Kalata Yopita kwa Filimoni
1 Ine Paulo, mkaidi+ chifukwa cha Khristu Yesu, ndili limodzi ndi Timoteyo+ mʼbale wathu, ndipo ndikulembera iwe Filimoni wantchito mnzathu wokondedwa, 2 limodzi ndi mlongo wathu Apiya ndiponso msilikali mnzathu Arikipo+ ndi mpingo umene umasonkhana mʼnyumba mwako:+
3 Kukoma mtima kwakukulu ndiponso mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu, zikhale nanu.
4 Nthawi zonse ndimayamika Mulungu wanga ndikamakutchula mʼmapemphero anga,+ 5 ndikamva za chikhulupiriro chako ndiponso mmene umakondera Ambuye Yesu komanso oyera onse. 6 Ndimapemphera kuti chikhulupiriro chimene iweyo ndi anthu ena muli nacho, chikuthandize kuzindikira chinthu chilichonse chabwino chimene tili nacho kudzera mwa Khristu. 7 Chikondi chako mʼbale chandisangalatsa ndi kundilimbikitsa kwambiri, chifukwa walimbikitsanso mitima ya oyera.
8 Choncho ngakhale kuti mʼdzina la Khristu ndili ndi ufulu waukulu wa kulankhula, moti nditha kukuuza zoyenera kuchita, 9 ndikuona kuti ndi bwino ndichite kukupempha mwachikondi. Ineyo Paulo, amene ndine wachikulire komanso mkaidi chifukwa cha Khristu Yesu, 10 ndikukupempha za mwana wanga Onesimo,+ amene ndakhala bambo wake+ pamene ndili kundende kuno. 11 Kale anali wosathandiza kwa iwe, koma panopa ndi wothandiza kwa iwe ndi ine. 12 Tsopano ndikumutumizanso kwa iwe. Iye ndi munthu wapamtima panga.
13 Ndikanakonda kukhala nayebe kuti mʼmalo mwa iwe, apitirize kunditumikira pamene ndili kundende kuno chifukwa cha uthenga wabwino.+ 14 Koma sindikufuna kuchita chilichonse popanda chilolezo chako, kuti zabwino zimene ungachite zisakhale zochita kukukakamiza, koma uzichite mwa kufuna kwako.+ 15 Mwina nʼchifukwa chake anachoka kumeneko kwa nthawi yochepa,* kuti udzakhale nayenso kwamuyaya. 16 Sukhala nayenso monga kapolo,+ koma akhalanso mʼbale wokondedwa,+ amene ine ndimamukonda kwambiri. Koma iweyo uyenera kumukonda koposa pamenepo chifukwa ndi kapolo wako komanso mʼbale wako mwa Ambuye. 17 Choncho ngati umandionadi kuti ndine mnzako, umulandire ndi manja awiri ngati mmene ungalandirire ineyo. 18 Komanso ngati anakulakwira kanthu kalikonse kapena ngati ali nawe ngongole, ngongoleyo ikhale kwa ine. 19 Ine Paulo, ndikulemba ndi dzanja langa: Ndidzabweza ngongoleyo. Ndipo sindikufunikira kuchita kukuuza zimenezi, paja iwenso uli ndi ngongole kwa ine ya moyo wako. 20 Chonde mʼbale, ndithandizeko mwa Ambuye: Ulimbikitse mtima wanga monga munthu wotsatira Khristu.
21 Ndikukulembera zimenezi chifukwa ndikukhulupirira kuti uzichitadi. Ndikudziwanso kuti uchita ngakhale zoposa zimene ndanenazi. 22 Komanso ukonzeretu chipinda choti ndidzafikiremo. Ndikukhulupirira kuti chifukwa cha mapemphero anu, ndimasulidwa kuti ndidzakutumikireni.+
23 Epafura,+ mkaidi mnzanga mwa Khristu Yesu, akupereka moni. 24 Maliko, Arisitako,+ Dema+ ndi Luka,+ omwe ndi antchito anzanga, akuperekanso moni.
25 Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu Khristu kukhale nanu chifukwa cha mzimu umene mumasonyeza.