Pitirizanibe Kumangirirana
“Nkhani yonse yovunda isatuluke m’kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira.”—AEFESO 4:29.
1, 2. (a) Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe moyenerera kuti kulankhula kuli chozizwitsa? (b) Kodi ndichenjezo lotani limene liri loyenerera ponena za mmene timagwiritsirira ntchito lilime lathu?
“KULANKHULA ndiko ulusi wodabwitsa umene umamangirira mabwenzi, mabanja ndi zitaganya pamodzi . . . Mwakugwiritsira ntchito maganizo aumunthu ndi kugwirira ntchito pamodzi kwa minyewa ya [lilime], timaumba mawu amene amasonkhezera chikondi, nsanje, ulemu—ndipotu malingaliro alionse aumunthu.”—Hearing, Taste and Smell.
2 Lilime lathu siliri chabe chiŵalo chomezera kapena cholaŵira; liri mbali ya luso lathu lakukambitsirana zimene tikulingalira ndi kuganiza. “Lilimenso liri chiŵalo chaching’ono,” analemba motero Yakobo. “Timayamika [Yehova, NW] ndi Atate nalo; nalonso timatemberera anthu, okhala monga mwa mafanizidwe a Mulungu.” (Yakobo 3:5, 9) Inde, tingathe kugwiritsira ntchito malilime athu m’njira zabwino, zonga ngati kutamanda Yehova. Koma pokhala opanda ungwiro, tingathe mosavuta kugwiritsira ntchito malilime athu kulankhula zinthu zovulaza kapena zoipa. Yakobo analemba kuti: “Abale anga, izi siziyenera kutero.”—Yakobo 3:10.
3. Kodi tiyenera kuika chisamaliro pazinthu ziŵiri zotani za kulankhula kwathu?
3 Popeza palibe munthu amene angalamulire lilime lake kotheratu, ndithudi tiyenera kuyesetsa kuwongokera. Mtumwi Paulo akutipatsa uphungu wakuti: “Nkhani yonse yovunda isatuluke m’kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.” (Aefeso 4:29) Tawonani kuti chichizo limeneli liri ndi mbali ziŵiri: zimene tiyenera kuyesetsa kupeŵa ndi zimene tiyenera kuyesa kuchita. Tiyeni tipende mbali ziŵiri zimenezi.
Kupeŵa Kulankhula Kovunda
4, 5. (a) Kodi Akristu ali ndi nkhondo yotani ponena za kutukwana? (b) Kodi nchitsanzo chotani chimene chingayenerere mawu akuti “nkhani yovunda”?
4 Choyamba Aefeso 4:29 ikutifulumiza kuti: “Nkhani yonse yovunda isatuluke m’kamwa mwanu.” Zimenezo zingakhale zovuta. Chifukwa chimodzi nchakuti kutukwana kuli kofala kwambiri m’dziko lotizinga. Achichepere ambiri Achikristu amamva kutukwana masiku onse, pakuti anzawo akusukulu angaganize kuti kutero kumawonjezera chigogomezero kapena kuwachititsa kuwonekera amphamvupo. Sitingathe kupeŵa kotherathu kumva mawu otukwana, koma tingathe ndipo tiyenera kuyesayesa zolimba kusamwerekera nawo. Alibe malo m’maganizo kapena m’kamwa mwathu.
5 Logogomezera mawu a Paulo ndilo liwu Lachigiriki limene limasonya kunsomba kapena chipatso chowola. Tayerekezerani zimenezi: Mukuwona munthu akutaya mtima ndiyeno kukwiya kotherathu. Potsirizira pake ayamba kulalata, ndipo muwona nsomba yovunda ikutuluka m’kamwa mwake. Ndiyeno muwona zipatso zovunda, zonunkha zikutuluka, kumwazikira onse ali pafupi. Kodi munthuyo ndani? Kukakhala koipa chotani nanga ngati anali mmodzi wa ife! Komabe, chitsanzo chimenechi chingayenerere ngati ‘titulutsa nkhani yonse yovunda m’kamwa mwathu.’
