2 Samueli
22 Davide analankhula ndi Yehova mawu a nyimbo iyi,+ pa tsiku limene Yehova anamulanditsa kwa adani ake+ onse ndiponso m’manja mwa Sauli.+ 2 Iye anati:
“Yehova ndiye thanthwe langa,+ malo anga achitetezo+ ndiponso Wopereka chipulumutso kwa ine.+
3 Mulungu wanga ndiye thanthwe langa.+ Ine ndidzathawira kwa iye,
Iye ndi chishango changa,+ nyanga* yanga+ ya chipulumutso ndi malo anga okwezeka achitetezo.+
Iye ndi malo anga othawirako,+ Mpulumutsi wanga.+ Mumandipulumutsa ku chiwawa.+
5 Pakuti mafunde akupha anandizungulira.+
Panali chikhamu cha anthu opanda pake amene anali kundiopseza.+
7 Pa nthawi ya zowawa zanga ndinaitana Yehova,+
Ndinaitana Mulungu wanga.+
Pamenepo iye anamva mawu anga ali m’kachisi wake,+
Makutu ake anamva kulira kwanga kopempha thandizo.+
8 Dziko lapansi linayamba kugwedezekera uku ndi uku ndiponso kutekeseka.+
Maziko a kumwamba anagwedezeka.+
Anagwedezekera uku ndi uku chifukwa Mulungu anakwiya.+
9 Utsi unatuluka m’mphuno mwake, ndipo moto wotuluka m’kamwa mwake unanyeketsa.+
Makala onyeka anatuluka mwa iye.+
13 M’kuwala kochokera pamaso pake munatuluka makala oyaka moto.+
14 Ali kumwamba, Yehova anayamba kugunda ngati mabingu,+
Wam’mwambamwamba anayamba kutulutsa mawu ake.+
16 Ndipo ngalande za pansi pa nyanja zinaonekera,+
Maziko a dziko lapansi+ anakhala poonekera,
Zinatero chifukwa cha kudzudzula kwa Yehova, chifukwa cha mphamvu ya mpweya wa m’mphuno mwake.+
18 Anandilanditsa kwa mdani wanga wamphamvu,+
Anandilanditsa kwa odana nane chifukwa anali amphamvu kuposa ine.+
21 Yehova amandipatsa mphoto mogwirizana ndi chilungamo changa.+
Amandibwezera mogwirizana ndi kuyera kwa manja anga.+
22 Pakuti ndasunga njira za Yehova,+
Sindinachoke kwa Mulungu wanga.+ Ndikanatero, ndikanachita chinthu choipa.
25 Yehova andibwezere mogwirizana ndi chilungamo changa,+
Andibwezere mogwirizana ndi kukhala kwanga woyera pamaso pake.+
26 Munthu wokhulupirika, mudzamuchitira mokhulupirika.+
Munthu wamphamvu wopanda cholakwa, mudzamuchitira mwachilungamo.+
27 Kwa munthu wokhalabe woyera, mudzadzisonyeza kuti ndinu woyera,+
Kwa munthu wopotoka maganizo mudzachita zinthu ngati wopusa.+
30 Pakuti ndi thandizo lanu ndingathamangitse gulu la achifwamba.+
Ndi thandizo la Mulungu wanga ndingakwere khoma.+
31 Njira ya Mulungu woona ndi yangwiro.+
Mawu a Yehova ndi oyengeka bwino.+
Iye ndi chishango kwa onse othawira kwa iye.+
33 Mulungu woona ndiye malo anga otetezeka kwambiri,+
Ndipo adzasalaza njira yanga.+
34 Iye adzachititsa mapazi anga kukhala aliwiro ngati a mbawala zazikazi,+
Ndipo adzandiimiritsabe pamalo okwezeka kwa ine.+
36 Inu mudzandipatsa chishango chanu cha chipulumutso,+
Ndipo kudzichepetsa kwanu n’kumene kumandikweza.+
38 Ndidzathamangitsa adani anga kuti ndiwafafanize,
Ndipo sindidzabwerera kufikira nditawawononga onse.+
39 Ndidzawawononga onse ndi kuwaphwanya zibenthuzibenthu+ kuti asadzukenso.+
Iwo adzagwa pansi ndipo ndidzawapondaponda ndi mapazi anga.+
41 Koma mudzachititsa adani anga kugonja* pamaso panga,+
Anthu odana nane kwambiri, ndidzawakhalitsa chete.+
42 Adzafuula kupempha thandizo, koma sipadzapezeka wowapulumutsa,+
Adzafuulira Yehova, koma sadzawayankha.+
43 Ndidzawapera kukhala ngati fumbi la padziko lapansi.
Ndidzawapondaponda ngati matope a mumsewu,+
Ndipo ndidzawasasantha.
44 Inu mudzandipulumutsa kwa anthu a mtundu wanga onditola zifukwa.+
Mudzanditeteza kuti ndikhale mtsogoleri wa mitundu yonse.+
Anthu amene sindikuwadziwa adzanditumikira.+
47 Yehova ndi wamoyo.+ Lidalitsike Thanthwe langa.+
Mulungu wanga, thanthwe limene limandipulumutsa likhale lokwezeka.+
48 Mulungu woona ndiye Wobwezera adani anga,+
Iye amaika mitundu ya anthu kunsi kwa mapazi anga.+
49 Iye amandichotsa pakati pa adani anga.+
Ndipo mudzandikweza pamwamba pa anthu amene amandiukira.+
Mudzandilanditsa kwa munthu wochita zachiwawa.+