Masalimo
Pemphero la munthu wosautsika pamene walefuka ndipo akutula nkhawa zake kwa Yehova.+
2 Musandibisire nkhope yanu pa tsiku limene ndili m’masautso aakulu.+
Tcherani khutu lanu kwa ine.+
Fulumirani kundiyankha pa tsiku limene ndikuitana.+
3 Pakuti masiku a moyo wanga atha ndi kuzimiririka ngati utsi,+
Ndipo mafupa anga atentha kwambiri ngati ng’anjo.+
8 Tsiku lonse adani anga amanditonza.+
Anthu ondinyoza amagwiritsa ntchito dzina langa potemberera ena.+
9 Pakuti ndadya phulusa ngati chakudya.+
Ndipo zakumwa zanga ndazisakaniza ndi misozi,+
10 Chifukwa cha kudzudzula kwanu kwamphamvu ndi mkwiyo wanu.+
Inu mwandikweza m’mwamba kuti munditaye.+
11 Masiku a moyo wanga ali ngati chithunzithunzi chimene chimazimiririka dzuwa likalowa,+
Ndipo ndauma ngati udzu.+
13 Inu mudzanyamuka ndi kusonyeza Ziyoni chifundo,+
Pakuti imeneyi ndi nyengo yomukomera mtima,
Chifukwa nthawi yoikidwiratu yakwana.+
15 Mitundu ya anthu idzaopa dzina lanu, inu Yehova,+
Ndipo mafumu onse a padziko lapansi adzaopa ulemerero wanu.+
17 Iye adzamvetsera pemphero la anthu amene alandidwa chilichonse,+
Ndipo sadzapeputsa pemphero lawo.+
19 Iye wayang’ana pansi ali kumalo oyera, okwezeka,+
Yehova wayang’ana dziko lapansi ali kumwambako,+
20 Kuti amve kuusa moyo kwa akaidi,+
Ndi kumasula anthu opita kukaphedwa.+
21 Wachita izi kuti dzina la Yehova lilengezedwe m’Ziyoni,+
Ndi kuti atamandidwe mu Yerusalemu,+
22 Pamene mitundu ya anthu idzasonkhanitsidwa pamodzi,+
Komanso maufumu, kuti atumikire Yehova.+
24 Ine ndinati: “Inu Mulungu wanga,
Musadule pakati masiku a moyo wanga.+
Mudzakhalapo ku mibadwomibadwo.+