Ezara
1 Mʼchaka choyamba cha Koresi+ mfumu ya Perisiya, pokwaniritsa mawu a Yehova amene analankhula kudzera mwa Yeremiya,+ Yehova analimbikitsa Koresi mfumu ya Perisiya kuti alengeze mu ufumu wake wonse, zomwenso iye analemba mʼmakalata,+ kuti:
2 “Koresi mfumu ya Perisiya wanena kuti, ‘Yehova Mulungu wakumwamba wandipatsa maufumu onse apadziko lapansi.+ Iye wandituma kuti ndimumangire nyumba ku Yerusalemu+ mʼdziko la Yuda. 3 Aliyense amene ali pakati panu mwa anthu onse amene amamutumikira, Mulungu wake akhale naye ndipo apite ku Yerusalemu mʼdziko la Yuda nʼkukamanganso nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli. Iye ndi Mulungu woona ndipo nyumba yake inali ku Yerusalemu.* 4 Aliyense amene akukhala monga mlendo+ kulikonse, anthu oyandikana naye amuthandize pomupatsa siliva, golide, katundu, ziweto, limodzi ndi nsembe yaufulu ya nyumba ya Mulungu woona,+ yomwe inali ku Yerusalemu.’”
5 Ndiyeno atsogoleri a mabanja a fuko la Yuda, la Benjamini, ansembe, Alevi ndi aliyense amene Mulungu woona analimbikitsa mtima wake, anakonzeka kuti apite kukamanganso nyumba ya Yehova, yomwe inali ku Yerusalemu. 6 Anthu onse oyandikana nawo anawathandiza* powapatsa ziwiya zasiliva, zagolide, ziweto, zinthu zina zamtengo wapatali komanso katundu wosiyanasiyana, kuwonjezera pa zonse zimene zinaperekedwa mwaufulu.
7 Mfumu Koresi inabweretsanso ziwiya zamʼnyumba ya Yehova. Ziwiyazo nʼzimene Nebukadinezara anatenga ku Yerusalemu nʼkukaziika mʼkachisi wa mulungu wake.+ 8 Koresi mfumu ya Perisiya anatuma msungichuma Mitiredati kuti abweretse ziwiyazo nʼkuziwerenga. Atatero anazipereka kwa Sezibazara*+ mtsogoleri wa Yuda.
9 Ziwiyazo zinali zochuluka chonchi: ziwiya 30 zagolide zooneka ngati mabasiketi, ziwiya 1,000 zasiliva zooneka ngati mabasiketi ndi ziwiya 29 zowonjezera. 10 Panalinso mbale 30 zingʼonozingʼono zolowa zagolide, mbale 410 zingʼonozingʼono zolowa zasiliva zogwiritsira ntchito zina ndi ziwiya zina 1,000. 11 Ziwiya zonse zagolide ndi zasiliva zinalipo 5,400. Sezibazara anatenga zinthu zonsezi pamene anthu amene anagwidwa ukapolo+ ankachoka ku Babulo kupita ku Yerusalemu.