Habakuku
1 Uwu ndi uthenga umene ine, mneneri Habakuku,* ndinalandira mʼmasomphenya. Ndinati:
2 “Inu Yehova, kodi ndidzalirira thandizo koma inu osandimva mpaka liti?+
Kodi ndidzapempha thandizo kuti mundipulumutse ku chiwawa koma inu osachitapo kanthu mpaka liti?+
3 Nʼchifukwa chiyani mukundichititsa kuona zinthu zoipa?
Nʼchifukwa chiyani mukulekerera kuponderezana?
Nʼchifukwa chiyani kuwononga zinthu komanso chiwawa zikuchitika pamaso panga?
Ndipo nʼchifukwa chiyani mikangano ndi kumenyana zachuluka?
4 Choncho lamulo latha mphamvu,
Ndipo anthu sakuchitanso chilungamo.
Oipa akupondereza anthu olungama,
Nʼchifukwa chake chilungamo chikupotozedwa.+
5 Yangʼanani pakati pa mitundu ya anthu ndipo muyangʼanitsitse.
Muyangʼane modabwa. Dabwani ndithu.
Chifukwa pali zimene zichitike mʼmasiku anu,
Zimene simungakhulupirire ngakhale wina atakufotokozerani.+
Umene umathamanga mʼmadera ambiri apadziko lapansi,
Kukalanda nyumba zimene si zawo.+
7 Mtundu umenewu ndi woopsa ndiponso wochititsa mantha.
Umapanga malamulo akeake ndipo umadzipatsa wokha ulamuliro.+
Mahatchi ake ankhondo amathamanga kwambiri.
Mahatchi awo amachokera kutali.
Ndipo amauluka ngati chiwombankhanga chimene chikuthamanga kuti chikapeze chakudya.+
9 Mtunduwo umabwera wonse kuti udzachite chiwawa.+
Ukakumana pamodzi umayenda ngati mphepo yochokera kumʼmawa,+
Ndipo anthu amene wagwira umawakokolola ngati mchenga.
Umasekanso malo alionse okhala ndi mpanda wolimba,+
Ndipo umaunjika dothi kenako nʼkulanda malowo.
11 Kenako mtunduwo umayenda ngati mphepo ndipo umadutsa mʼdziko.
Koma udzapalamula,+
Chifukwa choganiza kuti mulungu wawo ndi amene wawapatsa mphamvu.”*+
12 Inu Yehova, mwakhala mulipo kuyambira kalekale.+
Inu Mulungu wanga, Mulungu wanga Woyera, inu simufa.*+
Inu Yehova, mwasankha Akasidi kuti apereke chiweruzo chanu.
13 Maso anu ndi oyera kwambiri moti simungaonerere zinthu zoipa,
Ndipo simungalekerere khalidwe loipa.+
Ndiye nʼchifukwa chiyani mukulekerera anthu achinyengo,+
Komanso mukukhala chete pamene munthu woipa akumeza munthu wolungama kuposa iyeyo?+
14 Nʼchifukwa chiyani mukuchititsa munthu kukhala ngati nsomba zamʼnyanja,
Ndiponso ngati zokwawa zimene zilibe mtsogoleri?
15 Iye* amakola zonsezi ndi mbedza,
Ndipo amazikokolola ndi khoka lake.
Nʼkuzisonkhanitsa muukonde wophera nsomba.
Nʼchifukwa chake iye amasangalala kwambiri.+
16 Nʼchifukwa chake amapereka nsembe kwa khoka lake,
Ndipo amapereka nsembe yautsi kwa ukonde wake wophera nsomba.
Iye amatero chifukwa khoka ndi ukondewo zimamuthandiza kupeza chakudya chambiri.*
Ndipo chakudya chake ndi chapamwamba.
17 Ndiye kodi adzapitirizabe kukhuthula nsomba zamʼkhoka* lake?
Kodi iye adzapitirizabe kupha mitundu ya anthu mopanda chifundo?+