Kalata yachiwiri yopita kwa Timoteyo
2 Choncho iwe mwana wanga,+ pitiriza kupeza mphamvu mʼkukoma mtima kwakukulu kwa Khristu Yesu. 2 Zinthu zimene unazimva kwa ine ndi kwa mboni zambiri,+ uziphunzitse kwa anthu okhulupirika ndipo nawonso adzakhala oyenerera kuphunzitsa ena. 3 Monga msilikali wabwino+ wa Khristu Yesu, khala wokonzeka kukumana ndi mavuto.+ 4 Msilikali sachita nawo* zamalonda* zimene anthu ena amachita, pofuna kukondweretsa amene anamulemba usilikali. 5 Ngakhalenso pa mpikisano, munthu salandira mphoto* akapanda kupikisana nawo motsatira malamulo.+ 6 Mlimi wakhama ayenera kukhala woyambirira kudya zipatso za mbewu zake. 7 Nthawi zonse uziganizira zimene ndikukuuzazi ndipo Ambuye adzakuthandiza kumvetsa zinthu zonse.
8 Kumbukira kuti, mogwirizana ndi uthenga wabwino umene ndikulalikira,+ Yesu Khristu anaukitsidwa+ ndipo anali mbadwa ya Davide.+ 9 Chifukwa cha uthengawu, ndikuvutika ndipo ndatsekeredwa mʼndende ngati chigawenga.+ Komabe mawu a Mulungu samangika.+ 10 Choncho ndikupirirabe zinthu zonse chifukwa cha anthu osankhidwa,+ kuti nawonso alandire chipulumutso kudzera mwa Khristu Yesu komanso alandire ulemerero wosatha. 11 Mawu awa ndi oona: Ndithudi, ngati tinafa naye limodzi, tidzakhalanso ndi moyo limodzi naye.+ 12 Tikapitiriza kupirira, tidzalamuliranso naye monga mafumu.+ Tikamukana, iyenso adzatikana,+ 13 koma tikakhala osakhulupirika, iye adzakhalabe wokhulupirika, chifukwa sangadzikane.
14 Uziwakumbutsa zimenezi nthawi zonse. Uziwalangiza* pamaso pa Mulungu, kuti asamakangane pa mawu. Kuchita zimenezi kulibe phindu mʼpangʼono pomwe chifukwa kumawononga chikhulupiriro cha omvetsera. 15 Chita chilichonse chotheka kuti usonyeze kuti ndiwe wovomerezeka pamaso pa Mulungu, munthu wosachita manyazi ndi ntchito imene wagwira ndiponso wophunzitsa ndi kufotokoza bwino mawu a choonadi.+ 16 Koma uzipewa nkhani zopeka zimene zimaipitsa zinthu zoyera+ chifukwa zimachititsa kuti anthu ambiri asamaope Mulungu, 17 ndipo mawu awo amafalikira ngati chilonda chonyeka. Ena mwa anthu amenewo ndi Hemenayo ndi Fileto.+ 18 Anthu amenewa akupotoza choonadi, ponena kuti akufa anauka kale+ ndipo akuwononga chikhulupiriro cha ena. 19 Komabe, maziko olimba a Mulungu adakalipo, ndipo ali ndi chidindo cha mawu akuti: “Yehova* amadziwa anthu ake,”+ ndiponso akuti: “Aliyense woitana pa dzina la Yehova*+ aleke kuchita zosalungama.”
20 Mʼnyumba yaikulu simukhala zinthu* zagolide ndi zasiliva zokha, koma mumakhalanso zamtengo ndi zadothi. Zinthu zina zimakhala za ntchito yolemekezeka, koma zina zimakhala za ntchito yonyozeka. 21 Choncho ngati munthu akupewa zinthu za ntchito yonyozekazo, adzakhala chinthu* cha ntchito yolemekezeka, choyera, chofunika kwa mwiniwake, ndi chokonzeka kugwira ntchito iliyonse yabwino. 22 Choncho thawa zilakolako za unyamata, koma tsatira chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere limodzi ndi anthu oitana pa Ambuye ndi mtima woyera.
23 Ndiponso, uzipewa kutsutsana pa zinthu zopusa ndi zopanda nzeru+ chifukwa zimayambitsa mikangano. 24 Kapolo wa Ambuye sayenera kukangana ndi anthu. Koma ayenera kukhala wodekha kwa onse,+ woyenerera kuphunzitsa, wougwira mtima ena akamulakwira+ 25 ndiponso wotha kulangiza mofatsa anthu otsutsa+ kuti mwina Mulungu angawalole kulapa* nʼkudziwa choonadi molondola.+ 26 Komanso mwina nzeru zingawabwerere nʼkupulumuka mumsampha wa Mdyerekezi, chifukwa wawagwira amoyo pofuna kuti azichita zofuna zake.+