1 Samueli
14 Ndiyeno tsiku lina zinachitika kuti Yonatani+ mwana wa Sauli anauza mtumiki wake womunyamulira zida kuti: “Tiye tiwolokere kumudzi wa asilikali a Afilisiti umene uli patsidyapo.” Koma Yonatani sanauze bambo ake zimenezi.+ 2 Pa nthawiyi Sauli anali kukhala kunja kwa mzinda wa Gibeya+ pansi pa mtengo wa makangaza* umene uli ku Migironi. Iye anali ndi amuna pafupifupi 600.+ 3 (Ahiya ndiye anali kunyamula efodi.+ Iye anali mwana wa Ahitubu,+ m’bale wa Ikabodi,+ mwana wa Pinihasi,+ mwana wa Eli,+ wansembe wa Yehova ku Silo.)+ Koma anthu sanadziwe kuti Yonatani wachoka. 4 Tsopano pakati pa mipata imene Yonatani anafuna kudutsa kuti akamenyane ndi mudzi wa asilikali+ a Afilisiti, panali thanthwe looneka ngati dzino kumbali ina, ndi lina looneka ngati dzino kumbali inanso. Limodzi mwa matanthwewo dzina lake linali Bozezi ndipo linalo linali Sene. 5 Thanthwe limodzi looneka ngati dzinolo linali kumpoto ndipo linaima ngati chipilala moyang’ana ku Mikimasi,+ ndipo linalo linali kum’mwera moyang’ana ku Geba.+
6 Choncho Yonatani anauza mtumiki wake womunyamulira zida uja kuti: “Tiye tiwolokere kumudzi wa amuna osadulidwawa.+ Pakuti mwina Yehova adzatithandiza, chifukwa palibe chimene chingalepheretse Yehova kupulumutsa anthu ake pogwiritsa ntchito anthu ambiri kapena ochepa.”+ 7 Pamenepo mtumiki wakeyo anamuuza kuti: “Chita zimene mtima wako ukufuna. Tiye kulikonse kumene ukufuna. Ine ndili nawe limodzi kuti ndichite zofuna za mtima wako.”+ 8 Ndiyeno Yonatani anati: “Tsopano tikuwoloka kupita kwa anthuwa, ndipo tidzionetsere kwa iwo. 9 Iwo akatiuza kuti, ‘Imani pomwepo, ife tikubwera kumeneko!’ ife tiimedi pomwepo, osapitiriza kupita kumene iwo ali. 10 Koma akatiuza kuti, ‘Bwerani kuno mudzamenyane nafe!’ ife tipita chifukwa Yehova adzawaperekadi m’manja mwathu, ndipo chimenechi ndicho chizindikiro chathu.”+
11 Atatero, onse awiri anadzionetsera kumudzi wa asilikali a Afilisiti, ndipo Afilisitiwo anayamba kunena kuti: “Taonani Aheberi akutuluka m’maenje amene anabisala.”+ 12 Pamenepo amuna a m’mudzi wa asilikaliwo anauza Yonatani ndi mtumiki wake uja kuti: “Bwerani kuno, ndipo tikukhaulitsani!”+ Nthawi yomweyo Yonatani anauza mtumiki wakeyo kuti: “Nditsatire chifukwa Yehova awapereka ndithu amenewa m’manja mwa Isiraeli.”+ 13 Ndiyeno Yonatani anapita chokwawa,+ mtumiki wake akum’tsatira pambuyo. Pamenepo Yonatani+ anayamba kukantha Afilisitiwo ndipo mtumiki wake uja anali kumalizitsa kupha anthuwo m’mbuyo mwake.+ 14 Nthawi yoyamba imene Yonatani ndi mtumiki wakeyo anakantha Afilisitiwo anapha anthu 20, pamalo okwana pafupifupi hafu ya m’litali mwa ekala.*
15 Kenako anthu amene anali kutchire mumsasa ndi anthu onse kumudzi wa asilikaliwo anayamba kunjenjemera.+ Anthu olanda katundu+ nawonso anali kunjenjemera, ndipo nthaka inayamba kugwedezeka.+ Zimenezi zinali zochokera kwa Mulungu.+ 16 Alonda a Sauli ku Gibeya+ wa ku Benjamini anaona zimene zinali kuchitika, ndipo anaona kuti chipwirikiti chafalikira paliponse mumsasamo.+
