Chaputala 11
Yerusalemu Wapadziko Lapansi Mosiyana ndi Yerusalemu Wakumwamba
1. (a) Kodi kuwonongedwa kwa Yerusalemu kukakhala chinthu chatsopano? (b) Kodi nchifukwa ninji sikukakhala tsoka la mtundu wonse ngati Yerusalemu angawonongedwenso kachiŵiri?
AWO amene lerolino ali Ayuda akuthupi amatsimikiza kuti Yerusalemu wa ku Middle East adzakhalako kosatha. Ngakhale anthu a Dziko Lachikristu akali kulemekezabe mzinda umenewo umene Yesu anamalizirako uministala wake. Koma kodi zonsezi zimatsimikizira kupitirizabe kukhalako kwa mzindawo? Uwo unawonongedwapo kale, mu 607 B.C.E. ndi Ababulo ndi mu 70 C.E. ndi Aroma. Kodi kungatanthauze tsoka kwa anthu onse ngati kachiŵirinso ungawonongedwe? Ayi, mzindawo suuli wofunika kaamba ka madalitso a pangano la Abrahamu kuti asefukire kwa anthu. Ngakhale ponena za Abrahamu kwalembedwa: “Pakuti analindirira mudzi wokhala nawo maziko, mmisiri wake ndi womanga wake ndiye Mulungu.”—Ahebri 11:10.
2. (a) Kodi mtumwi Paulo amasonyeza motani kuti pali Yerusalemu wokwezeka kwambiri? (b) Kodi ndani amene ali Mwamuna wa Yerusalemu ameneyo, ndipo kodi ndani amene ali ana ake amene iye amambalira?
2 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Koma Yerusalemu wakumwamba uli waufulu, ndiwo amayi ŵathu.” (Agalatiya 4:26) Pamenepo iye anasonyeza kuti, Yerusalemu wakumwamba, anayenerana ndi Sara ndipo anali gulu longa mkazi la Abrahamu Wamkulu, Yehova Mulungu. Chifukwa chake, ana a “Yerusalemu wakumwamba” ndiwo Akristu obadwa ndi mzimu, monga Paulo.
“Yerusalemu Wakumwamba” Akhala Mzinda Wachifumu
3. (a) Kodi Yehova Mulungu mwiniyo anayamba liti kulamulira? (b) Kodi Yesu Kristu anakhazikitsidwira kuti pampando wachifumu, ndipo kodi zimenezi zinali ndi chiyambukiro chotani pa ufumu wa Yehova mwiniyo?
3 “Yerusalemu wakumwamba” wakhala ndi mbali yachifumu chiyambire kutha kwa “nthaŵi zoikidwiratu za amitundu” mu 1914. (Luka 21:24) Kuyambira panthaŵiyo kumkabe mtsogolo, Salmo 97:1 limagwira ntchito: “Yehova achita ufumu; dziko lapansi likondwere.” Mofananamo Salmo 99:1, 2 limagwira ntchito: “Yehova ndiye mfumu. . . . Yehova ndiye wamkulu m’Ziyoni; ndipo akwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.” Mu 1914 nthaŵi inadza yakuti iye aimike kupondereza Ufumuwo mu mzera wachifumu wa Davide, monga momwe unaimiridwira ndi mzinda umene kale unali wachifumu wa Yerusalemu. Chifukwa chake, iye anakhazika pampando wachifumu Mwana wake, Yesu Kristu, monga Mfumu padzanja Lake lamanja mu “Yerusalemu wakumwamba,” mwanjirayi kuupangitsa kukhala mzinda wachifumu. Ufumu wa Yehova mwini ukuchirikizidwa kapena kukulitsidwa ndi kuikidwa pampando wachifumu kwa Yesu Kristu kukhala Mfumu.
4. Kodi ndimwazochitika zotani zimene “Yerusalemu wakumwamba” amafikira kukhala mzinda wachifumu chiyambire 1914?
4 Chotero pambuyo pa kubadwa kwa Ufumu wakumwamba mu 1914 ndipo pambuyo pa kuchotsedwa kumwamba kwa Satana ndi ziŵanda zake, kunali koyenerera kulengeza kuti: “Tsopano zafika chipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Kristu wake; pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu, wa kuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku.” (Chivumbulutso 12:1-10) “Ulamuliro wa Kristu wake” unali wakuti Ameneyu alamulire monga Mfumu mu “Yerusalemu wakumwamba.” Ndithudi, uwo unafikira kukhala mzinda wachifumu m’chaka chosaiwalika chimenecho cha 1914.
