Ekisodo
19 Mʼmwezi wachitatu kuchokera pamene Aisiraeli anatuluka mʼdziko la Iguputo, tsiku lomwelo* iwo analowa mʼchipululu cha Sinai. 2 Ananyamuka ku Refidimu+ nʼkulowa mʼchipululu cha Sinai ndipo anamanga msasa wawo mʼchipululumo. Aisiraeli anamanga msasawo pafupi ndi phiri la Sinai.+
3 Kenako Mose anakwera mʼphirimo kukaonekera kwa Mulungu woona.+ Ndipo Yehova analankhula naye mʼphirimo kuti: “Ukanene mawu awa kunyumba ya Yakobo kapena kuti kwa Aisiraeli, 4 ‘Inu munaona nokha zimene ndinachitira Aiguputo,+ kuti ndikunyamuleni pamapiko a chiwombankhanga nʼkukubweretsani kwa ine.+ 5 Tsopano mukadzamvera mawu anga mosamala ndi kusunga pangano langa, mudzakhaladi chuma changa chapadera pa anthu onse,+ chifukwa dziko lonse lapansi ndi langa.+ 6 Inuyo mudzakhala ufumu wanga wa ansembe komanso mtundu wanga woyera.’+ Ukanene mawu amenewa kwa Aisiraeli.”
7 Choncho Mose anatsika ndipo anaitanitsa akulu onse a anthu nʼkuwauza mawu onse amene Yehova anamulamula.+ 8 Kenako anthu onse anayankhira pamodzi kuti: “Zonse zimene Yehova wanena tidzachita zomwezo.”+ Nthawi yomweyo Mose anabwerera kwa Yehova nʼkukamuuza zimene anthuwo anayankha. 9 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Tamvera! Ndibwera kwa iwe mumtambo wakuda kuti anthu azimva ndikamalankhula nawe komanso kuti azikukhulupirira nthawi zonse.” Apa nʼkuti Mose atanena mawu a anthuwo kwa Yehova.
10 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Pita kwa anthu, ukawayeretse lero ndi mawa ndipo achape zovala zawo. 11 Pa tsiku lachitatu adzakhale okonzeka, chifukwa pa tsiku lachitatulo Yehova adzabwera paphiri la Sinai pamaso pa anthu onse. 12 Anthuwo uwaikire malire kuzungulira phiri lonse nʼkuwauza kuti, ‘Samalani kuti musakwere mʼphiri kapena kukhudza mʼmunsi mwake. Aliyense wokhudza phirili adzaphedwa ndithu. 13 Munthu aliyense asadzakhudze wolakwayo, koma adzaponyedwe miyala kapena kulasidwa.* Kaya ndi nyama kapena munthu, adzaphedwa.’+ Koma lipenga la nyanga ya nkhosa likadzalira,+ anthu onse adzayandikire phirilo.”
14 Ndiyeno Mose anatsika mʼphirimo kupita kwa anthu nʼkuyamba kuwayeretsa ndipo iwo anachapa zovala zawo.+ 15 Iye anauza anthuwo kuti: “Pofika tsiku lachitatu mukhale okonzeka. Amuna asagone ndi akazi awo.”*
16 Pa tsiku lachitatu mʼmawa, kunachita mabingu ndi mphezi ndipo mtambo wakuda+ unakuta phiri. Kunamvekanso kulira kwamphamvu kwambiri kwa lipenga la nyanga ya nkhosa, moti anthu onse mumsasawo anayamba kunjenjemera.+ 17 Zitatero Mose anatulutsa anthuwo mumsasa kuti akaime pamaso pa Mulungu woona, ndipo anaima mʼmunsi mwa phirilo. 18 Phiri la Sinai linafuka utsi paliponse, chifukwa chakuti Yehova anabwera paphiripo mʼmoto.+ Utsi wakewo unkakwera kumwamba ngati utsi wa uvuni ndipo phiri lonse linkanjenjemera kwambiri.+ 19 Pamene kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosako kunkapitiriza kukwera, Mose analankhula ndipo Mulungu woona anamuyankha.
20 Choncho Yehova anafika pamwamba pa phiri la Sinai. Kenako Yehova anaitana Mose kuti akwere pamwamba pa phirilo ndipo Mose anakweradi.+ 21 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Tsika ukachenjeze anthuwo kuti asayese kudumpha malire kufika kwa Yehova kuti amuone, chifukwa onse ochita zimenezi adzafa. 22 Ndipo ansembe amene amayandikira kwa Yehova kawirikawiri adziyeretse, kuti Yehova asawaphe.”+ 23 Kenako Mose anauza Yehova kuti: “Anthuwa sangafike paphiri la Sinai, chifukwa inu munawachenjeza kale pamene munandiuza kuti: ‘Udule malire kuzungulira phiri ndipo muziliona kuti ndi lopatulika.’”+ 24 Koma Yehova anamuuza kuti: “Tsika, ndipo ukabwerenso limodzi ndi Aroni. Koma ansembe ndiponso anthu asadumphe malire nʼkukwera kwa Yehova kuti asawaphe.”+ 25 Choncho Mose anatsika nʼkupita kwa anthuwo ndipo anawauza zonsezi.