6. Kodi ndimotani mmene Aefeso 4:29 amagwirira ntchito m’kalankhulidwe kotsutsa ndi kosuliza?
6 Kugwira ntchito kwina kwa Aefeso 4:29 nkwakuti ife tipeŵe kusuliza mosalekeza. Kunena zawona, tonsefe tiri ndi malingaliro ndi zosankha ponena za zinthu zimene sitimakonda kapena kuvomereza, koma kodi munakhalapo pafupi ndi munthu amene amawonekera kukhala ndi mawu otsutsa (kapena mawu ochuluka) ponena za munthu aliyense, malo, kapena chinthu chotchulidwa? (Yerekezerani ndi Aroma 12:9; Ahebri 1:9.) Zolankhula zake zimalefula, zimavutitsa maganizo, kapena kuwononga. (Salmo 10:7; 64:2-4; Miyambo 16:27; Yakobo 4:11, 12) Iye sangazindikire mmene amafananirana ndi osuliza ofotokozedwa ndi Malaki. (Malaki 3:13-15) Angazizwe chotani nanga ngati munthu woima pafupi amuuza kuti nsomba yovunda kapena zipatso zovunda zinali kutuluka m’kamwa mwake!
7. Kodi nkudzipenda kotani kumene aliyense wa ife ayenera kuchita?
7 Popeza kuti nkosavuta kuzindikira pamene munthu wina mosalekeza alankhula mawu otsutsa kapena osuliza, tadzifunsani kuti, ‘Kodi ndimakhoterera kukukhala wotero? Kodi ndimaterodi?’ Kukakhala kwanzeru kusinkhasinkha nthaŵi ndi nthaŵi pampangidwe wa mawu athu. Kodi kwakukulukulu ali otsutsa, osuliza? Kodi timamveka mofanana ndi otonthoza atatu onyenga a Yobu? (Yobu 2:11; 13:4, 5; 16:2; 19:2) Bwanji osapeza mbali yabwino yonena? Ngati makambitsirano ali kwakukulukulu osuliza, bwanji osawasinthira kunkhani zomangirira?
8. Kodi Malaki 3:16 amapereka phunziro lotani ponena za kalankhulidwe, ndipo tingasonyeze motani kuti tikugwiritsira ntchito phunzirolo?
8 Malaki anasonyeza kusiyana kotere: “Iwo akuwopa Yehova analankhulana wina ndi mnzake; ndipo Yehova anawatchera khutu namva, ndi bukhu la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuwopa Yehova, nakumbukira dzina lake.” (Malaki 3:16) Kodi mwawona mmene Mulungu analabadirira kulankhula komangirira? Kodi chiyambukiro chothekera cha kukambitsirana kotero pa atsamwali chinali chotani? Ife enife tingaphuzire ponena za kalankhulidwe kathu ka tsiku ndi tsiku. Kudzakhala bwino koposa chotani nanga ngati kukambitsirana kwathu ndi kwa ena nthaŵi zonse kumasonyeza ‘nsembe yathu yakuyamika Mulungu.’—Ahebri 13:15.
Yesetsani Kumangirira Ena
9. Kodi nchifukwa ninji misonkhano Yachikristu iri nthaŵi yabwino kwambiri yakumangirira ena?
9 Misonkhano yampingo iri nthaŵi yabwino kwambiri yakulankhula ‘zirizonse zomangirira monga momwe kungafunikire, kuti zipatse chisomo kwa iwo akumva.’ (Aefeso 4:29) Tingathe kuchita zimenezo pokamba nkhani yopereka chidziŵitso cha Baibulo, kukhala ndi phande m’chitsanzo, kapena kupereka ndemanga m’nkhani zamafunso ndi mayankho. Motero timatsimikizira mawu a Miyambo 20:15 kukhala owona: “Milomo yodziŵa ndiyo chokometsera chamtengo wapatali.” Ndipo adziŵa ndani kuchuluka kwa mitima imene timafika kapena kumangirira?
10. Pambuyo pakupenda amene talankhula nawo kaŵirikaŵiri, kodi ndikusintha kotani kumene kungayenerere? (2 Akorinto 6:12, 13)
10 Nthaŵi imene msonkhano usanayambe kapena pambuyo pake njoyenerera kumangirira ena ndi makambitsirano abwino kwa omvetsera. Kungakhale kosavuta kuthera nyengo zimenezi m’kukambitsirana kosangalatsa ndi achibale ndi mabwenzi angapo apamtima amene timapeza bwino kukhala nawo. (Yohane 13:23; 19:26) Komabe, mogwirizana ndi Aefeso 4:29, bwanji osafunafuna ena olankhula nawo? (Yerekezerani ndi Luka 14:12-14.) Tikhoza kukonzekera pasadakhale kunena zoposa chabe moni wa muli bwanji wamasiku onse kapena wachidule kwa atsopano akutiakuti, okalamba, kapena achichepere, ngakhale kukhala pansi ndi achichepere kotero kuti tilingane ndi msinkhu wawo. Chikondwerero chathu chowona ndi nyengo zakulankhulana komangirira zidzachititsa ena kukhaladi okhoza kubwereza malingaliro a Davide pa Salmo 122:1.
