‘Opatsidwa’ Ali Mphatso ya Yehova
“Ndipo alendo adzaimirira ndi kudyetsa magulu ako.”—YESAYA 61:5.
1. Kodi nchifukwa ninji liwu lakuti ‘opatsidwa’ limatikumbutsa Yehova?
HA, Mulungu ali wopatsa wowoloŵa manja chotani nanga! Mtumwi Paulo anati: “[Yehova] apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse.” (Machitidwe 17:25) Aliyense wa ife akhoza kupindula mwakulingalira pa ‘mphatso iriyonse yabwino, ndi chininkho chirichonse changwiro’ zimene timalandira kwa Mulungu.—Yakobo 1:5, 17: Salmo 29:11; Mateyu 7:7; 10:19; 13:12; 21:43.
2, 3. (a) Kodi tiyenera kulabadira motani ku mphatso za Mulungu? (b) Kodi Alevi anali ‘opatsidwa’ mwanjira yotani?
2 Ndi chifukwa chabwino, wamasalmo anasinkhasinkha mmene akabwezera kwa Yehova. (Salmo 116:12) Mlengi wathu samasoŵa kalikonse kamene anthu alinako kapena kamene angakapatse. (Salmo 50:10, 12) Ngakhale ndichoncho, Yehova amasonyeza kuti zimamkondweretsa pamene anthu adzipereka okha ku kulambira kwake kowona. (Yerekezerani ndi Ahebri 10:5-7.) Anthu onse ayenera kudzipereka okha kudzipatulira kwa Mlengi wawo, ndipo nayenso, angapereke mwaŵi wowonjezereka, monga momwe zinakhalira kwa Alevi akale. Ngakhale kuti Aisrayeli onse anali odzipatulira kwa Mulungu, iye anasankha banja la Alevi la Aroni monga ansembe opereka nsembe pachihema ndi pakachisi. Bwanji ponena za Alevi ena onsewo?
3 Yehova anauza Mose kuti: ‘Sendera nalo kuno fuko la Levi . . . Ndipo asunge zipangizo zonse za chihema chokomanako . . . Ndipo udzipereka Alevi kwa Aroni ndi kwa ana ake amuna; apatsidwa [Chihebri, nethu·nimʹ] kwa iye ndithu, ochokera kwa ana a Israyeli.’ (Numeri 3:6, 8, 9, 41) Alevi anali ‘opatsidwa’ kwa Aroni kumatumikira m’ntchito za m’kachisi, choncho Mulungu anati: ‘Pakuti aperekedwa konse kwa ine ochokera mwa ana a Israyeli.’ (Numeri 8:16, 19; 18:6) Alevi ena anachita ntchito zotsika; ena analandira mwaŵi waukulu wa mautumiki, monga ngati kuphunzitsa malamulo a Mulungu. (Numeri 1:50, 51; 1 Mbiri 6:48; 23:3, 4, 24-32; 2 Mbiri 35:3-5) Tsopano tiyeni tichoke apa tipende anthu ena ‘opatsidwa’ ndi kufanana kwake kwa makono.
Aisrayeli Abwerako ku Babulo
4, 5. (a) Kodi ndi Aisrayeli otani emene anabwerera kuchokera ku ukapolo ku Babulo? (b) M’nthaŵi zamakono, kodi nchiyani chimene chimafanana ndi kubwerera kwa Aisrayeli kuchokera ku ukapolo?
4 Ezara ndi Nehemiya amasimba mmene Aisrayeli otsalira, otsogozedwa ndi Kazembe Zerubabele, anabwererera ku dziko lakwawo kuchokera ku Babulo, kukabwezeretsa kulambira kowona. Nkhani zonse ziŵiri zimasimba kuti obwerera ameneŵa anali okwanira 42,360. Zikwi za chiŵerengero chimenecho anali “amuna a anthu a Israyeli.” Chotsatira, nkhanizo zimatchula ansembe. Ndiyeno Alevi pafupifupi 350, kuphatikizapo Alevi oimba ndi odikira pachipata. Ezara ndi Nehemiya analembanso za zikwi zowonjezereka zomwe mwachiwonekere anali Aisrayeli, mwina ngakhale ansembe, koma omwe sanadziŵe bwino mzera wawo wobadwira.—Ezara 1:1, 2; 2:2-42, 59-64; Nehemiya 7:7-45, 61-66.
