Kwa Agalatiya
4 Tsopano ndikunena kuti, wolandira cholowa akakhala mwana wamngʼono, iye sasiyana ndi kapolo, ngakhale kuti ndi mwiniwake wa zinthu zonse. 2 Koma amakhalabe pansi pa amuna oyangʼanira ana ndiponso anthu oyangʼanira zinthu za mbuye wawo, mpaka tsiku limene bambo ake anaikiratu. 3 Nʼchimodzimodzinso ifeyo. Pamene tinali ana, tinali akapolo chifukwa tinkayendera mfundo zimene anthu amʼdzikoli amayendera.*+ 4 Koma nthawi itakwana, Mulungu anatumiza Mwana wake, amene anabadwa kudzera mwa mkazi+ ndipo anakhala pansi pa chilamulo.+ 5 Anachita zimenezi kuti apereke malipiro omasulira anthu amene anali pansi pa chilamulo+ nʼcholinga choti Mulungu atitenge nʼkukhala ana ake.+
6 Tsopano popeza ndinu ana ake, Mulunguyo watumiza mzimu+ wa Mwana wake mʼmitima yathu+ ndipo mzimuwo ukufuula kuti: “Abba,* Atate!”+ 7 Choncho aliyense wa inu si kapolo, koma mwana. Ndipo ngati ndiwe mwana, ndiye kuti ndiwenso wolandira cholowa chimene Mulungu adzakupatse.+
8 Ngakhale zili choncho, pamene simunkadziwa Mulungu, munali akapolo a zinthu zimene kwenikweni si milungu. 9 Koma panopa mwadziwa Mulungu, kapena tinene kuti tsopano mwadziwidwa ndi Mulungu. Ndiye mukubwereranso bwanji ku mfundo zimene anthu amʼdzikoli amayendera, zomwe ndi zosathandiza+ ndiponso zopanda pake, nʼkumafuna kukhalanso akapolo ake?+ 10 Mukuchita zikondwerero pa masiku, miyezi,+ nyengo ndi zaka zimene mukuganiza kuti nʼzapadera. 11 Ndikuda nkhawa kuti mwina ntchito imene ndinagwira pokuthandizani yangopita pachabe.
12 Ndikukupemphani abale anga kuti mukhale ngati ine chifukwa inenso poyamba ndinali ngati inuyo.+ Simunandilakwire ayi. 13 Koma mukudziwa kuti ndinapeza mwayi wolengeza uthenga wabwino koyamba kwa inu chifukwa chakuti ndinkadwala. 14 Ndipo ngakhale kuti matenda anga anali mayesero kwa inu, simunanyansidwe kapena kuipidwa nane.* Koma munandilandira ngati mngelo wa Mulungu kapena ngati Khristu Yesu. 15 Ndiye chimwemwe chimene munali nacho poyamba chija chili kuti? Chifukwa ndikutsimikiza kuti, ngati zikanakhala zotheka, mukanatha kukolowola maso anu nʼkundipatsa.+ 16 Kodi pano ndakhala mdani wanu chifukwa ndakuuzani zoona? 17 Anthu ena akuyesetsa kwambiri kuti akukopeni nʼcholinga choti muziwatsatira. Iwo sakuchita zimenezi ndi zolinga zabwino, koma akufuna kuti akuchotseni kwa ine, kuti inuyo muziwatsatira. 18 Zili bwino ngati munthu akukusonyezani chidwi kwambiri ndi zolinga zabwino osati pokhapokha pamene ndili limodzi ndi inu, koma nthawi zonse. 19 Inu ana anga,+ ndayambanso kumva kupweteka chifukwa cha inu ngati mayi amene watsala pangʼono kubereka. Ndipitiriza kumva kupweteka kumeneku mpaka mudzayambe kusonyeza makhalidwe a Khristu. 20 Panopa ndikanakonda ndikanakhala nanu limodzi kuti ndikulankhuleni mwa njira ina, chifukwa mwandithetsa nzeru.
21 Tandiuzani, inu amene mukufuna kuti muzitsatira chilamulo, Kodi simukumva zimene Chilamulocho chikunena? 22 Mwachitsanzo, Malemba amanena kuti Abulahamu anabereka ana aamuna awiri, wina kwa kapolo wamkazi+ ndipo wina kwa mkazi amene anali mfulu.+ 23 Koma mwana amene anabadwa kwa kapolo wamkazi uja anabadwa monga mmene ana onse amabadwira,+ pamene mwana winayo amene anabadwa kwa mkazi yemwe anali mfulu anabadwa kudzera mu lonjezo.+ 24 Zinthu zimenezi zili ndi tanthauzo lophiphiritsira, chifukwa azimayi amenewa akuimira mapangano awiri. Loyamba ndi pangano la paphiri la Sinai,+ limene limabereka ana oti akhale akapolo. Pangano limenelo ndi Hagara uja. 25 Tsopano, Hagara ameneyu akutanthauza Sinai,+ phiri lomwe lili ku Arabiya, ndipo masiku ano akufanana ndi Yerusalemu, chifukwa ali mu ukapolo pamodzi ndi ana ake. 26 Koma Yerusalemu wamʼmwamba ndi mfulu ndipo ndi mayi athu.
27 Chifukwa Malemba amati: “Sangalala, mkazi wosabereka iwe amene sunaberekepo mwana. Fuula mosangalala, iwe mkazi amene sunamvepo zowawa za pobereka, chifukwa ana a mkazi wosiyidwa ndi ambiri kuposa ana a mkazi amene ali ndi mwamuna.”+ 28 Tsopano inuyo abale, ndinu ana amene munabadwa chifukwa cha lonjezo la Mulungu mofanana ndi Isaki.+ 29 Koma mofanana ndi mmene zinalili pa nthawiyo, kuti amene anabadwa ngati mmene ana onse amabadwira anayamba kuzunza amene anabadwa kudzera mwa mzimu,+ ndi mmenenso zilili masiku ano.+ 30 Ngakhale zili choncho, kodi Malemba amati chiyani? “Thamangitsani kapolo wamkaziyu pamodzi ndi mwana wakeyu pano, chifukwa mwana wa kapolo ameneyu sadzakhala wolandira cholowa pamodzi ndi mwana wa mkazi amene ndi mfulu.”+ 31 Choncho abale, ife ndife ana a mkazi yemwe ndi mfulu, osati a kapolo wamkazi.