11. (a) Kodi ndichizoloŵezi chotani chimene ena akulitsa ponena za malo okhala? (b) Kodi nchifukwa ninji ena mwadala amasinthasintha mipando yokhala?
11 China chothandizira kukambitsirana komangirira ndicho kusinthasintha mipando imene timakhalapo pamisonkhano. Nakubala amene ali ndi mwana angafunikire kukhala pafupi ndi chimbudzi, kapena wodwala angafunikire mpando wam’mbali, koma bwanji enafe? Chizoloŵezi wamba chingatichititse kukakhala pampando kapena mbali yakutiyakuti; ngakhale mbalame imabwerera mwachibadwa kuchisa chake. (Yesaya 1:3; Mateyu 8:20) Komabe, kunena mosabisa mawu, popeza kuti tingakhale paliponse, bwanji osasinthasintha malo athu—mbali ya kumanja, mbali ya kumanzere, pafupi ndi kutsogolo, ndi kwina kotero—ndipo motero kukhala wozoloŵerana bwinopo ndi abale osiyanasiyana? Popeza kuti palibe lamulo lakuti tichite zimenezi, akulu ndi ena okula msinkhu amene amasinthasintha mipando akupeza kukhala kosavutirapo kugaŵira zabwino kwa ambiri mmalo mwa mabwenzi apamtima angapo chabe.
Mangirirani mwa Njira Yaumulungu
12. Kodi ndichikhoterero choipa chotani chimene chawonekera m’mbiri yonse?
12 Chikhumbo cha Mkristu chakumangirira ena chiyenera kumsonkhezera kutsanzira Mulungu m’nkhaniyi koposa kutsatira chikhoterero chaumunthu chakupanga malamulo ambirimbiri.a Anthu opanda ungwiro kwazaka zambiri akhoterera kukulamulira anthu owazinga, ndipo ngakhale ena a atumiki a Mulungu agonja kuchikhoterero chimenechi. (Genesis 3:16; Mlaliki 8:9) M’nthaŵi ya Yesu atsogoleri Achiyuda ‘anamanga akatundu olemera pa ena koma iwo eni sanafune kuwasuntha.’ (Mateyu 23:4) Anasanduliza miyambo yosavulaza kukhala miyambo yofunikira kusungidwa. Chifukwa cha kupereka chisamaliro chawo chonkitsa kumalamulo aumunthu, ananyalanyaza zinthu zimene Mulungu anati nzofunika kwambiri. Palibe aliyense amene anamangiriridwa ndi kupanga kwawo malamulo osakhala amalemba; njira yawo sinali konse ya Mulungu.—Mateyu 23:23, 24; Marko 7:1-13.
13. Kodi nchifukwa ninji kuli kosayenera kupangira Akristu anzathu malamulo ambirimbiri?
13 Akristu amafuna kumamatira mowona mtima kumalamulo a Mulungu. Komabe, ngakhale ife tikhoza kukhala mikhole yachikhoterero chakupanga malamulo ambiri othodwetsa. Chifukwa ninji? Choyamba, zokonda kapena zofuna zimasiyana, chotero ena angavomereze zimene ena samakonda ndi kulingalira kuti ziyenera kupeŵedwa. Ndiponso Akristu amasiyana m’kupita kwawo patsogolo kulinga kuuchikulire wauzimu. Koma kodi kupanga malamulo ambiri kuli njira yaumulungu yothandizira wina kupita patsogolo kulinga kuuchikulire? (Afilipi 3:15; 1 Timoteo 1:19; Ahebri 5:14) Ngakhale pamene munthu akulondoladi njira imene ikuwonekera kukhala yonkitsa kapena yaupandu, kodi lamulo loletsa ndilo njira yothandizira yabwino koposa? Njira ya Mulungu njakuti oyeneretsedwa ayese kubwezeretsa wolakwayo mwakukambitsirana naye mofatsa.—Agalatiya 6:1.
