Numeri
32 Tsopano ana a Rubeni+ ndi ana a Gadi+ anali ndi ziweto zambiri ndipo anaona kuti dera la Yazeri+ komanso la Giliyadi, anali malo abwino a ziweto. 2 Choncho ana a Gadi ndi ana a Rubeniwo anapita kwa Mose, wansembe Eleazara ndi atsogoleri a gululo, nʼkukawauza kuti: 3 “Ataroti, Diboni, Yazeri, Nimira, Hesiboni,+ Eleyale, Sebamu, Nebo+ komanso Beoni,+ 4 ndi madera amene Yehova anawagonjetsa kuti akhale a Aisiraeli.+ Madera amenewa ndi abwino kwa ziweto, ndipo atumiki anufe tili ndi ziweto zambiri.”+ 5 Anapitiriza kuti: “Ngati mungatikomere mtima atumiki anufe, mutipatse madera amenewa kuti akhale cholowa chathu. Tisawoloke nawo Yorodano.”
6 Koma Mose poyankha, anafunsa ana a Gadi ndi ana a Rubeniwo kuti: “Kodi mukufuna kuti abale anu apite kunkhondo inu mutatsala kuno? 7 Nʼchifukwa chiyani mukufuna kufooketsa Aisiraeli kuti asawolokere kudziko limene Yehova anatsimikiza mtima kuwapatsa? 8 Nʼzimenenso makolo anu anachita ku Kadesi-barinea, nditawatuma kuti akafufuze dziko.+ 9 Iwo atafika kuchigwa cha Esikolo*+ nʼkuliona dzikolo, anafooketsa Aisiraeli kuti asakalowe mʼdziko limene Yehova anatsimikiza mtima kuwapatsa.+ 10 Pa tsiku limenelo Yehova anakwiya koopsa, ndipo analumbira kuti:+ 11 ‘Amuna amene anatuluka mu Iguputo kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, sadzaliona dziko+ limene ndinalumbira kuti ndidzapereka kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo,+ chifukwa sanandimvere ndi mtima wonse. 12 Koma Kalebe+ mwana wa Yefune Mkenizi, ndi Yoswa+ mwana wa Nuni, adzaliona dzikolo chifukwa akhala akumvera Yehova ndi mtima wonse.’+ 13 Yehova anawakwiyira koopsa Aisiraeli ndipo anawachititsa kuti azingoyendayenda mʼchipululu kwa zaka 40,+ mpaka mʼbadwo wonse wochita zoipa pamaso pa Yehova utatha.+ 14 Inunso mukuchita zoipa mofanana ndi makolo anu, ndipo mukuchititsa kuti mkwiyo woyaka moto wa Yehova uwonjezeke pa Isiraeli. 15 Mukasiya kumumvera, ndithu iye adzachititsanso anthu onsewa kukhalabe mʼchipululu muno ndipo mudzachititsa kuti anthu onsewa azunzike kwambiri.”
16 Kenako iwo anapitanso kwa iye nʼkunena kuti: “Mutilole timange makola amiyala a ziweto zathu kunoko ndi mizinda ya ana athu. 17 Koma ifeyo tikonzeka kuti tikamenye nkhondo+ ndipo tikhala patsogolo pa Aisiraeli mpaka titakawafikitsa kumalo awo. Koma ana athu tiwasiya mʼmizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri kuti tiwateteze kwa anthu a dziko lino. 18 Sitidzabwerera kunyumba zathu mpaka aliyense wa Aisiraeli atalandira malo ake kuti akhale cholowa chake.+ 19 Ife sitidzalandira nawo cholowa tsidya ilo la Yorodano kupita kutsogoloko, chifukwa talandira cholowa chathu kutsidya lakumʼmawa kwa Yorodano.”+
20 Mose anawauza kuti: “Chabwino, koma zitheka ngati mutachita izi: Mutenge zida nʼkukamenya nkhondo pamaso pa Yehova.+ 21 Komanso ngati aliyense wa inu atatenga zida zake zankhondo nʼkuwoloka Yorodano pamaso pa Yehova, mpaka atathamangitsa adani ake pamaso pake,+ 22 ndiponso mpaka dzikolo litagonjetsedwa pamaso pa Yehova.+ Pambuyo pake mukhoza kudzabwerera+ ndipo mudzakhala opanda mlandu kwa Yehova ndi kwa Isiraeli. Kenako dzikoli lidzakhala lanu pamaso pa Yehova.+ 23 Koma mukapanda kuchita zimenezi, mudzakhala kuti mwachimwira Yehova. Ndipo mukatero, dziwani kuti tchimo lanu lidzakutsatani. 24 Ndiye mukhoza kumanga mizinda ya ana anu ndi makola a ziweto zanu.+ Koma muchitedi zimene mwalonjeza.”
