Obadiya
1 Awa ndi masomphenya a Obadiya:*
Zimene Yehova Ambuye Wamkulu Koposa akunena zokhudza Edomu+ ndi izi:
“Ife tamva uthenga wochokera kwa Yehova,
Ndipo nthumwi yatumidwa kwa anthu amitundu ina kukanena kuti:
‘Konzekani! Tiyeni tikamenyane naye.’”+
2 “Taona! Ndakuchititsa kukhala wosafunika pakati pa mitundu ina,
Ndipo ikukuona kuti ndiwe wonyozeka kwambiri.+
3 Mtima wako wodzikuza wakupusitsa,+
Iwe amene ukukhala mʼmalo obisika amʼthanthwe,
Uli pamwamba pa phiri nʼkumanena mumtima mwako kuti,
‘Ndani angandigwetsere pansi?’
4 Ngakhale utamakhala mʼmwamba* ngati chiwombankhanga,
Kapena utamanga chisa chako pakati pa nyenyezi,
Ine ndidzakugwetsapo pamenepo,” akutero Yehova.
5 “Akuba atabwera kwa iwe, kapena mbava zitabwera usiku,
Kodi sangabe zokhazo zimene akufuna?
(Koma ndiye udzawonongedwatu!)*
Kapena okolola mphesa atabwera kwa iwe,
Kodi sangasiyeko zina zoti munthu nʼkukunkha?+
6 Koma Esau ndiye wafufuzidwatu!
Anthu asakasaka chuma chake chonse chobisika nʼkuchitenga.
7 Anthu amene unachita nawo mgwirizano* akuthamangitsira kumalire.
Onsewo akupusitsa.
Anthu amene unkakhala nawo mwamtendere akugonjetsa.
Anthu amene ukudya nawo limodzi adzakutchera ukonde,
Koma iwe sudzazindikira.”
8 Yehova akuti: “Kodi pa tsiku limenelo,
Sindidzawononga anthu anzeru mu Edomu,+
Komanso anthu ozindikira mʼdera lamapiri la Esau?
9 Iwe Temani,+ asilikali ako adzachita mantha,+
Chifukwa aliyense mʼdera lamapiri la Esau adzaphedwa.+
10 Popeza unachitira nkhanza mʼbale wako Yakobo,+
Udzachititsidwa manyazi kwambiri.+
Udzaphedwa ndipo sudzakhalaponso mpaka kalekale.+
11 Pa tsiku limene unangoima nʼkumaonerera,
Pa tsiku limene adani* anagwira gulu la asilikali a mʼbale wako nʼkupita nawo ku ukapolo,+
Ndiponso pamene anthu akudziko lina analowa mumzinda* wake nʼkuchita maere+ pa Yerusalemu,
Iwe unali ngati mmodzi wa adaniwo.
12 Iwe sumayenera kunyadira pa tsiku limene mʼbale wako anakumana ndi tsoka,+
Sumayenera kusangalala pa tsiku limene anthu a ku Yuda ankawonongedwa,+
Sumayeneranso kulankhula modzitama pa tsiku limene ankazunzika.
13 Iwe sumayenera kulowa mumzinda* wa anthu anga pa tsiku limene anakumana ndi tsoka.+
Sumayenera kunyadira pamene mʼbale wako ankavutika pa tsiku limene anakumana ndi tsoka.
Ndipo sumayeneranso kutenga chuma chake pa tsiku limene anakumana ndi tsoka.+
14 Iwe sumayenera kuima panjira kuti uzipha anthu ake amene akuthawa.+
Sumayeneranso kugwira anthu ake amene apulumuka nʼkuwapereka kwa adani awo pa tsiku limene ankazunzika.+
15 Tsiku la Yehova limene adzalange mitundu yonse ya anthu lili pafupi.+
Zimene wachitira mʼbale wako, iwenso adzakuchitira zomwezo.+
Zimene unachitira anthu ena zidzakubwerera pamutu pako.
16 Mmene wamwera vinyo paphiri langa loyera,
Ndi mmenenso mitundu ina yonse ya anthu izidzamwera mkwiyo wanga nthawi zonse.+
Iwo adzamwa ndi kugugudiza mkwiyo wanga,
Ndipo zidzakhala ngati sanakhalepo nʼkomwe.
17 Anthu onse opulumuka adzakhala paphiri la Ziyoni+
Ndipo phiri limeneli lidzakhala loyera.+
Anthu a mʼbanja la Yakobo adzatenganso zinthu zimene zinali zawo.+
18 A mʼbanja la Yakobo adzakhala ngati moto,
A mʼbanja la Yosefe adzakhala ngati malawi a moto,
Ndipo a mʼbanja la Esau adzakhala ngati mapesi.
Moto wawo udzayatsa ndi kunyeketsa mapesiwo,
Ndipo palibe aliyense wa mʼbanja la Esau amene adzapulumuke,+
Chifukwa Yehova ndi amene wanena.
19 Iwo adzatenga dera la Negebu ndi dera lamapiri la Esau,+
Komanso dera la Sefela ndi dera la Afilisiti.+
Adzatenganso madera a Efuraimu ndi Samariya,+
Ndipo Benjamini adzatenga dera la Giliyadi.
20 Anthu amene anatengedwa pamalo okwera omenyerapo nkhondowa nʼkupita nawo kudziko lina,+
Amene ndi Aisiraeli, adzatenga dziko la Akanani mpaka kukafika ku Zarefati.+
Anthu amene anatengedwa kuchokera ku Yerusalemu, amene anali ku Sefaradi, adzatenga mizinda ya Negebu.+