17 Ndiyeno Sauli anauza anthu amene anali naye kuti: “Werengani anthu kuti muone amene wachoka.” Atawerenga anthuwo, anapeza kuti Yonatani ndi mtumiki wake womunyamulira zida palibe. 18 Pamenepo Sauli anauza Ahiya+ kuti: “Bweretsa likasa la Mulungu woona!”+ (Pakuti masiku amenewo likasa la Mulungu woona linali ndi ana a Isiraeli.)+ 19 Ndiyeno zimene zinachitika n’zakuti, pamene Sauli anali kulankhula ndi wansembe,+ chipwirikiti mumsasa wa Afilisiti chinapitiriza kuwonjezeka, ndipo chinali kukulirakulira. Kenako Sauli anauza wansembeyo kuti: “Basi, siya zimenezi.” 20 Choncho Sauli ndi anthu onse amene anali naye anasonkhana pamodzi kuti apite kukamenyana ndi Afilisiti.+ Ndiyeno anayenda mpaka kukafika kumene kunali nkhondoko, ndipo anapeza kuti aphana okhaokha ndi lupanga,+ moti chipwirikiti chake chinali chosaneneka. 21 Ndipo Aheberi amene anali atagwirizana ndi Afilisiti+ poyamba, amene anali atapita kukakhala mumsasa wa Afilisiti, nawonso anakhala kumbali ya Aisiraeli amene anali ndi Sauli ndi Yonatani. 22 Nawonso amuna onse a Isiraeli amene anali atabisala+ m’dera lamapiri la Efuraimu anamva kuti Afilisiti athawa, choncho Aisiraeliwo anayamba kuthamangitsa Afilisitiwo ndi kuwathira nkhondo. 23 Pa tsiku limenelo Yehova anapulumutsa+ Isiraeli, ndipo nkhondoyo inapitirira mpaka ku Beti-aveni.+
24 Motero amuna a Isiraeli anatopa kwambiri pa tsiku limenelo, komabe Sauli analumbirira+ anthuwo kuti: “Munthu aliyense wodya mkate dzuwa lisanalowe, komanso ndisanabwezere+ adani anga, ndi wotembereredwa!” Choncho panalibe aliyense mwa anthuwo amene anadya mkate.+
25 Ndiyeno anthu onse a m’dzikomo anapita kunkhalango, pa nthawi imene uchi+ unali pena paliponse kutchireko. 26 Anthuwo atalowa m’nkhalangomo, anaona uchi+ ukukha. Pa nthawiyi panalibe amene anadya, chifukwa anali kuopa lumbiro lija.+ 27 Koma Yonatani sanamve pamene bambo ake analumbirira anthu.+ Chotero anatambasula dzanja lake ndi kukhudza chisa cha uchi ndi ndodo. Kenako ananyambita ndodoyo, ndipo atatero, anayera m’maso.+ 28 Pamenepo mmodzi mwa anthuwo anamuuza kuti: “Bambo ako alumbirira anthu kuti, ‘Munthu aliyense wodya mkate lero ndi wotembereredwa!’”+ (Apa n’kuti anthuwo atayamba kutopa.)+ 29 Poyankha, Yonatani anati: “Bambo anga achititsa kuti dziko lonse livutike.+ Taonani mmene maso anga ayerera chifukwa ndalawa uchi pang’ono chabe.+ 30 Anthu akanadya+ zimene afunkha kwa adani awo,+ Afilisiti tikanawagonjetsa. Koma onani, sitinawakanthe mokwanira.”+
31 Choncho pa tsiku limenelo, iwo anapitiriza kupha Afilisiti kuyambira ku Mikimasi+ mpaka ku Aijaloni,+ moti anthu anatopa kwambiri.+ 32 Zitatero, anthuwo anayamba kuthamangira zofunkha mosusuka+ ndi kutenga nkhosa, ng’ombe ndi ana a ng’ombe. Zimenezi anali kuziphera pansi, ndipo anthuwo anayamba kudya nyamayo pamodzi ndi magazi ake.+ 33 Tsopano anthu anauza Sauli kuti: “Taonani! Anthu akuchimwira Yehova mwa kudya nyama pamodzi ndi magazi ake.”+ Chotero iye anati: “Mwachita zinthu mosakhulupirika. Choyamba, kunkhunizani chimwala mubwere nacho kuno.” 34 Kenako Sauli anati: “Pitani pakati pa anthu ndipo muwauze kuti, ‘Aliyense wa inu abweretse kwa ine ng’ombe yake yamphongo ndi nkhosa, ndipo mudzaziphere ndi kuzidyera pano. Musachimwire Yehova mwa kudya nyama pamodzi ndi magazi ake.’”+ Usiku umenewo, aliyense mwa anthuwo anabweretsa ng’ombe yamphongo imene anali nayo ndi kuiphera pamenepo. 35 Zitatero, Sauli anamangira Yehova guwa lansembe,+ limene linali guwa lake loyamba kumangira Yehova.+
