Levitiko
6 Yehova anapitiriza kuuza Mose kuti: 2 “Munthu akachimwa ndipo wachita mosakhulupirika kwa Yehova+ ponamiza mnzake pa chinthu chimene anamusungitsa,+ kapena chimene anamubwereka, kapena wamubera mnzake, kapena wamuchitira chinyengo, 3 kapena watola chinthu chotayika koma akukana kuti sanachitole, ndipo ngati walumbira monama pa tchimo lililonse limene angachite,+ azichita izi: 4 Ngati wachimwa ndipo wapalamula mlandu, azibweza zinthu zimene anabazo, kapena zinthu zimene analanda mwachinyengo, kapena chimene anamʼsungitsa, kapena chinthu chotayika chimene anatola, 5 kapena chilichonse chimene analumbira monama. Azibweza chinthucho+ nʼkuwonjezerapo limodzi mwa magawo ake 5. Azibweza zimenezi kwa mwiniwake pa tsiku limene wapezeka kuti ndi wolakwa. 6 Ndipo azibweretsa kwa wansembe nkhosa yamphongo yopanda chilema kuti ikhale nsembe yake yakupalamula, yoperekedwa kwa Yehova, mogwirizana ndi mtengo umene wagamulidwa kuti ikhale nsembe yakupalamula.+ 7 Wansembe aziphimba machimo a munthuyo pamaso pa Yehova, ndipo adzakhululukidwa chilichonse chimene wachita chimene chapangitsa kuti apalamule mlandu.”+
8 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 9 “Lamula Aroni ndi ana ake kuti, ‘Ili ndi lamulo la nsembe yopsereza:+ Nsembe yopsereza izikhala pamoto, paguwa lansembe, usiku wonse mpaka mʼmawa ndipo moto wapaguwapo uzikhala ukuyaka nthawi zonse. 10 Wansembe azivala zovala zake zogwirira ntchito+ komanso azivala kabudula wansalu+ wobisa* thupi lake. Kenako azichotsa phulusa*+ la nsembe yopsereza imene yawotchedwa pamoto wapaguwalo ndipo aziika phulusalo pambali pa guwa lansembe. 11 Ndiyeno azivula zovalazo+ nʼkuvala zina. Akatero azitenga phulusalo nʼkupita nalo kumalo oyera, kunja kwa msasa.+ 12 Moto wapaguwa lansembe uziyaka nthawi zonse. Usamazime. Wansembe aziikapo nkhuni+ mʼmawa uliwonse nʼkuikapo nsembe yopsereza. Akatero aziwotcha mafuta a nsembe yamgwirizano pamotopo.+ 13 Motowo uziyaka nthawi zonse paguwa lansembe. Usamazime.
14 Tsopano lamulo la nsembe yambewu+ ndi ili: Ana a Aroni azibweretsa nsembeyi pamaso pa Yehova patsogolo pa guwa lansembe. 15 Mmodzi mwa iwo azitapako ufa wosalala wa nsembe yambewu kudzaza dzanja limodzi komanso azitengako mafuta ake ndi lubani yense amene ali pansembe yambewuyo. Akatero, aziziwotcha paguwa lansembe kuimira nsembe yonseyo kuti zikhale kafungo kosangalatsa* kwa Yehova.+ 16 Aroni ndi ana ake azidya zotsala za nsembe imeneyi.+ Azipanga mkate wopanda zofufumitsa ndi kudya mkatewo mʼmalo oyera. Aziudyera mʼbwalo la chihema chokumanako.+ 17 Pophika, musaikemo zofufumitsa zilizonse.+ Ndaupereka monga gawo lawo kuchokera pansembe zanga zowotcha pamoto.+ Zimenezi nʼzopatulika koposa+ mofanana ndi nsembe yamachimo komanso nsembe yakupalamula. 18 Mwamuna aliyense mwa ana a Aroni azidya mkatewo.+ Limeneli ndi gawo lawo lochokera pansembe zowotcha pamoto+ zoperekedwa kwa Yehova, mʼmibadwo yanu yonse mpaka kalekale. Chilichonse chimene chingakhudze nsembezi chidzakhala choyera.’”
19 Yehova analankhulanso ndi Mose kuti: 20 “Iyi ndi nsembe imene Aroni ndi ana ake ayenera kupereka kwa Yehova pa tsiku limene akudzozedwa:+ ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa*+ uzikhala nsembe yambewu+ yoperekedwa nthawi zonse. Hafu ya ufawo azipereka mʼmamawa ndipo hafu inayo madzulo. 21 Nsembeyo izikhala yophika ndi mafuta mʼchiwaya.+ Izikhala yosakaniza bwino ndi mafuta. Uzipereka mitanda yophika ya nsembe yambewu monga kafungo kosangalatsa* kwa Yehova. 22 Wansembe wodzozedwa amene adzalowe mʼmalo mwake, kuchokera pakati pa ana ake,+ azipereka nsembeyo. Aziwotcha nsembe yonseyo kuti ikhale nsembe yoperekedwa kwa Yehova. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale. 23 Nsembe iliyonse yambewu ya wansembe iziwotchedwa yonse. Sikuyenera kudyedwa.”
24 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 25 “Uza Aroni ndi ana ake kuti, ‘Ili ndi lamulo la nsembe yamachimo:+ Pamalo amene mukuphera nyama ya nsembe yopsereza+ muzipheraponso nyama ya nsembe yamachimo pamaso pa Yehova. Nsembeyi ndi yopatulika koposa. 26 Wansembe amene waipereka monga nsembe yamachimo aziidya.+ Aziidyera kumalo oyera, mʼbwalo la chihema chokumanako.+
27 Chilichonse chimene chingakhudze mnofu wake chidzakhala choyera, ndipo ngati munthu wadonthezera ena mwa magazi a nyamayo pachovala, chovala chimene wadonthezera magazicho muzichichapira kumalo oyera. 28 Ndipo chiwiya chadothi chimene mungawiritsiremo nyamayo muzichiswa. Koma mukawiritsira mʼchiwiya chakopa,* muzichikwecha nʼkuchitsuka ndi madzi.
29 Mwamuna aliyense amene ndi wansembe azidya nyamayo.+ Ndi yopatulika koposa.+ 30 Koma nyama ya nsembe yamachimo sikuyenera kudyedwa ngati ena mwa magazi ake analowa nawo mʼchihema chokumanako kuti aphimbire machimo mʼmalo oyera.+ Imeneyo muziiwotcha pamoto.’”