5 Aisrayeli otsalira ameneŵa otengedwa ku ukapolo amene pambuyo pake anabwerera ku Yerusalemu ndi Yuda anasonyeza kudzipatulira kwapadera kwa Mulungu ndi kudzipereka kwakuya ku kulambira kowona. Monga momwe kwasonyezedwera, timawona m’nthaŵi zamakono kufananako mwa otsalira a Israyeli wauzimu amene anatuluka muukapolo ku Babulo Wamkulu mu 1919.
6. Kodi Mulungu wagwiritsira ntchito motani Aisrayeli auzimu m’nthaŵi yathu?
6 Chiyambire kumasulidwa kwawo mu 1919, otsalira a abale a Kristu odzozedwa apita patsogolo mwachangu m’kulambira kowona. Yehova wadalitsa zoyesayesa zawo zakusonkhanitsa omalizira a 144,000 kupanga “Israyeli wa Mulungu.” (Agalatiya 6:16; Chivumbulutso 7:3, 4) Onse pamodzi, otsalira odzozedwa amapanga gulu la “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” limene likugwiritsiridwa ntchito kupereka chakudya chauzimu chokwanira chopatsa moyo, chimene agwira ntchito zolimba kuchigaŵira padziko lonse lapansi.—Mateyu 24:45-47.
7. Kodi ndani amene amagwirizana ndi odzozedwa m’kulambira kowona?
7 Monga momwe nkhani yapitayo inasonyezera, anthu a Yehova tsopano amaphatikizapo mamiliyoni a “nkhosa zina,” omwe ali ndi chiyembekezo choperekedwa ndi Mulungu chakupulumuka chisautso chachikulu chirinkudza posachedwapa. Iwo amafunadi kumtumikira Yehova kunthaŵi zomka muyaya padziko lapansi, pamene sadzamvanso njala kapena ludzu ndipamene sadzagwetsanso misozi ya chisoni. (Yohane 10:16; Chivumbulutso 7:9-17; 21:3-5) Kodi m’nkhani ya obwerako ku Babulo tikupezamo chirichonse chofanana ndi oterowo? Inde!
Nawonso Osakhala Aisrayeli Anabwerera
8. Kodi ndayani amene anatsagana ndi Aisrayeli pobwerera kuchokera ku Babulo?
8 Pamene chiitano chinaperekedwa chakuti okonda Yehova m’Babulo abwerere ku Dziko Lolonjezedwa, zikwi za osakhala Aisrayeli analabadira. Pa ndandanda zoperekedwa ndi Ezara ndi Nehemiya, timaŵerengapo za “Anetini” (kutanthauza, ‘Opatsidwa’) ndi “ana a akapolo a Solomo,” amene kuwaphatikiza pamodzi anakwanira 392. Nkhanizo zimatchulanso ena oposa 7,500: ‘akapolo aamuna ndi aakazi,’ limodzinso ndi ‘oimba aamuna ndi aakazi’ osakhala Alevi. (Ezara 2:43-58, 65; Nehemiya 7:46-60, 67) Kodi nchiyani chimene chinasonkhezera ambiri osakhala Aisrayeli kubwerera nawonso?
9. Kodi mzimu wa Mulungu unachita mbali yanji m’kubwerera kuchokera ku ukapolo?
9 Ezara 1:5 amalankhula za “onse amene Mulungu adzawautsira mzimu wawo akwere kukamanga nyumba ya Yehova.” Inde, Yehova anasonkhezera onse omwe anabwerera. Anasonkhezera mzimu wawo, ndiko kuti, kaimidwe ka maganizo awo. Ngakhale kuchokera kumwamba, Mulungu anakhoza kuchita zimenezi mwakugwiritsira ntchito mzimu wake woyera, mphamvu yake yogwira ntchito. Motero, onse omwe ‘anakwera kukamanga nyumba ya Yehova’ anathandizidwa ndi “mzimu” wa Mulungu.—Zekariya 4:1, 6; Hagai 1:14.
Kufanana Kwamakono
10, 11. Kodi pali kufanana kotani ndi osakhala Aisrayeli omwe anabwerera kuchokera ku Babulo?
10 Kodi ndani amene akuchitiridwa chithunzi ndi obwerera amenewo osakhala Aisrayeli? Akristu ambiri angayankhe kuti: ‘Anetini anaimira “nkhosa zina” za lerolino.’ Nzowona, koma sanali Anetini okha; popeza kuti osakhala Aisrayeli onse omwe anabwerera akuimira Akristu lerolino omwe sali a Israyeli wauzimu.
