Miyambo
2 Munthu adzadya zinthu zabwino kuchokera pa zipatso zapakamwa pake,+
Koma anthu achinyengo amalakalaka kuchita zachiwawa.
3 Amene amayangʼanira pakamwa pake* amateteza moyo wake,+
Koma amene amatsegula kwambiri pakamwa pake adzawonongeka.+
6 Chilungamo chimateteza munthu wosalakwa,+
Koma kuchita zoipa kumachititsa kuti wochimwa awonongeke.
7 Pali munthu amene amadzionetsa ngati wolemera koma chonsecho alibe chilichonse.+
Pali munthu winanso amene amadzionetsa ngati wosauka koma ali ndi chuma chambiri.
9 Kuwala kwa nyale ya anthu olungama kukuwonjezeka kwambiri.*+
Koma nyale ya anthu oipa idzazimitsidwa.+
11 Chuma chimene munthu amachipeza mofulumira* sichichedwa kutha,+
Koma chuma cha munthu amene wachipeza pangʼonopangʼono* chidzawonjezeka.
12 Chinthu chimene umayembekezera chikalephereka, mtima umadwala.+
Koma chomwe umalakalaka chikachitika, chimakhala ngati mtengo wa moyo.+
13 Aliyense amene safuna kutsatira malangizo, adzakumana ndi mavuto chifukwa cha zochita zakezo,+
Koma munthu amene amamvera malamulo adzalandira mphoto.+
14 Zimene munthu wanzeru amaphunzitsa* zimapereka moyo,+
Chifukwa zimapulumutsa munthu kumisampha ya imfa.
15 Munthu wozindikira kwambiri, anthu amamukomera mtima,
Koma anthu achinyengo moyo wawo umakhala wodzaza ndi mavuto.
18 Aliyense amene amanyalanyaza malangizo* amasauka ndipo amanyozeka,
Koma amene amamvera akadzudzulidwa adzalemekezedwa.+
19 Zimene munthu amalakalaka zikakwaniritsidwa amasangalala.+
Koma opusa amadana ndi zoti asiye zinthu zoipa.+
20 Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru,+
Koma amene amachita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.+
22 Munthu wabwino amasiyira cholowa zidzukulu zake,
Koma chuma cha munthu wochimwa chidzasungidwa kuti chidzakhale cha munthu wolungama.+
23 Munda wa munthu wosauka akaulima umatulutsa chakudya chochuluka,
Koma chingathe kutengedwa* ndi anthu opanda chilungamo.