Mwana Wamkazi wa “Yerusalemu Wakumwamba”
5, 6. (a) Pa Chivumbulutso 21:1, 2, kodi Yohane akuwona mzinda watsopano wophiphiritsira wotani? (b) Kodi ndani amene amalandira mfumu monga momwe kwasonyezedwera pa Zekariya 9:9, 10, ndipo mwa mawu otani?
5 Zaka zoposa makumi aŵiri mphambu zisanu pambuyo pa chiwonongeko cha Yerusalemu ndi magulu ankhondo a Roma mu 70 C.E., mtumwi Yohane anapatsidwa masomphenya odabwitsa m’bukhu la Chivumbulutso. M’Chivumbulutso 21:1, 2 Yohane akulankhula za “Yerusalemu Watsopano.” Ali awo amene amapanga “Yerusalemu Watsopano” ameneyu amene amalandira Mfumu yatsopanoyo yoikidwa pampando wachifumu ya kudza m’dzina la Yehova mwachisangalalo, monga momwe akuuzidwira kuchita pa Zekariya 9:9, 10, m’mawu awa:
6 “Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; tawona, mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu . . . ndipo ndidzawononga magaleta kuwachotsa m’Efraimu, ndi akavalo kuwachotsa m’Yerusalemu; ndi uta wa nkhondo udzawonongeka; ndipo adzanena za mtendere kwa amitundu; ndi ufumu wake udzakhala kuyambira kunyanja kufikira nyanja, ndi kuyambira ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko.”
7. Kodi ndani amene akwaniritsa ulosi umenewu mkati mwa “mapeto a dongosolo iri la zinthu,” ndipo mwa njira yotani?
7 Ulosi umenewo unali ndi kukwaniritsidwa kwakung’ono panthaŵi ya kukwera pabulu kwachipambano kwa Yesu Kristu kuloŵa m’Yerusalemu mu 33 C.E. Kuyambira 1919 wakhala ndi kukwaniritsidwa kwake komalizira pa otsalira odzozedwa a Israyeli wauzimu. Palibe magaŵano pakati pa mamembala a otsalira odzozedwa amenewo, monga amene anabuka pakati mafuko a Efraimu wakale ndi Yerusalemu, malikulu a Ufumu wamafuko aŵiri wa Yuda. Mwa kutumikira mu umodzi zinthu za Ufumu Waumesiya kaamba ka chifuno cha kukwaniritsa ulosi wa Yesu wa pa Mateyu 24:14 ndi Marko 13:10, iwo akupitirizabe kutamanda Mfumu yolakika, Yesu Kristu. M’chigwirizano chosasweka iwo akugonjera mokhulupirika ku ulamuliro wake waufumu mkati mwa ‘mapeto ameneŵa a dongosolo la zinthu.’—Mateyu 24:3.
8. (a) Kodi ndani amene amalephera kulandira Mfumu yolakikayo? (b) Kodi anthu ameneŵa akumka kuti ndipo kuchiyani?
8 Mwa chisoni, mitundu yotchedwa Yachikristu imene imapanga Dziko Lachikristu limodzi ndi Yerusalemu wa Lipabuliki la Israyeli siimavomereza Mfumu yolakikayo imene imadza m’dzina la Yehova. Ngakhale ziri choncho, pali awo amene ali mboni za Uyo amene amadza m’dzina lake, Amamtumikira mwachisangalalo m’kachisi Wake. (Yesaya 43:10-12) Maso awo auzimu atsegudwa kuti awone kuti Lipabuliki la Israyeli limodzi ndi mitundu ina yonse mkati ndi kunja kwa UN tsopano iri pafupi ndi ‘malo otchedwa m’Chihebri Harmagedo.’ (Chivumbulutso 16:16) Nkhondo ya Mulungu Wamphamvuyonse yayandikira!