11 Bukhu lakuti You May Survive Armageddon Into God’s New Worlda linanena kuti: “Otsalira a Israyeli okwanira 42,360 ndi kazembe Zerubabele sanali okhawo amene anasiya Babulo . . . Panali zikwi za osakhala Aisrayeli . . . Kupatulapo Anetini, analipo ena osakhala Aisrayeli, akapolo, akatswiri oimba aamuna ndi aakazi ndi mbadwa za ana a akapolo a Mfumu Solomo.” Bukhulo linalongosola kuti: “Anetini, akapolo, oimba ndi ana a akapolo a Solomo, onsewo osakhala Aisrayeli, anachoka m’dziko laukapolo ndi kubwerera pamodzi ndi otsalira a Israyeli . . . Choncho kodi nkoyenera kulingalira kuti lerolino anthu a mitundu yosiyanasiyana omwe sali Aisrayeli auzimu amagwirizana ndi otsalira a Israyeli wauzimu ndi kupititsa patsogolo kulambira Yehova Mulungu? Inde.” Oterowo ‘akhala Anetini ophiphitsiridwa, oimba, ndi ana a akapolo a Solomo amakono.’
12. Kodi Mulungu amagwiritsira ntchito motani mzimu wake mwanjira yapadera kwa Aisrayeli auzimu, koma nchifukwa ninji tingakhale otsimikiza kuti ukhoza kuperekedwa kwa olambira ake onse?
12 Monga momwe zidaliri m’chitsanzo chakalecho, Mulungu amaperekanso mzimu wake kwa okhala ndi chiyembekezo chakukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi. Kunena zowona, iwo samabadwanso. Aliyense wa a 144,000 amabadwanso kamodzi kokha monga mwana wa Mulungu ndi kudzozedwa ndi mzimu woyera. (Yohane 3:3, 5; Aroma 8:16; Aefeso 1:13, 14) Ndithudi, kudzoza kumeneko kuli chisonyezero chapadera cha mzimu wa Mulungu kaamba ka kagulu ka nkhosa. Koma mzimu wa Mulungu umafunikiranso kaamba ka kuchita chifuniro chake. Motero, Yesu anati: ‘Atate wanu wakumwamba adzapatsa mzimu woyera kwa iwo akupempha iye.’ (Luka 11:13) Kaya wopempheyo ali ndi chiyembekezo chakumwamba kapena ali wa nkhosa zina, mzimu wa Yehova ulipo wochuluka wochitira chifuniro Chake.
13. Kodi ndimotani mmene mzimu ungagwirire ntchito kwa atumiki onse a Mulungu?
13 Mzimu wa Mulungu unasonkhezera ponse paŵiri Aisrayeli ndi osakhala Aisrayeli kubwerera ku Yerusalemu, ndipo umalimbitsa ndi kuthandiza anthu ake onse okhulupirika lerolino. Kaya ngati Mkristu ali ndi chiyembekezo choperekedwa ndi Mulungu cha moyo wakumwamba kapena moyo wapadziko lapansi, iye ayenera kulalikira mbiri yabwino, ndipo mzimu woyera umamkhozetsa kukhala wokhulupirika m’zimenezo. Aliyense wa ife—kaya chiyembekezo chathu nchotani—ayenera kukulitsa zipatso za mzimu, zimene tonsefe timazifunikira pamlingo wokwanira.—Agalatiya 5:22-26.
Opatsidwa Kaamba ka Utumiki Wapadera
14, 15. (a) Pakati pa osakhala Aisrayeli amene anabwerera, kodi ndi magulu aŵiri ati omwe anatchulidwa? (b) Kodi Anetini anali ayani, ndipo anachita ntchito yanji?
14 Pakati pa zikwi za osakhala Aisrayeli amene mzimu unasonkhezera kubwerera panali magulu aŵiri aang’ono amene Mawu a Mulungu amawatchula—Anetini ndi ana a akapolo a Solomo. Kodi iwo anali ayani? Kodi anachita ntchito yanji? Ndipo kodi zimenezi ziyenera kutanthauzanji lerolino?
