Danieli
4 “Uwu ndi uthenga wochokera kwa ine mfumu Nebukadinezara wopita kwa anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana amene akukhala padziko lonse lapansi:+ Mukhale ndi mtendere wochuluka.+ 2 Ndaona kuti n’kwabwino kuti ndikuuzeni+ zizindikiro ndi zodabwitsa zimene Mulungu Wam’mwambamwamba wandichitira. 3 Zizindikiro zake n’zazikulu ndipo zodabwitsa zake n’zamphamvu.+ Ufumu wake udzakhalapo mpaka kalekale+ ndipo ulamuliro wake udzakhalapo ku mibadwomibadwo.+
4 “Ine Nebukadinezara ndinali kukhala mosatekeseka+ m’nyumba mwanga ndipo zinthu zinali kundiyendera bwino m’nyumba yanga yachifumu.+ 5 Kenako ndinalota maloto amene anayamba kundichititsa mantha.+ Ndili pabedi langa ndinaona zithunzithunzi ndi masomphenya m’maganizo mwanga. Zimenezi zinayamba kundichititsa mantha.+ 6 Pamenepo ndinalamula kuti amuna onse anzeru a m’Babulo abwere kwa ine kuti adzandimasulire malotowo.+
7 “Chotero ansembe ochita zamatsenga, anthu olankhula ndi mizimu, Akasidi*+ ndi okhulupirira nyenyezi+ anabwera kwa ine ndipo ndinawauza malotowo, koma iwo sanathe kuwamasulira.+ 8 Kenako Danieli, amene ndinamupatsa dzina lakuti Belitesazara+ pofuna kulemekeza mulungu wanga,+ amenenso mwa iye muli mzimu wa milungu yoyera,+ anabwera kwa ine ndipo ndinamuuza malotowo. Ndinati:
9 “‘Iwe Belitesazara mkulu wa ansembe ochita zamatsenga,+ ndikudziwa bwino kuti mzimu wa milungu yoyera uli mwa iwe+ ndipo palibe chinsinsi chimene umavutika nacho.+ Chotero ndiuze zimene ndinaona m’maloto anga ndi kumasulira kwake.+
10 “‘Ine ndinaona masomphenya nditagona pabedi langa.+ Ndinaona mtengo+ wautali kwambiri+ uli pakati pa dziko lapansi. 11 Mtengowo unakula ndipo unakhala wamphamvu kwambiri. Unatalika mpaka kufika kumwamba ndipo unali kuonekera ngakhale kumalekezero a dziko lonse lapansi.+ 12 Masamba ake anali okongola ndipo unali ndi zipatso zambiri. Mumtengomo munali zakudya zokwanira chamoyo chilichonse. Nyama zakutchire+ zinali kukhala mumthunzi wake.+ Mbalame zam’mlengalenga zinali kukhala panthambi zake+ ndipo zamoyo zonse zinali kupeza chakudya mmenemo.
13 “‘Nditagona pabedi langa, ndinapitiriza kuona masomphenya ndipo ndinangoona mlonda+ woyera+ akutsika kuchokera kumwamba. 14 Mlondayo anali kulankhula mofuula kuti: “Gwetsani mtengowo+ ndipo dulani nthambi zake. Yoyolani masamba ake ndi kumwaza zipatso zake. Nyama zithawe pansi pake ndipo mbalame zichoke panthambi zake,+ 15 koma musiye chitsa chake munthaka. Chitsacho muchikulunge ndi mkombero wachitsulo ndi wamkuwa. Chikhale pakati pa udzu wakutchire ndipo chizinyowa ndi mame akumwamba. Chikhalenso pakati pa nyama zakutchire ndi udzu wa padziko lapansi.+ 16 Mtima wake usinthidwe kuchoka kumtima wa munthu n’kukhala mtima wa nyama+ ndipo padutse nthawi zokwanira 7.+ 17 Alonda+ ndi amene alamula zimenezi. Angelo oyera* ndi amene apempha zimenezi ndi cholinga chakuti anthu adziwe kuti Wam’mwambamwamba ndiye Wolamulira wa maufumu a anthu,+ ndiponso adziwe kuti iye akafuna kupereka ulamuliro kwa munthu aliyense, amamupatsa+ ndipo amaika ngakhale munthu wonyozeka kwambiri kuti azilamulira.”+
18 “‘Amenewa ndiwo maloto amene ine Mfumu Nebukadinezara ndinalota. Tsopano iwe Belitesazara umasulire malotowa, pakuti amuna ena onse anzeru a mu ufumu wanga alephera kuwamasulira.+ Koma iwe ungathe kuwamasulira chifukwa mzimu wa milungu yoyera uli mwa iwe.’+
19 “Pa nthawi imeneyo Danieli, wotchedwa Belitesazara,+ anada nkhawa kwa kanthawi ndipo anachita mantha.+
“Chotero mfumuyo inamuuza kuti, ‘Iwe Belitesazara, malotowa ndi kumasulira kwake zisakuchititse mantha.’+
“Belitesazara anayankha kuti, ‘Inu mbuyanga, zikanakhala bwino malotowa akanakhala okhudza anthu amene amadana nanu. Zikanakhalanso bwino kumasulira kwake kukanakhala kokhudza adani anu.+