14. Kodi malamulo amene Mulungu anapatsa Aisrayeli anatumikira zifuno zotani?
14 Zowona, pamene anali kugwiritsira ntchito Aisrayeli monga anthu ake, Mulungu anaperekadi malamulo mazana ambiri onena za kulambira pakachisi, nsembe, ngakhale ukhondo. Ameneŵa anali oyenerera mtundu wapaderawo, ndipo ambiri a malamulowo anali ndi tanthauzo laulosi ndipo anathandizira kutsogolera Ayuda kwa Mesiya. Paulo analemba kuti: “Chilamulo chidakhala namkungwi wathu wakutifikitsa kwa Kristu, kuti tikayesedwe olungama ndi chikhulupiriro. Koma popeza chadza chikhulupiriro, sitikhalanso omvera namkungwi.” (Agalatiya 3:19, 23-25) Pamene Chilamulo chinafafanizidwa pamtengo wozunzirapo, Mulungu sanapatse Akristu mpambo waukulu wa malamulo okhudza mbali zochuluka za moyo, monga ngati kuti amenewo anali njira yowamangiririra m’chikhulupiriro.
15. Kodi ndichitsogozo chotani chimene Mulungu wapereka kwa olambira Achikristu?
15 Ndithudi, sikuti tiri opanda lamulo. Mulungu amatilamula kupeŵa kupembedza mafano, dama ndi chigololo, ndi kugwiritsira ntchito mwazi molakwa. Iye mwachindunji amaletsa kuchita mbanda, kunama, kulambira mizimu, ndi machimo ena osiyanasiyana. (Machitidwe 15:28, 29; 1 Akorinto 6:9, 10; Chivumbulutso 21:8) Ndipo amapereka m’Mawu ake uphungu womvekera bwino pankhani zambiri. Komabe, kumlingo waukulu koposa Aisrayeli, tiri ndi thayo la kuphunzira ndi kugwiritsira ntchito malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo. Akulu angathe kumangirira ena mwakuwathandiza kupeza ndi kupenda malamulo amakhalidwe abwino ameneŵa mmalo mwa kungofunafuna kapena kupanga malamulo.
Akulu Amene Amamangirira
16, 17. Kodi atumwi anapereka chitsanzo chabwino chotani ponena za kupangira olambira anzawo malamulo?
16 Paulo analemba kuti: “Kumlingo umene ife tapanga kupita patsogolo, tiyeni tipitirizebe kuyenda molongosoka m’njira imodzimodziyi.” (Afilipi 3:16, NW) Mogwirizana ndi lingaliro laumulungu limenelo, mtumwiyo anachitira ena mwa njira imene inawamangirira. Mwachitsanzo, funso linabuka lakuti kaya kudya nyama imene ingakhale itachokera kukachisi wa mafano kukakhala koyenera. Kodi mkulu ameneyu, mwinamwake ncholinga cha kusasiyanitsa kapena kukhweketsa zinthu, anakhazikitsa lamulo lakutilakuti la Akristu onse mumpingo woyambirira? Ayi. Iye anazindikira kuti kusiyana kwa chidziŵitso ndi kupita patsogolo kulinga kuuchikulire kukanachititsa Akristuwo kupanga zosankha zosiyana. Ponena za iye, anali wotsimikiza mtima kupereka chitsanzo chabwino.—Aroma 14:1-4; 1 Akorinto 8:4-13.
17 Malemba Achikristu Achigiriki amasonyeza kuti atumwi anapereka uphungu wothandiza pankhani zina zaumwini, zonga ngati kavalidwe ndi kapesedwe, koma sanapange malamulo ogwira ntchito m’mikhalidwe yonse. Lerolino chimenechi nchitsanzo chabwino kwa oyang’anira Achikristu, amene ali okondweretsedwa m’kumangirira gulu. Ndipo chikupitirizadi njira yoyambirira imene Mulungu anatsatira ngakhale kwa Israyeli wamakedzana.