15 Anetini anali gulu la anthu amene sanali mbadwa za Israyeli omwe anapatsidwa mwaŵi wakutumikira pamodzi ndi Alevi. Kumbukirani Akanani a ku Gibeoni omwe anakhala ‘otema nkhuni ndi otungira madzi msonkhanowo ndi guwa la Yehova.’ (Yoswa 9:27) Mwinamwake ena a mbadwa zawo anali pakati pa Anetini omwe anabwerera kuchokera ku Babulo, pamodzi ndi ena omwe anaphatikizidwapo monga Anetini mkati mwa ulamuliro wa Davide ndi panthaŵi zina. (Ezra 8:20) Kodi Anetini anachita ntchito yanji? Alevi anagaŵiridwa kuthandiza ansembe, ndipo pambuyo pake Anetini anagaŵiridwa kuthandiza Alevi. Mwaŵi umenewu unaperekedwa ngakhale kwa alendo odulidwa.
16. Kodi ndimotani mmene malo a Anetini anasinthira mkupita kwa nthaŵi?
16 Pamene gululo linabwerera kuchokera ku Babulo, lidali ndi Alevi ochepa, poyerekezera ndi ansembe kapena Anetini ndi “ana a akapolo a Solomo.” (Ezara 8:15-20) Dictionary of the Bible, yolembedwa ndi Dr. James Hastings, imati: “Tikupeza kuti pambuyo panthaŵi yakutiyakuti [Anetini] anakhazikika kotheratu monga gulu la nduna zopatulika, namalandira mwaŵi wa mautumiki.” Magazini aukatswiri otchedwa Vetus Testamentum amati: “Panakhala kusintha. Atabwerako ku Ukapolo, [alendo] ameneŵa sanawonedwenso monga akapolo a m’Kachisi, koma monga atumiki a m’menemo, nakhala ndi malo monga a mabungwe ena, omwe anatsogolera m’Kachisi.”—Onani bokosi lakuti “Kusintha Malo.”
17. Kodi nchifukwa ninji Anetini analandira zambiri zochita, ndipo kodi pali umboni wa Baibulo wotani wa zimenezi?
17 Ndithudi, Anetini sanalingane ndi ansembe ndi Alevi. Magulu enaŵa anali Aisrayeli, omwe anasankhidwa ndi Yehova iyemwini ndi osafunika kulandidwa malo ndi osakhala Aisrayeli. Komabe, Baibulo limasonyeza kuti chifukwa cha kuchepa kwa Alevi, Anetini anawonjezeredwa ntchito muutumiki wa Mulungu. Anapatsidwa nyumba zokhala pafupi ndi kachisi. M’tsiku la Nehemiya, iwo anagwira ntchito pamodzi ndi ansembe m’kukonzanso malinga a Yerusalemu. (Nehemiya 3:22-26) Ndipo mfumu ya Peresiya inalamula kuti Anetini apatulidwe pakukhoma msonkho, monga momwe Alevi anapatulidwira chifukwa cha utumiki wawo wapakachisi. (Ezara 7:24) Izi zimasonyeza mmene ‘opatsidwa’ ameneŵa (Alevi ndi Anetini) analiri ogwirizana m’nkhani zauzimu ndi mmene ntchito za Anetini zinawonjezeredwa malinga ndi kusoŵa, ngakhale kuti sanawonedwe konse monga Alevi. Pamene Ezara pambuyo pake anasonkhanitsa okhala muukapolo kuti abwerere, poyamba panalibe Mlevi aliyense pakati pawo. Chotero iye anayesayesa mokulira kuti asonkhanitse ena a iwo. Ndipo panakhala Alevi 38 ndi Anetini 220 omwe anabwerera kukatumikira monga “otumikira za nyumba ya Mulungu wanthu.”—Ezara 8:15-20.
18. Kodi ana a akapolo a Solomo ayenera kuti anachita ntchito yanji?
18 Gulu lina lotchulidwa la osakhala Aisrayeli linali la ana a akapolo a Solomo. Baibulo silimafotokoza zambiri ponena za iwo. Ena anali “ana a Sofereti.” Ezara akuikako liwu lotsimikizira ku dzinalo, kukhala Has·so·pheʹreth, lothekera kutanthauza “mlembiyo.” (Ezara 2:55; Nehemiya 7:57) Chotero iwo mwina anali bungwe la alembi kapena ojambula, kwenikweni alembi apakachisi kapena oyendetsa ntchito. Ngakhale kuti anali mbadwa zachilendo, ana a akapolo a Solomo anatsimikizira kudzipereka kwawo kwa Yehova mwakuchoka m’Babulo ndi kubwerera kukakhala ndi phande m’kubwezeretsa kulambira Kwake.