20 “‘Inu munaona mtengo umene unakula kwambiri ndipo unakhala wamphamvu kwambiri. Mtengowo unatalika mpaka kufika kumwamba ndipo unali kuoneka padziko lonse lapansi.+ 21 Masamba ake anali okongola ndipo unali ndi zipatso zambiri. Mumtengomo munali zakudya zokwanira chamoyo chilichonse. Nyama zakutchire zinali kukhala pansi pake.+ Mbalame zam’mlengalenga zinali kukhala panthambi zake. 22 Mtengowo ndinuyo mfumu,+ chifukwa mwakula ndipo mwakhala ndi mphamvu. Ulemerero wanu wakula mpaka kufika kumwamba+ ndipo ulamuliro wanu wafika kumalekezero a dziko lapansi.+
23 “‘Chifukwa chakuti inu mfumu munaona mlonda woyera+ akutsika kuchokera kumwamba, akunena kuti: “Gwetsani mtengowo ndipo muuwononge, koma musiye chitsa chake munthaka, mutachikulunga ndi mkombero wachitsulo ndi wamkuwa, chikhale pakati pa udzu wakutchire ndipo chizinyowa ndi mame akumwamba, chikhale limodzi ndi nyama zakutchire kufikira patadutsa nthawi zokwanira 7,”+ 24 lamulo+ la Wam’mwambamwamba+ ligwera inu mbuyanga mfumu,+ ndipo kumasulira kwake ndi uku: 25 Inuyo adzakuthamangitsani pakati pa anthu ndipo muzidzakhala pakati pa nyama zakutchire.+ Muzidzadya udzu ngati ng’ombe+ ndipo muzidzanyowa ndi mame akumwamba. Ndiyeno padzadutsa nthawi zokwanira 7+ kufikira mutadziwa kuti Wam’mwambamwamba ndiye Wolamulira wa maufumu a anthu,+ ndiponso kuti akafuna kupereka ulamuliro kwa munthu aliyense, amamupatsa.+
26 “‘Popeza ananena kuti asiye chitsa cha mtengowo,+ inu mudzayambiranso kulamulira mu ufumu wanu mutadziwa kuti Mulungu ndiye akulamulira kumwamba.+ 27 Chotero inu mfumu, chonde mverani malangizo anga+ ndipo chotsani machimo anu pochita zolungama.+ Muchotsenso zolakwa zanu pochitira chifundo osauka.+ Mukatero, mwina zinthu zidzapitiriza kukuyenderani bwino kwa nthawi yaitali.’”+
28 Zonsezi zinagweradi mfumu Nebukadinezara.+
29 Patapita miyezi 12 kuchokera pamene analota maloto amenewa, Nebukadinezarayo anali kuyenda padenga* la nyumba yachifumu ya ku Babulo. 30 Mfumuyo inali kunena kuti:+ “Kodi uyu si Babulo Wamkulu amene ine ndamanga ndi mphamvu zanga zazikulu+ ndiponso ndi ulemerero wanga waukulu ndi cholinga chakuti kukhale nyumba yachifumu?”+
31 Mfumuyo ili mkati molankhula mawu amenewa, kumwamba kunamveka mawu akuti: “Tamvera iwe mfumu Nebukadinezara! ‘Ufumu wachoka m’manja mwako,+ 32 ndipo akuthamangitsa pakati pa anthu. Uyamba kukhala pakati pa nyama zakutchire+ ndipo uzidzadya udzu ngati ng’ombe. Ndiyeno padutsa nthawi zokwanira 7 kufikira utadziwa kuti Wam’mwambamwamba ndiye Wolamulira wa maufumu a anthu, ndiponso kuti akafuna kupereka ulamuliro kwa munthu aliyense, amamupatsa.’”+
33 Nthawi yomweyo+ mawuwa anakwaniritsidwa pa Nebukadinezara ndipo anathamangitsidwa pakati pa anthu. Iye anayamba kudya udzu ngati ng’ombe ndipo thupi lake linkanyowa ndi mame akumwamba. Tsitsi lake linatalika kwambiri ngati nthenga za chiwombankhanga ndipo zikhadabo zake zinatalika ngati za mbalame.+
34 “Pamapeto pa masiku amenewa,+ ine Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba+ ndipo nzeru zanga zinayamba kubwerera. Ndinatamanda Wam’mwambamwamba+ ndipo amene adzakhalapo mpaka kalekale ndinamutamanda ndi kumulemekeza,+ chifukwa ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo ufumu wake udzakhalapo ku mibadwomibadwo.+ 35 Iye amaona anthu onse okhala padziko lapansi ngati opanda pake+ ndipo amachita zinthu mogwirizana ndi chifuniro chake pakati pa makamu akumwamba ndi pakati pa anthu okhala padziko lapansi.+ Palibe aliyense amene angaletse dzanja+ lake kapena kumufunsa kuti, ‘Mukuchita chiyani?’+
36 “Ndiyeno kuti ndipezenso ulemerero wa ufumu wanga, ukulu ndi nzeru zanga zinayamba kubwerera kwa ine.+ Pamenepo alangizi anga ndi nduna zanga anayamba kufunsiranso malangizo anga. Kenako ndinabwezeretsedwa pampando wanga wachifumu ndipo anthu anayamba kundipatsa ulemu waukulu.+
37 “Tsopano ine Nebukadinezara ndikutamanda, kukweza ndi kulemekeza Mfumu yakumwamba,+ chifukwa ntchito zake zonse ndizo choonadi, njira zake ndi zolungama,+ ndiponso amatha kutsitsa anthu onyada.”+