Nehemiya
13 Pa tsiku limenelo buku la Mose linawerengedwa anthu onse akumva.+ Iwo anapeza kuti mʼbukumo analembamo kuti mbadwa iliyonse ya Amoni ndi ya Mowabu+ isamaloledwe kukhala mʼgulu la anthu a Mulungu woona,+ 2 chifukwa iwowa sanapatse Aisiraeli chakudya ndi madzi. Mʼmalomwake, analemba ganyu Balamu kuti awatemberere.+ Koma Mulungu wathu anasintha temberero limenelo kukhala dalitso.+ 3 Choncho atangomva Chilamulocho, anayamba kuchotsa anthu a mitundu ina pakati pa Aisiraeli.+
4 Zimenezi zisanachitike, wansembe amene ankayangʼanira zipinda zosungira katundu* mʼnyumba* ya Mulungu wathu+ anali Eliyasibu,+ ndipo anali wachibale wa Tobia.+ 5 Eliyasibu anapatsa Tobia chipinda chachikulu chosungira katundu.* Poyamba mʼchipindachi ankaikamo nsembe yambewu, lubani,* ziwiya, chakhumi cha mbewu, vinyo watsopano ndi mafuta+ zimene Alevi,+ oimba ndi alonda apageti ankayenera kulandira, komanso zimene ankapereka kwa ansembe.+
6 Nthawi yonseyi ine sindinali ku Yerusalemu, chifukwa mʼchaka cha 32+ cha ulamuliro wa Aritasasita+ mfumu ya Babulo, ndinabwerera kwa mfumu. Ndiyeno patapita nthawi, ndinapempha mfumuyo kuti ndichoke kwakanthawi. 7 Kenako ndinafika ku Yerusalemu ndipo ndinaona zoipa zimene Eliyasibu+ anachita popatsa Tobia+ chipinda mʼbwalo la nyumba ya Mulungu woona. 8 Zimenezi zinandinyansa kwambiri. Choncho ndinataira panja katundu yense wa Tobia amene anali mʼchipinda chosungiramo zinthu.* 9 Zitatero ndinalamula kuti ayeretse zipinda zosungira katundu.* Kenako ndinabwezera pamalo pake ziwiya za mʼnyumba ya Mulungu+ woona komanso zopereka zambewu ndi lubani.+
10 Ndinazindikiranso kuti Alevi sankapatsidwa magawo awo, moti Alevi+ ndiponso oimba amene ankatumikira anachoka,+ ndipo aliyense anapita kumunda wake.+ 11 Choncho ndinadzudzula atsogoleriwo+ ndipo ndinawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani nyumba ya Mulungu woona yasiyidwa chonchi?”+ Kenako ndinawasonkhanitsa nʼkuwabwezera pa ntchito zawo. 12 Ayuda onse anabweretsa chakhumi+ cha mbewu, vinyo watsopano ndiponso mafuta kuzipinda zosungira katundu.+ 13 Ndiyeno ndinaika Selemiya wansembe, Zadoki wokopera Malemba* ndi Pedaya Mlevi, kuti aziyangʼanira zipinda zosungira katundu. Ndipo Hanani mwana wa Zakuri amene anali mwana wa Mataniya, anali wachiwiri wawo chifukwa anthuwa ankaonedwa kuti ndi okhulupirika. Iwowa anapatsidwa udindo wogawa zinthu kwa abale awo.