Kudzipereka Ife Eni Lerolino
19. Kodi pali unasi wotani lerolino pakati pa odzozedwa ndi nkhosa zina?
19 M’nthaŵi yathu, Mulungu wagwiritsira ntchito kwambiri otsalira odzozedwa m’kufalitsa kulambira kowona ndi kulengeza mbiri yabwino. (Marko 13:10) Ha, iwo akhala ndi chimwemwe chotani nanga kuwona zikwi makumi ambiri, zikwi mazana ambiri, ndiyeno mamiliyoni a nkhosa zina akugwirizana nawo m’kulambira! Ndipo pakhala kugwirizana kosangalatsa kotani nanga pakati pa otsalira ndi nkhosa zina!—Yohane 10:16.
20. Kodi ndikalongosoledwe katsopano komveka kotani ponena za kufanana ndi Anetini ndi ana a akapolo a Solomo? (Miyambo 4:18)
20 Onse osakhala Aisrayeli omwe anabwerera kuchokera ku ukapolo m’Babulo wakale amafanana ndi nkhosa zina zimene tsopano zikutumikira ndi otsalira a Israyeli wauzimu. Ngakhale ndi choncho, kodi nchifukwa ninji Baibulo lingotchula Anetini ndi ana a akapolo a Solomo? M’chitsanzocho, tikuwona kuti Anetini ndi ana a akapolo a Solomo anapatsidwa mwaŵi wa mautimiki oposa a obwerera ena osakhala Aisrayeli. Izi ziyenera kukhala zinachitira chithunzi kuti Mulungu lerolino wapereka mwaŵi ndi ntchito zowonjezereka kwa nkhosa zina zofikapo ndi zofunitsitsa.
21. Kodi ndimotani mmene abale ena okhala ndi chiyembekezo chapadziko lapansi alandirira ntchito zowonjezereka ndi mathayo?
21 Mwaŵi wowonjezereka wa Anetini unali wochita mwachindunji ndi ntchito zauzimu. Ana a akapolo a Solomo mwachiwonekere analandira mathayo auyang’aniro. Mofananamo lerolino, Yehova wadalitsa anthu ake ndi “mphatso mwa amuna” zakusamalira zosoŵa zawo. (Aefeso 4:8, 11, 12, NW) Ophatikizidwa m’mphatso zimenezi ndiwo mazana ambiri a abale, ofikapo ndi ozoloŵera amene akukhala ndi phande ‘m’kuweta nkhosa,’ akutumikira monga oyang’anira dera ndi chigawo ndi m’Makomiti Anthambi m’nthambi zokwanira 98 za Watch Tower Society. (Yesaya 61:5) Pamalikulu a dziko lonse a Sosaite, pansi pa chitsogozo cha “mdindo wokhulupirika” ndi Bungwe lake Lolamulira, amuna okhoza amaphunzitsidwa kuthandiza kukonza chakudya chauzimu. (Luka 12:42) Antchito odzifunira achiyambakale aphunzitsidwa kuyendetsa nyumba za Beteli ndi mafakitale ndi kuyang’anira maprogramu apadziko lonse akumanga nthambi zatsopano ndi maholo a kulambira kwa Chikristu. Iwo apambanadi m’kutumikira monga othandiza a otsalira odzozedwa, amene amapanga mbali ya ansembe achifumu.—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 4:17; 14:40; 1 Petro 2:9.
22. Kodi nchifukwa ninji kuli koyenera kuti ena a nkhosa zina apatsidwe mathayo okulirapo tsopano, ndipo kodi tiyenera kulabadira motani ku zimenezi?
22 M’nthaŵi zakale, ansembe ndi Alevi anapitiriza kutumikira pakati pa Ayuda. (Yohane 1:19) Komabe, lerolino otsalira a Israyeli wauzimu padziko lapansi ayenera kupitirizabe kucheperachepera. (Siyanitsani ndi Yohane 3:30.) Pomalizira pake, pambuyo pa kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu, a 144,000 onse ‘osindikizidwa chizindikiro’ adzakhala kumwamba kaamba ka ukwati wa Mwanawankhosa. (Chivumbulutso 7:1-3; 19:1-8) Koma tsopano nkhosa zina ziyenera kumkabe niziwonjezereka. Chenicheni chakuti ena a iwo, kuyerekezera ndi Anetini ndi ana a akapolo a Solomo, tsopano akugaŵiridwa mathayo olemera pansi pa chiyang’aniro cha otsalira odzozedwa sichimawapangitsa kudzitama kapena kudzikweza. (Aroma 12:3) Ichi chimatipatsa chidaliro chakuti pamene anthu a Mulungu ‘akutuluka m’chisautso chachikulu,’ padzakhala amuna achidziŵitso—“akalonga”—okonzekeretsedwa kutsogolera pakati pa nkhosa zina.—Chivumbulutso 7:14; Yesaya 32:1; yerekezerani ndi Machitidwe 6:2-7.