25 Ana a Gadi ndi ana a Rubeni anayankha Mose kuti: “Ife atumiki anu tichita zonse zimene mwalamula mbuyathu. 26 Ana athu ndi akazi athu atsala kuno mʼmizinda ya Giliyadi,+ limodzi ndi ziweto zathu zonse. 27 Koma atumiki anufe tiwoloka, aliyense atatenga zida kukamenya nkhondo pamaso pa Yehova,+ mogwirizana ndi zimene mwanena mbuyathu.”
28 Choncho Mose anapereka lamulo lokhudza iwowo kwa wansembe Eleazara, Yoswa mwana wa Nuni ndi kwa atsogoleri a mafuko a Isiraeli. 29 Iye anawauza kuti: “Ngati ana a Gadi ndi ana a Rubeni atawoloka nanu Yorodano, aliyense atatenga zida kuti akamenye nkhondo pamaso pa Yehova, nʼkugonjetsa dzikolo pamaso panu, mudzawapatse dziko la Giliyadi kuti likhale cholowa chawo.+ 30 Koma akapanda kutenga zida nʼkuwoloka nanu limodzi, basi azidzakhala pakati panu mʼdziko la Kanani.”
31 Ana a Gadi ndi ana a Rubeni atamva mawuwo anati: “Tidzachita zimene Yehova walankhula kwa atumiki anufe. 32 Tidzawoloka ndi zida kukamenya nkhondo pamaso pa Yehova kudziko la Kanani.+ Koma tidzalandira cholowa chathu tsidya lino la Yorodano.” 33 Choncho Mose anapereka malo kwa ana a Gadi, ana a Rubeni+ komanso hafu ya fuko la Manase+ mwana wa Yosefe. Anawapatsa malo a ufumu wa Sihoni+ mfumu ya Aamori, malo a ufumu wa Ogi+ mfumu ya Basana ndi dera lonse la mizinda komanso midzi yozungulira.
34 Ndipo ana a Gadi anamanga* mizinda ya Diboni,+ Ataroti,+ Aroweli,+ 35 Atiroti-sofani, Yazeri,+ Yogebeha,+ 36 Beti-nimira+ ndi Beti-harana.+ Mizinda imeneyi inali ndi mipanda yolimba kwambiri komanso inali ndi makola a ziweto amiyala. 37 Ana a Rubeni anamanga mizinda ya Hesiboni,+ Eleyale,+ Kiriyataimu,+ 38 Nebo,+ Baala-meoni,+ ndi Sibima. Mayina a mizindayi anawasintha, nʼkuipatsa mayina ena atsopano.
39 Ana a Makiri+ mwana wa Manase, anaukira mzinda wa Giliyadi nʼkuulanda ndipo anathamangitsa Aamori amene ankakhala mumzindawo. 40 Choncho Mose anapereka mzinda wa Giliyadi kwa Makiri mwana wa Manase, ndipo iye anayamba kukhala mmenemo.+ 41 Yairi mwana wa Manase anaukira Aamori nʼkulanda midzi yawo ingʼonoingʼono. Midzi imeneyi anayamba kuitchula kuti Havoti-yairi.*+ 42 Noba nayenso anaukira nʼkulanda mzinda wa Kenati ndi midzi yake yozungulira. Mzindawo anaupatsa dzina lake, loti Noba.