. Zimenezo ndi ndalama zoposa $3,000 pachaka pa mwamuna, mkazi, ndi mwana aliyense m’dziko limenelo, ndipo mtengo wa munthu aliyense m’maiko otukuka suli wosiyana kwambiri.
2 Kodi kuwonongedwa konseku kwa nthaŵi, mphamvu, ndi ndalama kwadzetsanji? Ndithudi palibe amene angakane kuti, kwakukulukulu, tili ndi zipatala ndi makonzedwe opita patsogolo kwambiri lerolino kuposa panthaŵi ina m’mbiri. Komabe, zimenezi sizimangodzetsa moyo wathanzi pamenepo. Kwenikweni, m’nkhani yofotokoza programu yazaumoyo yolinganizidwa kaamba ka United States, prezidenti ananena kuti kuwonjezera pa “mtengo wopambanitsa wa chiwawa m’dziko lino,” nzika za United States “zili ndi ziŵerengero zapamwamba za AIDS, za kusuta ndi kumwa kopambanitsa, za kutenga mimba paubwana, za ana obadwa osakhwima” kuposa dziko lina lililonse lotukuka. Kodi anamaliza motani? “Tiyenera kusintha njira zathu ngati tifunadi kukhala athanzi monga anthu.”—Agalatiya 6:7, 8.
Njira Yolamitsa ya Moyo
3. Polingalira mwambo wamakedzana Wachigiriki, kodi ndi uphungu wotani umene Paulo anapereka?
3 M’zaka za zana loyamba, Agiriki anali otchuka chifukwa cha kudzipereka kwawo pa mwambo wolimbitsa thupi, kukuza thupi, ndi mipikisano yamaseŵera. Chifukwa cha mkhalidwe umenewu, mtumwi Paulo anauziridwa kulembera wachichepere Timoteo kuti: “Chizoloŵezi cha thupi chipindula pang’ono, koma chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.” (1 Timoteo 4:8) Chotero, Paulo anali kunena zimene anthu lerolino akuyamba kuvomereza, ndiko kuti, makonzedwe azamankhwala kapena olimbitsa thupi samalonjeza njira yolamitsa ya moyo. Komabe, Paulo akutitsimikizira kuti chofunika koposa ndicho kukulitsa thanzi lauzimu ndi kupembedza.
4. Kodi ndi ati amene ali mapindu a kupembedza?
4 Njira yotero ili yopindulitsa mu “moyo uno” chifukwa chakuti imapereka chinjirizo ku zinthu zonse zovulaza zimene anthu osapembedza, kapena awo amene ali chabe ndi “maonekedwe a chipembedzo,” amadzidzetsera. (2 Timoteo 3:5; Miyambo 23:29, 30; Luka 15:11-16; 1 Akorinto 6:18; 1 Timoteo 6:9, 10) Awo amene amalola chipembedzo kuumba miyoyo yawo ali ndi ulemu woyenera pa malamulo ndi zofuna za Mulungu, ndipo umenewo umawasonkhezera kupangitsa chiphunzitso cholamitsa cha Mulungu kukhala njira yawo ya moyo. Njira yotero imawadzetsera thanzi lauzimu ndi lakuthupi, chikhutiro, ndi chimwemwe. Ndipo iwo ‘akudzikundikira okha maziko okoma ku nyengo ikudzayi, kuti akagwire moyo weniweniwo.’—1 Timoteo 6:19.
5. Kodi ndi malangizo otani amene Paulo anapereka m’chaputala chachiŵiri cha kalata yake kwa Tito?
5 Popeza kuti moyo wotsogozedwa ndi chiphunzitso cholamitsa cha Mulungu umadzetsa madalitso otero tsopano ndi mtsogolo, tifunikira kudziŵa, mwanjira zogwira ntchito, mmene tingapangire chiphunzitso cholamitsa cha Mulungu kukhala njira yathu ya moyo. Mtumwi Paulo anapereka yankho m’kalata yake kwa Tito. Tidzasamalira kwambiri chaputala chachiŵiri cha buku limenelo, mmene iye analangiza Tito ‘kulankhula zimene ziyenera chiphunzitso cholamitsa.’ Ndithudi, tonsefe, achichepere ndi achikulire, amuna ndi akazi, tingapindule ndi “chiphunzitso cholamitsa” chotero lerolino.—Tito 1:4, 5; 2:1.