23. Kodi nchifukwa ninji tonsefe tiyenera kukulitsa mzimu wakupatsa ponena za utumiki wa Mulungu?
23 Onse amene anabwerako ku Babulo anali ofunitsitsa kugwira ntchito zolimba ndi kutsimikizira kuti anaika maganizo awo onse ndi mtima pakulambiridwa kwa Yehova. Zirinso choncho ndi lerolino. Pamodzi ndi otsalira odzozedwa, ‘alendo . . . akuimirira ndi kudyetsa magulu.’ (Yesaya 61:5) Chotero, mosasamala kanthu ndi chiyembekezo choperekedwa ndi Mulungu chimene tiri nacho, ndipo mosasamala kanthu ndi mwaŵi wautumiki umene akulu oikidwa ndi mzimu angapatsidwe tsiku la kulemekezedwa kwa Yehova lisanafike pa Armagedo, tonsefe tikulitsetu mzimu wakupanda dyera, waubwino ndi wakupatsa. Ngakhale kuti sitingambwezere Yehova kaamba ka mapindu aakulu ambirimbiri, tiyeni tikhaletu a mtima wonse m’kalikonse kamene tikachita m’gulu lake. (Salmo 116:12-14; Akolose 3:23) Chotero tonsefe tingadzipereke tokha ku kulambira kowona, pamene nkhosa zina zikutumikira mwathithithi ndi odzozedwa, omwe ‘adzachita ufumu padziko.’—Chivumbulutso 5:9, 10.
[Mawu a M’munsi]
a Masamba 142-8; lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Mfundo Zofunika Kuzikumbukira
◻ Kodi ndimotani mmene Alevi analiri ‘opatsidwa’ mu Israyeli wakale?
◻ Kodi ndi osakhala Aisrayeli otani amene anabwerera kuchokera ku ukapolo, akuchitira ndani chithunzi?
◻ Kodi ndikusintha kotani kumene kukuwonekera kuti kunachitika kwa Anetini?
◻ Ponena za Anetini ndi ana a akapolo a Solomo, kodi ndikufanana kotani kumene tsopano kwazindikiridwa?
◻ Kodi kugwirizana kwa odzozedwa ndi nkhosa zina kumapereka chidaliro chotani?
[Bokosi patsamba 14]
KUSINTHA MALO
Ambiri a madikishonale a Baibulo ndi mabuku anazonse amathirira ndemanga pamasinthidwe omwe anachitika kwa ena osakhala Aisrayeli omwe anabwerera kuchokera ku ukapolo. Mwachitsanzo, pansi pamutu wakuti “Kusintha kwa Malo awo,” Encyclopædia Biblica imanena kuti: “Malo awo m’chitaganya, monga kwasonyezedwa kale, anakwezedwa mofunikira. [Anetini] sanalinso akapolo malinga ndi tanthauzo lenileni la liwulo.” (Yokonzedwa ndi Cheyne ndi Black, Volyumu III, tsamba 3399) Mu The Cyclopædia of Biblical Literature, John Kitto analemba kuti: “Sikunayembekezeredwe kuti ambiri a iwo [Anetini] akabwerera pamalo otsika ameneŵa mu Palesitina . . . Kudzipereka kodzifunira kosonyezedwa ndi anthuŵa kunakweza mokulira malo a Anetini.” (Volyumu II, tsamba 417) The International Standard Bible Encyclopedia imati: “Polingalira za kugwirizana kumeneku ndi mbiri yawo m’nyengo ya Solomo, tikhoza kulingalira kuti akapolo a Solomo adali ndi mathayo aakulu m’kachisi wachiŵiri.”—Lokonzedwa ndi G. W. Bromiley, Volyumu 4, tsamba 570.
[Chithunzi patsamba 15]
Pamene Aisrayeli anabwerera kukamanganso Yerusalemu, zikwi za osakhala Aisrayeli anatsagana nawo
[Mawu a Chithunzi]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Chithunzi patsamba 17]
Komiti ya Nthambi mu Korea. Monga momwe Anetini akale anachitira, amuna ankhosa zina ali ndi mathayo okulirapo m’kulambira kowona lerolino