18. Kodi Yehova anapereka malamulo otani kwa Aisrayeli onena za kavalidwe?
18 Mulungu sanapatse Aisrayeli malamulo opambanitsa a kavalidwe. Mwachiwonekere amuna ndi akazi ankavala zofunda zofanana, kapena malaya akunja, ngakhale kuti a mkazi angakhale anali okometseredwa kapena amawonekedwe okongola kwambiri. Ndiponso amuna ndi akazi onse ankavala sa·dhinʹ, kapena theŵera. (Oweruza 14:12; Miyambo 31:24; Yesaya 3:23) Kodi ndimalamulo akavalidwe otani amene Mulungu anapereka? Amuna sanayenera kuvala zovala za akazi ndipo akazi nawonso sanayenera kuvala za amuna, mwachiwonekere ndi zolinga zakuchita mathanyula. (Deuteronomo 22:5) Kuti asonyeze kukhala kwawo osiyana ndi mitundu yowazinga, Aisrayeli anayenera kuika mphonje kumalaya awo, ndi chingwe cha bluu pamwamba pa mphonjezo, ndipo mwinamwake kuika thonje m’mphepete mwa chofunda. (Numeri 15:38-41) Kwakukulukulu chimenecho ndicho chitsogozo chokha chimene Chilamulo chinapereka ponena za kavalidwe.
19, 20. (a) Kodi ndichitsogozo chotani chimene Baibulo limapatsa Akristu chonena za kavalidwe ndi kapesedwe? (b) Kodi ndilingaliro lotani limene akulu ayenera kukhala nalo ponena za kupanga malamulo ophatikizapo mawonekedwe aumwini?
19 Popeza kuti Akristu sali pansi pa Chilamulo, kodi tiri ndi malamulo ena atsatanetsatane onena za kavalidwe kapena kukometsera operekedwa kwa ife m’Baibulo? Osati kwenikweni. Mulungu anapereka malamulo amakhalidwe abwino achikatikati amene tingathe kugwiritsira ntchito. Paulo analemba kuti: “Akazi adziveke okha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso; osati ndi tsitsi lake loluka, ndi golidi kapena malaya a mtengo wake wapatali.” (1 Timoteo 2:9) Petro anafulumiza kuti mmalo mosumika chisamaliro pakukometsera kwa kuthupi, akazi Achikristu ayenera kusumika chisamaliro pa “munthu wobisika wamtima, m’chovala chosawola cha mzimu wofatsa ndi wachete.” (1 Petro 3:3, 4) Chenicheni chakuti uphungu umenewo unalembedwa chimapereka lingaliro lakuti Akristu ena m’zaka za zana loyamba angakhale anafunikira kukhala odekha ndi odziletsa koposerapo m’kavalidwe ndi kapesedwe kawo. Komabe, mmalo mosankha—kapena kuletsa—masitayela ena, atumwiwo anangopereka uphungu womangirira.
20 Mboni za Yehova ziyenera ndipo zimalemekezedwa ndi anthu ambiri chifukwa cha mawonekedwe awo odekha. Komabe, masitayela amasiyana m’maiko osiyanasiyana ndipo ngakhale m’dera kapena mpingo. Ndithudi, mkulu amene ali ndi malingaliro amphamvu kapena wokonda kavalidwe ndi kapesedwe kakutikakuti angadzisankhire iyemwini zimenezo ndi banja lake. Koma ponena za gulu, iye afunikira kukumbukira mfundo ya Paulo yakuti: “Sikuti tichita ufumu pa chikhulupiriro chanu, koma tikhala othandizana nacho chimwemwe chanu; pakuti ndi chikhulupiriro muimadi.” (2 Akorinto 1:24) Inde, pokana zisonkhezero zirizonse zakukhazikitsira mpingo malamulo, akulu amayesayesa kumangirira chikhulupiriro cha ena.
