Yoswa
18 Kenako gulu lonse la Aisiraeli linasonkhana ku Silo,+ ndipo kumeneko anamanga chihema chokumanako,+ popeza pa nthawiyo nʼkuti atagonjetsa dzikolo.+ 2 Koma panali mafuko 7 a Aisiraeli amene anali asanagawiridwebe cholowa. 3 Choncho Yoswa anafunsa Aisiraeli kuti: “Kodi muzengereza mpaka liti osapita kukalanda dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu wakupatsani?+ 4 Sankhani amuna atatu pa fuko lililonse oti ndiwatume. Akayendere dzikolo nʼkulemba mmene lilili kuti lidzagawidwe mogwirizana ndi cholowa cha mafuko awo. Akatero adzabwerere kwa ine. 5 Ndiyeno adzagawe dzikolo mʼzigawo 7.+ Fuko la Yuda lidzakhalabe kugawo lawo kumʼmwera,+ ndipo a mʼbanja la Yosefe adzakhalabe kugawo lawo kumpoto.+ 6 Koma inuyo mukagawe dzikolo mʼzigawo 7 ndipo mukazilembe. Kenako mukabwere nazo kuno kuti ndidzakuchitireni maere+ pamaso pa Yehova Mulungu wathu. 7 Koma Alevi sadzapatsidwa gawo pakati panu,+ chifukwa cholowa chawo ndi unsembe wa Yehova.+ Fuko la Gadi, Rubeni ndi hafu ya fuko la Manase+ analandira kale cholowa chawo, chimene Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa kutsidya lakumʼmawa la Yorodano.”
8 Choncho amuna aja anakonzeka kuti azipita, ndipo Yoswa anawalamula kuti: “Pitani mukayendere dzikolo nʼkulemba mmene lilili. Mukatero mukabwere kuno, ndipo ndidzakuchitirani maere pamaso pa Yehova ku Silo kuno.”+ 9 Amunawo anapitadi kukayendera dzikolo ndipo analigawa mʼzigawo 7 potsatira mizinda yake nʼkulemba mʼbuku. Atamaliza anabwerera kwa Yoswa kumsasa ku Silo. 10 Kenako Yoswa anawachitira maere pamaso pa Yehova ku Silo+ ndipo anagawira Aisiraeli dzikolo moti fuko lililonse analipatsa gawo limodzi.+
11 Maere oyamba anagwera fuko la Benjamini motsatira mabanja awo, ndipo anapatsidwa dera limene linali pakati pa ana a Yuda+ ndi ana a Yosefe.+ 12 Kumpoto, malire a gawo lawo anayambira ku Yorodano nʼkupitirira kukafika kumalo otsetsereka akumpoto kwa Yeriko,+ nʼkukwera phiri chakumadzulo, nʼkukathera kuchipululu cha Beti-aveni.+ 13 Malirewo anapitirira kukafika kumʼmwera kwa malo otsetsereka otchedwa Luzi, kutanthauza Beteli.+ Kuchokera ku Luzi anatsetserekera ku Ataroti-adara,+ nʼkukadutsa paphiri lakumʼmwera kwa Beti-horoni Wakumunsi.+ 14 Kumadzulo kwa gawolo, malirewo anakhotera kumʼmwera, paphiri loyangʼanizana ndi kumʼmwera kwa Beti-horoni. Kuchokera pamenepo anakathera ku Kiriyati-baala, kutanthauza Kiriyati-yearimu,+ womwe ndi mzinda wa Yuda. Amenewa ndi malire akumadzulo a gawo la Benjamini.
15 Malire akumʼmwera a gawolo anayambira kumapeto kwa Kiriyati-yearimu, nʼkulowera chakumadzulo, nʼkupitirira kukafika kukasupe wa madzi a Nafitoa.+ 16 Malirewo anakafika kumapeto kwa phiri loyangʼanizana ndi chigwa cha Mwana wa Hinomu,+ limene linathera kumpoto kwa chigwa cha Arefai.+ Kenako anatsetserekera kuchigwa cha Hinomu kumʼmwera kwa malo otsetsereka otchedwa Yebusi+ mpaka kukafika ku Eni-rogeli.+ 17 Analowera chakumpoto nʼkukafika ku Eni-semesi mpaka kumzinda wa Gelilotu, womwe uli kutsogolo kwa chitunda cha Adumi.+ Kuchokera pamenepo, anatsetserekera kumwala+ wa Bohani,+ mwana wa Rubeni. 18 Anapitirira nʼkukafika kumalo otsetsereka akumpoto amene ali kutsogolo kwa Araba, nʼkutsetsereka kukafika ku Araba. 19 Malirewo anapitirira mpaka kumalo otsetsereka akumpoto kwa Beti-hogila,+ nʼkukathera kugombe lakumpoto kwa Nyanja Yamchere,*+ kumapeto kwa mtsinje wa Yorodano mbali yakumʼmwera. Awa anali malire akumʼmwera a gawo la Benjamini. 20 Kumʼmawa, malire ake anali mtsinje wa Yorodano. Ichi chinali cholowa cha ana a Benjamini motsatira mabanja awo, ndi malire ake kuzungulira gawo lonse.
21 Mizinda ya fuko la Benjamini motsatira mabanja awo inali Yeriko, Beti-hogila, Emeki-kezizi, 22 Beti-araba,+ Zemaraimu, Beteli,+ 23 Aavi, Para, Ofira, 24 Kefara-amoni, Ofini ndi Geba.+ Mizinda 12 ndi midzi yake.
25 Kunalinso Gibiyoni,+ Rama, Beeroti, 26 Mizipe, Kefira, Moza, 27 Rekemu, Iripeeli, Tarala, 28 Zela,+ Ha-elefi, Yebusi, kutanthauza Yerusalemu,+ Gibea+ ndi Kiriyati. Mizinda 14 ndi midzi yake.
Chimenechi chinali cholowa cha ana a Benjamini motsatira mabanja awo.