Uphungu kwa Amuna Akulu
6. Kodi ndi uphungu wotani wa “[amuna] okalamba” umene Paulo anapereka, ndipo nchifukwa ninji kuchita kwake zimenezo kunali kukoma mtima?
6 Choyamba, Paulo anali ndi uphungu kwa amuna akulu mumpingo. Chonde ŵerengani Tito 2:2. “[Amuna, NW] okalamba,” monga gulu, amalemekezedwa ndipo amayembekezeredwa kukhala zitsanzo za chikhulupiriro ndi kudalirika. (Levitiko 19:32; Miyambo 16:31) Chifukwa cha zimenezi, ena angazengereze kupereka uphungu kapena malingaliro kwa amuna akulu pankhani zimene sizili zazikulu kwambiri. (Yobu 32:6, 7; 1 Timoteo 5:1) Chifukwa chake, Paulo akusonyeza kukoma mtima mwa kuyamba kukambitsirana ndi amuna akulu, ndipo kungakhale bwino kwa iwo kulabadira mawu a Paulo ndi kutsimikizira kuti iwowo, mofanana ndi Paulo, ayenera kutsanziridwa.—1 Akorinto 11:1; Afilipi 3:17.
7, 8. (a) Kodi kukhala “odzisunga” kumaphatikizaponji? (b) Kodi nchifukwa ninji kukhala “olemekezeka” kuyenera kulinganizidwa ndi kukhala “olama m’maganizo”?
7 Choyamba, amuna akulu Achikristu ayenera kukhala “odzisunga.” Ngakhale kuti liwu loyambirira linganene za chizoloŵezi cha kumwa (“osaledzera,” Kingdom Interlinear), lilinso ndi tanthauzo la kukhala atcheru, anzeru, kapena kukhala amaso. (2 Timoteo 4:5; 1 Petro 1:13) Chotero, kaya ndi m’kumwa kapena m’zinthu zina, amuna akulu ayenera kukhala odzisunga, osachita monkitsa kapena mopambanitsa.
8 Ndiyeno, ayeneranso kukhala “olemekezeka” ndi “olama m’maganizo.” (NW) Kukhala olemekezeka, kapena aulemu, olambika, ndi oyenerera ulemu, kaŵirikaŵiri kumadza ndi msinkhu. Komabe, ena angakhale olemekezeka mopambanitsa, akumakhala osalola njira zochita zinthu mwamphamvu za achichepere. (Miyambo 20:29) Nchifukwa chake, ‘kulemekezeka’ kwalinganizidwa ndi ‘kulama m’maganizo.’ Amuna akulu afunikira kusunga kulemekezeka koyenerana ndi msinkhu, koma panthaŵi imodzimodziyo kukhala achikatikati, akumalamulira kotheratu malingaliro awo ndi mtima.
9. Kodi nchifukwa ninji amuna akulu ayenera kukhala olama m’chikhulupiriro ndi m’chikondi ndipo makamaka m’chipiriro?
9 Chotsirizira, amuna akulu ayenera kukhala “olama m’chikhulupiriro, m’chikondi, m’chipiriro.” M’zolemba zake, Paulo nthaŵi zambiri anaika chikhulupiriro ndi chikondi pamodzi ndi chiyembekezo. (1 Akorinto 13:13; 1 Atesalonika 1:3; 5:8) Panopa anaika “chipiriro” m’malo mwa “chiyembekezo.” Mwinamwake nchifukwa chakuti kutaya mtima kungayambe mosavuta chifukwa cha ukalamba. (Mlaliki 12:1) Komabe, monga momwe Yesu anasonyezera, “iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.” (Mateyu 24:13) Ndiponso, achikulire ali zitsanzo zabwino kwa onse osati chabe chifukwa cha msinkhu kapena chidziŵitso koma chifukwa cha mikhalidwe yauzimu yolimba—chikhulupiriro, chikondi, ndi chipiriro.
Kwa Akazi Akulu
10. Kodi ndi uphungu wotani umene Paulo akupereka kwa “akazi okalamba” mumpingo?
10 Kenako Paulo anatembenuzira maganizo ake kwa akazi akulu mumpingo. Chonde ŵerengani Tito 2:3. “Akazi okalamba” ndiwo ziŵalo zokulirapo pakati pa akazi mumpingo, kuphatikizapo akazi a “amuna okalamba” ndi amayi ndi agogo aakazi a ziŵalo zina. Pokhala otero, angakhale ndi chisonkhezero chokulirapo, chabwino kapena choipa. Nchifukwa chake Paulo anayamba mawu ake mwa kunena kuti “momwemonso,” kutanthauza kuti “akazi okalamba” nawonso ali ndi mathayo ena ake amene ayenera kuchita kuti akwaniritse mbali yawo mumpingo.
