Wolembedwa ndi Luka
16 Kenako anauzanso ophunzira ake kuti: “Munthu wina wolemera anali ndi mtumiki woyangʼanira nyumba yake, amene anthu ena anamuneneza kuti akumusakazira chuma. 2 Choncho anamuitana nʼkumuuza kuti, ‘Ndamva zoipa zimene ukuchita. Pita ukalembe lipoti la mmene wakhala ukugwirira ntchito yoyangʼanira nyumba ino nʼkundipatsa, chifukwa supitiriza kuyendetsa ntchito zapanyumba pano.’ 3 Ndiyeno mtumikiyo mumtima mwake anati, ‘Nditani ine? Abwana anga akufuna kundichotsa ntchito. Sindingathe kulima chifukwa ndilibe mphamvu ndipo ndikuchita manyazi kuti ndikhale wopemphapempha. 4 Eya! Ndadziwa zoti ndichite kuti akandichotsa ntchito, anthu akandilandire bwino mʼnyumba zawo.’ 5 Ndiyeno anaitana amene anali ndi ngongole kwa bwana wake mmodzi ndi mmodzi, ndipo anafunsa woyamba kuti, ‘Uli ndi ngongole yochuluka bwanji kwa bwana wanga?’ 6 Iye anayankha kuti, ‘Mitsuko* 100 ya mafuta a maolivi.’ Iye anamuuza kuti, ‘Tenga kalata ya mgwirizano wa ngongole yako ndipo ukhale pansi nʼkulemba mitsuko 50 mwamsanga.’ 7 Kenako anafunsa wina kuti, ‘Nanga iwe, ngongole yako ndi yochuluka bwanji?’ Iye anayankha kuti, ‘Madengu 100 a tirigu.’* Iye anamuuza kuti, ‘Tenga kalata ya mgwirizano wa ngongole yako ndipo ulembepo madengu 80.’ 8 Bwana wake uja anayamikira mtumiki ameneyu, ngakhale kuti anali wosalungama, chifukwa anachita zinthu mwanzeru.* Chifukwa ana a mu nthawi ino* amachita mwanzeru akamachita zinthu ndi anthu a mʼbadwo wawo kuposa ana a kuwala.+
9 Inunso ndikukuuzani kuti: Pezani anzanu pogwiritsa ntchito chuma chosalungama,+ kuti chumacho chikatha, akakulandireni mʼmalo okhala amuyaya.+ 10 Munthu amene ndi wokhulupirika pa chinthu chachingʼono amakhalanso wokhulupirika pa chinthu chachikulu, ndipo munthu amene ndi wosakhulupirika pa chinthu chachingʼono amakhalanso wosakhulupirika pa chinthu chachikulu. 11 Choncho ngati simunasonyeze kuti ndinu wokhulupirika pa chuma chosalungama, ndi ndani amene angakupatseni ntchito yoyangʼanira chuma chenicheni? 12 Komanso ngati simunasonyeze kuti ndinu wokhulupirika pa zinthu za ena, ndi ndani angakupatseni mphoto imene anakusungirani?+ 13 Mtumiki sangakhale kapolo wa ambuye awiri, chifukwa akhoza kudana ndi mmodzi nʼkukonda winayo, kapena angakhale wokhulupirika kwa mmodzi nʼkunyoza winayo. Simungakhale akapolo a Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.”+
14 Tsopano Afarisi amene ankakonda kwambiri ndalama, ankamvetsera zonsezi ndipo anayamba kumunyoza.+ 15 Choncho iye anawauza kuti: “Inu ndi amene mumanena pamaso pa anthu kuti ndinu olungama,+ koma Mulungu akudziwa mitima yanu.+ Chifukwa chimene anthu amachiona kuti ndi chapamwamba ndi chonyansa pamaso pa Mulungu.+
16 Anthu ankalalikira za Chilamulo ndi zimene aneneri analemba kudzafika mʼnthawi ya Yohane. Kuyambira nthawi imeneyo, uthenga wabwino umene ukulengezedwa ndi wokhudza Ufumu wa Mulungu, ndipo anthu osiyanasiyana akuyesetsa mwakhama kuti akalowemo.+ 17 Ndithudi, nʼzosavuta kuti kumwamba ndi dziko lapansi zichoke kusiyana ndi kuti kachigawo kakangʼono ka chilembo cha mʼChilamulo kasakwaniritsidwe.+
18 Aliyense amene wasiya mkazi wake nʼkukwatira wina, wachita chigololo ndipo aliyense amene wakwatira mkazi wosiyidwayo nayenso wachita chigololo.+
19 Panali munthu winawake wolemera amene ankakonda kuvala zovala zapepo ndi nsalu zabwino kwambiri. Iye ankasangalala komanso kudyerera tsiku ndi tsiku. 20 Komanso panali munthu wina wopemphapempha, amene anali ndi zilonda thupi lonse dzina lake Lazaro ndipo anthu ankamukhazika pageti la munthu wachumayo. 21 Iyeyo ankalakalaka kudya nyenyeswa zakugwa patebulo la wachuma uja. Agalu nawonso ankabwera kudzanyambita zilonda zakezo. 22 Patapita nthawi wopemphapempha uja anamwalira ndipo angelo anamutenga kukamuika pambali pa Abulahamu.*
Munthu wachuma ujanso anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda. 23 Ali mʼMandamo* komanso akuzunzika, anakweza maso ake nʼkuona Abulahamu ali chapatali ndipo Lazaro anali pambali pake.* 24 Choncho anaitana kuti, ‘Atate Abulahamu, ndichitireni chifundo. Mutume Lazaro kuti aviike nsonga ya chala chake mʼmadzi kuti aziziritse lilime langa, chifukwa ndikuzunzika mʼmoto wolilimawu.’ 25 Koma Abulahamu anati, ‘Mwanawe, kumbukira kuti unalandiriratu zabwino zako zonse pamene unali moyo, ndipo Lazaro analandira zinthu zoipa. Ndiye panopa akusangalala kuno koma iwe ukuzunzika. 26 Komanso pakati pa ife ndi inu paikidwa phompho lalikulu kwambiri, moti amene akufuna kubwera kumeneko kuchokera kuno sangathe. Komanso anthu sangaoloke kuchokera kumeneko kubwera kuno.’ 27 Ndiyeno munthu wachuma uja anati, ‘Popeza zili choncho, ndikukupemphani atate kuti mumutumize kunyumba ya bambo anga. 28 Chifukwa ndili ndi azichimwene anga 5 kumeneko, choncho apite akawapatse umboni wokwanira, kuti nawonso asadzabwere kumalo ozunzikira kuno.’ 29 Koma Abulahamu ananena kuti, ‘Kumeneko ali ndi zolemba za Mose komanso za aneneri, amvere zimenezo.’+ 30 Kenako iye anati, ‘Ayi chonde atate Abulahamu, koma ngati wina wochokera kwa akufa angapite kumeneko, iwo adzalapa ndithu.’ 31 Koma iye anamuuza kuti, ‘Ngati sakumvera zolemba za Mose+ komanso za aneneri, sangathekebe ngakhale wina atauka kwa akufa.’”