36 Kenako Sauli anati: “Tiyeni tipite kwa Afilisiti usiku kuti tikafunkhe zinthu zawo kufikira kutacha,+ ndipo tisasiyepo ngakhale munthu mmodzi pakati pawo.”+ Anthuwo poyankha anati: “Chitani chilichonse chimene mukuona kuti n’chabwino.” Ndiyeno wansembe anati: “Tiyeni tifikire Mulungu woona pamalo ano.”+ 37 Chotero Sauli anayamba kufunsira kwa Mulungu, kuti: “Kodi ndipite kwa Afilisiti?+ Kodi muwapereka m’manja mwa Isiraeli?”+ Koma Mulungu sanamuyankhe pa tsikuli.+ 38 Choncho Sauli ananena kuti: “Bwerani kuno,+ inu nonse atsogoleri a anthu,+ ndipo tifufuze ndi kudziwa mmene tchimoli lachitikira lero. 39 Ndithu, pali Yehova Mulungu wamoyo, Mlanditsi wa Isiraeli, munthu amene wachititsa tchimoli ayenera kufa ndithu,+ ngakhale atakhala Yonatani mwana wanga.” Koma panalibe ngakhale munthu mmodzi womuyankha mwa anthu onsewo. 40 Ndiyeno anapitiriza kuuza Aisiraeli onse kuti: “Inuyo mukhale kumbali ina, ndipo ine ndi mwana wanga Yonatani tikhalanso ku mbali ina.” Pamenepo anthuwo anauza Sauli kuti: “Chitani zimene mukuona kuti n’zabwino.”+
41 Ndiyeno Sauli anauza Yehova kuti: “Mulungu wa Isiraeli inu, tiyankheni kudzera mwa Tumimu!”+ Atatero, Tumimuyo analoza kwa Yonatani ndi Sauli, ndipo anthuwo anachoka.+ 42 Kenako Sauli anati: “Chitani maere+ pakati pa ine ndi Yonatani mwana wanga.” Zitatero, maerewo anagwera Yonatani. 43 Tsopano Sauli anafunsa Yonatani kuti: “Ndiuze, Wachita chiyani?”+ Poyankha, Yonatani anamuuza kuti: “Zoonadi, ndalawa uchi pang’ono kunsonga ya ndodo imene ili m’manja mwangayi.+ Ndiye ndiphenitu!”
44 Pamenepo Sauli anati: “Mulungu andilange mowirikiza+ ngati suufa ndithu,+ Yonatani.” 45 Koma anthu anauza Sauli kuti: “Kodi Yonatani amene wagwira ntchito yobweretsa chipulumutso chachikulu chimenechi+ mu Isiraeli afe? Sizitheka zimenezo!+ Pali Yehova, Mulungu wamoyo,+ ngakhale tsitsi limodzi+ la m’mutu wake siligwa pansi, pakuti iye wachita zimenezi lero mothandizidwa ndi Mulungu.”+ Ndi mawu amenewa anthuwo anapulumutsa+ Yonatani, moti sanafe.
46 Choncho Sauli anasiya kutsatira Afilisiti, moti nawonso Afilisiti anabwerera kwawo.+
47 Tsopano Sauli analimbitsa ufumu wake mu Isiraeli+ ndipo anamenya nkhondo ndi adani ake onse om’zungulira. Iye anamenyana ndi Mowabu,+ ana a Amoni,+ Edomu,+ mafumu a Zoba+ ndi Afilisiti.+ Kulikonse kumene anali kutembenukira anali kuwalanga.+ 48 Iye anapitiriza kuchita chamuna+ ndipo anapha Aamaleki+ ndi kulanditsa Isiraeli m’manja mwa wofunkha.
49 Ana aamuna a Sauli anali Yonatani,+ Isivi ndi Malikisuwa.+ Ndipo mayina a ana ake awiri aakazi ndi awa: Woyamba kubadwa anali Merabu,+ ndipo wamng’ono anali Mikala.+ 50 Mkazi wa Sauli dzina lake anali Ahinowamu, mwana wamkazi wa Ahimazi. Mkulu wa gulu lake lankhondo anali Abineri+ mwana wa Nera, m’bale wa bambo ake a Sauli. 51 Bambo ake a Sauli anali Kisi,+ ndipo Nera,+ bambo ake a Abineri, anali mwana wa Abiyeli.
52 M’masiku onse a Sauli, Afilisiti anali kupanikizidwa ndi nkhondo.+ Ndipo Sauli akaona munthu aliyense wamphamvu kapena wolimba mtima, anali kum’tenga kuti akhale msilikali wake.+