11. Kodi makhalidwe oyenera anthu oyera n’ngotani?
11 Choyamba, “akazi okalamba akhale nawo makhalidwe oyenera anthu oyera,” anatero Paulo. “Makhalidwe” ali chisonyezero chakunja cha mkhalidwe wamkati ndi umunthu wa munthu, zosonyezedwa ponse paŵiri ndi khalidwe ndi kaonekedwe. (Mateyu 12:34, 35) Pamenepa, kodi mkhalidwe kapena umunthu wa mkazi wokalamba Wachikristu uyenera kukhala wotani? Monga mwa mawuwo, ‘woyenera anthu oyera.’ Ameneŵa atembenuzidwa kuchokera ku liwu Lachigiriki limene limatanthauza “chimene chili choyenera mwa anthu, zochita kapena zinthu zopatulidwira Mulungu.” Ndithudi umenewu ndi uphungu woyenera polingalira za chisonkhezero chimene iwo ali nacho pa ena, makamaka akazi ang’ono mumpingo.—1 Timoteo 2:9, 10.
12. Kodi ndi kugwiritsira ntchito molakwa lilime kotani kumene kuyenera kupeŵedwa?
12 Kenako pakutsatira zinthu zoipa ziŵiri: “osadyerekeza, osakodwa nacho chikondi cha pa vinyo.” Kuikidwa m’gulu limodzi kwa zinthu ziŵiri zimenezi nkokondweretsa. “M’nthaŵi zamakedzana, pamene vinyo anali chakumwa chokha,” akutero Profesa E. F. Scott, “panali patimapwando tawo tavinyo pamene akazi okalamba anali kuwonongera mbiri ya anansi awo.” Kaŵirikaŵiri akazi amadera nkhaŵa anthu kwambiri kuposa amuna, zimene zili bwino. Komabe, nkhaŵayo ingazimiririke nkukhala miseche ndipo ngakhale kudyerekeza, makamaka pamene lilime lamasulidwa ndi vinyo. (Miyambo 23:33) Kunena zoona, onse amene akulondola njira yolamitsa ya moyo, amuna ndi akazi, angachite bwino kusamala za mbuna imeneyi.
13. Kodi ndi mwanjira zotani zimene akazi akulu angakhalire aphunzitsi?
13 Kuti agwiritsire ntchito nthaŵi imene ali nayo mwanjira yabwino, akazi akulu akulimbikitsidwa kukhala “akuphunzitsa zokoma.” Kwinakwake, Paulo anapereka malangizo omveka akuti akazi sayenera kukhala aphunzitsi mumpingo. (1 Akorinto 14:34; 1 Timoteo 2:12) Komabe, zimenezi sizimawaletsa kugaŵira mabanja awo ndi anthu onse chidziŵitso chamtengo wapatali cha Mulungu. (2 Timoteo 1:5; 3:14, 15) Akhozanso kuchita zabwino zochuluka mwa kukhala zitsanzo Zachikristu kwa akazi ang’ono mumpingo, monga momwe mavesi otsatira asonyezera.
Kwa Akazi Ang’ono
14. Kodi ndimotani mmene akazi ang’ono Achikristu amasonyezera kulinganizika posamalira ntchito zawo?
14 Polimbikitsa akazi akulu kukhala “akuphunzitsa zokoma,” Paulo kwenikweni anatchula akazi ang’ono. Chonde ŵerengani Tito 2:4, 5. Pamene kuli kwakuti ochuluka a malangizowo asumikidwa pa nkhani zapanyumba, akazi ang’ono Achikristu sayenera kupyola malire, akumalola nkhaŵa ya zinthu zakuthupi kulamulira miyoyo yawo. Mmalomwake, iwo ayenera kukhala “[olama m’maganizo, oyera, NW], . . . okoma,” ndipo koposa zonse, okonzeka kuchirikiza makonzedwe Achikristu aumutu, “kuti mawu a Mulungu angachitidwe mwano.”