14 Mundikumbukire,+ inu Mulungu wanga, chifukwa cha zinthu zimenezi ndiponso chikondi chokhulupirika chimene ndinasonyeza chifukwa cha nyumba ya Mulungu wanga ndi zonse zochitika kumeneko.+
15 Masiku amenewo ndinaona anthu ku Yuda akuponda moponderamo mphesa pa tsiku la Sabata.+ Ankabweretsa mbewu ndipo ankazikweza pa abulu. Ankabweretsanso vinyo, mphesa, nkhuyu ndi katundu wosiyanasiyana ku Yerusalemu pa tsiku la Sabata.+ Choncho ndinawadzudzula pa nkhani yogulitsa zinthu pa tsiku limenelo.* 16 Anthu a ku Turo amene ankakhala mumzindawu ankabweretsa nsomba ndi zinthu zosiyanasiyana nʼkumagulitsa kwa anthu a ku Yuda ndiponso mu Yerusalemu pa tsiku la Sabata.+ 17 Choncho ndinadzudzula anthu olemekezeka a ku Yuda nʼkuwauza kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukuchita zinthu zoipa mpaka kufika poipitsa tsiku la Sabata? 18 Kodi izi si zimene makolo anu anachita, moti Mulungu wathu anabweretsa tsoka lonseli pa ife ndi mzindawu? Ndiye inu mukuchititsa kuti akwiyire kwambiri Aisiraeli poipitsa Sabata?”+
19 Ndiyeno mthunzi utafika pamageti a Yerusalemu, Sabata lisanayambe, ndinalamula kuti zitseko zitsekedwe. Ndinalamulanso kuti asatsegule zitsekozo mpaka Sabata litatha. Ndipo ndinaika mʼmageti atumiki anga ena kuti katundu aliyense asalowe pa tsiku la Sabata. 20 Choncho amalonda osiyanasiyana anagona panja pa Yerusalemu, mwinanso kawiri konse. 21 Kenako ndinawachenjeza kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukugona kunja kwa mpanda? Mukachitanso zimenezi, ndidzachita kukuthamangitsani.” Kuyambira nthawi imeneyo sanabwerenso pa tsiku la Sabata.
22 Ndiyeno ndinauza Alevi kuti azidziyeretsa nthawi zonse komanso azibwera kudzalondera mageti a mzinda kuti tsiku la Sabata likhale loyera.+ Inu Mulungu wanga, mundikumbukirenso pa zimenezi ndipo mundichitire chifundo mogwirizana ndi kuchuluka kwa chikondi chanu chokhulupirika.+
23 Pa nthawi imeneyo ndinaonanso kuti Ayuda ena anali atakwatira akazi+ a Chiasidodi,+ a Chiamoni ndi a Chimowabu.+ 24 Hafu ya ana awo aamuna ankalankhula Chiasidodi ndipo hafu ina inkalankhula zilankhulo za anthu a mitundu ina koma panalibe amene ankatha kulankhula chilankhulo cha Ayuda. 25 Choncho ndinawadzudzula ndiponso kuwatemberera. Ena mwa amunawa ndinawamenya+ komanso kuwazula tsitsi ndipo ndinawalumbiritsa pamaso pa Mulungu kuti: “Musapereke ana anu aakazi kwa ana awo aamuna, ndipo musalole kuti ana awo aakazi akwatiwe ndi ana anu aamuna kapenanso inuyo.+ 26 Kodi si akazi amenewa amene anachimwitsa Solomo mfumu ya Isiraeli? Pa mitundu yonse ya anthu panalibe mfumu yofanana ndi iye.+ Iye ankakondedwa ndi Mulungu wake,+ moti anamuika kukhala mfumu ya Aisiraeli onse. Koma akazi a mitundu ina anamuchimwitsa.+ 27 Nʼzodabwitsa kuti inunso mukuchita choipa chachikulu chimenechi, ndipo mukukwatira akazi a mitundu ina, zomwe nʼkusakhulupirika kwa Mulungu wathu.”+
28 Mmodzi mwa ana aamuna a Yoyada,+ mwana wa Eliyasibu,+ mkulu wa ansembe anali mkamwini wa Sanibalati+ wa ku Beti-horoni. Choncho ndinamuthamangitsa.
29 Inu Mulungu wanga, akumbukireni amenewa chifukwa anaipitsa unsembe+ ndiponso pangano limene munachita ndi ansembe ndi Alevi.+
30 Ndiyeno ndinawayeretsa ku zinthu zonse zodetsa za anthu a mitundu ina. Komanso ndinapereka ntchito kwa ansembe ndi Alevi, aliyense ndinamʼpatsa ntchito yake.+ 31 Ndinakonzanso zoti ena azibweretsa nkhuni+ pa nthawi zoikidwiratu ndiponso mbewu zoyamba kucha.
Inu Mulungu wanga, mundikumbukire pa zabwino zimene ndinachita.+