Miyambo
13 Mwana amakhala wanzeru ngati akulandira malangizo* kuchokera kwa bambo ake.+ Koma amene sanamve chidzudzulo amakhala wonyoza.+
2 Munthu adzadya zipatso zabwino kuchokera pa zipatso za pakamwa pake.+ Koma moyo wa anthu ochita zachinyengo umalakalaka kuchita chiwawa.+
3 Amene amayang’anira pakamwa pake amasunga moyo wake.+ Amene amatsegula kwambiri pakamwa pake adzawonongeka.+
4 Waulesi amalakalaka zinthu, chonsecho moyo wake ulibe chilichonse.+ Koma anthu akhama adzanenepa.+
5 Wolungama amadana ndi lilime lonama,+ koma anthu oipa amachita zinthu zochititsa manyazi ndipo amadzibweretsera manyazi.+
6 Chilungamo chimateteza munthu amene sachita zopweteka ena,+ koma wochimwa amawonongedwa ndi zoipa.+
7 Pali munthu amene amadzionetsera kuti ndi wolemera koma alibe kalikonse.+ Ndiponso pali munthu amene amaoneka ngati wosauka koma ali ndi zinthu zambiri zamtengo wapatali.
8 Moyo wa munthu udzawomboledwa ndi chuma chake,+ koma munthu wosauka sadzudzulidwa.+
9 Kuwala kwa anthu olungama kudzawachititsa kusangalala.+ Koma nyale ya anthu oipa idzazimitsidwa.+
10 Chifukwa cha kudzikuza, munthu amangoyambitsa mavuto,+ koma anthu amene amakhala pamodzi n’kumakambirana amakhala ndi nzeru.+
11 Zinthu zamtengo wapatali zimene zimapezedwa m’njira yachinyengo zimacheperachepera,+ koma wozisonkhanitsa ndi dzanja lake ndi amene amazichulukitsa.+
12 Chinthu chimene unali kuyembekeza chikalephereka, chimadwalitsa mtima.+ Koma chomwe unali kufuna chikachitika, chimakhala ngati mtengo wa moyo.+
13 Wokana kusunga mawu,+ wangongole adzamulanda chikole. Koma munthu amene amaopa lamulo ndiye adzalandire mphoto.+
14 Lamulo la munthu wanzeru ndilo kasupe wa moyo,+ chifukwa limapulumutsa munthu kumisampha ya imfa.+
15 Munthu wozindikira bwino, anthu amam’komera mtima.+ Koma njira ya anthu ochita zachinyengo imakhala yodzaza ndi zopweteka ndiponso mavuto.+
16 Aliyense wochenjera amachita zinthu mozindikira,+ koma wopusa amafalitsa uchitsiru.+
17 Mthenga woipa amayambitsa mavuto,+ koma nthumwi yokhulupirika imachiritsa.+
18 Munthu wonyalanyaza malangizo amasauka ndipo amadzichotsera ulemu.+ Koma amene amamvera chidzudzulo ndi amene amalemekezedwa.+
19 Zimene umakhumba zikapezeka, moyo umasangalala.+ Koma opusa, kusiya zoipa kumawanyansa.+
20 Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru,+ koma wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.+
21 Tsoka limatsatira ochimwa,+ koma olungama ndi amene amalandira mphoto zabwino.+
22 Munthu wabwino adzasiyira cholowa zidzukulu zake, ndipo chuma cha wochimwa chimasungidwa kuti chidzakhale cha munthu wolungama.+
23 Munda wa munthu wosauka akaulima umatulutsa chakudya chochuluka,+ koma pali munthu amene wasesedwa chifukwa chosowa chilungamo.+
24 Munthu wosakwapula mwana wake ndiye kuti akumuda,+ koma womukonda ndi amene amamuyang’anira kuti amulangize.+
25 Wolungama amadya n’kukhuta,+ koma mimba za anthu oipa zidzakhala zopanda kanthu.+