15. Kodi nchifukwa ninji akazi ang’ono ambiri mumpingo ayenera kuyamikiridwa?
15 Lerolino, mkhalidwe wabanja wasintha kwambiri kusiyana ndi mmene unalili m’tsiku la Paulo. Mabanja ambiri ali ogaŵanika pa chikhulupiriro, ndipo ena ali ndi kholo limodzi lokha. Ngakhale mu otchedwa mabanja amwambo, sikofala kwambiri kwa mkazi kapena mayi kukhala wosunga panyumba wanthaŵi yonse. Zonsezi zimaika chitsenderezo ndi thayo lalikulu pa akazi ang’ono Achikristu, koma zimenezi sizimawachotsera mathayo awo a Malemba. Chotero, nkosangalatsa kuona akazi ang’ono ambiri okhulupirika akulimbikira kulinganiza ntchito zawo namakhozabe kuika zinthu Zaufumu poyamba, ena akumakhala ngakhale muutumiki wanthaŵi yonse monga apainiya othandiza kapena okhazikika. (Mateyu 6:33) Iwo ayeneradi kuyamikiridwa!
Kwa Anyamata
16. Kodi ndi uphungu wotani umene Paulo anali nawo kwa anyamata, ndipo nchifukwa ninji uli wapanthaŵi yake?
16 Ndiyeno Paulo anatchula anyamata, kuphatikizapo Tito. Chonde ŵerengani Tito 2:6-8. Polingalira za njira zopulupudza ndi zowononga za achichepere ambiri lerolino—kusuta, kugwiritsira ntchito molakwa anamgoneka ndi zakumwa zoledzeretsa, chisembwere, ndi zochita zina zadziko, zonga maseŵera achiwawa ndi nyimbo ndi zosangulutsa zoipa—umenewu ulidi uphungu wapanthaŵi yake kwa achichepere Achikristu amene akufuna kutsatira njira yolamitsa ndi yokhutiritsa ya moyo.
17. Kodi mnyamata angakhale motani ‘wolama m’maganizo’ ndi “chitsanzo cha ntchito zabwino”?
17 Mosiyana ndi achichepere a dziko, mnyamata Wachikristu ayenera kukhala ‘wolama m’maganizo’ ndi “chitsanzo cha ntchito zabwino.” Paulo anafotokoza kuti maganizo olama ndi achikulire amapezedwa, osati ndi awo amene amangophunzira, koma ndi awo amene “mwa kuchita nazo anazoloŵeretsa zizindikiritso zawo kusiyanitsa chabwino ndi choipa.” (Ahebri 5:14) Nkwabwino chotani nanga kuona achichepere akupereka nthaŵi yawo ndi nyonga kuti akhale ndi phande lokwanira m’ntchito zambiri za mumpingo Wachikristu, mmalo mwa kuwonongera nyonga yawo yaunyamata pa zinthu zadyera! Mwa kuchita motero, iwo, mofanana ndi Tito, angakhale zitsanzo za “ntchito zabwino” mumpingo Wachikristu.—1 Timoteo 4:12.
18. Kodi kumatanthauzanji kukhala osavunda m’chiphunzitso, olemekezeka m’zochita, ndi mawu olama?
18 Anyamata akukumbutsidwa kuti ayenera ‘m’chiphunzitso [chawo] aonetsere chosavunda, ulemekezeko, mawu olama osatsutsika.’ Chiphunzitso chomwe chili “chosavunda” chiyenera kuzikidwa zolimba pa Mawu a Mulungu; nchifukwa chake, anyamata ayenera kukhala ophunzira Baibulo akhama. Mofanana ndi amuna akulu, anyamata ayeneranso kukhala olemekezeka. Afunikira kuzindikira kuti kukhala mtumiki wa Mawu a Mulungu kuli thayo lalikulu, ndipo chotero ayenera kukhala ndi ‘mayendedwe oyenera Uthenga Wabwino.’ (Afilipi 1:27) Mofananamo mawu awo ayenera kukhala “olama” ndi “osatsutsika” kotero kuti asapatse otsutsa chifukwa chodandaulira.—2 Akorinto 6:3; 1 Petro 2:12, 15.
Kwa Akapolo ndi Atumiki
19, 20. Kodi ndimotani mmene awo olembedwa ntchito ndi anthu ena ‘angakometsere chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu’?
19 Pomalizira pake, Paulo anatembenukira kwa awo amene ali olembedwa ntchito ndi anthu ena. Chonde ŵerengani Tito 2:9, 10. Lerolino ambiri mwa ife sali akapolo kapena atumiki, koma ambiri ali olembedwa ntchito ndi antchito opereka utumiki kwa ena. Chotero, malamulo a mkhalidwe otchulidwa ndi Paulo amagwiranso ntchito lerolino.