21. Kodi ndimotani mmene akulu angaperekere chithandizo chomangirira ngati wina achita monkitsa m’kavalidwe?
21 Monga momwe zinaliri m’zaka za zana loyamba, nthaŵi zina munthu watsopano kapena wofooka kuuzimu angalondole njira yokaikiritsa kapena yosonyeza kupanda nzeru m’kavalidwe kapena kugwiritsira ntchito zodzola kumaso kapena majuwelo. Kodi nchiyani chingachitidwe? Panonso, Agalatiya 6:1 amapereka chitsogozo kwa akulu Achikristu amene mowona mtima amafuna kuthandiza. Mkulu asanagamule kupereka uphungu, angathe kupempha malingaliro kwa mkulu mnzake, kwenikweni sayenera kupita kwa mkulu amene iye amamdziŵa kuti amagwirizana ndi zofuna kapena malingaliro ake. Ngati mkhalidwe waudziko m’kavalidwe kapena kapesedwe uwonekera kukhala ukuyambukira ambiri mumpingo, bungwe la akulu likhoza kukambitsirana mmene lingaperekere chithandizo chabwino koposa, chonga ngati kukamba nkhani yomangirira mokoma mtima pamsonkhano kapena kupereka chithandizo kwa munthu aliyense payekha. (Miyambo 24:6; 27:17) Chonulirapo chawo chingakhale kuchirikiza lingaliro losonyezedwa pa 2 Akorinto 6:3 lakuti: ‘Sitikupatsa chokhumudwitsa konse m’chinthu chirichonse, kuti utumikiwo usanenezedwe.’
22. (a) Kodi nchifukwa ninji siziyenera kukhala zokhumudwitsa ngati pali malingaliro osiyana pang’ono? (b) Kodi nchitsanzo chabwino chotani chimene Paulo anapereka?
22 Akulu Achikristu ‘oŵeta gulu la Mulungu liri mwa iwo’ amafuna kuchita monga momwe Petro ananenera, ndiko kuti, osati ‘monga ochita ufumu pa iwo amene ali choloŵa cha Mulungu.’ (1 Petro 5:2, 3) Pochita ntchito yawo yachikondi, mafunso angabuke onena za nkhani zimene zingakhale ndi zokonda zathu zosiyana. Mwinamwake chingakhale chizoloŵezi cha m’malowo kuimirira poŵerenga ndime pa Phunziro la Nsanja ya Olonda. Makonzedwe a kagulu a utumiki wakumunda ndi zofunika zina zambiri zonena za uminisitala weniweniwo zingasamaliridwe malinga ndi zizoloŵezi zakumaloko. Komabe, kodi pangakhale cholakwa ngati wina achita mwanjira yosiyana pang’ono? Oyang’anira achikondi amakhumba kuti “zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka,” mawu amene Paulo anagwiritsira ntchito ponena za mphatso zozizwitsa. Koma mawu apatsogolo ndi apambuyo akusonyeza kuti cholinga chachikulu cha Paulo chinali cha “kumangirira . . . mpingo.” (1 Akorinto 14:12, 40) Sanasonyeze chikhoterero chirichonse chakupanga malamulo ambiri osatha, ngati kuti kulingana kotheratu kapena kugwira mtima kotheratu pochita zinthu ndiko kunali chonulirapo chake chachikulu. Iye analemba kuti: ‘Ambuye anatipatsa [ulamuliro] wakukumangirirani, ndipo sikugwetsera kwanu.’—2 Akorinto 10:8.
23. Kodi ndinjira zina zotani zimene tingatsanzirire chitsanzo cha Paulo cha kumangirira ena?
23 Mosakaikira Paulo anayesayesa kumangirira ena ndi mawu abwino ndi olimbikitsa. Mmalo moyanjana ndi kagulu kakang’ono ka mabwenzi, anayesetsa kucheza ndi abale ndi alongo ambiri, ponse paŵiri olimba kuuzimu ndi amene anafunikira kumangiriridwa kwambiri. Ndipo anagogomezera chikondi—mmalo mwa malamulo—pakuti “chikondi chimangirira.”—1 Akorinto 8:1.
[Mawu a M’munsi]
a M’banja malamulo osiyanasiyana angawonekere kukhala oyenerera, malinga ndi mikhalidwe. Baibulo limaloleza makolo kupangira ana awo aang’ono zosankha.—Eksodo 20:12; Miyambo 6:20; Aefeso 6:1-3.
Mfundo Zopenda
◻ Kodi nchifukwa ninji kusintha kuli koyenera ngati tikhoterera kukalankhulidwe kotsutsa kapena kosuliza?
◻ Kodi tingachitenji kuti tikhale omangirira kwambiri mumpingo?
◻ Kodi chitsanzo chaumulungu chonena za kupangira ena malamulo ambiri nchotani?
◻ Kodi nchiyani chidzathandiza akulu kupeŵa kupangira gulu malamulo aumunthu?