9. Kodi mtsogolo mwa Yerusalemu wa padziko lapansi mumasiyana motani ndi mwa Yerusalemu Watsopano?
9 Mkhalidwe wa Yerusalemu wa padziko lapansi ngwomvetsa chisoni, koma wa Yerusalemu Watsopano ngwokondweretsa. M’nthaŵi yokwanira, “nyanga khumi” za “chirombo” chandale zadziko, limodzi ndi “chirombo” chenichenicho zitembenukira kuda dongosolo la hule, Babulo Wamkulu, ulamuliro wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga. Iwo adzasonyeza udani wawo wachiwawa motsutsana ndi Yerusalemu wapadziko lapansi wolemekezedwa mwachipembedzo ndipo adzamuwononga monga ngati kuti wawotchedwa ndi moto. (Chivumbulutso 17:16) Koma iwo sadzakhala okhoza konse kukhudza Yerusalemu Watsopano wakumwamba.
10. Kodi Yerusalemu wa padziko lapansi amalondola motani njira yosiyana ndi imene Akristu odzozedwa ndi mzimu ndi “khamu lalikulu,” atsamwali awo amalondola?
10 Otsalira a Akristu odzozedwa ndi mzimu amene akuyembekezera kukhala mbali ya Yerusalemu Watsopano akupitirizabe kutamanda Mfumu ndi Mkwatiyo Yesu Kristu, limodzi ndi “khamu lalikulu” la mboni zina za Yehova. Mwa khalidwe lokhulupirika limeneli, iwo akuima padera mosiyana ndi Yerusalemu wakale. Chiyambire kukhazikitsidwa kwa Lipabuliki la Israyeli, Yerusalemu amene tsopano ali kwakukulukulu mzinda wa Ayuda, akulondola khalidwe la nzika za Yerusalemu wa m’zaka za zana loyamba. Mosonkhezeredwa ndi chipembedzo chochititsa khungu, iye akupitirizabe kukana Yesu Kristu, Iye amene ali ndi kuyenera ndi mphamvu za kulamulira mu Ufumu wakumwamba.
11, 12. (a) Kodi kukwaniritsidwa kwapadera kwa ulosi wa Yesu pa Mateyu 24:14 kwachitidwa makamaka ndi ayani? (b) Kodi Sosaite imene iwo akugwira nayo ntchito iri ndichiyani m’Lipabuliki la Israyeli lerolino?
11 Ndithudi, chiyambire mapeto a Nthaŵi za Akunja mu 1914, “Kalonga wa Mtendere” wakhala akulamulira m’miyamba, yosawoneka kumaso aumunthu. Komabe, kuyambira pamene Yerusalemu analandidwa ndi Angelezi m’Nkhondo Yadziko I ndi pamene Chigwirizano cha Mitundu chinapereka mphamvu ya kulamulira ku Britain, mbiri yabwino ya Ufumu wakumwamba m’manja mwa Mwana wa Mfumu Davide Waumesiya yakhala ‘ikulalikidwa m’dziko lonse lapansi, ukhale umboni kwa anthu amitundu yonse,’ monga momwe Yesu Kristu mwiniyo adaneneratu.—Mateyu 24:14.
12 Kukwaniritsidwa kwaulosi kwapadera kumeneko kwakwaniritsidwa ndi Mboni za Yehova motsogozedwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society. Gulu limeneli liri ndi ofesi yanthambi mu Tel Aviv mwenimwenimo, kumene ntchito ya Mboni za Yehova m’gawo lonse la Israyeli ikutsogozedwerako. Mulinso mipingo ya Mboni za Yehova zokangalika imene tsopano ikulengeza uthenga wa Ufumu m’dzikolo.
13. (a) Kodi nchiyani chimene chidzachitika pambuyo pa kulalikidwa mokwanira kwa mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu? (b) Kodi padzakhalanso kufunikira Yerusalemu wina wa padziko lapansi, kapena kulandiranso Davide m’chiukiriro?