20 Kukhala ‘omvera ambuye awo . . . m’zonse’ kumatanthauza kuti Akristu olembedwa ntchito ayenera kusonyeza ulemu weniweni kwa owalemba ntchito ndi akapitawo. (Akolose 3:22) Ayeneranso kukhala ndi mbiri ya kukhala antchito oona mtima, akumachita ntchito yonse ya patsiku monga mangawa a wowalemba ntchito. Ndipo ayenera kusunga miyezo yapamwamba ya khalidwe Lachikristu kumalo awo a ntchito mosasamala kanthu za makhalidwe a ena kumeneko. Zonsezi zili choncho “kuti akakometsere chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu m’zinthu zonse.” Ndi nthaŵi zambiri chotani nanga pamene timamva zotulukapo zokondweretsa pamene openyerera oona mtima alabadira choonadi chifukwa cha khalidwe labwino la Mboni zimene amagwira nazo ntchito kapena zolembedwa ntchito! Imeneyi ndi mphotho imene Yehova amaika pa awo amene amatsatira chiphunzitso cholamitsa ngakhale kumalo awo a ntchito.—Aefeso 6:7, 8.
Anthu Oyeretsedwa
21. Kodi nchifukwa ninji Yehova wapereka chiphunzitso cholamitsa, ndipo tiyenera kulabadira motani?
21 Chiphunzitso cholamitsa chimene Paulo anafotokoza sichili chabe mpambo wa malamulo a khalidwe kapena malingaliro a makhalidwe umene tingaonemo pamene tifuna. Paulo anapitiriza kulongosola chifuno chake. Chonde ŵerengani Tito 2:11, 12. Chifukwa cha chikondi chake ndi chisomo pa ife, Yehova Mulungu wapereka chiphunzitso cholamitsa kotero kuti tingaphunzire kukhala ndi moyo wachifuno ndi watanthauzo m’nthaŵi zino zovuta ndi zowopsa. Kodi muli wofunitsitsa kulandira ndi kupanga chiphunzitso cholamitsa kukhala njira yanu ya moyo? Kuchita motero kudzatanthauza chipulumutso chanu.
22, 23. Kodi timapeza madalitso otani mwa kupanga chiphunzitso cholamitsa kukhala njira yathu ya moyo?
22 Koposa zimenezo, kupanga chiphunzitso cholamitsa kukhala njira yathu ya moyo kumatidzetsera mwaŵi wapadera tsopano lino ndi chiyembekezo cha mtsogolo chachimwemwe. Chonde ŵerengani Tito 2:13, 14. Ndithudi, kupanga chiphunzitso cholamitsa kukhala njira yathu ya moyo kumatilekanitsa ndi dziko loipa ndi lomafa monga anthu oyeretsedwa. Mawu a Paulo amafanana ndi zikumbutso za Mose kwa ana a Israyeli pa Sinai: “Ndipo Yehova . . . akukulitseni koposa amitundu onse anawalenga, wolemekezeka, womveka dzina, ndi waulemu; ndi kuti mukhale mtundu wa anthu wopatulikira Yehova Mulungu wanu monga ananena.”—Deuteronomo 26:18, 19.
23 Tiyenitu tisamalire mwaŵi wa kukhala anthu oyeretsedwa a Yehova mwa kupanga chiphunzitso cholamitsa kukhala njira yathu ya moyo! Nthaŵi zonse khalani atcheru kukana mtundu uliwonse wa kusapembedza ndi zilakolako zadziko, motero kukhalabe oyeretsedwa ndi oyenera kugwiritsiridwa ntchito ndi Yehova m’ntchito yaikulu imene akuichititsa lerolino.—Akolose 1:10.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi nchifukwa ninji chipembedzo chipindula zonse?
◻ Kodi amuna ndi akazi akulu Achikristu angalondole motani chiphunzitso cholamitsa monga njira ya moyo?
◻ Kodi nchiphunzitso cholamitsa chiti chimene Paulo anali nacho kaamba ka anyamata ndi akazi ang’ono mumpingo?
◻ Kodi nziti zimene zili mwaŵi ndi dalitso zimene tingakhale nazo ngati tipanga chiphunzitso cholamitsa kukhala njira yathu ya moyo?
[Zithunzi patsamba 18]
Ambiri lerolino akugwiritsira ntchito uphungu wa pa Tito 2:2-4