13 Yesu Kristu analosera kuti “mbiri yabwino imeneyi ya ufumu” itatha kulalikidwa mokwanira, “mapeto” akafikira dongosolo laudziko la zinthu limeneli. (Mateyu 24:14, NW) Chotero tsopano mapeto a Yerusalemu wa padziko lapansi ayandikira. Panthaŵi ino, kukuwonekera kuti palibe kufunikira kwa kumangidwa kwa Yerusalemu wina pamalo akale, kapena ngakhale kulandira amene panthaŵi ina anali mfumu ya Yerusalemu, Davide, mwa chiukiriro kuchokera kwa akufa mu Ufumu wa Zaka Chikwi wa Yesu Kristu, mbadwa yake yachifumu. (Yohane 5:28, 29) Komabe, mwa chiwonekere Davide adzaukitsidwira m’chigawo chimene kalero anatumikiriramo Yehova Mulungu.
Nthaŵi ya Chisangalalo
14, 15. (a) Kodi mtumwi Yohane amalongosola motani Yerusalemu Watsopano waulemerero ndi kutsika kwake kuchokera kumwamba kaamba ka dalitso la anthu? (b) Kodi nchifukwa ninji yathuyi iri nthaŵi ya kusangalala, ndipo kodi ndichochitika chotani chosangalatsa chilengedwe chonse chimene chayandikira?
14 Yerusalemu watsopano ngwogwirizana ndi dongosolo latsopano la zinthu la ulemerero. Mtumwi Yohane akuti: “Ndinawona m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m’mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka, ndipo kulibenso nyanja. Ndipo ndinawona mzinda woyerawo, Yerusalemu watsopano, uli kutsika kumwamba kwa Mulungu, wokonzeka ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wake. Ndipo ndinamva mau aakulu ochokera kumpando wachifumu, ndi kunena Tawonani, chihema cha Mulungu chiri mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo.” (Chivumbulutso 21:1-3) Motero, Yerusalemu Watsopano adzakhala dalitso kwa anthu onse.
15 Zimenezi zikupangitsa yathuyi kukhala nthaŵi yachisangalalo. Kuwonjezera ku chisangalalo chonsechi, chochitika chokondweretsa chilengedwe chonse ndi chosangalatsa m’chilengedwe chonse chikuyandikira. Ndiwo ukwati wa kagulu kamkwatibwi kokwanira m’chiŵerengero, Yerusalemu Watsopano, ndi Kristu Yesu Mfumuyo. Monga momwe kwalembedwera pa Chivumbulutso 19:6-9: “Ndipo ndinamva [ine mtumwi Yohane] ngati mawu a khamu lalikulu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mawu a mabingu olimba, nizinena, Haleluya; pakuti achita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvuyonse. Tikondwere, tisekerere, ndipo tipatse ulemerero kwa iye; pakuti wadza ukwati wa Mwanawankhosa [Yesu Kristu]; ndipo mkazi wake wazikonzera. Ndipo anampatsa iye avale bafuta wonyezimira woti mbuu; pakuti bafuta ndiye zolungama za oyera mtima. Ndipo ananena ndi ine, Lemba, wodala iwo amene aitanidwa kuphwando la ukwati wa Mwanawankhosa.”
16. (a) Mwa ukwati wake wakumwamba ndi Mwanawankhosa, kodi Yerusalemu Watsopano akhala amayi wayani? (b) Kodi Yerusalemu Watsopano adzakhala dalitso mogwirizana mokwanira nchiyani?
16 Mgwirizano umenewu wa ukwati wa Mwanawankhosa Yesu Kristu udzatanthauza chisangalalo chosaneneka ku Yerusalemu Watsopano wophiphiritsira wakumwamba. Kupyolera mwa iye adzakhala ‘mayi wa ana wokondwera.’ (Salmo 113:9) Inde, iye adzakhala amayi wakumwamba wa anthu onse, amoyo ndi akufa, amene mwamuna wake wokondedwa anaombola mwa nsembe yake yaumunthu yangwiro zaka mazana 19 zapitazo. Mogwirizana kotheratu ndi pangano la Yehova la Abrahamu la zaka zikwi zambiri zapitazo, Yerusalemu Watsopano adzatsimikizira kukhala dalitso kumabanja onse a dziko lapansi.
[Chithunzi patsamba 96]
M’dongosolo latsopano la zinthu, Yerusalemu Watsopano adzadalitsa anthu onse